Kodi Mumadera Nkhaŵa Ponena za Ana Anu?
MUMATERODI! Matenda, kumwerekera kwa mankhwala, ndi kuchimwa ali kokha atatu a mavuto omwe inu mukudziwa kuti amapereka chiopsyezo kwa ana anu. Chiri chachibadwa kaamba ka makolo kukhala odera nkhawa ponena za ana awo—angakhale kudandaula ponena za iwo.
Mmenemo ndi mmene makolo ochuluka amamverera kudzera mu mbiri, monga momwe Baibulo limasonyezera. Kumbukirani kuti Yakobo anatumiza Yosefe kukazonda abale ake chifukwa Yakobo anali wodera nkhawa ponena za iwo. (Genesis 37:13, 14) Yobu, nayenso, anadandaula, angakhale kuti ana ake anali aakulu ndipo anali ndi mabanja awo awo. Iye anaganiza: “Kapena anachimwa ana anga, nachitira Mulungu mwano m’mtima mwawo.”—Yobu 1:4, 5.
Ndi chifukwa ninji, angakhale Yosefe ndi Mariya anali odera nkhawa ponena za mwana wawo wangwiro Yesu! Mu chenicheni, nthawi ina pamene Yesu anali wa zaka 12 zakubadwa, iwo anakhala odera nkhawa kwambiri ponena za iye, popeza anapeza kuti iye anali kusowa. Mosasamala kathu, mwana wawo Yesu anali wokhulupirika kwa iwo, ndipo analibe chifukwa cha kudzitonza iwo eni. Tiyeni tiwone kwenikweni chomwe chinachitika patsiku lokumbukirika limenelo ndi kulingalira ndi maphunziro otani amene makolo amakono angatenge kuchokera ku ilo.
Mwana Wotaika
Ngati inu muli kholo, mwina mwake mungadandaule ndi malingaliro a Mariya pamene iye mokalipira ananena kwa Yesu kuti: “Mwanawe, wachitiranji ife chotero? Atate wako ndi ine tinalikufunafuna iwe ndi kuda nkhawa.” Yosefe ndi Mariya anapatulidwa kuchoka kwa Yesu kwa masiku atatu. Mungayamikire nchifukwa ninji anali odera nkhawa ponena za kumene mnyamata wa zaka 12 anali.—Luka 2:48, Today’s English Version.
Nchifukwa ninji Yosefe ndi Mariya anamutaya Yesu? Wopereka ndemanga wotchuka kwambiri anasuliza iwo kaamba ka ichi, akumalemba: “Podziwa za chuma chomwe iwo anali nacho, kodi iwo akanakhala bwanji utali umenewo popanda kuyang’ana mu icho? Kodi matumbo ndi kufunsafunsa kofewa kwa mayi wake kunali kuti?” Koma kwenikwenidi, monga mmene tidzawonera, kuyang’ana kosamalitsa kwa nkhaniyi kumamasula Yosefe ndi Mariya kuliwongo lalikulu limenelo.
Chenicheni chiri chakuti Baibulo limasonyeza kuti Mariya anali mkazi wabwino ndi mayi wabwino. Mngelo Gabrieli, pamene anabwera kudzalosera za kubadwa kwa Yesu, ananena kuti iye wapeza “chisomo ndi Mulungu.” (Luka 1:28, 30) Iye mofunitsitsa analandira thayo limeneli lakubala mwana wamwamuna wapadera ameneyu, limodzi ndi thayo lolemetsa lomukulitsa ndi kumphunzitsa. Iye anali mkazi wodzichepetsa ndi wachikhulupiriro cholimba mwa Mulungu. Pambuyo pa kubadwa kwa Yesu, iye anachita chiri chonse chofunidwa ndi lamulo la Yehova, “monga mmene chalembedwera.”—Luka 1:38, 45-48; 2:21-23, 39.
Yosefe, mwamuna amene anakwatira Mariya ndi kukhala tate wolera wa Yesu, analinso mwamuna wabwino, wolungama yemwe anakambitsirana ndi angelo a Yehova pa nthawi zinayi. (Mateyu 1:19, 20; 2:13, 19, 22) Kumbukirani, Yehova anasankha Yosefe ndi Mariya kulera Mwana wake wa mtengo wapatali, wobadwa yekha. Kodi Mulungu akanachita chochepera kuposa kusankha awiri omwe akanachita bwino mkuthandiza mwana ameneyo kukula mu nzeru ya umulungu?
Komabe, makolo lerolino mosakaikira amadera nkhawa ponena za ana awo chifukwa cha mkhalidwe wangozi ndi woipa womwe ali nawo. Ndipo amadziwa kuti ana awo sali angwiro monga mmene Yesu analiri. Komabe, tingapeze phindu ku chitsanzo cha Yosefe, Mariya, ndi Yesu.