Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 1/15 tsamba 7-9
  • Mboni za Yehova M’munda wa Umishonale

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni za Yehova M’munda wa Umishonale
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusiyana kwa Kaonedwe ka Zinthu
  • Kukwaniritsa Zosowa Zauzimu za Anthu
  • Kupanga Ophunzira Enieni Lerolino
    Galamukani!—1995
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Ntchito Yongodzipereka Yokhala ndi Mapindu Okhalitsa
    Galamukani!—2001
  • Amishonale Amapita “Kumalekezero a Dziko Lapansi”
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 1/15 tsamba 7-9

Mboni za Yehova M’munda wa Umishonale

A Mishonale a Mboni za Yehova mu Asia ndi kwina kuli konse kawirikawiri amafunsidwa: “Kodi nchifukwa ninji simukhala ndi makalasi a Chingelezi monga amishonale ena onse?” “Kodi muli ndi masukulu omwe ndingatumizeko ana anga kapena zipatala kaamba ka odwala?” Yankho, kwenikweni liri ayi. Koma kodi nchifukwa ninji ayi? Mu chenicheni, nchiyani chomwe chiri cholinga cha Mboni za Yehova? Ndipo nchiyani chomwe iwo achita kaamba ka anthu mu maiko amenewa?

Kusiyana kwa Kaonedwe ka Zinthu

Chiri chosakanidwa kuti amishonale a Chipembedzo cha Dziko apanga atembenuki ambiri mwanjira ya mautumiki amayanjano omwe iwo anapereka. Koma chifukwa chakuti ntchito zimenezi zimalunjikitsidwa kwenikweni pa kukhutiritsa zosowa za kuthupi za anthu mmalo mwa zosowa zawo za kuuzimu, amishonale amenewa sanakhale opambana m’kupanga ophunzira enieni a Yesu Kristu. (Mateyu 7:22, 23; 28:19, 20) Chofunika kwambiri, iwo sanakhoze kuloza kuyankho lenileni lokhazikika ku zovuta zamayanjano zomwe iwo akuyesayesa kuzilaka.

Mboni za Yehova, kumbali ina, ziri zodera nkhawa kwambiri ndi ntchito yofunika kwambiri ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. (Mateyu 24:14) Ichi sichiri chifukwa chakuti iwo sali ozindikira kapena ali osadera nkhawa ponena za kuvutika konse kwa mtundu wa anthu ndi kupanda chilungamo komwe iwo amakuwona. M’malo mwake, chiri chifukwa chakuti iwo amazindikira kuti mankhwala okha kaamba ka mavuto aakulu amenewa ali, osati m’manja mwa anthu, koma mu Ufumu wa Mulungu.​—Masalmo 146:3-10.

Chimenecho chinali kwenikweni chimene Yesu ndi otsatira ake analalikira mu zana loyamba. “Kundiyenera Ine ndilalikire [Mbiri yabwino NW] ya Ufumu wa Mulungu,” Yesu anatero, “chifukwa ndinatumizidwa kudzatero.” (Luka 4:43) Yesu analoza ku Ufumu wa Mulungu ndi kulalikira ponena za iwo monga mankhwala okha enieni, chifukwa chakuti iye anadziwa kuti mavuto a m’dziko anali aakulu kwambiri kaamba ka munthu kuchita nawo iye yekha. Ngakhale Yesu anapanga kuchiritsa kozizwitsa kochuluka, iye analimbikitsa ophunzira ake, “muthange mwafuna Ufumu choyamba ndi chilungamo [cha Mulungu], ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.”​—Mateyu 6:33.

Pambuyo pake, pamene Yesu anatumiza ophunzira ake kunja, iye poyamba anawauza iwo: “Ndipo pamene mulikupita lalikirani kuti, ‘Ufumu wa kumwamba wayandikira.’” Kenaka iye anawonjezera: “Chiritsani akudwala, ukitsani akufa, konzani akhate, turutsani ziwanda.”(Mateyu 10:7, 8) Icho chimakhazikitsa chinthu choyambirira kaamba ka otsatira a Yesu amakono. Iwo, kawirinso, ayenera kuika kulalikira mbiri ya Ufumu monga chonulirapo chawo choyamba, pamwamba ndi kuposa kuchita ntchito za umunthu. Ichi ndi chimene amishonale a Mboni za Yehova amakalamira kuchita.

Kukwaniritsa Zosowa Zauzimu za Anthu

Monga gulu la Akristu, Mboni za Yehova zimalowetsedwa mu programu yaikulu yodzipereka yakupereka maphunziro a Baibulo kaamba ka anthu. Kukhala ofalitsa a mbiri yabwino, iwo ali okondweretsedwa m’kuthandiza ena kupindula kuchokera ku nzeru ya Baibulo ndi uphungu, ponse pawiri tsopano ndi mtsogolo. (Salmo 68:11) Nchifukwa ninji ichi chiri choncho?

Mboni za Yehova zimazindikira kuti pamene anthu akuthandizidwa kumvetsetsa ndi kutsatira uphungu wa Baibulo, iwo amakhala okonzekeretsedwa bwino kuchita ndi mavuto ndi zitsenderezo za moyo. Kumbali ina, iwo amapeza kulimbika mtima kofunikira kaamba ka makhalidwe abwino kulaka ukapolo ndi zizolowezi zowononga mwakuthupi mongangati kusuta fodya, kumwa kopitirira muyezo, kugwiritsira ntchito kolakwika kwa mankhwala, uve, njuga, ndi kukhalira pamodzi kosaloledwa kwa anthu a ziwalo zosiyana. Kumbali ina, chowonadi cha Baibulo chimathandiza iwo kusintha malingaliro awo, kuwa bweretsera iwo chifuno m’moyo ndi chiyembekezo chenicheni kaamba ka mtsogolo.

Mwakutero, mwa kupereka mtundu wapamwamba kwambiri wa maphunziro—umene umabwera kuchokera mu Mau a Mulungu, Baibulo—Mboni za Yehova zikupanga chopereka cha chindunji kulinga ku kukulitsa ma khalidwe abwino ndi umoyo wakuthupi wa m’madera m’mene iwo amakhala ndi kulalikira. Kawirikawiri ichi chimawonedwa ndi ena omwe amayang’ana iwo ndi cholinga. Mwachitsanzo, Dr. Bryan Wilson wa ku Oxford University, yemwe anaphunzira ntchito za Mboni za Yehova mu Afirika, ananena mu kalata yake ku London Times:

“Mboni za Yehova ziri zogwira ntchito molimbika ndipo mochulukira mosamalitsa ndipo mofunitsitsa kuposa avereji ya pakati pa nzika zinzawo. Iwo amakakamizidwa ndi atsogoleri awo kupereka msonkho mwamsanga, kusatenga mbali mu upandu, ndi kupewa kupereka milandu. Iwo ali adongosolo, owona mtima ndi osaledzera. Mikhalidwe imeneyi inali ya mtengo wapatali koposa mu kupita patsogolo kwa sosaite ya Kumadzulo mu zachuma ndi mayanjano, ndipo sikungakhale kunena kopambanitsa ku nena kuti Mboni za Yehova ziri pakati pa nzika zowongoka mtima ndi zachangu m’maiko a mu Afirika.”

M’mawu ofananawo, woyang’anitsitsa wina mu South America ananena ichi munyuzipepala ya editorial:

“Mboni za Yehova ali anthu ogwira ntchito kwambiri, owona mtima, ndi owopa Mulungu. Iwo ali osungirira ndipo okonda mwambo ndipo chipembedzo chawo chiri chozikidwa pa chiphunzitso cha Baibulo.”

Chotero pamene Mboni za Yehova siziyika chigogomezero pa chomwe mwachizolowezi chimadziwika monga uthenga wabwino wa mayanjano, iwo mokangalika amawonjezera ku zikondwerero za kumaloko mwa kuwathandiza ena kubweretsa miyoyo yawo m’chigwi rizano ndi malamulo apamwamba amakhalidwe abwino a Baibulo. (Aroma 12:1, 2) Chofunika kwambiri, iwo akuthandizanso anthu kulikonse kuyang’ana kuposa pa chisaweruziko ndi kusalingana kwa dongosolo la zinthu lomaipaipabe mofulumira iri ku dongosolo latsopano la zinthu lopangidwa ndi Mulungu, lomwe liri pafupi kudza.​—Chivumbulutso 21:5.

[Zithunzi patsamba 8, 9]

Mayankho ku Mavuto a Mayanjano ndi Ufumu wa Mulungu

Werengani mu Baibulo lanu malemba otsatirawa ndi kupeza chitonthozo mwakuona ndi motani mmene Mulungu akulonjezera kuchotsa mavuto a lerolino ndi mavuto amayanjano mu magawo otsatirawa:

Umoyo Yesaya 33:24; 35:5, 6; Chivumbulutso 21:4

Maphunziro Yesaya 11:9; Habakuku 2:14

Ntchito Yesaya 65:21-23

Chakudya Salmo 67:6; 72:16; Yesaya 25:6

Chilungamo Yesaya 11:3-5; 32:1, 2

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena