Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 7/15 tsamba 10-14
  • Kodi Mapemphero Anu Ali a Tanthauzo Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mapemphero Anu Ali a Tanthauzo Motani?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zitsanzo za Mapemphero a Tanthauzo
  • Zophophonya Chifukwa cha Kupanda Ungwiro kwa Umunthu
  • Kulaka Zophophonya
  • Zothandiza Mkupereka Mapemphero a Tanthauzo
  • Mapemphero Amene Amayankhidwa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Ndimapemphero Ayani Omwe Amayankhidwa?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Kupemphera Kumathandizadi?
    Nsanja ya Olonda—2000
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 7/15 tsamba 10-14

Kodi Mapemphero Anu Ali a Tanthauzo Motani?

“Ndaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova.​—MASALMO 119:145.

1, 2. (a) Kodi ndi fanizo la Yesu liti limene limachita ndi pemphero? (b) Kodi ndi mapeto otani amene Yesu anapeza kuchokera ku mapemphero awiri, ndipo kodi nchiyani chimene ichi chiyenera kutisonyeza ife?

Kodi mtundu wanji wa mapemphero amene Mlengi, Yehova Mulungu, amamva? Fanizo limene Yesu Kristu anapereka limasonyeza umodzi wa mkhalidwe weniweni kaamba ka Mulungu kuyankha mapemphero. Yesu ananena kuti amuna awiri anali kupemphera mu kachisi mu Yerusalemu. M’modzi anali m’Farisi wolemekezedwa kwambiri, winayo anali wosonkhetsa misonkho wonyozedwa. M’Farisi anapemphera: “Mulungu, ndikuyamikani kuti sindiri monga anthu onse ena . . . kapenanso monga wamsonkho uyu. Ndisala chakudya kawiri sabata limodzi; ndipereka limodzi la magawo khumi la zonse ndiri nazo.” Koma wosonkhetsa msonkho wodzichepetsayu “anadziguguda pachifuwa chake nanena, Mulungu mundichitire chifundo, ine wochimwa.”’​—Luka 18:9-13.

2 M’kuchitira ndemanga pa mapemphero awiri amenewa, Yesu anati: “Ndinena ndi inu, anatsikira kunyumba kwake woyesedwa wolungama uyutu, [wosonkhetsa msonkho] osati uja ayi [m’Farisi] pakuti yense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa; koma wodzichepetsa yekha adzakulitsidwa.” (Luka 18:14) Momvekera, Yesu anasonyeza kuti kungopemphe-ra kokha kwa Atate wakumwamba sikuli kokwanira. Mmene timapempherera​—mkhalidwe wathu wa maganizo​—ulinso wofunika kwambiri.

3. (a) Tchulani malamulo ena okhazikitsidwa otsogoza pemphero. (b) Kodi ndi mkhalidwe wotani umene pemphero liyenera kutenga?

3 Pemphero liridi, mwawi wapadera, wolemera, wosamalitsa, ndipo Akristu onse ophunzitsidwa bwino ali ozolowerana ndi malamulo oyambirira omwe amalamulira ilo. Mapemphero ayenera kutsogozedwa kwa Mulungu wowona, Yehova. Iwo ayenera kunenedwa m’dzina la Mwana wake, Yesu Kristu. Kuti alandiridwe, ayenera kuperekedwa mu chikhulupiriro. Inde, “iye wakufikira Mulungu ayenera kukhulupirira kuti ali.” Mkuwonjezerapo, pemphero lanu liyenera kukhala m’chigwirizano ndi chifuniro cha Mulungu. (Ahebri 11:6; Masalmo 65:2; Mateyu 17:20; Yohane 14:6, 14; 1 Yohane 5:14) Ndipo kuchokera mu zitsanzo za m’Malemba, timaphunzira kuti mapemphero angatenge mtundu wa kulemekeza, kuyamikira, kupembedzera, ndi kupempha.​—Luka 10:21; Aefeso 5:20; Afilipi 4:6; Ahebri 5:7.

Zitsanzo za Mapemphero a Tanthauzo

4. (a) Kodi ndi zitsanzo ziti zapemphero latanthauzo zimene Mose ndi Yoswa anapereka? (b) Kodi ndi zitsanzo ziti zimene Davide ndi Mfumu Hezekiya anapereka? (c) Kodi ndi chinthu chofanana chiti chimene ambiri amapemphero amenewo anali nacho?

4 Pamene mavuto olemetsa ayenera kuyang’anizidwa, zosankha zosamalitsa zimafunikira, zolakwa zazikulu zakhala zitapangidwa, kapena miyoyo yathu kuwopsyezedwa, mapemphero athu mwapadera amatenga kufunitsitsa ndi kukhala atanthauzo. Chifukwa chakuti Aisrayeli anaukira pambuyo pa kumva nkhani yosasangalatsa ya azondi khumi osakhulupirika, Yehova anauza Mose kuti anthuwo anayenera kuwonongedwa. M’pemphero lowona mtima ndi latanthauzo, Mose anapempha Yehova kusachita kachitidweka chifukwa chakuti dzina Lake linalowetsedwamo. (Numeri 14:11-19) Pamene Israyeli anagonjetsedwa ku Ai chifukwa chadyera la Akani, Yoswa ananenanso kuchonderera kwenikweni pa maziko a dzina la Yehova. (Yoswa 7:6-9) Ambiri amasalmo a Davide ali mtundu wa mapemphero ofunitsitsa, chitsanzo chowonekera kwambiri chomakhala Masalmo 51. Pemphero la Mfumu Hezekiya panthaŵi ya kulowerera mu Yuda kwa Mfumu Sanakeribu ya AsUri chiri chitsanzo china chabwino chapemphero latanthauzo, ndipo kachiŵirinso dzina la Yehova linaphatikizidwamo.​—Yesaya 37:14-20

5. Tiri ndi zitsanzo zina ziti za mapemphero atanthauzo onenedwa ndi atumiki ena a Yehova?

5 Bukhu la Maliro linganenedwe kukhala pemphero lalitali, lofunitsitsa loperekedwa ndi Yeremiya kupempherera anthu ake, popeza Yehova mobwerezabwereza akutchulidwa momwemo. (Maliro 1:20; 2:20; 3:40-45, 55-66; 5: 1-22) Ezara ndi Danieli nawonso anapereka mapemphero atanthauzo ndi ofunitsitsa kupempherera anthu awo, kuwulula zolakwa za mtundu wawo ndi kupempha kaamba ka chikhululukiro. (Ezara 9:5-15; Danieli 9:4-19) Ndipo tingakhale otsimikizira kuti pemphero limene Yona anapereka pamene iye anali m’mimba ya chinsomba chachikulu linali lofunitsitsa ndi latanthauzo.​—Yona 2:1-9.

6. (a) Yesu anatipatsa ife zitsanzo ziti za mapemphero atanthauzo? (b) Kodi ndi mbali yeniyeni iti imene ikufunika kupanga mapemphero athu kukhala atanthauzo?

6 Asanasankhe atumwi 12, Yesu anachezera usiku wonse m’pemphero kuti chifuno cha Atate wake chichitike m’kupanga zosankha. (Luka 6:12-16) Palinso pemphero latanthauzo la Yesu pa usiku wa kuperekedwa kwake, monga kwalembedwera pa Yohane mutu 17. Mapemphero onsewa amapereka umboni wokhutiritsa ku unansi wabwino ndi Yehova Mulungu womwe unasangalalidwa ndi awo omwe anapereka iwo. Mosakaikira, iyi iyenera kukhala mbali yoyamba m’mapemphero athu ngati iwo ayenera kukhala atanthauzo. Ndipo ayenera kukhala ofunitsitsa ndi atanthauzo ngati ayenera kukhala ‘amphamvu’ ndi Yehova Mulungu.​—Yakobo 5:16, The Jerusalem Bible.

Zophophonya Chifukwa cha Kupanda Ungwiro kwa Umunthu

7. Kodi ndi mafunso otani amene tingadzifunse ife eni ponena za mapemphero athu?

7 Monga mmene chasonyezedwera, pansi pa mikhaliawe yotsendereza mapemphero athu mwachiwonekere amakhala ofunitsitsa ndi atanthauzo. Koma bwanji ponena za mapemphero athu a tsiku ndi tsiku? Kodi iwo amapereka chitsimikiziro cha unansi wotentha, woyandikira mwathithithi umene timaumva ndi Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu? Chanenedwa bwino lomwe kuti: “Pemphero liyenera kutanthauza chinachake kwa ife ngati liyenera kutanthauza chinachake kwa Mulungu. Kodi ife timapatsa mapemphero athu lingaliro limene amafunikira ndi kutsimikizira kuti iwo mowonadi amachokera mu mtima wathu wophiphiritsira?

8. Mapemphero athu angakhale ndi zophophonya ziti chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu?

8 Chiri chapafupi kulola mapemphero anthu kusowa mphamvu mu nkhanizi. Chifukwa cha zikhoterero zathu zopanda ungwiro za cholowa, mitima yathu ingatinyenge ife mosavuta, kulanda mapemphero athu mikhalidwe yomwe ayenera kukhala nayo. (Yeremiya 17:9) Kokha ngati, pa nthawi zina, tiima ndi kuganizira tisanapemphere, tingapeze kuti chikhoterero chiri chakuti mapemphero athu amakhala osasonkhezeredwa ndi chifuno, kubwerezabwereza, olingana. Kapena iwo angakhale obwerezabwereza, chomwe chimatikumbutsa zimene Yesu ananena ponena za njira yosayenera ‘imene anthu amitundu amapemphera.’ (Mateyu 6:7, 8) Kapena mapemphero athu angakhale omachita ndi zinthu zofala m’malo mwakuchita ndi nsonga zenizeni kapena anthu.

9. Kodi ndi misampha ina iti imene ingabuke m’chigwirizano ndi mapemphero athu, ndipo kodi ndi chiti chomwe chiri chifukwa chimodzi chosakaikirika cha misampha imeneyi?

9 Nthawi zina tingakhale oyedzamira pa kupereka mapemphero athu mofulumira. Koma kofunikira kudziwa kuli kayang’anidweka: “Ngati muli wotanganitsidwa kwambiri kuti mupemphere, muli wotanganitsidwa kwambiri.” Sitiyenera kufuna kuloweza mawu ena ndipo kenaka kungowabwereza iwo nthawi iriyonse pamene tipemphera; ndipo sichingakhalenso choyenera kwa Mboni ya Yehova kuwerenga pemphero lake, monga ngati pa msonkhano wapoyera. Mosakaikira zophophonya zonsezi zingabuke, mwinamwake kumbali ina, kuchokera ku chenicheni chakuti mwakuthupi sitingathe kumuwona Yehova Mulungu, M’modzi amene timapemphera kwa iye. Komabe, sitingamuyembekezere iye kukhala wosangalatsidwa ndi mapemphero oterowo, ndiponso sitipindula mkuwakamba iwo.

Kulaka Zophophonya

10. (a) Kodi ndi khalidwe lotani limene lingasonyeze kusoweka kwa chiyamikiro kaamba ka kufunika kwa pemphero? (b) Kodi ndi chochitika cha Malemba chiti chimene chadziwitsidwa?

10 Tidzakhala okhoza kuchinjiriza zophophonya zotchulidwazo kufikira ku utali umene tidzayamikira kufunika kwa mapemphero athu a tsiku ndi tsiku ndi kukhala ndi unansi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba. Popeza kuti chinthu chimodzi, chiyamikiro choterocho chidzatithandiza ife kuchinjiriza kukamba mapemphero athu mwamsanga ngati kuti tinafunikira kupita ku zinthu zina zofunikira koposa. Palibe china chirichonse chingakhale chofunikira koposa kuposa kulankhula ndi Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, Yehova Mulungu. Zowonadi, pangakhale nthawi pamene nthawi iri yosakwanira. Mwachitsanzo, pamene Mfumu Aritasasta anafunsa woperekera chikho wake Nehemiya, “Ufunanji?” Nehemiya ‘pamenepo anapemphera kwa Mulungu wakumwamba.’(Nehemiya 2:4) Popeza mfumuyo inali kuyembekezera yankho lamwamsanga, Nehemiya sakanachedwa kwambiri mu pemphero limenelo. Koma tingakhale otsimikizira kuti linali latanthauzo ndipo linali lochokera mu mtima mwake chifukwa Yehova mwamsanga analiyankha ilo. (Nehemiya 2:5, 6) Komabe kungopatula pa zochitika zasawonekawoneka zimenezo, tiyenera kutenga nthawi kaamba ka mapemphero athu ndi kulola zinthu zina kudikira. Ngati mapemphero athu ali ndi chizolowezi chofulumizidwa, sitiyamikira mokwanira kufunika kwa pemphero.

11. Kodi ndi msampha wina uti umene tiyenera kudzichinjiriza, ndipo kodi ndi chitsanzo chabwino chotani chimene Yesu anakhazikitsa m’chigwirizano ndi ichi?

11 Chophophonya china chimene tifunikira kupewa chiri chija chobwerezabwereza zinthu zachisawawa. Mapemphero oterowo amalepheranso kuchita chilungamo ku mwawi wapadera wa pemphero. M’pemphero lake lachitsanzo, Yesu anakhazikitsa chitsanzo chabwino kaamba ka ife mu njirayi. Iye anatchula mapemphero asanu ndi awiri apadera: atatu ochita ndi chipambano cha chilungamo, limodzi lochita ndi zosowa zathu za tsiku ndi tsiku, ndipo atatu ochita ndi umoyo wathu wauzimu.​—Mateyu 6:9-13.

12. Paulo anapereka zitsanzo zabwino ziti za kukhala achindunji m’mapemphero athu?

12 Mtumwi Paulo anakhazikitsanso chitsanzo chabwino kaamba ka ife mnkhaniyi. Iye anafunsa kuti ena amupempherere iye ‘kuti kuthekera kwakulankhula molimba mtima kuperekedwe kwa iye.’ (Aefeso 6:18-20) Iye anali wachindunji mofananamo m’mapemphero ake kulinga kwa ena. “Ndipo ichi ndipempha,” anatero Paulo, “kuti chikondi chanu chisefukire chiwonjezere, m’chidziwitso, ndi kuzindikira konse; kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima wowona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Kristu; odzala nacho chipatso cha chilungamo, chimene chiri mwa Yesu Kristu, kuchitira Mulungu ulemerero ndi Chiyamiko.​—Afilipi 1:9-11.

13. Kodi ndimotani mmene tinganenere mapemphero atanthauzo ponena za zinthu zosiyanasiyana za utumiki wathu kwa Yehova?

13 Inde, mapemphero athu ayenera kuchitandi zinthu zachindunji, ndipo ichi chimafunikira kuti tipereke lingaliro ku mapemphero athu. (Yerekezani ndi Miyambo 15:28. ) Pamene tiri mu utumiki wa m’munda, tingafunse Mulungu osati kokha kaamba ka dalitso lake pa zoyesayesa zathu komanso kaamba ka nzeru, luntha, kukoma mtima, ufulu wakulankhula, kapena thandizo kaamba ka chifooko china chirichonse chomwe chingayese kusokoneza kuthekera kwathu mu umboni. M’kuwonjezerapo, kodi sitingamufunse Mulungu kutitsogoza ife kwa awo anjala ndi ludzu kaamba ka chilungamo? Tisanapereke nkhani yapoyera kapena kukhala ndi mbali mu Msonkhano wa Ntchito kapena mu Sukulu ya Utumiki Yateokratiki, tingapemphe Yehova kupangitsa mzimu wake woyera kukhala wolemerera pa ife. Chifukwa ninji? Kotero kuti tikakhale ndi chidaliro ndi bata, tikalankhule ndi kukhutiritsa ndi chitsimikiziro, kotero kuti tikabweretse ulemu ku dzina la Yehova ndi kumangilira abale athu. Mapemphero oterowo alinso oyenerera ku kukhala kwathu ndi mkhalidwe wabwino wa maganizo pamene tikulankhula.

14. Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala khalidwe lathu ponena za zifooko zakuthupi zovuta kuzilaka?

14 Kodi tiri ndi chifooko chakuthupi chomwe chimamenyana nkhondo ndi uzimu wathu ndipo chimawonekera kukhala chovuta kuchilaka? Tiyenera kufuna kuchita ndi icho mwachindunji m’mapemphero athu. Ndipo musakhale okhumudwitsidwa, sitiyenera kutopa ndi kupempha modzichepetsa ndipo mofunitsitsa kupempha Mulungu kuti atithandize ife ndi kutipatsa chikhululukiro. Inde, pansi pa mikhalidwe yoteroyo, tiyenera kufuna kupita kwa Yehova monga momwe mwana amapitira kwa atate wake pamene ali m’vuto, mosasamala kanthu kuti ndi mwakawirikawiri chotani mmene tingapempherere kwa Mulungu ponena za chofooka chimodzimodzicho. Ngati tiri owona mtima, Yehova adzatipatsa ife thandizo ndi chitsimikiziro chakuti iye atikhululukira ife. Pansi pa mikhalidwe yoteroyo, tingapezenso chitonthozo kuchokera ku kulapa kwa mtumwi Paulo kwakuti iye anali ndi vuto.​—Aroma 7:21-25.

Zothandiza Mkupereka Mapemphero a Tanthauzo

15. Kodi tiyenera kufikira Yehova m’mapemphero ndi mkhalidwe wotani wa maganizo?

15 Kuti mapemphero athu akhale mowonadi atanthauzo, tiyenera kupanga kuyesayesa kuchotsa zolingalira zonse zakunja ndi kumamatira pa nsonga yakuti tikubwera pamaso pa Mulungu Wamkulu Yehova. Tiyenera kumfikira iye ndi ulemu wokulira, kuyamikira kuwopsya kwake. Monga mmene Yehova anamuuzira Mose, palibe munthu angawone Mulungu ndi kukhala ndi moyo. (Eksodo 33:20) Chotero tifunikira kumfikira Yehova ndi kudzichepetsa ndi kudekha, imene iri nsonga imene Yesu anagogomezera m’fanizo lake la m’Farisi ndi wosonkhetsa msonkho. (Mika 6:8; Luka 18: 9-14) Yehova ayenera kukhala weniweni kwa ife. Tiyenera kukhala ndi mkhalidwe wa maganizo wofanana ndi umene Mose anali nawo. “Anapirira molimbika monga ngati kuwona wosawonekayo.” (Ahebri 11:27) Zikhoterero zoterezo zimachitira umboni kuti tiri ndi unansi wabwino ndi Atate wathu wakumwamba.

16. Kodi ndi mbali iti imene mitima yathu imagwira ntchito m’kupereka mapemphero atanthauzo?

16 Mapemphero athu adzakhalanso atanthauzo ngati tibwera kwa Yehova ndi mitima yodzaza ndi chikondi ndi chiyamikiro kwa iye. Mwachitsanzo, ndi chiyamikiro chotani nanga cha Yehova Mulungu ndi chikondi kaamba ka iye chimene wamasalmo Davide anasonyeza mu Masalmo 23 ndi 103! Palibe kukaikira ponena za unansi wabwino womwe Davide anali nawo ndi Mbusa Wamkulu, Yehova Mulungu. Mu Sukulu ya Utumiki Yateokratiki, timapatsidwa uphungu wakulankhula ndi kutenthedwa maganizo ndi kumvera. Ichi chiyenera kukhala mwapadera chotero pamene tikuwerenga malemba ndipo moposerapo pamene tikupemphera kwa Atate wathu wakumwamba. Inde, tiyenera kudzimva monga momwe anachitira Davide pamene iye anapemphera: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’chowonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.” Ndiponso osonyeza mmene tingamverere ali mawu awa a wamasalmo wina: “Ndinaitana ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Yehova.”​—Masalmo 25:4, 5; 119:145.

17. Kodi ndimotani mmene tingapangire mapemphero athu kusakhala obwerezabwereza?

17 Kuti tisunge mapemphero athu kukhala atanthauzo ndi kupewa kungokhala obwerezabwereza, tidzachita bwino kusiyanitsa malingaliro ake. Lemba la Baibulo la tsikulo kapena chofalitsidwa china Chachikristu chimene takhala tikuwerenga chingapereke lingaliro. Mutu wa phunziro la Nsanja ya Olonda, wa nkhani yapoyera, kapena wa msonkhano kapena msonkhano waukulu umene tingakhale tikupezekako ungatumikire kaamba ka chifunochi.

18. Kuti tipange mapemphero athu kukhala atanthauzo kwambiri, kodi nchiyani chimene tiyenera kusunga m’chigwirizano ndi mawu ndi zitsanzo za m’Baibulo?

18 Kuti tithandizidwe kukhala mu mkhalidwe wapemphero ndi kupanga mapemphero athu kukhala atanthauzo mokulira, chiri chabwino kusintha kakhalidwe kathu ka kuthupi. Pa mapemphero a poyera, mwachibadwa timaweramitsa mitu yathu. Koma kaamba ka mapemphero aumwini kwambiri, ena achipeza icho kukhala chabwino kugwada pamaso pa Yehova pamene akupemphera monga aliyense payekha kapena monga banja chifukwa amapeza kakhalidwe kameneko kukhala koyenerera ku kukhala kwawo ndi mkhalidwe wa maganizo wodzichepetsa. Pa Salmo 95:6 tikufulumizidwa: “ Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso paYehova, amene anatilenga.” Solomo anagwada pamene anali kupereka pemphero lake lakuperekedwa kwa kachisi ya Yehova, ndipo Danieli anachipanga kukhala chizolowezi cha kugwada pamene anali kupemphera.​—2 Mbiri 6:13; Danieli 6:10.

19. Awo okhala ndi thayo la kupereka mapemphero apoyera angachite bwino kukhala ndi nsonga ziti m’maganizo?

19 M’chiyang’aniro cha kufunika kwa pemphero, akulu osankhidwa ayenera kugwiritsira ntchito kuweruza kwabwino ponena za amene ayenera kuitanidwa kukapereka pemphero lapoyera m’malo mwa mpingo. Munthu wobatizidwa woimira mpingo ayenera kukhala mtumiki Wachikristu wachikulire. Pemphero lake liyenera kuvumbulutsa kuti iye ali ndi unansi wabwino ndi Mulungu. Ndipo awo opatsidwa mwawi wakupereka mapemphero oterowo ayenera kupereka lingaliro kukumvedwa, popeza kuti iwo akupemphera osati kokha m’malo mwa iwo eni komanso m’malo mwa mpingo wonse. Kupanda apo, ndimotani mmene mpingo wonse ukagwirizanira mkunena kuti “Amen” pamapeto a pempherolo? (1 Akorinto 14:16) Komabe, kuti onse akhale okhoza kunena “Amen” watanthauzo, ayenera kumvetsera mosamalitsa, osalola maganizo awo kuyendayenda, koma mowonadi kulipanga pempherolo kukhala lawolawo. Liwu lina lachenjezo lomwe lingawonjezeredwe liri lakuti popeza kuti mapemphero oterowo amaperekedwa kwa Yehova Mulungu, iwo sayenera kugwiritsiridwa ntchito monga chodzikhululukira chakulalikira kwa omvetsera kapena chakuperekera maganizo ena aumwini.

20. Chifukwa chakuti mapemphero atanthauzo operekedwa mwapoyera amapereka dalitso kwa omvetsera, kodi ndi lingaliro lotani limene laperekedwa?

20 Pamene mapemphero athu amene alankhulidwa mofuula alidi mowona atanthauzo, iwo amapereka dalitso kwa omvetsera. Popeza ichi chiri tero, anthu okwatirana ndi mabanja angachite bwino tsiku lirilonse kukhala ndi chifupifupi pemphero limodzi. Mu ilo, munthu m’modzi, monga ngati mutu wa banja, angalankhule kaamba ka wina kapena kaamba ka onse.

21. Kuti mapemphero athu akhale atanthauzo, kodi ndi nkhani ina iti imene idzafunikira kulingalirapo kwathu?

21 Kuti mapemphero athu akhaledi mowona atanthauzo, pali nkhani inanso yomwe ifunikira chisamaliro chathu. Ichi chiri chenicheni chakuti tiyenera kukhala okhazikika ponena za mapemphero athu, ichi chimatanthauza chiyani? Kuti tiyenera kukhala m’chigwirizano ndi mapemphero athu ndipo kuti tiyenera kugwirira ntchito pa zimene timapempherera. Mbaliyi ya mapemphero athu idzalingaliridwa mu nkhani yotsatira.

Kodi Mudzayankha Motani?

◻ Kodi ndi mapemphero ena ati atanthauzo amene ali olembedwa m’Malemba?

◻ Chifukwa chakupanda ungwiro kwaumunthu, kodi ndimotani mmene mapemphero athu angakhalire ndi zophophonya?

◻ Kodi ndimotani mmene tingalakire zophophonya zina m’mapemphero athu?

◻ Kodi ndi zothandizira zina zotani zimene zaperekedwa m’kupereka kwathu mapemphero atanthauzo?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena