Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 4/1 tsamba 4-7
  • Mmene Tingamudziwire Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Tingamudziwire Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Baibulo​—Bukhu la Mulungu
  • Kumudziwa Mulungu mwa Thithithi
  • Kuwerenga Baibulo Kumatibweretsa Ife Kufupi ndi Mulungu
  • Mapindu Aakulu Kuchokera ku Kudziwa Mulungu
  • Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kudziwa Bwino Mulungu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kodi Mulungu Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Kodi N’zothekadi ‘Kuyandikira Mulungu’?
    Yandikirani Yehova
  • Muziphunzira Zambiri Zokhudza Yehova Poona Chilengedwe Chake
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 4/1 tsamba 4-7

Mmene Tingamudziwire Mulungu

ANTHU ena amakhulupirira kuti Mulungu ali paliponse. Ali mu nyenyezi ndi mapulaneti, mu utawaleza, m’mapiko ambalame, mu udzu. Komabe, Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu, monga munthu ali ndi malo okhazikika. Mfumu ya nzeru Solomo inanena mwa pemphero kwa Mulungu: “Pamenepo mverani inu pemphero ndi pembedzero lawo m’Mwamba mokhala inumo, ndi kulimbitsa mlandu wawo.” Ndipo mu bukhu la Baibulo la Yesaya, Mulungu iye mwini anagwidwa mawu akunena kuti: MKumwamba ndi mpando wanga wachifumu.”​—1 Mafumu 8:49; Yesaya 66:1.

Ngakhale kuti Mulungu iye mwini sali mzolengedwa zake, mikhalidwe ya umunthu wake inawonetsedwa mu izo. Anatero mtumwi Paulo pa Aroma 1:20: “Pakuti chilengedwere dziko lapansi zawoneka bwino zosawoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa.” Wamasalmo Davide mofananamo analemba: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo liwonetsa ntchito ya manja ake. Usana ndi usana uchurukitsa mawu, ndipo usiku ndi usiku uwonetsa nzeru.​—Masalmo 19:1, 2.

Inde, yang’anani kunja usiku wanyenyezi ndi kulingalira kwakamphindi nzeru yaikulu ndi mphamvu yofunikira kulenga ndi kusunga dziko lathu! (Yerekezani ndi Yesaya 40:26.) Indedi, chilengedwe chiri ndi magwero osatopetsedwa achidziwitso ponena za umunthu wa Mulungu. Ndipo munthu mokwanira sangazindikire ukulu wa umboni umene iwo umafuula ponena za mikhalidwe ya Mulungu ndi ulemerero. Bukhu la Yobu limatikumbutsa ife: “Tawonani! awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za iye ndi chinong’onezo chaching’ono.” (Yobu 26:14) Pali mwambo wakale wa chiSwedish: ”Mbuye ali wamkulu kuposa ntchito zake.’ Mofananamo, ngati chilengedwe chiri chachikulu, Mulungu ayenera kukhala wokulirapo; ngati chilengedwe chimasonyeza nzeru, Mulungu ayenera kukhala wanzeru yoposerapo; ngati chilengedwe chimasonyeza mphamvu, Mulungu ayenera kukhala wamphamvu koposa!

Baibulo​—Bukhu la Mulungu

Chilengedwe motero chimapereka chidziwitso chambiri ponena za Mulungu. Komabe, kodi kuphunzira kwa chilengedwe kungakuuzeni inu dzina la Mulungu? Kodi iko kungavumbulutse nchiyani chiri chifuno chachilengedwe kapena nchifukwa ninji iye walola kuipa kupitirirabe? Mayankho ku mafunso amenewa amafunikira koposa kuphunzira ntchito ya kuthupi ya Mulungu. Mwamwawi, Mulungu anawona ku icho kuti chidziwitso choterocho ponena za iye chaikidwa mu Baibulo.

Mmenemo Mulungu sasonyezedwa konse kukhala monga wosawoneka, nzeru yosatheka kuilongosola kapena mphamvu yokhala ponseponse kapena nyonga. Pa Machitidwe 3:19 timawerenga ponena za “munthu wa Yehova.” Pamene Mwana wake, Yesu Kristu, anawukitsidwa kuchokera kwa akufa, Baibulo limanena kuti iye analowa m’mwamba momwe, kukawonekera kwa munthu [“pamaso”], pa Mulungu.” (Ahebri 9:24, Kingdom Interlinear) Motsimikizirika, Yesu sanamutchule Mulungu kukhala mphamvu yaikulu, nzeru yosalongosoleka, kapena liwu lina lake losonyeza chosawoneka pamene iye analankhula ponena za iye ndi kupemphera kwa iye. Mosiyanako, iye kawirikawiri anamutchula iye Atate wakumwamba, liwu lovumbulutsa unansi wake wathithithi ndi Mulungu.​—Mateyu 5:48; 6:14, 26, 32.

Mulungu chotero sali “Chinthu china chake” chopanda dzina mmalo mwake iye ali munthu wokhala ndi dzina. Amatero Masalmo 83:18: “Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” Zowona, Baibulo limagwiritsiranso ntchito maina kapena mawu olongosola kaamba ka Mulungu: “Wamphamvuyonse,” “Mfumu yosatha,” “Mpulumutsi,” “Mbusa,” “Nkhalamba yakale lomwe,” “woyang’anira,” “Mlangizi Wamkulu,” “Wopanga wamkulu,” “Thanthwe.” (Rute 1:20; 1 Timoteo 1:17; Yesaya 43:11; Masalmo 23:1; Danieli 7:9, 13, 22; 1 Petro 2:25; Yesaya 30:20; 54:5; Deutronomo 32:4) Mawu amenewo, ngakhale kuli tero, amavumbulutsa mbali zambiri zaumunthu wa Mulungu, monga ngati mphamvu yake, kudera nkhawa kwake kwa chikondi kaamba ka anthu ake ndi nzeru yake yosatha.

Chifukwa Mulungu ali munthu, iyenso ali ndi zimene amakonda ndi zimene sakonda​—ngakhalenso malingaliro. Baibulo limatiuza ife kuti iye amakonda anthu ache (1 Mafumu 10:9), kusangalala m’ntchito yake (Masalmo 104:31), kudana ndi kulambira mafano (Deutronomo 16:22), ndi kupwetekedwa chifukwa cha kuipa. (Genesis 6:6) Pa 1 Timoteo 1:11 iye akutchedwa “Mulungu wachimwemwe.”

Kumudziwa Mulungu mwa Thithithi

Zowona, palibe maganizo a munthu amene ali ndi malo okwanira kusunga zovumbulutsidwa zonse zaumunthu wa Mulungu. “Ha! kuya kwake kwa ulemerero ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka! Pakuti ‘anadziwitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wake ndani?’” (Aroma 11:33, 34) Mosasamala kanthu za zimenezo, kwa amene ali ndi chikhulupiriro, Mulungu angakhale weniweni monga munthu wina. Baibulo limatiuza ife kuti “Nowa anayenda ndi Mulungu wowona,” monga ngati kuti Yehova anali pambali pake. (Genesis 6:9) Mulungu analinso weniweni kwa Mose chakuti chinali ngati kuti iye anali “kuwona wosaonekayo” (Ahebri 11:27) Ndipo ponena za Abrahamu chinanenedwa kuti iye anali “bwenzi la Yehova.”​—Yakobo 2:23.

Komabe, Mulungu mwaumwini anadzivumbulutsa iye mwini kwa Nowa, Abrahamu ndi Mose. ‘Chabwino, ngati Mulungu angadzivumbulutse iye mwini kwa ine mu njira ya umwini imeneyo,’ ena angatero, ‘iye angakhale weniweni kwa inenso.’ Kumbukirani, ngakhale kuli tero, Nowa, Abrahamu ndi Mose sanali ndi Baibulo. Iwo sanadziwe ponena za Yesu Kristu ngakhale za unyinji wa maulosi amene iye anakwaniritsa. Monga chotulukapo chake, zonse zimene Yesu anavumbulutsa ponena za Mulungu zinali zosadziwika kwa iwo. Pansi pa mikhalidwe yotero, chinali choyenerera ndi chofunikira kaamba ka Mulungu kupanga zivumbulutso za chindunji za zimenezo za iye mwini.

Lerolino, ngakhale kuli tero, tiri ndi ponse paŵiri Baibulo ndi kumvetsetsa kwa mazana akukwaniritsa kwa maulosi a Baibulo. Tiri ndi mbiri ya Uthenga wamoyo, ntchito, ndi mawu a Yesu Kristu. Monga mmene Paulo ananenera: “Pakuti mwa iye [Kristu] chikhalira chidzalo cha Umulungu m’thupi.” (Akolose 2:9) Inde, ife tiri mu mkhalidwe wakudziwa Mulungu ndi unansi wathithithi womwe sunali wothekera m’masiku amakolo. Kodi chimenechi mopambanitsa sichimakwaniritsa kaamba ka chenicheni chakuti iye samadzivumbulutsa mwa chindunji kwa ife?

Kuwerenga Baibulo Kumatibweretsa Ife Kufupi ndi Mulungu

Timaŵerenga pa Yakobo 4:8: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu,” Mwa kuŵerenga Baibulo, tingayandikire kwa Mulungu. Koma motani? Choyamba, mwakuwerenga mbali ya Baibulo tsiku liri lonse, mumaphunzira mbali ndi ulemerero watsopano wa umunthu wake. Pamene mukuwerenga, mobwerezabwereza imani ndi kudzifunsa inu mwini: Kodi nchiyani chomwe ndaphunzira ponena za Mulungu mu versi iri kapena mbaliyi? Kuwonjezerapo, mungapemphere kaamba ka mzimu wa Mulungu kugwira ntchito monga “wothandiza” mkumvetsetsa kwanu ndi mkuyandikira kwanu kwa Mulungu.​—Yohane 14:26.

“Ndayamikira kukhala ndi kumvetsetsa kwa Yehova monga munthu,” analengeza motero mkazi mmodzi Wachikristu amene anawerenga Baibulo kuyambira kuchikuto kufika kuchikuto. Iye anali wophunzira pa Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, yomwe imaphunzitsa amishonale omwe amatumizidwa kuzungulira padziko lonse lapansi. Kodi ndi mtundu wanji wakuphunzitsa Baibulo umene umagwiritsidwa ntchito pa sukulu imeneyi? Akulongosola mmodzi wa alangizi: “Tinayamba projekiti yakuphunzira Baibulo lonse monga gulu. Tinatenga masamba 10 kapena 15 patsiku, ndi onse . . . ophunzira akupanga kufufuzafufuza ndi kuperekako china chake kukukambitsirana kwathu. Ngati tinakumanizana ndi versi lovuta, tinalingalira (1) nkhani yonse, (2) mkhalidwe panthawi imene linalembedwa, ndi (3) tanthauzo la mawu amfungulo mu lembalo. Mokhazikika tinali kufunsa, ’Kodi nchiyani chimene ichi chimatiuza ponena za Yehova ndi mikhalidwe yake? Tinapeza kuti nthawi zonse linatiuza ife china chake ponena za iye.”

Ngakhale kuti simungakhale ndi mwawi wakuphunzira Baibulo mu sukulu imeneyi, zina za njira zimenezi zophunzirira zingagwire ntchito bwino kwa inu ndi banja lanu. Mwachitsanzo, pakati pa Mboni za Yehova uli mwambo kuphunzira mitu ya Baibulo yochepa mlungu uli wonse mchigwirizano ndi misonkhano yawo ya mpingo. Bwanji osatsatira ndandanda ya kuwerenga Baibulo monga banja? Kuwonjezerapo, Watch Tower Society inafalitsa ziwiya zothandizira kufufuzira, monga ngati Aid to Bible Understanding ndi New World Translation Reference Bible, lomwe lingakuthandizeni inu ndi mbali zovuta za Baibulo.a Programu yokhazikika ya kuwerenga Baibulo ingakulitse chiyamikiro chanu cha umunthu wa Yehova.

Mungasankhenso mbali ya Baibulo yomwe iri yoyenerera kwa inu. Ngati, mwachitsanzo, musankhapo kuphunzira maversi 17 a mu Salmo 86, mungapeze chifupifupi mbali 15 zaumunthu wa Mulungu: Iye ali wabwino, wokonzekera kukhululukira, wakukoma mtima kokulira, wokonzekera kuyankha mapemphero, wosayerekezeka ndi milungu ina, wosayerekezeka monga wantchito yachilengedwe, wolamulira wa dziko lonse, mpangi wamkulu wa zinthu zosangalatsa, wopulumutsa kuchokera ku imfa, wachifundo, wachisomo, wosakwiya msanga, waukulu mu chowonadi, mthandizi, ndi mtonthozi. Kodi ndi chonulirapo chabwinopo chotani chimene mungakhale nacho koposa kuyesetsa kuphunzira ponena za Mlengi Wanu?

Mapindu Aakulu Kuchokera ku Kudziwa Mulungu

Kuchifikira chonulirapo chathu chapamwamba chamoyo wosatha liri chabe phindu limodzi lochokera kukudziwa Mulungu. (Yohane 17:3) Kuwonjezerapo, pali phindu lakukhala ndi bwenzi la tsiku ndi tsiku lomwe limadera nkhawa ponena za inu ndipo lokhazikika monga thanthwe. (Masalmo 18:31) Pamene Mfumu Davide anadzimva kukhala atazingidwa ndi adani ndi wothodwetsedwa ndi mavuto, iye anapeza kuti Mulungu anali mthandizi weniweni yekha yemwe analipo. Iye chotero anati: “Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakugwiriziza; nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.”​—Masalmo 55:22.

Inunso, mungasangalale ndi unansi wotero ndi Mulungu, ngati inu mutenga nthawi ya kumudziwa iye. Sichiri chovuta kwambiri. Pangani kuyesayesa kwa kuwerenga Mawu ake. Yanjanani ndi awo amene miyoyo yawo imasonyeza kuti iwo amadziwa Mulungu, monga ngati awo amene anakubweretserani magazini iyi. Itanani pa Yehova mu pemphero. Popeza Mulungu sali mphamvu yopanda umunthu kuti sadzamva kulira kwanu. Iye ali Mulungu wa moyo ndi “Wakumva pemphero.” Ndipo “mukamufunafuna iye mudzamupeza.”​—Masalmo 65:2; 1 Mbiri 28:9.

[Mawu a M’munsi]

a Watch Tower Publications Index 1930-1985 idzakuthandizani inu kupeza malongosoledwe ndi kukambitsirana kwa ndime zoterozo mu zofalitsidwa zothandiza mu kufufuza kumeneko.

[Chithunzi patsamba 5]

Mulungu mwaumwini anadzivumbulutsa iye mwini kwa Nowa Abrahamu ndi Mose

[Chithunzi patsamba 7]

Chilengedwe chiri magwero Osatopa achidziwitso ponena za umunthu wa Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena