NYIMBO 105
“Mulungu Ndi Chikondi”
Losindikizidwa
1. Mulungu ndi wachikondi ndiye
Tiyende naye.
Tikonde M’lungu ndi anthu.
Tizichita zabwino.
Tidzasangalala ndithu,
Tidzapezanso moyo.
Tizisonyeza chikondi
Ngati cha Yesu Khristu.
2. Tikakonda choonadi
Tidzachita zabwino.
Tikalakwitsa ndi kugwa
M’lungu amatidzutsa.
Chikondi chilibe nsanje
Ndipo chimapirira.
Tikamakonda anzathu
Tidzadalitsidwadi.
3. Musalole kuti mkwiyo
Ukulamulireni.
Khulupirirani M’lungu,
Adzakuphunzitsani
Kukonda M’lungu ndi anthu.
N’chikondi chenicheni.
Tizisonyeza anzathu
Chikondi cha Mulungu.
(Onaninso Maliko 12:30, 31; 1 Akor. 12:31–13:8; 1 Yoh. 3:23.)