23 DAVIDE
Analimba Mtima Kumenyana Ndi Chimphona
DAVIDE ankayang’ana munthu wina yemwe anaima m’chigwa cha Ela. Munthuyo anali Goliyati. Munthu amene ankamunyamulira zida Goliyati, anali ndi msinkhu wofanana ndi anthu ena onse. Koma Goliyati anali wamtali modabwitsa komanso wadzitho. Anali wamtali pafupifupi mamita atatu. Anthu ambiri akangomuona, ayenera kuti ankadziona kuti ndi aang’ono kwambiri komanso opanda mphamvu. Koma Davide ataona Goliyati, sanachite naye mantha.
Davide anali atadzozedwa ndi mneneri Samueli ndipo Samueliyo ananena kuti Davide adzakhala mfumu yotsatira ya Isiraeli. Kungoyambira pamenepo, mzimu wa Yehova unayamba kugwira ntchito kwambiri pa mnyamatayu. Tsiku lina Davide anafika kumalo kumene asilikali a Isiraeli ankamenyerako nkhondo chifukwa choti bambo ake, a Jese, anamutuma kuti akaone azichimwene ake. N’kutheka kuti iye anali asanakwanitse zaka 20. Ngakhale kuti anali wamng’ono moti sangakhale msilikali, anayamba kudziwika kuti ndi “mwamuna wolimba mtima komanso msilikali wamphamvu.”
Davide atafika kuchigwa cha Ela, anaona kuti asilikali a Isiraeli ndi a Afilisti, anali atakhala kwa mawiki asakumenyana. Pakati pa asilikali a Aisiraeli ndi asilikali a Afilisiti panali chigwa. Kenako Goliyati yemwe anali chimphona cha Afilisiti anatulukira n’kuyamba kunyoza Aisiraeli. Davide anakhumudwa ndi zimene anamva chifukwa zimene msilikaliyu ankachitazi ankanyoza Yehova Mulungu. Davide anayamba kufunsa asilikali zokhudza Goliyati komanso kuti Mfumu Sauli idzam’patsa chiyani munthu amene angagonjetse Mfilisiti ameneyu yemwe ankanyoza asilikali a Yehova. Eliyabu, yemwe anali mchimwene wake wamkulu wa Davide, anayamba kudzudzula Davideyo komanso kukayikira zolinga zake. Koma Davide anapitiriza kulimbikitsa asilikali kuti amenyane ndi chimphonacho.
Anthu anakauza Mfumu Sauli zimene Davide ananena ndipo Sauli anamuitanitsa. Davide analimbikitsa mfumuyo ponena kuti: “Aliyense asachite mantha ndi [Goliyati].” Iye anadzipereka kuti apita yekha ‘kukamenyana ndi Mfilisitiyo.’ Poyamba Sauli anamukaniza chifukwa ankakhulupirira kuti Davide akaphedwa. Koma Davide anauza mfumu mmene Yehova anamuthandizira kuchita zinthu zodabwitsa monga kupha mkango komanso chimbalangondo zomwe zinagwira nkhosa za bambo ake. Kenako Davide anavomera ndipo anam’patsa zovala zake za nkhondo ndi lupanga. Koma Davide anali asanazolowere kuvala zovala zotero choncho anazivula ndipo anagwiritsa ntchito ndodo ndi gulaye, zida zomwe ankatenga ku ubusa. Kenako anayamba ulendo wopita kuchigwa kuja.
Atafika kumtsinje anatola miyala 5 yosalala. Kenako anakafika pamene panali chimphona chija. Chimphonacho chitangoona mnyamatayo, chinayamba kumuderera komanso kumunyoza ponena kuti anapita kwa iyeyo atanyamula “ndodo.” N’kutheka kuti Goliyati sanaone gulaye uja chomwe chinali chida champhamvu kwa Davide. Mfilisitiyo “anatemberera Davide m’dzina la milungu yake” ndipo analonjeza kuti mtembo wake aupereka kwa mbalame komanso zilombo zakutchire.
Ali mnyamata, Davide anamenyana ndi chimphona kuti ateteze dzina la Yehova
Davide anayankha kuti: “Iwe ukubwera kudzamenyana ndi ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikubwera kudzamenyana nawe mʼdzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa asilikali a Isiraeli, amene iweyo wamunyoza.” Apatu Davide anafotokoza chimene chinkamulimbitsa mtima. Iye sankadziyerekezera ndi Goliyati koma ankayerekezera Goliyatiyo ndi Yehova Mulungu. Choncho Davide sankakayikira kuti apha Goliyati komanso kuti Afilisiti sapambana pa nkhondoyo.
Davide anathamangira komwe kunali mdani wakeyo. Kenako anatenga mwala m’chikwama mwake, kuuika pagulaye n’kuyamba kupukusa. Tsopano Goliyati anaona gulaye uja koma sizikanathandiza chilichonse. Davide anaponya mwala uja ndipo sanaphonye moti unakafikira pachipumi cha Goliyati. Goliyatiyo “anagwa pansi chafufumimba.” Davide anathamanga n’kukatenga lupanga la Goliyati n’kumudula nalo mutu. Zitatero asilikali a Aisiraeli analimba mtima ndipo anayamba kufuula n’kupita kukamenyana ndi Afilisiti. Pa tsikuli, anthu a Mulungu anapambana. Kulimba mtima kwa Davide, yemwe pa nthawiyo anali mnyamata, kunawathandiza kwambiri ndipo kukuthandizabe anthu okhulupirika mpaka pano.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Davide anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Tchulani makolo ena akale a Davide omwe anali olimba mtima. (Mat. 1:5, 6; Luka 3:31-38; w12 10/1 24 ¶3)
2. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti nkhaniyi inachitikadi? (wp16.5 13) A
Collection the Israel Antiquities Authority. Photo © The Israel Museum, by Meidad Suchowolski
Chithunzi A: Mwala wa zaka za m’ma 800 B.C.E. pomwe pali mawu akuti “Nyumba ya Davide”
3. Fotokozani zimene zinkachitika pa moyo wa Davide ali m’busa. (w11 9/1 27 ¶1–28 ¶1) B
Todd Bolen/BiblePlaces.com
Chithunzi B
4. Kodi anthu ena ankamuona bwanji Davide? (w21.03 3 ¶6; it “Eliyabu” Na. 4 ¶1-wcgr)
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi chitsanzo cha Davide chingakuthandizeni bwanji kulimbana ndi . . .
mantha? C
Chithunzi C
kulakalaka kuchita zoipa?
Kodi kulimba mtima kwanu kungathandize bwanji anthu ena? (1 Sam. 17:50-53)
Kodi mungatsanzire Davide pa nkhani ya kulimba mtima m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Davide akadzaukitsidwa zokhudza nthawi imeneyi ya moyo wake?
Phunzirani Zambiri
Munyimbo, yomwe ndi ya ana, onani zimene zinathandiza Davide kukhala wolimba mtima.
Kodi abale angatani kuti anthu ena aziwalemekeza ngati mmene zinalili ndi Davide?
“Kodi Achinyamata Mungatani Kuti Anthu Ena Azikudalirani?” (w21.03 2-5 ¶1-11)