Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 3/1 tsamba 4-5
  • Mtsogolo Mwanu Njira Yabwinopo Yodziŵira Ponena za Imo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtsogolo Mwanu Njira Yabwinopo Yodziŵira Ponena za Imo
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Magwero Otsimikizirika a Chidziwitso
  • Ulosi Wokwaniritsidwa Lerolino
  • ‘Tukulani Mitu Yanu’
  • Kodi Nyenyezi Zingakuthandizeni Kudziwa Tsogolo Lanu?
    Galamukani!—2005
  • Okhulupirira Nyenyezi Anapita Kukaona Yesu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi “Anzeru a Kum’mawa” Anali Ndani? Kodi Mulungu Ndi Amene Anawachititsa Kuti Alondole Nyenyezi ya ku Betelehemu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Okhulupirira Nyenyezi Komanso Olosera Angatithandizedi Kudziwa Zam’tsogolo?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)——2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 3/1 tsamba 4-5

Mtsogolo Mwanu Njira Yabwinopo Yodziŵira Ponena za Imo

MU 1962 openda nyenyezi Achimwenye analosera za chiwonongeko cha dziko lonse “chifukwa cha kugwirizana kosawonekawoneka kwa mapulaneti asanu ndi atatu mu chizindikiro cha Capricorn.” Palibe chiri chonse chimene chinatuluka kwa icho. Posachedwapa, kumapeto kwa 1980, openda nyenyezi ambiri Achifrench anali ndi lingaliro lakuti amene anali prezidenti wa France, Giscard d’Estaing, adzasankhidwanso kwa nthawi yachiwiri. Koma wopikisana naye wake, Francois Mitterrand, anapambana masankho. Kulephera konga ngati uku kumatikumbutsa kuti kupenda nyenyezi sikumapereka njira yotsimikizirika yodziwira za mtsogolo.

Kodi iripo, ndiyeno, njira ina? Mwachitsanzo, kodi zoyesayesa za asayansi zakulosera za mtsogolo zidzakuthandizani inu? Chabwino, pano pali kulosera komwe kunapangidwa ndi McGraw Hill Institute (United States) mu 1970 ponena za zimene zidzachitika mu 1980: “Mankhwala othetsa kansa, zombo za mlengalenga zotsogozedwa ndi munthu kupita ku Mars ndi Venus, maziko okhazikika a mwezi, magalimoto akuyendera magetsi, kufalikira kwa makompyuta am’nyumba, kuthekera kwa kusankha chiwalo chogonanira cha mwana wanu, ndi matelevisioni ndi masinema a mbali zitatu.”

Kubwerera mbuyo mu 1970 asayansi a malo ophunzirira amenewa ananena kuti: “Njira iyi [yakulosera] ikulinga pa kufikira kunena za mtsogolo kodalirika mwalingariro la unyinji wa gulu la akatswiri.” Koma kulosera za mtsogolo kwa akatswiri amenewa kwatsimikizira kukhala konama m’mbali izi ndi zina zambiri, monga ngati mu ndale ndi zachuma.

Magwero Otsimikizirika a Chidziwitso

Ngati openda nyenyezi ndi asayansi sangathe kuwona ndi chitsimikiziro cha zomwe zidzachitika, kodi chimenecho chimatanthauza kuti chiri chosatheka kupeza chidziwitso chodalirika ponena za mtsogolo? Tisanataye mtima, tiyenera kuwona nchiyani chimene Baibulo limanena pa nkhaniyi. Kumbukirani, Yehova, Mlembi wa Baibulo, akulongosoledwa kukhala “wolalikira za chimariziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe.”​—Yesaya 46:10.

Mawu a Mulungu ali ndi maulosi ambiri. Kodi iwo amasiyana bwanji ndi zolosera za openda nyenyezi? Lotsatirari liri yankho la ntchito yokhala ndi mutu wakuti The Great Ideas (Maganizo Aakulu): “Koma malinga ndi nzeru yodziwa za mtsogolo ya munthu wokhoza kufa, aneneri Achihebri akuwoneka kukhala anali apadera. Mosiyana ndi olota achikunja kapena odziwa za mtsogolo, . . . iwo sakafunikira kugwiritsira ntchito luso kapena zipangizo kaamba ka kulowerera mu chinsinsi cha umulungu. . .Ku mbali yokulira mawu awo aulosi, mosiyana ndi awo a olosera, akuwoneka kukhala atanthauzo. Komabe zikuwoneka kuti cholinga chikuwoneka kukhala chakuvumbulutsa, osati kubisa, makonzedwe a Mulungu pa zinthu zimenezo monga momwe lye Mwini amafunira anthu kuwoneratu njira ya kukoma mtima kwa Mulungu.”

Monga chitsanzo cha ichi, chidziwitso chochuluka ponena za Yesu chinalembedwa mu Baibulo mazana ambiri iye asanabadwe. Kunaloseredwa kuti iye adzabadwira mu tauni ya Betelehemu ndi banja la nzera wa Jese, atate wa Mfumu Davide. (Mika 5:2; Yesaya 11:1, 10) Malemba ananeneratunso kuti iye adzaphedwa pa mtengo koma palibe liri lonse la mafupa ake lidzaswedwa, monga momwe unaliri mwambo ndi kupha koteroko. Tsatanetsatane ameneyu anatsimikizira kukhala wowona, ndipo izo ziri kokha zitsanzo zochepa za zimene wophunzira Baibulo mmodzi analingalira kukhala zoposa maulosi 120 omwe anakwaniritsidwa mwa Yesu.​—Masalmo 22:16, 17; 34:20.

Ulosi Wokwaniritsidwa Lerolino

Kuwonjezerapo, Baibulo liri ndi maulosi omwe amaloza ku tsiku lathu. Tiyeni tilingalire umodzi wa maulosi ofunika kwambiri amenewa. Iwo ukulongosola ndandanda ya zochitika zomwe zidzasonyeza nyengo mwamsanga patsogolo pa kulowerera kwa Ufumu wa Mulungu mu zochitika za pa dziko la pansi. Zochitika zimenezi zimaphatikizamo nkhondo za dziko, zivomezi, miliri, njala, ndi kuwonjezeka kwa kusaweruzika. Kodi kuipitsitsa kwa zinthu zimenezi sikunakhale kowonekera mu mbiri ya dziko mkati mwa zana lathu la 20?​—Mateyu 24:3, 7-14; Luka 21:7, 10, 11; 2 Timoteo 3:1-5.

Yesu analongosola kuti kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kudzalengeza kufika kwa Ufumu wake monga mmene motsimikizirika kuwoneka kwa mphukira pa mitengo kumalengeza kufika kwangululu. Iye ananena mwachindunji kuti izo zidzakwaniritsidwa mu mbadwo umodzi wokha. Mbali zonse za chizindikiro, kuphatikizapo tsatanetsatane wotchulidwa pamwambapa, wakwaniritsidwa mmaso athu kuyambira 1914.a Ife chotero tingakhale ndi chidaliro chotheratu kuti Ufumuwo udzachita kanthu posachedwapa.​—Luka 21:29-33.

Mbali ina yoloseledwa kaamba ka nthawi ino inali “chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru.” (Luka 21:25) Tsopano, kodi nchifukwa ninji pali chozizwitsa chotero lerolino ndi kupenda nyenyezi ndi mbali zina za kuwombeza? Nyuzipepala ya Chifrench Le Monde Dimanche ikuyankha kuti: “Atakumanizana ndi chiwopsezo, anthu sadzaima pa chiri chonse kupeza chirimbikitso. Kufufuza kwa malo a mizimu kumapereka chitonthozo chokulira kaamba ka kuyesayesa kochepera, ndipo mu mbadwo uno wa sayansi yokhala ndi zokwaniritsa zowopsa monga ngati luso la nyukiliya ndi kuphatikiza kwa magene anthu amayesedwa kuthamangira ku zosadziwika ndi zosalondoloka, kuyesera kuzindikiranso tanthauzo la moyo.” Chotero sitiyenera kudabwitsidwa pa kufala kwa chikondwerero mu kuwombeza, monga ngati kupenda nyenyezi. Iri imodzi ya zizindikiro za ‘chisauko” chomwe anthu akukumanizana nacho lero lino m’kukwaniritsa ulosi wa Yesu.

‘Tukulani Mitu Yanu’

Kodi nchiyani chimene Akristu ayenera kuchita pamene iwo awona zinthu izi? Kupereka njira kaamba kamantha, monga anthu owazinga iwo? Yesu anapereka uphungu wotsatirawu: “Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira.”—Luka 21:28. Kodi mungakonde kudziwa ponena za mtsogolo mwanu mwatsatanetsane? Chotero tengani nthawi ya kusanthula Baibulo mozama “ndi kuyesa mizimu ngati ichokera mwa Mulungu.” (1 Yohane 4:1) Mungachite ichi ndi thandizo la magazini ya Nsanjaya Olonda, yomwe mokhazikika imalongosola maulosi a Baibulo ndi kulongosola kugwira ntchito kwawo mu tsiku lathu. Chotero, pamene mukukhala okhutiritsidwa kuti mapeto a dziko lovutidwa liripoli ali pafupi, inunso, mudzakhoza “kutukula mutu wanu”. Mudzaphunziranso chimene muyenera kuchita kuti musangalale ndi madalitso a Ufumu wa Umesiya, womwe posachedwapa udzalowerera zochitika zadziko kaamba ka phindu la anthu onse oongoka mtima.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka tsatanetsatane ponena za kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kuyambira 1914, onani mutu 7 wa bukhu la True Peace and Security​—How Can You Find It? (Mu Chingelezi) lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Bokisi patsamba 5

“Ndipo chizindikirocho .  .. Chifika”

Kodi nchiyani chimene chiri cholakwika ndi kupita kwa mlauli kapena kuwerenga ponena za nyenyezi yanu mu nyuzipepala? Kodi ichi sichili chosangulutsa chopanda upandu chabe?’

Baibulo silimasamalira nkhaniyo mopepuka chotero. Mchenicheni, limatiika ife pa chinjirizo ponena za mizimu ya thupi ndi alauli. Mu bukhu la Deuteronomo, Yehova anapereka chenjezo lotsatirali: “Akauka pakati pa inu mneneri, kapena wakulota maloto . . . nakakupatsani chizindikiro kapena chozizwa; ndipo chizindikiro kapena chozizwa adanenachi chifika, ndi kuti, Titsate milungu yina,’. . . musamamvera mawu a mneneri uyu, kapena wolota maloto uyu.”​—Deuteronomo 13:1-3.

Zindikirani kuti Malembo sakufunsa chenicheni chakuti zina za zonenedweratu za mizimu ya kuthupi ndi openda nyenyezi zingakhale zoona. M’malo mwake, Baibulo likutichenjeza ife kuti, ngati zonenedweratu zimenezi ziri zozikidwa pa zizindikiro zakumwamba kapena njira zina za ulauli, izo zimachokera kwa ziwanda, ziri zonyenga, ndipo zingatembenuze anthu kuchoka kwa Mulungu wowona.​—Onani Machitidwe 16:16-18.

Kupereka chisamaliro kwa openda nyenyezi kapena kwa ena omwe amadzinenera kukhala odziwa kunenera za mtsogolo kuli kudziika pa ngozi kwa kupeza mavuto oopsa kwambiri akuuzimu ndi kuthera mu ukapolo ku “auzimu achoipa m’zakumwamba.” (Aefeso 6:12) Mwakutero, kufunsira anthu oterowo kuli kulingaliridwa ndi Mulungu kukhala chimo lalikulu kwambiri; awo amene amachita zinthu zoterozo ali onyansa m’maso mwake ndipo iwo sadzalowa mu Ufumu wake.​—Chivumbulutso 22:15.

Icho chotero chiri kaamba ka ubwino wathu kuti Baibulo limatiika ife pa chinjirizo motsutsana ndi kupenda nyenyezi ndi njira zina za kuwombeza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena