NYIMBO 145
Mulungu Watilonjeza Paradaiso
Losindikizidwa
1. M’lungu wathu watilonjeza
Madalitso posachedwa.
Adzachotsa uchimo, imfa,
Misozi ndi zopweteka.
(KOLASI)
Ndiye tidikirirebe
Ndipo tikhulupirire.
Khristu adzakwaniritsa
Chifuniro cha Mulungu.
2. Cholinga cha Mulungu n’choti
Adzaukitse akufa.
‘Udzakhala m’Paradaiso,’
N’zomwe Yesu ananena.
(KOLASI)
Ndiye tidikirirebe
Ndipo tikhulupirire.
Khristu adzakwaniritsa
Chifuniro cha Mulungu.
3. Tidzakhala m’Paradaiso,
Yesu ndiye Mfumu yathu.
Tithokoze Atate wathu
Kuchokera mumtimamu.
(KOLASI)
Ndiye tidikirirebe
Ndipo tikhulupirire.
Khristu adzakwaniritsa
Chifuniro cha Mulungu.
(Onaninso Mat. 5:5; 6:10; Yoh. 5:28, 29.)