Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 42 tsamba 192-tsamba 195
  • Analimba Mtima N’kuvomera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Analimba Mtima N’kuvomera
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Phunzirani Zambiri
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • “Ndinetu Kapolo wa Yehova!”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • “Ndinetu Mdzakazi wa Yehova!”
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Wachita Zimene Akanatha”
    Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 42 tsamba 192-tsamba 195

42 MARIYA

Analimba Mtima N’kuvomera

Losindikizidwa
Losindikizidwa

KODI utumiki wapadera kwambiri umene Yehova anaperekapo kwa munthu yemwe si wangwiro ndi uti? Taganizirani zimene zinachitikira namwali wina wa Chiyuda dzina lake Mariya. Tsiku lina Mariya ali kwawo ku Nazareti wa ku Galileya, analandira mlendo wapadera. Mlendoyu anali mngelo Gabirieli.

Mngeloyo ananena kuti: “Moni, iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova ali nawe.” Koma mawu amenewa “anamudabwitsa kwambiri” Mariya. Iye ankaona kuti sanali woyenera kutamandidwa choncho. Koma Gabirieli anamulimbikitsa pomuuza kuti: “Mulungu wakukomera mtima.” Kenako anamuuza za utumiki wapadera kwambiri umene Mulungu anamupatsa. Anayamba ndi mawu akuti: “Udzakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna.” Kenako anamuuza kuti: “Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzamupatsa mpando wachifumu wa Davide atate wake.”

Mariya analimba mtima n’kufunsa funso lomwe linali lomveka. Iye anali asanakwatiwe, koma anangokhala ndi chibwenzi ndipo anali asanagonepo ndi mwamuna. Mariya anafunsa kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji?” Gabirieli anafotokoza kuti mphamvu ya Mulungu kapena kuti mzimu woyera ‘udzamuphimba’ ndipo adzakhala woyembekezera n’kubereka mwana amene adzatchedwe “woyera, Mwana wa Mulungu.” Anamuuzanso zimene Yehova anachitira Elizabeti, yemwe anali wachibale wake. Atamva zimenezi analimba mtima moti anayankha kuti: “Ndine kapolo wa Yehova! Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.” Mariya ankaona kuti Yehova ndi Mbuye wake wachikondi ndipo iyeyo ndi kapolo wake woyenera kumvera. Iye ankakhulupirira kuti akamvera, Mulunguyo adzamuthandiza komanso kumuteteza. Zimenezi zinamuthandiza kukhala wolimba mtima n’kuvomera utumiki wovutawu.

Mariya akudabwa kwambiri, wagwada pansi ndipo akulankhula ndi mngelo Gabirieli.

Mngeloyo atachoka, Mariya ananyamuka n’kupita kwa Elizabeti. Azimayi awiriwa analimbikitsana kwambiri pa nkhani yokhudza udindo womwe anali nawo. Mariya analankhula mawu osonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro. Mawu akewo amatithandiza kudziwa chimene chinamuthandiza kuti alimbe mtima. Pakanthawi kochepa kokha, anatchula mawu a m’Malemba a Chiheberi maulendo 20. Mariya anakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa ankaganizira mozama Mawu a Mulungu. Choncho ankamudziwa bwino Yehova ndipo anali ndi chifukwa chomveka chokhulupirira zimene analonjeza. Mariya anakhala kwa Elizabeti miyezi itatu kenako anabwerera kwawo. Iye anafunika kulimba mtima kuti afotokozere Yosefe zoti ndi woyembekezera komanso zimene zinachititsa. Poyamba Yosefe anavutika kukhulupirira zimene Mariya anafotokoza, koma mngelo wa Yehova anamutsimikizira kuti Mariyayo akunena zoona.

Mariya ndi Yosefe anakwatirana ndipo nthawi yoti Mariya abereke inayandikira. Komabe Yosefe anapita naye ku Betelehemu pomvera lamulo la Kaisara loti akalembetse m’kaundula. Tikaganizira mmene Mariya analili, zinali zovuta kuti ayende pa bulu ulendo umenewu womwe unali wamakilomita 150. Koma anapitabe. Zotsatira zake anakaberekera komweko m’khola ndipo anagoneka mwana wakeyo modyeramo ziweto. Mariya anapitirizabe kuchita zinthu molimba mtima. Iye anachita zonse zimene akanatha kuti asamalire mwanayu pogwiritsa ntchito zinthu zimene anali nazo.

Mngelo anapatsa Mariya utumiki wapadera wochokera kwa Yehova umene munthu aliyense anali asanapatsidwepo

Mariya anafunikabe kupitiriza kukhala wolimba mtima. Mwachitsanzo, anafunika kulimba mtima pamene iyeyo ndi mwamuna wake anatenga mwana wawoyo n’kuthawira naye ku Iguputo kuti Mfumu Herode asamuphe. Popeza anali osauka, anafunika kulimba mtima kuti iye ndi mwamuna wake alere ana awo omwe analipo osachepera 6. Ankafunikanso kulimba mtima pamene mwamuna wake anamwalira, ndipo izi ziyenera kuti zinachitika Yesu asanakhale Mesiya. Pamene Yesu ankachoka pakhomo kuti akayambe utumiki wake, Mariya anafunikanso kulimba mtima. Iye anafunikanso kusonyeza kwambiri khalidweli pamene Yesu anamangidwa, kuimbidwa mlandu wabodza komanso kuphedwa. Kenako anafunikanso kulimba mtima kuti alowe m’gulu la otsatira a Yesu omwe ankanyozedwa ndi Ayuda.

Kunena zoona utumiki umene Mariya anapatsidwa unali wovuta. Ndiye kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti akhale wolimba mtima n’kukwanitsa kuchita utumikiwu? Baibulo limanena kuti Mariya akaphunzira mfundo inayake yomwe yalimbitsa chikhulupiriro chake, ankaisunga mumtima mwake. Choncho tingati anasunga chuma chauzimu mumtima mwake. Mfundo zina anaziphunzira m’Mawu a Mulungu, zina anazimva kwa angelo komanso atumiki ena a Yehova pomwe zina anazimva kwa mwana wake. Kuganizira mfundo za choonadi kunathandiza Mariya kuti apirire vuto lililonse lomwe anakumana nalo pa moyo wake.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Luka 1:​26-56; 2:​1-7, 19, 48-51

Funso lokambirana:

Kodi Mariya anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. Kodi pali umboni wotani wa mbiri yakale womwe umasonyeza kuti zimene zinalembedwa pa Luka 2:​1-3 ndi zoona? (g 4/11 11 ¶4-5) A

    British Library, London, UK, from the British Library archive/Bridgeman Images

    Chithunzi A: Lamulo lokhudza kalembera limene bwanamkubwa wa Chiroma wa ku Iguputo anapereka mu 104 C.E.

  2. 2. N’chifukwa chiyani ulendo wopita ku Betelehemu unali wovuta kwambiri kwa Mariya? (ia 153-155 ¶4-7)

  3. 3. Yesu ali wakhanda, Mariya anauzidwa kuti: “Lupanga lalitali lidzakubaya.” Kodi mawu amenewa anakwaniritsidwa bwanji? (Luka 2:35; w08 3/15 31 ¶1)

  4. 4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti panopa Mariya ali kumwamba? (w18.07 10 ¶14) B

    Mariya ndi ana ake atatu akuyenda mumsewu wa anthu ambiri ku Yerusalemu.

    Chithunzi B: Mariya ndi ana ake anali ku Yerusalemu pamene mwambo wa Pentekosite wa mu 33 C.E. unkayandikira

Phunzirani Zambiri

  • Pamene Mariya ankafunika kulimbikitsidwa, anapita kwa Elizabeti. (Luka 1:​39, 40) N’chifukwa chiyani tiyenera kupempha thandizo tikakumana ndi vuto kapena tikapatsidwa utumiki wovuta? C

    Zithunzi: 1. Mlongo yemwe akuoneka kuti wapanikizika wakhala pampando ndipo akuyang’ana laputopu yake ndi chipewa chogwirira ntchito. Kalendala yomwe palembedwa zochitika zosiyanasiyana yapachikidwa pakhoma. 2. Mlongo uja akulankhula ndi mlongo wachikulire pamene akulalikira kunyumba ndi nyumba.

    Chithunzi C

  • Ngakhale kuti Mariya anali pa chibwenzi ndi Yosefe, Yehova anatumiza mngelo kwa Mariya choyamba. Kodi zimenezi zikuphunzitsa kuti Yehova amawaona bwanji akazi okhulupirika?

  • Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Mariya m’njira ziti?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi mukumva bwanji mukaganizira kuti Mariya ayenera kuti ali m’gulu la anthu amene akalamulire ndi Khristu kumwamba?

Phunzirani Zambiri

Onani mmene Mariya anasonyezera khama komanso kusadzikonda polera ana ake.

“Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?” (w09 1/1 5 ¶5–6 ¶2)

Kodi Mariya ayenera kuti anamva bwanji Gabirieli atamuuza za utumiki wovuta umene anapatsidwa?

“Ndine Kapolo wa Yehova!” (3:40)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena