Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lmd phunziro 12
  • Kulangiza Molimba Mtima

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulangiza Molimba Mtima
  • Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Yesu Anachita
  • Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu
  • Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu
  • Muzithandiza Wophunzira Baibulo Kuti Abatizidwe
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 2
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
  • ‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzira Anga’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Muzikonda Anthu—Muziwaphunzitsa
lmd phunziro 12

KUPHUNZITSA ANTHU

Yesu ali ndi ophunzira ake ndipo akulankhula mokoma mtima ndi munthu amene wagwada patsogolo pawo.

Maliko 10:17-22

PHUNZIRO 12

Kulangiza Molimba Mtima

Mfundo yaikulu: “Mafuta ndi zofukiza zonunkhira n’zimene zimasangalatsa mtima. Chimodzimodzinso kukhala ndi mnzako wabwino amene amakupatsa malangizo mosapita m’mbali.”​—Miy. 27:9.

Zomwe Yesu Anachita

Yesu ali ndi ophunzira ake ndipo akulankhula mokoma mtima ndi munthu amene wagwada patsogolo pawo.

VIDIYO: Yesu Analangiza Wolamulira Wachinyamata

1. Onerani VIDIYO, kapena werengani Maliko 10:17-22. Kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  1. Kodi Yesu angakhale kuti anaona makhalidwe abwino ati mwa wolamulira wachinyamatayu?

  2. N’chifukwa chiyani pankafunika chikondi komanso kulimba mtima kuti amupatse malangizo?

Zomwe Tikuphunzira kwa Yesu

2. Kuti wophunzira wathu apite patsogolo mwauzimu, tiyenera kumulankhula mwachikondi koma mosabisa mawu.

Zomwe Mungachite Potsanzira Yesu

3. Muzimuthandiza kukhala ndi zolinga komanso mmene angazikwaniritsire.

  1. Muzigwiritsa ntchito mbali yakuti “Zolinga,” m’buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.

  2. Muzimuthandiza kudziwa zomwe angachite kuti akwaniritse zolinga zing’onozing’ono komanso zikuluzikulu.

  3. Muzimuyamikira chifukwa cha mmene akupitira patsogolo.

4. Muzizindikira zomwe zingamulepheretse kupita patsogolo, n’kumuthandiza.

  1. Dzifunseni kuti:

    • ‘N’chiyani chomwe chingakhale kuti chikumulepheretsa kupita patsogolo kuti abatizidwe?’

    • Ndingatani kuti ndimuthandize?

  2. Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kulankhula mwachikondi komanso mosabisa mawu pothandiza wophunzira wanu.

5. Muzisiya kuphunzira naye ngati sakupita patsogolo.

  1. Dzifunseni mafunso awa kuti mudziwe ngati phunzirolo likupitadi patsogolo kapena ayi:

    • ‘Kodi amagwiritsa ntchito zomwe amaphunzira?’

    • ‘Kodi amapezeka pamisonkhano komanso kuuza ena zokhudza choonadi?’

    • ‘Popeza waphunzira kwa nthawi yotalikirapo, kodi akufuna kukhala wa Mboni za Yehova?’

  2. Ngati wophunzira Baibulo sakupita patsogolo:

    • Mufunseni chimene chikumulepheretsa kuti asapite patsogolo.

    • Muuzeni mokoma mtima chifukwa chake simungapitirize kuphunzira naye.

    • Muuzeni zomwe angachite ngati atadzafunanso kupitiriza kuphunzira.

ONANINSO MALEMBA AWA

Sal. 141:5; Miy. 25:12; 27:6; 1 Akor. 9:26; Akol. 4:5, 6

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena