Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 1/1 tsamba 3
  • Lalikirani Ufulu!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Lalikirani Ufulu!
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Anakonza Zoti Tikhale ndi Ufulu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Chaka Choliza Lipenga cha Yehova—Nthawi Yathu Yakusangalala
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mtendere Weniweni—Kodi Udzachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Mtendere wa Umulungu Kaamba ka Awo Ophunzitsidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 1/1 tsamba 3

Lalikirani Ufulu!

MUNTHU WOKWANITSA BILIYONI YACHISANU pa dziko lapansi akunenedwa kukhala atabadwa pa July 7, 1986. Kodi ndi mtsogolo mwa mtundu wanji m’mene munthu wokwanitsa biliyoni yachisanu ameneyu, ndipo kwenikweni anthu onse, ayenera kukumanizana namo? Kodi pali kuthekera kulikonse kwakuti mabiliyoni a mtundu wa anthu tsiku lina lake angadzasangalale ndi ufulu weniweni? Motsimikizirika, tikunena kuti inde. Koma kodi ndi chiyani chomwe tikafunikira kumvetsetsa ponena za “ufulu”? Kodi icho chimatanthauza laisensi ya kuchita chiri chonse chomwe chimamukondweretsa munthu? Ai, popeza wolemba nkhani wa m’zana la 19 wa Chingelezi Charles Kingsley analemba kuti: “Pali ufulu uwiri, wabodza kumene munthu ali waufulu kuchita zomwe amakonda, ndipo wowona kumene munthu ali waufulu kuchita zomwe akufuna.”

Munthu adzapeza ufulu weniweni kokha mwakuchita “zomwe akufuna kuchita.” Ndipo ndi chiyani chomwe amafuna choti achite? Pamene Yesu anali pano pa dziko lapansi, iye analongosola momvekera bwino kuti pali malamulo a akulu awiri​—loyamba, kukonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo, maganizo, ndi nzeru, ndipo lachiwiri kukonda mnzako monga iwe mwini. (Marko 12:29-31) Ufulu weniweni umapezedwa kokha ndi awo amene moonadi amasonyeza chikondi chenicheni chimenechi—chikondi cha Mulungu ndi anthu anzawo.​—Yohane 8:31, 32.

Kodi dziko lerolino limasonyeza chikondi cha mtundu umenewo? Momvetsa chisoni, ai. Popanda chikondi, ufulu wa bodza umapambana. Umapuma dyera, mzimu wodziimira pawokha. Iwo umakakamiza pa ‘kuchita zinthu za iwo wokha,’ osalingalira konse za Mulungu kapena mnzao. Mzimu umenewu umapitirira kuposa pa umwini kufika ku magulu, mafuko, ndi mitundu. Pamene mkhalidwe wa ine—choyamba umapitirira, maziko kaamba ka ufulu, mtendere uli wonse, chimwemwe chiri chonse pa dziko lapansi, uli wogwedezeka. Kumbukirani, Yesu anati, “udzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.” Chikondi cha mnzathu chimenechi chiri chofunikira kaamba ka kusangalala ndi ufulu weniweni.

Gulu la Mitundu Yogwirizana linakhazikitsidwa kuwombola mtundu wa anthu mwa kubwezeretsa nkhalwe ya nkhondo ndi “mtendere ndi chisungiko.” Pa chikondwerero chake cha makumi anayi, UN inalengeza chaka cha 1986 kukhala Chaka Cha Mtendere wa Mitundu Yonse. Koma kodi ichi chafikira ku kulalikidwa kwa ufulu wokhala ndi zitsimikiziro zokhazikika za mtendere? Kodi ndalama zoonongeka zoonjezeka pa zida za nkhondo (zomafika tsopano ku chiwerengero choposa madola 1, 000 biliyoni pa chaka) zakhala zitatsekerezedwa? Kodi upandu ndi kuphulitsidwa kwa magalimoto kwachepekera? Kodi kuphana kozikidwa pa chipembedzo ku Northern Ireland, Middle East, ndi Asia kwathetsedwa? Atsogoleri achipembedzo akudzilowetsa mu ndale za dziko ndipo akulankhula kwambiri ponena za mtendere. Koma nkhunda ya mtendere weniweni ikuoneka kukhala itaulukira kutali kumene UN ndi zipembedzo za dziko sizingafike.

Kodi pali gulu lina lake lerolino lomwe latsutsa upandu, njira ya ine​—choyamba ya dziko? Inde, liripo! “Karonga wa Mtendere” wonenedweratu Yesu Kristu, wasonkhanitsa okonda mtendere ‘kuchokera ku mafuko onse, manenedwe, anthu, ndi mitundu.’ (Yesaya 2:3, 4; 9:6, 7; Chivumbulutso 5:9; 7:9) Iwo amasangalala kuti Ufumu wa Mulungu ndi Kristu watsala pang’ono kuthetsa kuipa konse ndi kubweretsa paradaiso wa mtendere pa dziko lonse lapansi, kumene ufulu weniweni udzakhalitsa. Gulu limeneli limadziwika monga Mboni za Yehova. (Danieli 2:31-35, 44; Yesaya 43:10, 12; 65:17-25) Mogwirizana, Akristu amenewa mwachimwemwe akulengeza mbali zophiphiritsidwira ndi kakonzedwe ka Chaka Choliza Lipenga mu Israyeli wakale. Mu liri lonse la maiko 200 ndi kuposa kuzungulira pa dziko lonse lapansi, iwo mwachimwemwe amamvera lamulo la Mulungu: “Lalikira ufulu kwa onse okhala m’dziko.” (Levitiko 25:10) Kodi mwamva ndi kulabadira mfuu yachimwemwe imeneyo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena