Kodi Nthawi Zonse Mumagwira Nsonga?
MBALE wamkulu anakwiya kwambiri. Chifukwa chaukali wake anali mbale wake wamng’ono. Ndipo choyambitsa chake? Mbale wake anapatsidwa chizindikiritso chimene iye anamanidwa. Pamene mkwiyo wake unakula, woyanjana naye wanzeru anampatsa iye uphungu kuletsa maganizo ake oipidwa. Kupanda apo china chake choipa chingachitike. Koma munthuyo ananyalanyaza uphungu wabwino umenewo. Mmalo mwake, mwangozi, iye anapha mbale wake wachichepere.
Munthu ameneyo anali Kaini, mwana woyamba wamwamuna wa makolo anthu oyambirira, Adamu ndi Hava. Kaini anapha mbale wake wamng’ono Abele pamene Yehova analandira nsembe ya Abele ndi kukana ya Kaini. Woyanjana naye wanzeru sanali wina wake koposa Yehova Mulungu, amene anapereka uphungu wachikondi umene Kaini anaukana. Monga chotulukapo chake, kupha kunalowerera mbanja latsopano la anthu, ndipo Kaini anapatsidwa chilango chakukhala moyo wake wonse monga wokanidwa. Ndi chotulukapo chomvetsa chisoni chotani nanga chochokera kukulephera kupeza nsonga yauphungu!—Genesis 4: 3-16.
Zaka mazana ambiri pambuyo pa Kaini, Mfumu Davide ya Israyeli inachita chigololo ndi Bateseba, mkazi wa Uriya Mhiti, ndipo mkaziyo anakhala ndi pakati. Davide anayesa kusamalira vutolo mwakukakamiza Uriya kugona ndi mkazi wake. Pamene iye anakana, Davide anakonza kaamba ka Uriya kuti afe pabwalo lankhondo ndipo kenaka kukwatira Bateseba, a kumuchinjiriza iye kuti asafe monga wochita chigololo. Mneneri wa Mulungu anabwera kwa Davide ndi kubweretsa ku chisamaliro chake kuwopsa kwa chimene iye anachita. Davide mwamsanga anapeza nsonga yauphunguwo. Chotero, ngakhale kuti kwa moyo wake wonse iye anavutika ndi zotulukapo za cholakwa chimenecho, Yehova analandira kulapa kwache kochokera mu mtima.—2 Samueli 11:1-12:14.
Zitsanzo ziwiri zimenezi zimasonyeza kufunika kwa kumvetsera uphungu. Kungapange kusiyana pakati pa chipambano ndi kulephera, chimwemwe ndi chisoni, ngakhale moyo ndi imfa. Nchosadabwitsa kuti Baibulo limati: “Njira ya chitsiru njolungama pamaso pake pake; koma wanzeru amamvera uphungu.” (Miyambo 12:15) Komabe sichiri chokhweka kumvetsera ku uphungu. Nchifukwa ninji ichi chiri tero? Kodi ndimotani mmene tingakulitsire kawonedwe kabwino ka Mfumu Davide m’chinthu ichi ndi kupewa chitsanzo choipa cha Kaini?
Kudzichepetsa Kumathandiza
Kawirikawiri anthu amachipeza icho kukhala chovuta kumvera uphungu chifukwa safuna kulandira chenicheni chakuti amawufunikira iwo. Kapena ngati iwo atero, iwo sawona nchifukwa ninji ayenera kulandira uphungu kuchokera kwa munthu uyu. Ndithudi, kumeneku kuli kunyada, ndipo kulingalira kowonjezerapo kungathandize kulaka iko. Mwachitsanzo, Paulo anati: “Pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Icho chimatiuza ife kuti aliyense wa ife amafunikira uphungu nthawi ndi nthawi. Chimatiuzanso ife kuti ngakhale awo amene amatipatsa ife uphungu ali ndi kuphophonya. Palibe wina aliyense amene angapatulidwe. Chotero musalole zophophonya zopitirira za munthu aliyense kukulepheretsani inu kulandira thandizo liri lonse limene iye angapereke.
Yesu anagogomezera kufunika kwa kuthetsa kunyada pamene iye anauza otsatira ake: “Indetu ndinena kwa inu, ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu ufumu wa kumwamba.” (Mateyu 18:3) Ana achichepere amapeza mlingo wa chisungiko pamene makolo awo awapatsa iwo uphungu ndi kuwawongolera iwo. Kodi mumamva mkhalidwe wofananawo pamene wina akupatsani uphungu, kuzindikira kuti uphungu wotero umatsimikizira chikondi chake ndi kudera nkhawa kwake kaamba ka inu? (Ahebri 12:6) Mfumu Davide, amene kudzichepetsa kwake kofunitsitsa kulandira uphungu kunatsegula njira kaamba ka Yehova kulandira kulapa kwake, anafulumizidwa kulemba: “Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo; akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu.”—Masalmo 141:5.
Mkhalidwe wodzichepetsa woterowo ungatithandize ife pamene uphungu umene talandira umakhudza madera awo amene palibe malamulo okhazikitsidwa. Mwachitsanzo, ngati tipatsidwa uphungu kuti kapesedwa kathu kapena kavalidwe kathu kakukhumudwitsa ena mu mpingo, kungatenge kudzichepetsa kwenikweni kuti tipeze nsonga. Mosasamala kanthu za zimenezo, kuchita tero kudzakhala kutsatira chenjezo la mtumwi Paulo: “Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.”—1 Akorinto 10:24.
Mwachimwemwe, Yehova wapereka Baibulo, lomwe ladzadza ndi uphungu wabwino koposa. Mchenicheni, liwu lakuti “uphungu” m’mbali zake zosiyanasiyana limapezeka mmenemo nthawi zoposa 170. Ndipo, iye watipatsa abusa achikondi kutithandiza ife mkugwiritsira ntchito uphungu umenewu. Makonzedwe abanja chiri choperekedwa china chochokera kwa Yehova kupereka thandizo lachikondi mwanjira ya uphungu kuchokera kwa makolo omwe ali ozindikira ponena za mathayo awo. Tiyeni nthawi zonse modzichepetsa timvetsere ku uphungu woterowo.
“Khalani Wotchera Khutu”
Yakobo 1:19 amapereka uphungu: “Munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.” Chiridi mwapadera chowona pamene tikulandira uphungu. Nchifukwa ninji? Choyamba, kodi sichiri chowona kuti kawirikawiri sitimazindikira ponena za zophophonya zathu, ndipo sizibwera monga chodabwitsa chenicheni pamene bwenzi lodera nkhawa liloza izo ndi kupereka uphungu? Icho mowonadi chimachipanga icho kukhala chokhweka kwa onse odera nkhawa ngati mwamsanga tizindikira chomwe akuyesa kutiuza ndipo modzichepetsa kulandira thandizo lachikondilo.
Pamene bwenzi litifikira ife ndi uphungu, tiyenera kukumbukira kuti iye (wamwamuna kapena wamkazi) angakhale ali wonjenjemera. Sichiri chokhweka kupereka uphungu. Mwina mwake woyembekezereka kukhala mphungu amakhala atapereka lingaliro lokulira ku mawu ndi kafikidwe komwe kayenera kugwiritsidwa ntchito. Mkulu angayambe kukambitsiranako mwakutiyamikira ife kaamba ka mbali zina zautumiki Wachikristu m’zimene takhala tikuchita bwino. Koma chimenecho sichiyenera kutipangitsa ife kufunsa zifuno zake pamene iye apitiriza kupereka uphungu. Amene akupereka uphungu sangalankhule mwachindunji poyamba, kusayesa kukhala wamachenjera kapena wolankhula mosalingalira. Kukhala kwathu wozindikira bwino kupeza nsonga mofulumira kudzathandiza wopereka uphungu m’ntchito yake ndipo mwina mwake kutipulumutsa ife kumaganizo opwetekedwa mtima.
Nthawi zina m’phungu angagwiritsire ntchito chitsanzo kapena fanizo kutithandiza ife kupeza nsonga. Mwamuna mmodzi wachichepere anali asanakhale wochimwa kopambanitsa, koma iye anali panjira yolakwa. Mkulingalira ndi iye, mwamuna wachikulire Wachikristu ananyamula rula yomwe inali pa desiki. Akumaipinda rulayo m’manja mwake, iye anafunsa: Ngati titaipinda rulayi chonchi, kodi ndingayesebe mzera wowongoka ndi iyo?” Mwamuna wachichepereyo anapeza nsonga. Iye anali kuyesera kupinda malamulo kuti agwirizane ndi zikhumbo za iye mwini. Fanizo linamthandiza iye kutsatira uphungu wanzeru wa Miyambo 19:20: “Tamvera uphungu, nulandire mwambo.”
Zindikirani Uphungu Wosakhala Wachindunji
Kuzindikira koteroko kungatithandize ife kupeza phindu kuchokera ku uphungu wosakhala wachindunji, ngakhale popanda kulowereramo kwa wina wake. Ichi chinachitika m’nkhani ya mwamuna wachichepere mu Portugal. Iye anali kuphunzira Baibulo ndipo anapeza kope ya Your Youth—Getting the Best out of It Kokha masiku ochepa pambuyo pake, iye anaulula kuti iye anali ataliŵerenga kale bukhulo nthawi zitatu ndipo anathandizidwa ndi ilo. M’njira yotani? Pano pali zimene wachichepereyo ananena: “Ndinalibe chiyembekezo chenicheni kaamba ka mtsogolo, koma mutu 2 [“Chifukwa Chake Mungayang’ane Kutsogolo ndi Chidaliro“] unandipatsa ine tanthauzo m’moyo. Ndiponso, ndakhala ndikuchita mphyotophyoto kwa zaka zingapo tsopano; palibe wina aliyense amene anandiuzapo nkomwe kuti chimenechi chinali chosasangalatsa kwa Mulungu limodzinso ndi chosakaza kwa ine. Pambuyo pakuwerenga mutu 5 [“Mphyotophyoto ndi Kugonana kwa Aziwalo Zofanana”], ndinapanga chosankha kusapitiriza mkhalidwewu. Mutu 7 [“Zovala Zanu ndi Kawonekedwe Zimalankhula—Ponena Za Inu”] unandithandiza ine kubwereramo m’kawonekedwe kanga ka umwini, ndipo monga mmene mungawonere, ndameta kale tsitsi langa.”
Iye anapitiriza: “Kwazaka zambiri ndakhala ndikusuta ndudu. Mutu 15 [“Mankhwala—Mfungulo ku Moyo Weniweni”] unandiwongolera ine pambali imeneyo. Ndakhala ndi kumapemphera kwa Yehova, ndipo kuyambira Sande sindinasute ndudu ina. Mukudziwa, kwanthawi yaitali ndakhala ndikugonana ndi bwenzi langa lachikazi, koma mutu 18 [“Kodi Kuipa kwa Kugonana Kumapanga Lingaliro”] unabweretsa kuchisamaliro changa kawonedwe ka Mulungu pankhaniyi. Ndinalankhula kale ndi iye ponena za nkhaniyi, ndipo iye analingalira kuthetsa unansi wathu.”
Chiri chosangalatsa chotani nanga kuwona kusintha koteroko mnthawi yochepera mmoyo wa munthu wachichepere! Kodi nchiyani chimene chinachipanga icho kukhala chothekera? Chenicheni chakuti iye anali wokhoza kuzindikira zimene anawerenga monga uphungu womwe unagwiritsidwa ntchito kwa iye mwaumwini.
Kulabadira Uphungu KumabweretsaMa pindu
Uphungu—kaya ubwera kwa ife mosakhala mwachindunji kudzera m’Baibulo kapena mabukhu a Baibulo, kapena mwachindunji kuchokera kwa bwenzi—ungakhale wopindulitsa. Ichi chikuwonedwa mchokumana nacho cha tate yemwe anafuna thandizo kuchokera kwa amuna achikulire auzimu mumpingo wake chifukwa chakuti mwana wake wamwamuna wa zaka 18 sanali kulabadira kuzoyesayesa zake zopereka chilango. Akulu Achikristu mwachikondi analingalira ndi tateyo, yemwe anali ndi changu mkutumikira Mulungu, mwachiwonekere anafunikira kulinganizitsa kokulira mkuchita kwake ndi banja lake.
Mawu a Paulo anawerengedwa kwa iye: “Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Tateyo anafunsidwa kuunikira: Kodi njira imene anayesera kulimbikitsa mwana wake, ngakhale kuti analiwatanthauzo labwino, inamupangitsa mnyamatayo kukwiya? Kodi inali nkhani yoyembekezera mwanayo kulowa mumzera limodzi ndi changu cha bambo wake kaamba ka misonkhano ya Chikristu ndi kutumikira popanda kuyesera kuzika chikondi kaamba ka zinthu zimenezo mumtima mwake? Kodi iye wathandiza mwana wake ‘kuphunzira kuwopa Yehova Mulungu wake.?—Deutronomo 31:12, 13.
Tateyo anamvetsera ku uphunguwo ndi kuugwiritsira ntchito. Chotulukapo chake? Mwana wake wamwamuna wa zaka 18 tsopano amapezeka pa misonkhano ya Chikristu, ndipo atate ake akutsogoza phunziro la Baibulo la mlungu ndi mlungu ndi iye. Ndipo monga mmene tate wachitira ndemanga, “Tsopano tiri ndi unansi wabwino wa tate ndi mwana.” Inde, onse aŵiri atate ndi mwana anayipeza nsonga ya uphungu.
Ndichosakayikirika kuti tonse timaphophonya ndipo timafunikira uphungu kuchokera nthawi ndi nthawi. (Miyambo 24:6) Ngati tipeza nsonga ndi kulabadira uphungu wanzeru, tidzasangalala ndi madalitso ochuluka. Pakati pa iwo Udzakhala dalitso lamtengo wapatali koposa wonse; kukulitsa ndi kusunga unansi watanthauzo, waumwini ndi Atate wathu wakumwamba wachikondi, Yehova. Chotero, tidzafuula mawu a Mfumu Davide: “Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu.—Masalmo 16:7.