Mawu kwa Osonkhana
OLANDIRA ALENDO Amene akulandira alendo ntchito yawo n’kukuthandizani. Choncho, tsatirani malangizo amene angakupatseni okhudza malo oyenera kuimika galimoto ndi njinga, njira zoyenera kudutsa polowa kapena potuluka pamalo a msonkhano, kusunga malo okhala komanso zinthu zina.
UBATIZO Anthu amene akonzekera kubatizidwa adzakhale m’mipando yakutsogolo imene awakonzera. Ngati pali malangizo ena osiyana ndi amenewa, adzalengezedwa. Anthuwa ayenera kudzakhala m’mipandoyi, Loweruka m’mawa nkhani ya ubatizo isanayambe. Aliyense ayenera kubweretsa chopukutira ndi zovala zoyenera zolowera m’madzi.
ZOPEREKA Pamafunika ndalama zambiri kuti tikhale ndi malo abwino ochitira msonkhano, zokuzira mawu, zipangizo zoonetsera mavidiyo komanso zinthu zina zothandiza kuti msonkhanowu ukhale wosangalatsa ndiponso kuti utithandize kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndalama zimene mungapereke mwakufuna kwanu pamsonkhanowu, zithandiza kulipirira zinthu zimenezi komanso zithandiza pa ntchito ya padziko lonse. Mabokosi olembedwa bwino amene mungaponyemo zopereka zanu, aikidwa m’malo osiyanasiyana pamsonkhanowu. Komabe, ngati n’zotheka mungapereke kudzera pa intaneti popita pa donate.jw.org. Timayamikira kwambiri zopereka zanu ndipo Bungwe Lolamulira likukuyamikirani chifukwa chothandiza ndi mtima wonse pa ntchito za Ufumu.
DIPATIMENTI YOTHANDIZA PANGOZI Kumbukirani kuti dipatimenti imeneyi imathandiza pa zochitika mwadzidzidzi zokha.
ZOTAYIKA NDI ZOPEZEKA Mukatola chinthu chilichonse, kachiperekeni ku Dipatimenti ya Zotayika ndipo ngati mwataya chilichonse, kafunseni kudipatimentiyi. Mukapeza mwana amene wasochera, kamuperekeni kudipatimenti imeneyi. Ngati ana anu atasowa zikhoza kukhudza anthu ambiri, ndiye chonde asamalireni ndipo nthawi zonse muzikhala nawo pamodzi.
MALO OKHALA Yesetsani kuganizira ena. Kumbukirani kuti anthu okhawo oyenera kuwasungira malo ndi am’banja lanu, amene mwabwera nawo pa galimoto imodzi kapena amene mukuphunzira nawo Baibulo. Musaike zinthu pamalo okhala, pokhapokha ngati mwasungira munthu wina malowo.
NTCHITO YONGODZIPEREKA Ngati mukufuna kuthandiza nawo ntchito zina pamsonkhanowu, pitani ku Dipatimenti Yothandiza Anthu Ndiponso Yoyang’anira Antchito Ongodzipereka.
Wokonzedwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova
© 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania