Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 1/15 tsamba 15-20
  • Dziko Lapansi Silinayenera Iwo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lapansi Silinayenera Iwo
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikhulupiriro cha Oweruza, Mafumu, ndi Aneneri
  • Ena a Chikhulupiriro cha Chitsanzo
  • Kuyang’anitsitsadwi pa Wokwaniritsa wa Chikhulupiriro Chathu
  • Sonyezani Chikhulupiriro Chozikidwa pa Chowonadi
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu N’cholimba Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Mumakhulupiriradi Uthenga Wabwino?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • “Tiwonjezereni Chikhulupiriro”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 1/15 tsamba 15-20

Dziko Lapansi Silinayenera Iwo

“Anaponyedwa miyala, anayesedwa, . . . ndipo dziko lapansi silinayenera iwo.”​—Ahebri 11:37, 38.

1, 2. Ndi pansi pa mikhalidwe yotani pamene mboni za Yehova za nthawi yakale zinasunga umphumphu, ndipo ndi motani m’mene zochita zawo zimayambukirira atumiki a Mulungu lero lino?

MBONI ZA YEHOVA za nthawi zakale zinasungirira umphumphu wawo kwa Yehova mosasamala kanthu za ziyeso zochuluka zomwe zinabweretsedwa pa iwo ndi mtundu waanthu osalungama. Mwachitsanzo, atumiki aYehova anaponyedwa miyala, ndi kuphedwa ndi lupanga. Iwo anachitidwa zoipa ndi kuvutitsidwa ndi nsautso. Komabe iwo sanagwedezeke mu chikulupiriro. Zowonadi, kenaka, monga momwe mtumwi Paulo ananenera “Dziko lapansi silinayenera iwo.”​—Ahebri 11:37, 38.

2 Zochitika za chikhulupiriro zouziridwa za umulungu za anthu a mu nthawi pamene chigumula chisanadze, makolo, ndi Mose zinafulumiza mboni za Yehova za makono kutumikira Mulungu mu chikhulupiriro. Koma bwanji ponena za ena otchulidwa mu Ahebri mutu 11 ndi 12? Kodi nchiyani chomwe tingapindule mwa kulingalira mbali za chikhulupiriro chawo?

Chikhulupiriro cha Oweruza, Mafumu, ndi Aneneri

3. Kodi ndi motani mmene zochitika zokhudza Yeriko ndi Rahabi zimasonyeza kuti chikhulupi riro chiyenera kusonyezedwa ndi ntchito?

3 Chikhulupiriro sichiri kokha kukhulupirira icho chiyenera kutsimikiziridwa ndi ntchito kapena machitidwe. (Werengani Ahebri 11:30, 31.) Pambuyo pa imfa ya Mose, chikhulupiriro chinabweretsera Aisrayeli chipambano chimodzi pambuyo pachinzake mu Kanani, koma ichi chinaitanira pa kuyesetsa kumbali yawo. Mwachitsanzo, ndi chikhulupiriro cha Yoswa ndi ena “malinga a Yeriko adagwa atazunguliridwa masiku asanu ndi awiri.” Koma “ndi chikhulu piriro Rahabi wadama uja sanaonongedwe pamodzi ndi osamverawo [nzika zopanda chikhulupiriro za m’Yeriko].” Nchifukwa ninji? “Popeza analandira ozonda [Aisrayeli] ndi mtendere,” kutsimikizira chikhulupiriro chake mwakuwabisa iwo kuchokera kwa Akanani. Chikhulupiriro cha Rahabi chinali ndi maziko olimba mu ripoti lakuti “Yehova anaumitsa madzi a m’Nyanja Yofiira” kuchoka pamaso pa Aisrayeli ndi kupatsa iwo chipambano pa mafumu awiri a Aamori Sihoni ndi Ogi. Rahabi anapanga kusintha koyenera kwa makhalidwe ndipo anadalitsidwa kaamba ka chikhulupiriro chake cha ntchito mwakusungidwa limodzi ndi a m’banja lake pamene Yeriko anagwa ndipo mwakukhala kholo lachikazi la Yesu Kristu.​—Yoswa 2:1-11; 6:20-23; Mateyu 1:1, 5; Yakobo 2:24-26.

4. Kodi nchiyani chimene zokumana nazo za Gideoni ndi Baraki zimagogomezera m’kusonyeza chikhulupiriro m’nthawi yangozi?

4 Chikhulupiriro chimasonyezedwa ndi chidaliro chotheratu pa Yehova mu nthawi ya mavuto. (Werengani Ahebri 11:32.) Paulo anavomereza kuti nthawi ikanaperewera ngati akadapitiriza kunena ponena za “Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita, Davide ndiponso Samueli ndi aneneri,” [ena, NW] amene zochita zawo zinapereka chitsimikiziro chachikulu cha chikhulupiriro ndi kudalira pa Yehova m’mikhalidwe yodetsa nkhawa. Mwakutero, ndi chikhulupiriro ndi khamu la amuna 300 okha, Woweruza Gideoni anapatsidwa mphamvu ndi Mulungu kuphwanya gulu lankhondo lamphamvu la Amidyani. (Oweruza 7:1-25) Olimbikitsidwa ndi mneneri wachikazi Debora, Woweruza Baraki wokhala ndi gulu la nkhondo la amuna oyenda pansi 10, 000 opanda zida zokwanira anapambana gulu lankhondo lamphamvu kwambiri la magareta a zitsulo 900 a Mfumu Yabini olamuliridwa ndi Sisera.​—Oweruza 4:1-5:31.

5. Kodi ndi mwanjira zotani mmene Samsoni ndi Yefita anasonyezera chikhulupiriro chomwe chinapereka chitsimikiziro cha chidaliro chotheratu pa Yehova?

5 Chitsanzo china cha chikhulupiriro mu masiku a nthawi ya oweruza a ana a Israyeli anali Samsoni, mdani wamphamvu wa Afilisti. Zowonadi, iye kenaka anakhala kapolo wawo wakhungu. Koma Samsoni anabweretsa imfa pa ambiri a iwo pamene anagwetsa mizati ya nyumbamu imene anali kupereka nsembe zazikulu kwa mulungu wawo wonyenga Dagoni. Inde, Samson anafa pamodzi ndi Afilisti amenewo, koma osati monga kudzipha kopanda chiyembekezo. Ndi chikhulupiriro iye anadalira pa Yehova ndipo anapemphera kwa iye kaamba kamphamvu yofunikira kubweretsa chilango pa adani a Mulungu ndi anthu ake amenewo. (Oweruza 16:18-30) Yefita, ku amene Yehova anapereka chipambano pa a Amoni, anasonyezanso chikhulupiriro chomwe chinapereka chitsimikizo cha chidaliro chake chotheratu pa Yehova. Kokha ndi chikhulupiriro choterocho kukanakhala kothekera kukwaniritsa chowinda chake kwa Mulungu mwa kupereka mwanawake wa mkazi ku utumiki wa Yehova monga namwali ku nthawi zonse.​—Oweruza 11:29-40.

6. Ndi motani mmene Davide anasonyezera chikhulupiriro chake?

6 Wodziwikanso kaamba ka chikhulupiriro chake anali Davide. Iye anali kokha mwamuna wachichepere pamene anapha chimphona cha Afilisti Goliati. ‘Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, mkondo, ndi nthungo,’ anatero Davide, ‘koma ine ndafika kwa iwe m’dzina la Yehova wa makamu.’ Inde, Davide anadalira pa Mulungu, anapha Mfilisti wokwezeka, ndi kupitirira kukhala mfumu ya nkhondo yamphamvu kumenya mu chikondwerero cha anthu a Mulungu. Ndipo chifukwa cha chikhulupiriro cha Davide, anali mwamuna wovomerezedwa m’mtima wa Yehova. (1 Samueli 17:4, 45-51; Machitidwe 13: 22) M’moyo wawo onse, Samueli ndi aneneri ena anasonyezanso chikhulupiriro chachikulu ndi chidaliro chotheratu pa Mulungu. (1 Samueli 1:19-28; 7:15-17) Ha ziri zitsanzo zabwino kwambiri chotani nanga kaamba ka atumiki a Yehova a mu nthawi yathu, achichepere ndi achikulire!

7. (a) Ndi ndani amene “mwa chikhulupiriro anagonjetsa maufumu omwe anali kulimbana nawo”?(b) Ndi ndani amene “anakwaniritsa chilungamo” mwa chikhulupiriro?

7 Ndi chikhulupiriro mwachipambano tingakumane ndi chiyeso chiri chonse chaumphumphu ndipo tingakwaniritse chiri chonse m’chigwirizano ndi chifuno chaumulungu. (Werengani Ahebri 11:33, 34.) Mu Kulozera ku zochitika za chikhulupiriro zowonjezereka, mwachiwonekere Paulo anali kulingalira za oweruza, mafumu, ndi aneneri Achihebri, popeza iye anali atagotchula kumene anthu amene wo. “Mwachikhulupiriro” oweruza monga ngati Gideoni ndi Yefita “anagonjetsa maufumu omwe anali kulimbana nawo.” Chimodzimodzinso Mfumu Davide, yemwe anagonjetsa Afilisti, Amoabu, Asuri, a Edomu, ndi ena. (2 Samueli 8:1-14) Ndiponso mwachikhulupiriro, oweruza olungama “anakhazikitsa chilungamo,” ndipo uphungu wolungama wa Samueli ndi aneneri ena unafulumiza chifupifupi kupewa kapena kusiya kupanga choipa.​—1 Samueli 12: 20-25; Yesaya 1:10-20.

8. Ndi lonjezo lotani limene Davide anapeza, ndipo kodi linatsogolera ku chiyani?

8 Davide anali m’modzi amene mwachikhulupiriro “analandira malonjezo.” Yehova anamulonjeza iye: “Mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.” (2 Samueli 7:11 16) Ndipo Yehova anasunga lonjezo limenelo mwa kukhazikitsa Ufumu Waumesiya mu 1914.​—Yesaya 9:6, 7; Danieli 7:13, 14.

9. Ndi pansi pa mikhalidwe yotani pamene ‘pakamwa pa mikango panatsekedwa mwa chikhulupiriro’?

9 Mneneri Danieli mwachipambano anakumana ndi chiyeso chaumphumphu pamene iye anapitirizabe kupemphera kwa Mulungu m’chigwirizano ndi mwambo wake wa tsiku ndi tsiku mosasamala kathu za chiletso chaufumu. Ndi chikhulupiriro chamsungiliri waumphumphu, Danieli mwakutero “anatseka pakamwa pa mikango” mwakuti Yehova anamusunga iye wa moyo mdzenje la mikango mu limene iye anaponyedwa.​—Danieli 6:4-23.

10. Ndani amene “analaka mphamvu yamoto” mwa chikhulupiriro, ndipo kodi nchiyani chomwe chikhulupiriro chofananacho chidzatithandiza ife kuchita?

10 Osunga umphumphu anzake a Danieli Achihebri Sadrake, Mesake, ndi Abedinego muchenicheni “analaka mphamvu ya moto.” Pamene anaopsezedwa ndi imfa m’ng’anjo yotentha kwambiri yamoto, iwo anauza Mfumu Nebukadinezara kuti, kaya Mulungu wawo akawapulumutsa iwo kapena ayi, iwo sadzatumikira milungu yake kapena kulambira fano lagolidi analiika. Yehova sanauzimitse moto m’ng’anjo imeneyo, koma anatsimikizira kuti siunawononge Ahebri atatu amenewo. (Danieli 3:1-30) Chikhulupiriro chofananacho chimatitheketsa ife kusunga umphumphu kulinga kwa Mulungu kumlingo wothekera angakhale ku imfa pamanja a adani.​—Chivumbulutso 2:10.

11. (a) Mwa chikhulupiriro, ndani amene “anapulumuka nsonga ya lupanga”? (b) Ndani amene“analimbikitsidwa” mwa chikhulupiriro? (c) Ndi ndani amene “anakhala olimbamtima mu nkho ndo” ndi “kupitikitsa magulu ankhondo achilendo”?

11 Davide “anapulumuka nsonga ya lupanga” ya amuna a Mfumu Sauli. (1 Samueli 19:9-17) Mneneri Eliya ndi Elisa nawonso anapulumuka imfa kuchoka ku lupanga. (1 Mafumu 19:1-3; 2 Mafumu 6:11-23) Koma ‘ndani amene kuchokera ku mkhalidwe wofooka analimbikitsidwa mwa chikhulupiriro’? Chabwino, Gideoni ana dzilingalira iye mwini ndi amuna ake kukhala ofooka kwambiri kupulumutsa Aisrayeli kuchoka kwa Amidyani. Koma iye “analimbikitsidwa” ndi Mulungu, yemwe anamupatsa chipambano​—ndipo ndi amuna 300 okha. (Oweruza 6:14-16; 7:2-7 22) “Kuchoka ku mkhalidwe wofooka” pamene tsitsi lake linametedwa, Samsoni “analimbikitsidwa” ndi Yehova ndi kubweretsa imfa pa Afilisti ambiri. (Oweruza 16:19-21, 28-30; yerekezani ndi Oweruza 15:13-19. ) Paulo angakhale atalingaliranso za Mfumu Hezekiya yemwe “analimbikitsidwa” kuchokera ku mkhalidwe wofooka mwa nkhondo ndipo angakhale mwakuthupi. (Yesaya 37:1-38:22) Pakati pa atumiki a Mulungu omwe “anakhala olimba mtima m’nkhondo” anali Woweruza Yefita ndi Mfumu Davide. (Oweruza 11:32, 33; 2 Samueli 22:1, 2, 30-38) Ndipo awo amene “anapitikitsa magulu ankhondo achilendo” anaphatikizapo Woweruza Baraki. (Oweruza 4:14-16) Zochitika zonsezi ziyenera kutitsimikizira ife kuti ndi chikhulupiriro tingapeze chipambano pa kukumanizana ndi chiyeso chamtundu uliwonse cha umphumphu wathu ndipo tingakwaniritse chiri chonse chomwe chiri m’chigwirizano ndi chifuno cha Yehova.

Ena a Chikhulupiriro cha Chitsanzo

12. (a) Ndi “akazi otani amene analandira akufa awo mwakuuka kwa akufa”? (b) Ndi mwanjira yotani m’mene chiukiriro cha amuna ena a chikhulupiriro chidzakhala “chabwinopo”?

12 Chikhulupiriro chimaphatikizapo kukhulupirira mu chiukiriro, chiyembekezo chomwe chimatithandiza ife kusunga umphumphu kulinga kwa Mulungu. (Werengani Ahebri 11: 35.) Chifukwa cha chikhulupiriro, “akazi analandira akufa awo mwa kuuka kwa akufa.” Mwa chikhulupiriro ndi mphamvu ya Mulungu, Eliya anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wa masiye wa ku Zarefati ndipo Elisa anaukitsa mwana wamwamuna wa mkazi wa ku Sunemu. (1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:17 37) “Koma amuna ena anazunzidwa koopsya [m’chenicheni, “kukwapulidwa ndi ndodo”] chifukwa sakanalola kuomboledwa ndi dipo lina lake, ndi cholinga chakuti iwo akalandire chiukiriro choposerapo.” Mwachiwonekere mboni za Yehova zosasonyezedwa mwa Malemba zimenezi zinamenyedwa ku imfa, kukana kulandira chipulumutso chofunikira kuti agonjere chikhulupiriro chawo. Chiukiriro chawo chidzakhala “chabwinopo” chifukwa chidzakhala chopanda chifuno chosapeweka cha kufa kachiwiri (monga ngati mmene analiri awo oukitsidwa ndi Eliya ndi Elisa) ndipo adzaoneka pansi pa ufumu wolamulira wa Yesu Kristu, “Tate Wosatha” yemwe dipo lake limapereka mwayi ku moyo wosatha pa dziko lapansi.​—Yesaya 9:6; Yohane 5:28, 29.

13. (a) Ndi ndani amene anazunzidwa mwa “kusekedwa ndi kumangidwa zingwe”? (b) Ndani amene anakumana “ndi kumangidwa ndi kuikidwa m’ndende”?

13 Ngati tiri ndi chikhulupiriro, tidzakhoza kupirira chizunzo. (Werengani Ahebri 11:36-38.) Pamene tikuzunzidwa, chingakhale chathandizo kukumbukira chiyembekezo cha chiukiriro mwa kuzindikira kuti Mulungu adzatithandiza ife monga m’mene anachitira ndi “ena [omwe] analandira chiyeso chawo [kapena, chiyeso chachikhulupiriro] mwa kusekedwa ndi kumangidwa zingwe, indedi, koposa chimenecho, ndi zingwe ndi ndende.” Aisrayeli “mopitirira anali kuseka aneneri ake, kufikira pamene mkwiyo wa Yehova unabwera pa anthu ake.” (2 Mbiri 36:15, 16) Ndi chikhulupiriro Mikaya, Elisa, ndi atumiki ena a Mulungu anapirira “kusekedwa.” (1 Mafumu 22:24; 2 Mafumu 2: 23, 24; Masalmo 42:3) “Kumangidwa zingwe” kunali kodziwika mu masiku a mafumu a Israyeli ndi aneneri, ndipo otsutsa “anamenya” Yeremiya, osati kokha kungomumenya monga woukira. “Zingwe ndi ndende” zingatikumbutse ife za zokumana nazo zake limodzi ndi za aneneri ena monga Mikaya ndi Hananiya. (Yere miya 20:l, 2; 37:15 1 Mafumu 12:11; 22:26, 27;2 Mbiri 16:7, 10) Chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro chofananacho, Mboni zaYehova zamakono zakhala zokhoza kupirira kuzunzika kofananako “kaamba ka chilungamo.”​—1 Petro3:14.

14. (a) Ndani amene anali pakati pa “oponyedwa miyala”? (b) Ndani amene mwina mwake“anachekedwa pakati”?

14 “Iwo anaponyedwa miyala,” anatero Paulo. Mwamuna mmodzi wa chikhulupiriro chotero anali Zekariya, mwana wa wansembe Yehoyada. Wokutidwa ndi mzimu wa Mulungu, iye analankhula motsutsa opanduka a Ayuda. Ndi choturukapo chotani? Ndi lamulo la Mfumu Yehoasi, achiwembu anamuponya iye miyala kufikira imfa mu mabwalo anyumba ya Yehova. (2 Mbiri 24:20-22; Mateyu 23:33-35) Paulo akuwonjezera: “Iwo anayesedwa, anachekedwa pakati.” Iye angakhale atalingalira za mneneri Mikaya monga m’modzi wa awo omwe “anayesedwa,” ndipo fuko lina losatsimikizirika la Chiyuda linati Yesaya anachekedwa pakati mkati mwa ulamuliro wa Mfumu Manase.​—1 Mafumu 22:24-28.

15. Kodi ndani amene “anachitidwa zoipa” ndi “kuyendayenda m’zipululu”?

15 Ena “anafa ndi lupanga,” monga, mwachitsanzo, aneneri a Mulungu anzake a Eliya “anaphedwa ndi lupanga” masiku a Mfumu yoyipa Ahabu. (1 Mafumu 19:9, 10) Eliya ndi Elisa anali pakati pa awo omwe anali ndi chikhulupiriro omwe “anayendayenda ovala zikopa zankhosa, ndi zikopa za mbuzi, nakhala osowa, osautsidwa, ochitidwa zoipa.” (1 Mafumu 19:5-8, 19; 2 Mafumu 1:8; 2:13; yerekezani ndi Yeremiya 38:6. ) Awo amene “anasokerera mumapululu ndi m’mapiri ndi m’mapanga ndim’mauna adziko” monga nkhole za chizunzo ayenera kuphatikiza osati kokha Eliya ndi Elisa komanso aneneri 100 omwe Obadiya anawabisa mu unyinji wa 50 m’mapanga, akumawapatsa iwo mkate ndi madzi pamene Mfumukazi Yezebeli wolambira mafano anayamba “kudula aneneri a Yehova.” (1 Mafumu 18:4, 13; 2 Mafumu2:13; 6:13, 30, 31) Ndi asungiriri aumphumphu a mtundu wotani nanga! Chosadabwitsa kuti Paulo akunena kuti: “Dziko lapansi [sosaite ya mtundu wa anthu osalungama] silinayenera iwo”!

16. (a) Kodi nchifukwa ninji mboni za Yehova za mu nthawi ya Chikristu chisanakhale sizinalandire “kukwaniritsidwa kwa lonjezo”? (b) Kwa mboni za Yehova za mu nthawi ya Chikristu chisanakhale, kukhala “wangwiro” kuyenera ku yerekezedwa ndi chiyani?

16 Chikhulupiriro chimatitsimikizira ife kuti mu nthawi yake Mulungu “adzakwaniritsa lonjezo” kwa awo omwe amamkonda iye. (Werengani Ahebri 11:39, 40.) Osunga umphumphu a Chikristu chisanakhale “anachitidwa umboni mwa chikhulupiriro chawo,” tsopano ziri m’zolembera za Malemba. Koma iwo sanalandire “kukwaniritsidwa kwa lonjezo” la Mulungu mwa chiukiriro pa dziko lapansi ndi ziyembekezo za moyo wosatha pansi pa ulamuliro wa Ufumu. Chifukwa ninji? “Kotero kuti iwo sayenera kupangidwa kukhala angwiro kokha kuchokeraku” otsatira odzozedwa a Yesu, kaamba ka amene “Mulungu anawakonzera kanthu koposa”​—moyo wosakhoza kufa kumwamba ndi mwawi wa kulamulira limodzi ndi Kristu Yesu. Mwachiukiriro chawo, choyamba pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu mu 1914, Akristu odzozedwa “amapangidwa kukhala angwiro” kumwamba Mboni za Yehova m’nthawi ya Chikristu chisanayambe zisanaukitsidwe pa dziko lapansi (1 Akorinto 15:50-57; Chivumbulutso 12:1-5) Kwa mboni zoyambirira zimenezo, kukhala “wangwiro” kuyenera kutanthauza kuukitsidwa kwawo pa dziko lapansi, ndipo;kenaka “kumasulidwa kuchokaku ukapolo kuchivundi,” ndi kupeza kwawo ungwiro waumunthu kudzera mu mautumiki a Wansembe Wamkulu Yesu Kristu ndi ansembe ake 144, 000 kumwa mba mkati mwa ulamuliro wake wa Zaka Chikwi.​—Aroma 8:20, 21; Ahebri 7:26; Chivumbulutso 14:1; 20:4-6.

Kuyang’anitsitsadwi pa Wokwaniritsa wa Chikhulupiriro Chathu

17, 18. (a) Kuti tipeze chipambano mu liwiro lathu kaamba ka moyo wosatha, ndi chiyani chomwe tiyenera kuchita? (b) Kodi ndi motani mmene Yesu Kristu aliri “wokwaniritsa wa chikhulupiriro chathu”?

17 Kukhala titakambitsirana za zochitika zaMboni za Yehova za m’nthawi pamene Chikristu chisanakhale, Paulo akuloza ku zitsanzo zoyambirira za chikhulupiriro. (Werengani Ahebri 12:1-3.) Ali magwero achilimbikitso otani kukhala ndi ‘mtambo waukulu wotere wa mboni wotizinga’! Ichi chimatifulumiza ife kuchotsa cholemera chiri chonse chomwe chingatsendereze kupita kwathu patsogolo kwa uzimu. Chimatithandiza ife kupewa chimo la kutaya kapena kusoweka chikhulupiriro ndi kuthamanga ndi chipiriro makani Achikristu kaamba ka moyo wosatha. Komabe, kuti tifikire chonulirapo chathu, tiyenera kuchita china chake. Koma kodi ndi chiyani chomwe icho chiri?

18 Ngati tikufuna kuti tipambane kaamba kamakani athu kaamba ka moyo wosatha m’dongosolo lazinthu latsopano la Mulungu, tikafunikira “kuyang’anitsitsa pa Magwero Enieni [kapena, Mtsogoleri Weniweni] ndi Mkwaniritsi wa chikhulupiriro chathu, Yesu.” Chikhulupiriro cha Abrahamu ndi osunga umphumphu ena omwe anakhala ndi moyo pambuyo pa uminisitala wa Yesu Kristu wa padziko lapansi anali opanda ungwiro, osakwanira, mchakuti iwo sanamvetsetse panthawiyo maulosi osa kwaniritsidwa onena za Mesiya. (Yerekezani ndi 1 Petro 1:10-12. ) Koma ndi kubadwa kwa Yesu, uminisitala, imfa, ndi chiukiriro, maulosi ambiri a Umesiya anakwaniritsidwa. Chotero chikhulupiriro m ’lingaliro laungwiro “chinafika” kudzera mwa Yesu Kristu. (Agalatiya 3: 24, 25) Kuwonjezerapo, kuchokera ku malo ake akumwamba Yesu akupitirizabe kukhala Wokwaniritsa wa chikhulupiriro cha otsatira ake, monga pamene iye anatsanulira pa iwo mzimu woyera pa Pentekoste wa 33 C.E. ndi kuvumbulutsidwa komapita mtsogolo kwa chikhulupiriro chawo chomakulakula. (Machitidwe 2:32, 33; Aroma 10:17; Chivumbulutso 1:1, 2; 22:16) Tiri oyamikira kwambiri chotani nanga kaamba ka “Mboni Yokhulupirika,” iyi “Mtsogoleri Weniweni” wa Mboni za Yehova!​—Chivumbulutso 1:5; Mateyu 23:10.

19. Kodi nchifukwa ninji Yesu ayenera ‘kulingaliridwa mosamalitsa’?

19 Popeza sichiri chapafupi kulaka zitonzo za osakhulupirira, Paulo akulimbikitsa: “Lingalirani mosamalitsa uyo [Yesu] amene wapirira kulankhula kotsutsa koteroko kochitidwa ndi ochimwa motsutsana ndi zabwino za iwo eni kuti inu musatope ndi kulefula miyoyo yanu.” Ndithudi, ngati tiika maso athu olunjikitsidwa pa “Mboni Yokhulupirika,” Yesu Kristu, ife sitidzatopa ndi kuchita chifuno chaumulungu.​—Yohane 4:34.

20. Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe mwaphunzi ra ponena za chikhulupiriro mwa kulingaliri Ahebri 11:1-12:3?

20 Kuchokera ku ‘mtambo waukulu wa mboni,’ tikuphunzira zambiri ponena za mbali za chikhulupiriro. Mwachitsanzo, chikhulupiriro chonga cha Abeli chimafulumiza chiyamikiro chathu kaamba ka nsembe ya Yesu. Chikhulupiriro chowona chimatipangitsa ife kukhala mboni zolimba mtima, monga momwe Enoke analankhulira uthenga wa Yehova molimba mtima. Monga Nowa, chikhulupiriro chathu chimatifulumiza ife kutsatira malangizo a Mulungu mosamalitsa ndi kutumikira monga ola likira achilungamo. Chikhulupiriro cha Abrahamu chimasindikiza pa ife kufunika kwa kumvera Mulungu ndi kudalira mu malonjezo ake, angakhale kuti ena a iwo sanakwaniritsidwe. Chitsanzo cha Mose chimasonyeza kuti chikhulupiriro chidzatitheketsa ife kukhala opanda mawanga ndi dziko iri ndi kuima kukhala anthu omvera a Mulungu. Zochitika zazikulu za oweruza, mafumu ndi aneneri a Israyeli zimatsimikizira kuti chikhulupiriro mwa Mulungu chingatithandize ife mkati mwa chizunzo ndi mayeso. Ndipo tiri oyamikira chotani nanga kuti chitsanzo chapamwamba kwambiri cha Yesu Kristu chimapangitsa chikhulupiriro chathu kukhala cholimba ndi chosagwedezeka! Chotero, ndi Yesu monga Mtsogoleri wathu ndi mu mphamvu ya Mulungu wathu, tiyeni tonse tipitirizetu kusonyeza chikhulupiriro chopirira monga Mboni za Yehova.

Kodi Mayankho Anu ndi Otani?

◻ Ndi machitidwe a mtundu wanji a mboni za Yehova za mu nthawi ya Chikristu chisanakhale omwe anatsimikizira kuti chikhulupiriro chimasonyezedwa mwakudalira kotheratu pa Mulungu mu nthawi yatsoka?

◻ Kodi ndi chifukwa ninji chinganenedwe uti ndi chikhulupiriro mwachipa mbano tingakumane ndi chiyeso chiri chonse chaumphumphu wathu?

◻ Ndi chitsimikiziro chotani chimene chiripo chakuti mwa chikhulupiriro tingapirire chizunzo?

◻ Ndi chifukwa ninji Yesu akutchulidwa kukhala “Wokwaniritsa wa chikhulupiriro chathu”?

◻ Kodi ndi ziti zomwe ziri mbali zina za mbali zambiri za chikhulupiriro?

Chithunzi patsamba 16, 17]

Davide anasonyeza chikhulupiriro mwa kudalira kotheratu pa Yehova. chitsanso chabwino kaamba ka anthu a Yehova lerolino!

[Chithunzi patsamba 18]

“Akazi analandira akufa awo mwa kuuka kwa akufa.” Chikhulupiriro mu chiukiriro chimatithandiza ife kusunga umphumphu kwa Yehova

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena