NYIMBO 118
“Tiwonjezereni Chikhulupiriro”
Losindikizidwa
1. Yehova ndifedi anthu ochimwa,
Mtima wathu umatipusitsa.
Pali tchimo lomwe limatikola,
Kuchepa kwa chikhulupiriro.
(KOLASI)
Mulungu wathu tiwonjezereni
Chikhulupiriro chilimbedi.
Mwa chifundo chanu mutithandize
Tikulemekezeni mu zonse.
2. Ngati sitikukhulupirirani
Sitingakusangalatsenidi.
Chikhulupiriro chimateteza
Ndipo chimatilimbitsa mtima.
(KOLASI)
Mulungu wathu tiwonjezereni
Chikhulupiriro chilimbedi.
Mwa chifundo chanu mutithandize
Tikulemekezeni mu zonse.
(Onaninso Gen. 8:21; Aheb. 11:6; 12:1.)