Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lmd phunziro 8
  • Kuleza Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuleza Mtima
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Yesu Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
  • Pitirizani Kukhala Oleza Mtima
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kugwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2016
  • Zimene Tingachite Kuti Nsembe ya Yesu Izitithandiza
    Nkhani Zina
  • Kuchita Chidwi ndi Anthu
    Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd phunziro 8

ULENDO WOBWEREZA

Yesu wakumana ndi mchimwene wake Yakobo mushopu yopalira matabwa ndipo Yakobo akudabwa pomuona.

Yohane 7:3-5; 1 Akor. 15:3, 4, 7

PHUNZIRO 8

Kuleza Mtima

Mfundo yaikulu: “Chikondi n’choleza mtima.”​—1 Akor. 13:4.

Zomwe Yesu Anachita

Yesu wakumana ndi mchimwene wake Yakobo mushopu yopalira matabwa ndipo Yakobo akudabwa pomuona.

VIDIYO: Yesu Anathandiza Mchimwene Wake Moleza Mtima

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Yohane 7:3-5 ndi 1 Akorinto 15:3, 4, 7. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi poyamba azichimwene ake a Yesu ankalandira bwanji uthenga wake?

  2. Tikutsimikiza bwanji kuti Yesu sanamugwere ulesi mchimwene wake Yakobo?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Tiyenera kukhala oleza mtima chifukwa anthu ena zimawatengera nthawi yaitali kuti alandire uthenga wabwino.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muziyesa njira ina. Ngati munthu sakuvomereza mwamsanga kuti muziphunzira naye, musamukakamize. Ngati ndi zotheka, mungamuonetse mavidiyo kapena kukambirana naye nkhani za m’mabuku athu pofuna kumuthandiza kudziwa mmene phunziro la Baibulo limachitikira komanso mmene angapindulire.

4. Musamamuyerekezere ndi munthu wina. Anthu amasiyana. Ngati wachibale kapena amene tinamulalikirapo nthawi ina akuzengereza kuti tiyambe kuphunzira naye, ganizirani chomwe chikuchititsa zimenezi. Kodi amakonda mwambo winawake wachipembedzo? Kodi akunyozedwa ndi achibale kapenanso anzake? M’patseni mpata woganizira zomwe mwamuuza kuti aone yekha ubwino wotsatira mfundo za m’Baibulo.

5. Muzimupempherera. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi luso komanso kuti musagwe ulesi. Mupempheni kuti akupatseni nzeru kuti muthe kuzindikira ngati munthuyo alibe chidwi kuti musiye kumuyendera.​—1 Akor. 9:26.

ONANINSO MALEMBA AWA

Maliko 4:26-28; 1 Akor. 3:5-9; 2 Pet. 3:9

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena