7 YAKOBO
Analimba Mtima Kuti Ateteze Banja Lake
ATATSALA pang’ono kufa, Yakobo anati nthawi imene anakhala ndi moyo, inali “zaka zowerengeka komanso zosautsa.” (Gen. 47:9) Iye anakumanadi ndi mavuto ambiri. Zaka zambiri m’mbuyomo Ali wachinyamata, anathawira ku Harana, mchimwene wake weniweni akufuna kumupha. Ali ku Haranako, Yakobo anakonda kwambiri Rakele ndipo ankafuna kumukwatira. Koma Labani yemwe anali bambo ake a Rakele, anamupusitsa n’kumuchititsa kuti akwatire kaye mkulu wake. Choncho Yakobo anali ndi akazi awiri omwe ankangokhalira kuyambana. Iye anagwirira ntchito Labani kwa zaka zambiri ndipo kwa zaka zonsezo, iwo ankafuna kumubera pomangosinthasintha malipiro ake. Komabe, Yakobo anali wolimba mtima, wokhulupirika komanso wopirira.
Tsiku lina Yehova anauza Yakobo kuti abwerere ku Kanani. Koma zimenezi zinali zoopsa chifukwa Labani anali wadyera ndipo ankaona kuti zinthu zonse zomwe Yakobo anali nazo zinali zake. Yakobo anakambirana ndi akazi ake zomwe Yehova anamuuza, ndipo anathawa ndi banja lake osamuuza Labani. Labani atadziwa za nkhaniyi, anasonkhanitsa amuna n’kuwatsatira. Atawapeza, Labani anakalipira Yakobo chifukwa chonyamuka mozemba. Anamuopsezanso kuti: “Ndikanatha kukuchitirani zoipa.” Koma molimba mtima Yakobo anadzudzula Labani. Anamuuza kuti wakhala akumupondereza komanso kumuchitira zachinyengo. Ngakhale zinali choncho, Yakobo anali wofunitsitsa kukhazikitsa mtendere, moti mmene ankasiyana analonjezana kuti azikhala mwamtendere.
Kodi Yakobo anakwanitsa bwanji kukhazikitsa mtendere ndi achibale ake komanso kulimbana ndi mngelo wamphamvu?
Yakobo ankayembekezeranso kukakumana ndi mchimwene wake Esau. Zaka zambiri m’mbuyomo, mayi awo anachenjeza Yakobo kuti Esau ankafuna kumupha. Esau ankaona kuti Yakobo anachita zachinyengo polandira madalitso amene ankayenera kukhala ake kuchokera kwa bambo awo. Koma pa nthawiyi Yakobo ankafuna kukhazikitsa mtendere ndi mchimwene wakeyo. Iye anamva kuti Esau akubwera limodzi ndi banja lake komanso ndi amuna 400. Yakobo anatumiza akapolo ake kuti akakumane ndi Esau n’kumupatsa mphatso zamtengo wapatali. Koma kodi zimenezi zinalidi zokwanira kukathetsa mkwiyo wa Esau? Baibulo limati: “Yakobo anachita mantha ndi kuda nkhawa kwambiri.” Koma kenako panachitika zodabwitsa.
Usiku, Yakobo ali yekhayekha, anaona munthu wachilendo. Munthuyo anali mngelo wa Yehova ndipo anayamba kulimbana naye. Iye anaganiza kuti mngeloyo akhoza kumudalitsa, choncho analimba mtima n’kuyamba kulimbana naye kwa maola angapo. Ngakhale kuti Yakobo anali ndi zaka 97 ndipo mngeloyo anali wamphamvu kwambiri, iye sanamusiye. Analimbana naye koopsa mpaka Yakobo anayamba kulira. (Hos. 12:4) Yakobo ankadziwa kuti madalitso a Yehova ndi ofunika kwambiri, choncho anatsimikiza kuchita chilichonse kuti awapeze. Kutacha, mngelo uja anagwira Yakobo polumikizana chiuno ndi fupa la ntchafu mpaka fupalo kuguluka. Mngeloyo anamuuza kuti dzina lake lidzakhala Isiraeli, kutanthauza kuti walimbana ndi Mulungu. Dzinali linali lomuyenereradi chifukwa sanagwe ulesi ndipo anagwiritsa ntchito mphamvu zake zonse kuti apeze madalitso a Yehova.
Kenako Yakobo anabwerera kwawo akutsimphina. Chapatali, anaona Esau akubwera limodzi ndi amuna 400. Yakobo anapita kuti akakumane nawo. Akuyandikira, anaweramitsa nkhope yake mpaka pansi maulendo 7. Kenako Esau anamuthamangira. Iye analibe chida chilichonse ndipo anahaga Yakobo. Kenako amuna awiriwa anayamba kulira. Kupatsa ndi kudzichepetsa kwa Yakobo, zinathandiza kuthetsa mkwiyo wa Esau. N’kutheka kuti Esau anachita chidwi ndi kulimba mtima komwe Yakobo anasonyeza. Yakobo anapeza njira yabwino kuti agwirizanenso ndi mchimwene wakeyu.
Kungoyambira pamenepo, Yakobo ankatsimphina chifukwa cha kuvulala kuja ndipo anakumana ndi mavuto enanso ambiri. Koma sananong’onezepo bondo chifukwa chomvera Yehova kapenanso chifukwa cholimbana ndi mngelo. Patapita zaka, lonjezo losangalatsa kwambiri limene Yehova anamulonjeza linakwaniritsidwa ndipo Aisiraeli anakhala mtundu waukulu. (Gen. 28:14) Komanso nthawi zambiri, Yehova ankadziwika kuti “Mulungu wa Yakobo.” (Eks. 3:6) Yesu Khristu anagwiritsaponso ntchito mawuwa. Iye anati Yehova “ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, chifukwa kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:37, 38) Choncho Yakobo ali ndi tsogolo labwino kwambiri, chifukwa adzakhala ndi moyo mpaka kalekale komanso wosangalala m’dziko latsopano.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Yakobo anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. N’chifukwa chiyani Yehova anaonetsetsa kuti Yakobo walandira madalitso ngati mwana woyamba kubadwa m’malo mwa Esau? (w03 10/15 29 ¶2)
2. Kodi Yehova analotetsa Yakobo maloto otani, nanga zimenezi zinamutsimikizira chiyani? (w03 10/15 28 ¶3–29 ¶1) A
Zithunzi A
3. N’chifukwa chiyani Yakobo sanakayikire kuti akhoza kudalitsidwa ndi mngelo? (w03 10/15 31 ¶1) B
Chithunzi B
4. Kodi Yakobo anachita chiyani pofuna kuteteza anthu am’banja lake kuti asatengere zochita za Akanani? (w95 9/15 21 ¶4, mawu a m’munsi-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
Yakobo ankaona kuti ali ndi udindo wosamalira nkhosa zonse za Labani. (Gen. 31:38-40) Kodi abusa a Chikhristu angasonyeze bwanji kuti amadera nkhawa kwambiri abale ndi alongo awo omwe ndi nkhosa za Yehova? C
Chithunzi C
Yakobo atachita mantha, anapemphera kwa Yehova. (Gen. 32:6-12) Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhani ya mmene tingamapempherere?
Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Yakobo?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yakobo akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Kodi tingatsanzire bwanji Yakobo tikazindikira kuti takhumudwitsa Mkhristu mnzathu?
Gwiritsirani ntchito zithunzi zofotokoza nkhani ya m’Baibulo zotsatirazi kuti muphunzitse banja lanu zokhudza Yakobo.