Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lmd phunziro 5
  • Kulankhula Mwaluso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulankhula Mwaluso
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Paulo Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Paulo
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Paulo
  • ‘Funafunani Mulungu ndi Kumupezadi’
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
  • Kudzichepetsa
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Kodi Anthu Am’gawo Lanu Mumawaona Bwanji?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Nkwandani Komwe Tingayang’ane Kaamba ka Chilungamo Chowona?
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd phunziro 5

ULENDO WOYAMBA

Mtumwi Paulo akukambirana ndi anthu a ku Atene.

Machitidwe 17:22, 23

PHUNZIRO 5

Kulankhula Mwaluso

Mfundo yaikulu: “Mawu anu azisonyeza kuti ndinu okoma mtima.”​—Akol. 4:6.

Zomwe Paulo Anachita

Mtumwi Paulo akukambirana ndi anthu a ku Atene.

VIDIYO: Paulo Analalikira Anthu a ku Atene

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Machitidwe 17:22, 23. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi Paulo anamva bwanji ataona miyambo ya chipembedzo chonyenga ku Atene?​—Onani Machitidwe 17:16.

  2. M’malo mowadzudzula, kodi Paulo anagwiritsa ntchito bwanji zomwe anthuwa ankakhulupirira kuti akwanitse kuwalalikira?

Zomwe Tikuphunzira kwa Paulo

2. Tikamasankha bwino zoti tilankhule, mmene tingazilankhulire komanso nthawi yoti tizilankhule, tidzathandiza anthu kufunitsitsa kumvetsera uthenga wathu.

Zomwe Mungachite Potsanzira Paulo

3. Muzisankha mawu mosamala. Mwachitsanzo, polankhula ndi munthu amene si Mkhristu, muyenera kusankha mawu abwino mukamanena za Baibulo kapena zokhudza Yesu.

4. Musamamudule mawu. M’patseni mpata wolankhula za kumtima kwake. Ngati atalankhula zina zake zomwe sizikugwirizana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa, musamutsutse. (Yak. 1:19) Mukamamumvetsera pomwe akulankhula, ndi pamene mumamvetsa bwino maganizo ake.​—Miy. 20:5.

5. Muzivomerezana naye komanso kumuyamikira pa mfundo zina. Akhoza kukhala wotsimikiza kuti zomwe chipembedzo chake chimakhulupirira ndi zolondola. Yambani ndi kukambirana zinthu zomwe mungagwirizane. Pomwe nthawi ikupita mungamuthandize kumvetsa mfundo zina za m’Baibulo.

ONANINSO MALEMBA AWA

Miy. 25:15; 2 Tim. 2:23-26; 1 Pet. 3:15

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena