Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 6/1 tsamba 19
  • Kugwirizananso Kwachimwemwe mu Brazil

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwirizananso Kwachimwemwe mu Brazil
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Nkhani Yofanana
  • Anali Kukondwera ndi Chilamulo cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Omaliza Maphunziro a Gileadi—“Amishonale Enieni!”
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Sukulu ya Gileadi—Ya Zaka 50 Ndipo Ikupitabe Patsogolo!
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Amishonale Amapita “Kumalekezero a Dziko Lapansi”
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 6/1 tsamba 19

Lipoti la Olengeza Ufumu

Kugwirizananso Kwachimwemwe mu Brazil

PA 67 a amishonale ophunzitsidwa pa Gileadi amene akutumikira mu Brazil 63 anafika pamodzi pa ofesi ya nthambi ndikuima kaamba ka chithunzi chopanga mbiri ichi. Kugwirizananso kwachimwemwe kumeneku kunachitika pa November 18, 1986, mkati mwa kuchezera kwa A. D. Schroeder, chiwalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova mu Brooklyn, New York.

Zinali zaka zoyambirira 41 chifupifupi pa tsiku lomwelo​—pa November 17, 1945—​pamene omaliza maphunziro awiri a kalasi loyambirira la Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower anafika ku Brazil. Kwa m’modzi wa iwo, Charles Leathco (kumbuyo, kumanzere kwa pakati), uku kunali kugwirizananso kwapadera chifukwa iye ndi mlendo wake Charlotte Schroeder anali mkalasi imodzi mu Gileadi, ndipo Mbale Schroeder anali mmodzi wa aphunzitsi awo.

Kuyambira kalasi yoyamba imeneyo, chiwonkhetso cha amishonale 258 abwera ku Brazil. Pakati pa iwo panali 16 a ku Brazil. Mmodzi wa iwo, Augusto Machado (kumanzere m’zera wakutsogolo), anaphunzira chowonadi kuchokera kwa amishonale oyambirira, kupita ku Gileadi, ndi kubwerera ku Brazil. Wakhala akutumikira pa ofesi ya nthambi kwa zaka 30 zapita ndipo tsopano ali mgwirizanitsi wa Komiti ya Nthambi. Ngakhale kuti ambiri a amishonalewo sakutumikiranso monga amishonale, ntchito yabwino imene anachita inatsalira. Mu1945 munali ofalitsa a Ufumu 344 okha mu dzikolo tsopano Brazil ikuyandikira chizindikiro cha 200, 000, kuchitira ripoti chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa 196, 948 mu chaka chautumiki cha 1986.

Chinali chimwemwe chotani nanga kwa amishonale AchiBrazil, achichepere ndi achikulire, kukumbutsanso pa kugwirizananso kwachimwemwe kumeneku ponena za ntchito yozizwitsa ya zaka 41 zapita.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena