Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 35 tsamba 158-tsamba 161
  • Analimba Mtima N’kulapa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Analimba Mtima N’kulapa
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • “Anakhazikitsa Pansi Mtima wa Yehova”
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Yehova Ndi Wofunitsitsa Kukukhululukirani
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Kulapa Kwenikweni N’kutani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Zimene Tikuphunzira kwa Mafumu a Chiisiraeli
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 35 tsamba 158-tsamba 161

35 MANASE

Analimba Mtima N’kulapa

Losindikizidwa
Losindikizidwa

MANASE anabadwa pambuyo poti bambo ake, Mfumu Hezekiya achiritsidwa modabwitsa. Yehova anatalikitsa moyo wa Hezekiya yemwe anali mfumu yabwino ndipo anabereka Manase. Koma n’zomvetsa chisoni kuti Hezekiya anamwalira Manase ali ndi zaka 12 zokha. Zitatero, Manase anakhala mfumu koma pasanapite nthawi yaitali, anasiya kutengera chitsanzo chabwino cha bambo ake ndipo sankatumikiranso Yehova mokhulupirika.

Manase anachita zinthu zoipa kwambiri. Pa zaka zimene anali mfumu anachita machimo akuluakulu monga kukhala wampatuko, kulambira mafano, kukhulupirira zamizimu komanso kupha ana ake. Pa nthawi ya ulamuliro wake, zachiwawa zinali ponseponse. Anachititsa kuti Yerusalemu, womwe unali mzinda wa Mulungu, ukhale ndi mlandu wa magazi chifukwa choti ankachita komanso kulimbikitsa zachiwawa. Ngakhale kuti Yehova anatumiza aneneri kuti akamuchenjeze, iye sanawamvere. Ndiye n’chifukwa chiyani tinganene kuti Manase anali chitsanzo chabwino pa nkhani ya kulimba mtima? Tiyeni tione.

Tsiku lina moyo wa Manase unasintha mwadzidzidzi. Chifukwa choti mfumuyi inakana kumvera machenjezo a Yehova kudzera mwa aneneri, Yehovayo analola kuti atsogoleri a asilikali a Asuri agonjetse Yuda. Baibulo limati: “Anagwira Manase ndi ngowe. Atatero anamʼmanga ndi matcheni awiri akopa nʼkupita naye ku Babulo.” Mfumu yonyada imeneyi iyenera kuti inachita manyazi kwambiri komanso inamva kupweteka chifukwa cha mavuto amene inakumana nawo pa ulendo wautali komanso wotopetsa umenewu.

Manase anachita zinthu zoipa kwambiri koma Yehova anamupatsa mwayi woti asinthe

Manase ali ku ukapolo ku Babulo, anavutika kwambiri mumtima ndipo anayamba kuganizira za moyo wake. Iye ankangoona kuti ali yekhayekha, alibenso mphamvu komanso palibe womuthandiza ndipo n’kutheka kuti anali asanamvepo chonchi pa moyo wake. Ayenera kuti anazindikira kuti kunali kupusa kulambira milungu yabodza ija ngakhalenso kupereka nsembe ana ake kwa milunguyi chifukwa inalephera kumuthandiza. Iye anaona kuti ankafunika kusintha. Choncho anapemphera kwa Yehova ndipo sanachite zimenezi modzikuza. M’malomwake, “anadzichepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ake.” Yehova anaona kuti wasintha ndipo anayankha pemphero lake. Pamene Manase anapitiriza kusonyeza kudzichepetsa kwambiri, Yehova anayamba kumukonda. (Sal. 138:6) Manase anapemphera kwa “Yehova Mulungu wake” kuti amuchitire chifundo ndipo anapitiriza kupemphera mwa njira imeneyi.

Kodi Yehova anaona bwanji mapemphero akewa? Baibulo limati: “Iye anamva pemphero lake lochonderera ndiponso lopempha chifundo.” Choncho Mulungu woona anamuchitira chifundo komanso anamuthandiza modabwitsa. “Anamʼbwezera ku Yerusalemu ndipo anakhalanso mfumu.” Tsopano Manase anali ndi mwayi wosonyeza kuti walapadi ndipo zimenezi zikanaonekera mwa zosankha zake.

Atabwerera ku Yerusalemu, Manase ankafunika kudalira Yehova komanso kuthandiza anthu kusintha makhalidwe awo oipa. Izi zinali choncho chifukwa kwa zaka zambiri, iye ndi amene anapangitsa kuti anthu azichita zoipa. N’kutheka kuti ankadera nkhawa kuti anthu samumvera kapena amukwiyira chifukwa choti wasintha. Ngati zinalidi choncho, ndiye kuti Manase analimba mtima n’kuchita zoyenera. Anamanga mpanda wolimba kuzungulira Yerusalemu kenako anachotsa mafano onse omwe anali mumzindawu kuphatikizapo omwe anali m’kachisi wa Yehova. Anamanga guwa lansembe la Yehova n’kuperekapo nsembe. N’kutheka kuti chinthu china chomwe chinali chovuta kwambiri ndi kulankhula ndi Ayuda. M’malo mowalimbikitsa kuti azilambira milungu yabodza ngati poyamba, iye analimbikitsa “Ayuda kuti azitumikira Yehova Mulungu wa Isiraeli.” Apa Manase yemwe poyamba anali woipa anasinthiratu n’kukhala munthu wabwino. Chitsanzo chakechi, chimasonyezeratu khalidwe la Yehova lokhala “wokonzeka kukhululuka.”—Sal. 86:5.

Manase akulankhula ndi anthu ku Yerusalemu pamsika pomwe pali mafano ambiri. Asilikali akugwetsa mizati yopatulika ndiponso kuwononga mafano.

N’zomvetsa chisoni kuti Manase sanakwanitse kuthetsa mavuto onse amene anayambitsa. Ngakhale kuti Yehova anakhululukira Manase, anapereka chilango kwa anthu achiwawa komanso omwe anapha anthu m’nthawi ya ulamuliro wake. Mosiyana ndi Manase, anthuwo sanafune kulapa. Ngakhalenso Amoni mwana wake, sanamumvere ndipo anapitiriza kuchita zoipa. Komabe zikuoneka kuti Manase anathandiza mdzukulu wake Yosiya, kuti azikonda Yehova. Yosiya ayenera kuti ankakumbukira zoti agogo ake anasonyeza kulimba mtima kuti adzichepetse komanso kulapa. Pambuyo pochita zoipa kwa zaka zambiri, Manase anasintha ndipo kwa moyo wake wonse ankakumbukira kuti Atate wake Yehova anamukhululukira.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • 2 Mafumu 21:​1-26

  • 2 Mbiri 33:​1-25

Funso lokambirana:

Kodi Manase anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Poyamba Aamori ankakhala m’dziko la Kanani. N’chiyani chikusonyeza kuti Manase anachita “zinthu zoipa kwambiri kuposa zonse zimene Aamori amene analiko iye asanakhale mfumu” anachita? (2 Maf. 21:11; w00 10/15 16 ¶5-6-wcgr; gl 10 ¶5, mawu a m’munsi)

  2. 2. Kodi zimene ofukula zinthu zakale apeza zimasonyeza bwanji kuti Manase anakhalako komanso kuti ulamuliro wa Asuri unali wamphamvu pa nthawiyo? (it “Manase” Na. 4 ¶2-wcgr) A

    © The Trustees of the British Museum. Licensed under CC BY-NC-SA 4.0. Source

    Chithunzi A: Mawu akuti “Manase, mfumu ya Yuda” anapezeka pachinthu chopangidwa ndi dongo chotchedwa Esarhaddon

  3. 3. N’chiyani chikusonyeza kuti Asuri ankagwiradi akapolo ndi ngowe? (2 Mbiri 33:11; it “Ngowe” ¶4-wcgr) B

    Chithunzi cha Asuri chosonyeza mfumu ili ndi akapolo atatu atawamanga ndi zingwe. Kuzingweko amangirirako ngowe yomwe awakola nayo pamlomo, uku mfumuyo itabaya kapolo wina padiso ndi mkondo.

    Chithunzi B: Chithunzi chojambulidwa pamanja cha Asuri cha zaka za m’ma 700 B.C.E.

  4. 4. Kodi Yehova ‘anayeza’ bwanji Yerusalemu ndi chingwe komanso kugwiritsa ntchito “levulo”? (2 Maf. 21:13; it “Levulo” ¶2-wcgr)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa chiyani zokhudza kulapa?

  • N’chifukwa chiyani tinganene kuti chitsanzo cha Manase chikusonyeza kuti ngakhale kuti Yehova amakhululukira munthu amene walapa, munthuyo amakumanabe ndi zotsatira za tchimo lake? (Yer. 15:​3-5) C

    Zithunzi: 1. Mnyamata akumwa mowa ndi anzake uku akuyenda pa galimoto usiku. 2. Patapita zaka wakhala panjinga ya anthu olumala ndipo akuyankha pamisonkhano. Mkono wake wakumanzere uli ndi matatuu.

    Chithunzi C

  • Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Manase m’njira ziti?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Manase akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Onani mmene chitsanzo cha Manase chinathandizira m’bale wina kuti abwerere kwa Yehova.

Kumangidwa Kunandithandiza Kuti Ndipeze Ufulu (5:10)

Ngati nthawi ina munadzionapo kuti ndinu wosafunika chifukwa cha machimo amene munachita m’mbuyomu, kodi nkhani imeneyi ingakuthandizeni bwanji?

“Anakhazikitsa Pansi Mtima wa Yehova” (w11 1/1 18)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena