Anthu Achimwemwe—Nchifukwa Ninji?
AKRISTU OWONA lerolino ali anthu achimwemwe. Indedi, timatumikira “Mulungu wachimwemwe,” (1 Timoteo 1:11) lye amatipatsa ife mzimu wake, ndipo chipatso cha mzimu umenewo chiri chimwemwe.—Agalatiya 5:22.
Chimwemwe chozama chimenecho chiri chokhazikika ndipo chimapirira zitsenderezo. Mwachitsanzo, Yesu Kristu anali pansi pa kupweteka kwa kupachikidwa ndi kunyazitsidwa ndi kuphedwa monga wochita mwano. Komabe, “kaamba ka chikondwerero chomwe chinali patsogolo pake iye anapirira mtengo wozunzirapo.” (Ahebri 12:2) Yesu anadziwa kuti kutsogolo kwake kunali nthawi yabwino ndi mwawi wapadera mchigwirizano ndi utumiki wake kwa Yehova. Kuyang’anitsitsa pa mwawi wapadera wa mtsogolo umenewu kunamuthandiza iye kusunga chimwemwe pakati pa kuvutika.
Yesu amafuna ophunzira ake kukhalanso achimwemwe. Iye anati: “Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe changa chikhale mwa inu. Ndikuti chimwemwe chanu chidzale.” (Yohane 15:11) Ichi chatsimikizira kukhala chowona ponena za Mboni za Yehova lerolino. Pali zifukwa zambiri zakuti tiri anthu achimwemwe. Timadziwa chowonadi, chomwe chimatimasula ife kuchoka ku kugwidwa kwa mizimu ndi zikhulupiriro zabodza za chipembedzo. (Yohane 8:32) Kenaka, kachiwirinso, timadziwa kumene tiri mu nyengo ya nthawi ndi kusangalala mu chiyembekezo cha chipulumuko chodzapezedwa posachedwapa. (Luka 21:28) Tirinso ochinjirizidwa kuchokera ku mavuto ambiri—pakati pa iwo matenda opatsirana mwa kugonana—okumanizana ndi awo amene samatsatira makhalidwe abwino ozikidwa mu Baibulo. Timasangalala ndi mayanjano abwino koposa ndi anthu okondweretsedwa kuchita chifuniro cha Mulungu. Ndipo, inde, tiri ndi mwawi waukulu wa padera wa kugawana mu kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu ndi kupanga ophunzira a awo onga nkhosa.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Koma pamene ichi chiri chowona ponena zaMboni za Yehova monga onse, bwanji ponena za inu mwini? Nchifukwa ninji chinganenedwe kuti muli ndi chifukwa cha kusangalala limodzi ndi gulu lonse la anthu a Yehova?
Kupeza Chimwemwe mu Ntchito Yolalikira
Koma ena amachipeza icho kukhala chovuta kudzilowetsa mu ntchito yolalikira ya kunyumba ndi nyumba. Mwina mwake iwo sali omasuka ponena za kufikira alendo ndi kuyambitsa kukambitsirana. Kapena iwo mwina mwake angadzimve kukhala osayenerera pamenezibwera ku kuphunzitsa ena. Kodi mumadzimvamwanjira imeneyo nthawi zina? Ngati ndi tero, ndimotani mmene mungapezere chimwemwe mu ntchito ya kulalikira?
Poyambirira, khalani ndi kawonedwe kabwino. Anthu ambiri angakhale osangalatsidwa kulembedwa ntchito ndi munthu wina wokondwereredwa kapena wandale wotchuka kwambiri. Koma ndi chimwemwe chowonjezereka chotani chimene tiyenera kuchipeza kukhala tikugwiritsiridwa ntchito ndi “Mfumu ya nthawi zonse,” Yehova Mulungu iye mwini!—1 Timoteo 1:17.
Kumbukirani, kachiwirinso, kuti iyi iri ntchito yomwe siidzabwerezedwanso. Tangoganizirani! Angelo iwo enieniwo akuwongolera ndi kutsogoza Akristu pano pa dziko lapansi mu zoyesayesa zawo za kupeza onga nkhosa. (Chivumbulutso 14:6) Kodi ichi sichimabweretsachimwemwe ku mtima wanu?
Kupeza Chimwemwe Mkuwonjezeka kwa Ufumu
Chifukwa china chakukhalira ndi kawonedwe koyenera mu ntchito ya kulalikira ndi chotulukapo chabwino chimene iyo ikukhala nacho. Baibulo linaneneratu: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ine Yehova ndidzafulumiza ichi mu nthawi yake.” (Yesaya 60:22) Lonjezo limenelo la Yehova lakhaladi lowona mu nthawi zaposachedwa. Mwachitsanzo, mkati mwa chaka cha utumiki cha 1986, 225, 868 anabatizidwa mchisonyezero mkudzipatulira kwawo kwamoyo wonse kwa Yehova Mulungu. Panali chiwonjezeko cha 6. 9 peresenti mu avereji ya chiwerengero cha ogawana mu kubukitsa chowonadi cha Baibulo kwa ena.
Mosakaikira kuwonjezeka kumeneko kuli kowonekera mu mpingo wanu kapena dera lanu. Atsopano akubwera ku misonkhano ndi kupanga kusintha koyenera mu miyoyo yawo koterokuti akhale okhoza kutumikira Mulungu. Kodi ichi sichimaloza ku chenicheni chakuti ntchito yolalikira iri ndi dalitso la Yehova? Kukhala ndi mbali mu chiwonjezeko chimenechi chotero chingakhale magwero achimwemwe chachikulu kwa inu. Zowonadi, inu mwaumwini mungakhale munaphunzira ndi wina wake kufikira kunsonga ya kubatizidwa kwake. Koma sitingatenge mphoto kaamba ka kumubweretsa wina wake mu chowonadi mu njira iri yonse. ‘Mulungu akulitsa,’ anatero Paulo. (1 Akorinto 3:6-9) Ziwalo zonse za mpingo ziri ndi mbali mkuthandiza achatsopano. Motani? Mwakukhalapo pa misonkhano, kupereka ndemanga, mwachiyanjo kuwapatsa moni achatsopano, ndi kudzitsogoza iwo eni mu njira imene imachipanga chowonadi kukhala chokhumbirika.
Komabe, chimwemwe chokulira chingapezedwe ngati inu muli ndi kugawana kwa chindunji mu ntchito yolalikira kunyumba ndi nyumba ndi ntchito ya maphunziro a Baibulo. Chaka chapita, pa avereji, maphunziro a Baibulo 2, 726, 252 anatsogozedwa pa mlungu. Bwanji osapanga kuyesayesa kowonjezereka kugawana mu ntchito yosangalatsa imeneyi? Perekani phunziro la Baibulo kwa wina wake amene mumamudziwa, kapena mnansi wanu kapena wina wake amene munamugawirako mabuku. Funsani Yehova kaamba ka thandizo mkuwapeza anthu onga nkhosa.
Kulaka Zipsinjo ku Chimwemwe
Komabe, ngati munthu adzimva kukhala wosayeneretsedwa kuphunzitsa ena, ichi chingakhale chipsinjo chenicheni ku kupeza chimwemwe mu utumiki wa m’munda. Kumbukirani, ngakhale kuli tero, kuti “kukhala kwathu oyeneretsedwa kuphunzitsa kumachokera kwa Mulungu.” (2 Akorinto 3:5) Ndipo kudzera mwa gulu lake Yehova akupereka zothandizira zabwino Zambiri kutithandiza ife kuyeneretsedwa monga aminisitala okhutiritsa.
Choyambirira, pali ambiri pakati pa ife omwe akhala akutumikira Yehova kwa nthawi yaitali ndipo ali ndi chizolowezi mu utumiki wa m’mu nda. Tingaphatikizane ndi aminisitala achizolowezi amenewa mu ntchito yawo ndi kuphunzira kuchokera kwa iwo. Kuwonjezerapo, mwezi uli wonse malingaliro abwino amapezeka mu Utu miki Wathu wa Ufumu. Kenaka pali chofalitsidwa cha Reasoning From the Scriptures, chomwe chiri ndi chuma cha chidzwitso chakuthwetsa maluso athu akulalikira. Gwiritsirani ntchito zida izi ndi kukonzekera bwino lomwe kaamba ka utumiki wa m’munda. Gani zirani za njira zatsopano ndi zosangalatsa za kudzidziwitsira inu mwini pakhomo. Kapena lingalirani njira zosiyana za kukokera mwini nyumba mkukambitsirana. Pamene mukhala wokhutiritsa kwambiri m’munda, mthumanzi yariu ndi chimwemwe chanu mu kulalikira mo sakaikira chidzawonjezeka.
Utumiki uli wosangalatsa kwambiri pamene muli wokhoza kulankhula kwa anthu. Mu maga wo ena ichi movomerezeka chiri vuto. Kodi mungakonze kugawana mu utumiki wa m’munda pa nthawi imene anthu ambiri ali kunyumba, monga ngati madzulo? Ambiri amapeza kuti kuchita chimenechi kuli kokhutiritsa kwambiri. Inunso mungatenge kulimba mtima ndi kulankhula ndi anthu lmlikonse kumene mungawapeze—mukhwalala, pamene mukhala pa mabenchi mu paki, kutsuka magalimoto awo. Kumbukirani kuti anthu akufunikira chowonadi ndipo kuti miyoyo iinazungulira pa icho. Ichi chingakuthandizeni inu kukufulumizani kulaka zikhoterero za kulinga ku manyazi. Pamene chiri chowona kuti khamu lalikulu la anthu silidzavomereza mwa chiyanjo, awo amene amatero amabweretsa chimwemwe chachikulu.
Komabe, thandizo limodzi lalikulu kwambiri ku kusunga kwathu chimwemwe liri pemphero Funsani Yehova kaamba ka mzimu wake kukupatsani mphamvu ndi kukulimbikitsani inu Paulo anati: “Ndikhoza zonse mwa iye wondipatsa mphamvuyo.” (Afilipi 4:13) Tingadzimve mwanjira yofananayo, nafenso, pamene tiku phunzira kudalira pa Yehova mokulira.
Kupirira monga Anthu Achimwemwe
Anthu ambiri samayamikira ntchito yathu. Yesu anali wodziwa kuti umu ndi mmene zidzakhalira. Chotero pamene anatumiza otsatira ake kukalalikira, iye anawachenjeza iwo: “Ndipo yemwe sadzalandira inu kapena kusamva mawu anu, pamene mulikuturuka m’nyumbamo kapena m’mudzimo sansani pfumbi m’mapazi anu. . . . Tawonani, ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa afisi [mimbulu]; chifukwa chache khalani ochenjera monga njoka, ndi owona mtima monga nkhunda.” Yesu ananenenso: “Tsitsi lonse la m’mutu mwanu lawerengedwa. Chifukwa chake musaopa.”—Mateyu 10:11-16, 30, 31.
Mawu amenewa amatithandiza ife kupirira mwachimwemwe. Amatithandiza ife kuzindikira kuti pamene tikumanizana ndi anthu amene sayamikira zoyesayesa zathu m’malo mwawo, ife tikulidziwikitsabe dzina la Yehova; tikumulemekezabe iye. (Masalmo 100:4, 5) Mosangalatsa, nthawi zina eni nyumba amene amakana kutsegula chitseko angamvedwe akunena kwa ena: “Zinali Mboni za Yehova.” Inde, tisananene mawu anthu, dzina la Yehova lakwezedwa, ndipo anthu alandira mwawi wakulandira kapena kukana chowonadi. (Mateyu 25:31, 32) Chotero ngakhale magawo osavomereza mwachimwemwe angapiriridwe.
Pambali pa icho, sitidziwa nkomwe ndi liti pamene anthu oterowo angasinthe kawonedwe kawo ka zinthu. Tsiku lina, mkazi wina yemwe anabweza mlongo Wachikristu pakhomo pake kwa nthawi zochulukira anamufunsa mlongoyo ngati anali ndi mabuku ena atsopano. Mlongoyo anali wodabwitsidwa ndi kupereka ndemanga kuti mkaziyo anali asanalandirepo nkale lonse bukhu la Baibulo chiyambire. Mkaziyo analongosola kuti mwamuna wake amagwira ntchito ndi mwamuna wina yemwe akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Iye anamupatsa iye ndi mwamuna wake chofalitsidwa chimodzi cha Watch Tower Society. Kaamba ka kufunitsitsa kudziwa, mkaziyo anachiwerenga icho ndipo anazindikira uthengawo monga chowonadi Chotero iye pa nthawi yomweyo anagamulapo kuti nthawi yotsatira Mboni idzaitana pa nyumba yake adzamulola iye kulowa. Phunziro la Baibulo linayambidwa, ndipo mkaziyo pambuyo pake anakhala Mboni yodzipereka ya Yehova!
Ife chotero tiri ndi mwawi waukulu—mwawi wachimwemwe—wa kulalikira uthenga wokha wa chiyembekezo mu dziko. Ndipo ntchito ya kulalikira iri ntchito imene Mulungu watipatsa ife mkati mwa masiku ano amapeto. Iyenera kuchitidwa mapeto asanafike. (Mateyu 24:14) Ndi ku utali wotani umene iyo idzakhalira asanafike mapeto a dongosolo loipa la zinthu la Satana? Tikudziwa kuti mapeto sadzafika mochedwa. (Yerekezani ndi Habakuku 2:3. ) Pa nthawi ino, padakali nthawi kaamba ka ena kuphunzira chowonadi. Tiyeni ife titenge mwawi wa nthawi iyi yotsalira ndipo mwachangu kukhala pa ntchito yathu yakulalikira. Ndipo tiyeni ife tikhale ndi kawonedwe kabwino, kumagwira ntchito molimbika kotero kuti ‘tidzipulumutse ife eni ndi awo akumva ife.’ (1 Timoteo 4:16) Mkuchita tero, tidzakhalabe anthu achimwemwe kugawana mu chiwonjezeko cha Ufumu.
[Chithunzi patsamba 27]
Ntchito yathu yolalikira iri magwero achimwemwe chenicheni—ngakhale pamene anthu samavomereza ku uthenga wa Ufumu