PHUNZIRO 08
Yehova Akhoza Kukhala Mnzanu
Yehova akufuna kuti mumudziwe bwino. Chifukwa chiyani? Amaona kuti mukadziwa bwino makhalidwe ake, mmene amachitira zinthu komanso cholinga chake mungafunitsitse kukhala mnzake. Koma kodi mukuona kuti n’zothekadi kuti inuyo mukhale mnzake wa Mulungu? (Werengani Salimo 25:14.) Kodi mungatani kuti mukhale mnzake wa Mulungu? Baibulo limayankha mafunso amenewa ndipo limasonyeza kuti kukhala mnzake wa Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kugwirizana ndi munthu wina aliyense.
1. Kodi Yehova akukupemphani kuti muchite chiyani?
Baibulo limanena kuti “Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobo 4:8) Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani? Yehova akukupemphani kuti mukhale mnzake. Anthu ena amaona kuti n’zosatheka kuti Mulungu akhale mnzawo chifukwa sangathe kumuona. Koma m’Baibulo, Yehova amafotokoza zonse zotithandiza kuti tidziwe makhalidwe ake n’cholinga choti tikhale anzake. Tikamawerenga uthenga umene Yehova watipatsa m’Baibulo, ubwenzi wathu ndi iye umalimba kwambiri ngakhale kuti sitinamuonepo.
2. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova akhoza kukhala Mnzanu wabwino kwambiri kuposa wina aliyense?
Tikutero chifukwa chakuti Yehova amakukondani kwambiri kuposa munthu wina aliyense. Iye amafuna kuti muzisangalala ndiponso kuti muzipemphera kwa iye nthawi zonse mukakumana ndi mavuto. Baibulo limati muzimutulira “nkhawa zanu zonse, chifukwa amakufunirani zabwino.” (1 Petulo 5:7) Yehova ndi wokonzeka kuthandiza, kutonthoza ndiponso kumvetsera anzake akamalankhula.—Werengani Salimo 94:18, 19.
3. Kodi Yehova amafuna kuti anzake azichita chiyani?
N’zoona kuti Yehova amakonda anthu onse, “koma anthu owongoka mtima [ndi amene] amakhala nawo pa ubwenzi wolimba.” (Miyambo 3:32) Yehova amafuna kuti anzake aziyesetsa kuchita zinthu zimene iye amaziona kuti ndi zabwino, n’kumapewa zinthu zimene iye amaziona kuti n’zoipa. Anthu ena amaona kuti sangakwanitse kuchita zinthu zonse zimene Yehova amafuna komanso kupeweratu zoipa zonse. Koma Yehova ndi Mulungu wachifundo. Iye amalola kuti munthu aliyense amene amamukonda ndi mtima wonse komanso amene amayesetsa kuchita zinthu zomusangalatsa akhale mnzake.—Salimo 147:11; Machitidwe 10:34, 35.
FUFUZANI MOZAMA
Onani zina zimene mungachite kuti Yehova akhale mnzanu ndiponso chifukwa chake iye angakhale Mnzanu wabwino kwambiri kuposa wina aliyense.
4. Abulahamu anali mnzake wa Yehova
Nkhani ya m’Baibulo yokhudza Abulahamu (yemwe ankadziwikanso kuti Abulamu) imatithandiza kudziwa zimene zimafunika kuti munthu akhale mnzake wa Mulungu. Werengani nkhani ya Abulahamu pa Genesis 12:1-4. Kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi Yehova anauza Abulahamu kuti achite chiyani Abulahamu?
Kodi Yehova anamulonjeza chiyani?
Kodi Abulahamu anachita chiyani atamva malangizo a Yehova?
5. Zimene Yehova amafuna kuti anzake azichita
Nthawi zambiri timafuna kuti anzathu azichita zinthu zinazake.
Kodi inuyo mumafuna kuti anzanu azikuchitirani zinthu ziti?
Werengani 1 Yohane 5:3, kenako mukambirane funso ili:
Kodi Yehova amafuna kuti anzake azichita chiyani?
Kuti timvere Yehova, tingafunike kusintha zinthu zina zimene timachita kapena khalidwe lathu. Werengani Yesaya 48:17, 18, kenako mukambirane funso ili:
N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti anzake asinthe zinthu zina?
Mnzathu wabwino amatiuza zinthu zimene zingatiteteze komanso kutithandiza. Yehova amachitanso chimodzimodzi kwa anzake
6. Zimene Yehova amachita kuti athandize anzake
Yehova amathandiza anzake kupirira mavuto. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso ili:
Muvidiyoyi, kodi Yehova anathandiza bwanji mayi wina kulimbana ndi maganizo oipa?
Werengani Yesaya 41:10, 13, kenako mukambirane mafunso otsatirawa:
Kodi Yehova akulonjeza kuti adzawachitira chiyani anzake onse?
Kodi mukuganiza kuti Yehova akhoza kukhala Mnzanu wabwino? N’chifukwa chiyani mukutero?
Anzanu apamtima amakuthandizani mukafunika thandizo. Nayenso Yehova adzakuthandizani
7. Kuti Yehova akhale mnzathu, tiyenera kulankhulana
Kulankhulana kumalimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Werengani Salimo 86:6, 11, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi tingalankhule bwanji ndi Yehova?
Kodi Yehova amalankhula nafe bwanji?
Timalankhula ndi Yehova m’pemphero; iye amalankhula nafe kudzera m’Baibulo
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “N’zosatheka kukhala mnzake wa Mulungu.”
Kodi mungagwiritse ntchito lemba liti posonyeza kuti n’zotheka kukhala mnzake wa Yehova?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Yehova akufuna kuti mukhale Mnzake, ndipo iye akuthandizani kuchita zimenezi.
Kubwereza
Kodi Yehova amathandiza bwanji anzake?
N’chifukwa chiyani Yehova amauza anzake kuti asinthe zinthu zina?
Kodi mukuganiza kuti Yehova amafuna kuti anzake azichita zinthu zomwe sangakwanitse? N’chifukwa chiyani mukutero?
ONANI ZINANSO
Kodi kukhala mnzake wa Mulungu kungakuthandizeni bwanji?
“Yehova Ndiye Mulungu Wofunika Kum’dziwa” (Nsanja ya Olonda, February 15, 2003)
Onani zimene mungachite kuti Mulungu akhale mnzanu.
Onani chifukwa chake mayi wina amaona kuti kukhala mnzake wa Yehova kunapulumutsa moyo wake.
Mvetserani pamene achinyamata akufotokoza mmene amaonera Yehova.