NYIMBO 116
Kukoma Mtima Ndi Kofunika Kwambiri
Losindikizidwa
1. Tikukutamandani Yehova,
Mwatipatsa Mawu.
Taona nzeru zanu zakuya
Ndi kukoma mtima kwanu.
2. Yesu akuuza ovutika
Apite kwa iye.
Akanyamule goli lakelo
Kuti atsitsimulidwe.
3. Mulungu wathu ndi Mwana wake
Ndi okoma mtima.
Nafe tikhale okoma mtima.
Tizilimbikitsa ena.
(Onaninso Mika 6:8; Mat. 11:28-30; Akol. 3:12; 1 Pet. 2:3.)