Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 8/15 tsamba 15-20
  • Achichepere—Kodi Mukupita Patsogolo Mwauzimu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achichepere—Kodi Mukupita Patsogolo Mwauzimu?
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ubatizo Uli Chitsimikiziro
  • Kutsimikiziridwa ndi Khalidwe
  • Kutsimikiziridwa ndi Phunziro la Baibulo
  • Kusonyezedwa pa Misonkhano ndi mu Utumiki
  • Mwa Mayanjano ndi Achikulire
  • Ntchito ya Makolo ndi Ena
  • Achichepere Kodi Mudzachitanji ndi Moyo wanu?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Achichepere Achimwemwe mu Utumiki wa Yehova
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Achichepere—Kodi Mukulondola Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Achinyamata—khalani ndi Zolinga Zolemekeza Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 8/15 tsamba 15-20

Achichepere​—Kodi Mukupita Patsogolo Mwauzimu?

“Izi uzisamalitse; mu izi ukhale, kuti kukula mtima kwako kuwonekere kwa onse.”​—1 TIMOTEO 4:15

1, 2. Kodi nchiyani chimatanthauza, ndipo nchiyani chimene sichitanthauza, kukhala wopita patsogolo mwauzimu?

Kodi chimatanthauzanji kukhala wopita patsogolo mwauzimu? Chimatanthauza kukhala monga Yesu wachichepere ndi Timoteo, amene anaika zikondwerero zauzimu poyamba mu miyoyo yawo. Ngati inu mukupita patsogolo mwauzimu, mudzadziwa chimene mukafunikira kuchita ndi moyo wanu. Simudzanena kuti: ‘Ndidzayamba kulingalira mosamalitsa ponena za kutumikira Yehova pamene ndakula.’ Ayi, mudzamtumikira iye tsopano!

2 Kumbali ina, kukhala wopita patsogolo mwauzimu sichimatanthauza kukhala monga anthu odzipereka kwa Mulungu kwanthawi yonse, kumavala mawonekedwe achipembedzo, kapena ngakhale kukhala munthu wowerenga bukhu mopambanitsa; ndipo sichimatanthauzanso kukhala wachisoni, wochedwa kuchita zinthu, ndipo wosayanjana ndi ena. (Yohane 2:1-10) Yehova ali Mulungu wachimwemwe, ndipo iye amafuna kuti ana ake a padziko lapansi akhale achimwemwe. Chotero kutenga mbali koyenerera mu masewera ndi machitachita osangulutsa ena ziri ndi chivomerezo cha Mulungu.​—1 Timoteo 1:11; 4:8.

Ubatizo Uli Chitsimikiziro

3. Ndi liti moyenerera pamene Timoteo anabatizidwa?

3 Kukonzekera ndi kubatizidwa ziri zitsimikiziro kuti wachichepere akupita patsogolo mwauzimu. Ngati, monga mmene chalingaliridwira, Timoteo anali adakali wa zaka za pakati pa 13 ndi 19 pamene anakhala mnzake wa mtumwi Paulo pa maulendo a umishonale, Timoteo mwinamwake anali wobatizidwa pamene anali mu zaka zake za pakati kapena kumayambiriro kwa zaka za pakati pa 13 ndi 19. Iye anaphunzitsidwa Malemba kuchokera ku ubwana, ndipo pamene anakonzekeretsedwa ndi chidziwitso chokwanira ndi chiyamikiro, iye sanachedwe kubatizidwa.​—2 Timoteo 3:15.

4. Kodi ndi funso lotani limene Filipo anafunsidwa, ndipo ngakhale kuti wofunsayo anali atangophunzira kumene ponena za Kristu, kodi nchifuwa ninji Filipo anapereka pempho lake?

4 Bwanji ponena za inu ana achichepere a zaka za pakati pa 13 ndi 19 omwe mwaphunzitsidwa mu Malemba? Kodi mwalingalira funso ili: “Kodi nchiyani chimene chindiletsa ine kubatizidwa?” Mu zaka za zana loyamba, funso limenelo linafunsidwa ndi mwamuna yemwe anali wodziwa bwino Malemba koma yemwe anali atangophunzira kumene za chizindikiritso cha Kristu. Zowona, munthuyu sanadziwe zonse zomwe ziripo zoyenerera kudziwa ponena za chifuno cha Mulungu, komabe iye anafulumizidwa ndi chiyamikiro chozama kaamba ka zimene anadziwa! Chotero, wophunzira Filipo analibe chifukwa chokhazikitsidwa mwalamulo cha kusamubatizira iye.​—Machitidwe 8:26-39.

5. Kodi nchiyani chimene chifunika kwa inu kuti mubatizidwe?

5 Kodi nchiyani chimene chimakuletsani inu kubatizidwa? Kuti muyenere, ngakhale kuli tero, kumafunikira kumvetsetsa zomwe zikulowetsedwamo. Inu mowonadi muyenera kufuna kutumikira Yehova chifukwa mumamkonda iye. Mumafunikiranso kupanga kudzipereka kwaumwini kwa iye mu pemphero. M’kuwonje- zerapo, muyenera kumamatira ku makhalidwe abwino ofunika a Mulungu ndi kukhala ndi chizolowezi chokwanira mu kugawana chikhulupiriro chanu ndi ena. Pamene mwayenerera motero, chiri chofunika kwambiri kutsatira ndi kubatizidwa.​—Mateyu 28:19, 20; Machitidwe 2:38.

6. Kodi ubatizo ungayerekezedwe ndi chiyani, ndipo kodi nchiyani chimene chiyenera kutsatira iwo?

6 Ngakhale kuti kubatizidwa chiri chitsimikiziro chakuti mukupita patsogolo mwauzimu, kumbukirani kuti kubatizidwa liri kokha sitepi loyambirira. Mwa kupanga kudzipereka kwa Yehova, mumakhala mlendo mu dziko lakale ili lolamuliridwa ndi Satana. Chotero kudzipereka kungayerekezedwe ndi kufunsira kaamba ka moyo wosatha mu dongosolo la Mulungu la kachitidwe ka zinthu katsopano, ndipo mwa- mbo wa nthawi zonse wa ubatizo uli, m’cheni- cheni, chisonyezero pamaso pa mboni kutsimikizira nsongayi. (Yohane 12:31; Ahebri 11:13) Pambuyo pake muyenera mokhulupirika kukhalira ku kudzipereka kwanu ndi cholinga cha kufuna kulandira mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha.​—Aroma 6:23.

Kutsimikiziridwa ndi Khalidwe

7. Kodi ndimotani mmene khalidwe lanu kulinga ku zinthu za kudziko limagwirizanira ndi kupita kwanu patsogolo kwauzimu?

7 Kaya mukupita patsogolo mwauzimu kapena ayi chidzatsimikiziridwanso ndi kayang’anidwe kanu kulinga ku zinthu za ku dziko. Zinthu ziti? Izo zimaphatikizamo njira ya moyo yaufulu, anamgoneka, ufulu wa kugonana, makanema osonyeza mkhalidwe woipa wa chisembwere, nyimbo zodzutsa chilakolako, nkhani zochititsa manyazi, kuvina kodzutsa chilakolako cha kugonana, kunyada kwa ufuko ndi utundu, ndi zina zotero. (1 Yohane 2:16; Aefeso 5:3-5) Achichepere, mwapadera, afunikira kukhala ogalamuka. Kumbukirani, njira imene mumachitira kulinga ku zinthu zimenezo idzavumbulutsa mkhalidwe wa moyo wanu wauzimu.​—Miyambo 20:11.

8. Kodi nchifukwa ninji achichepere ena amakaikira kubatizidwa?

8 Satana amawona ku icho kuti njira zoipa za dziko ziwoneke kukhala zokongola kwambiri. M’chenicheni, wa zaka 15 ananena kuti: “Mmene timawonera kugonana ndi anamgoneka mokulira pa TV, mokuliranso chimadzawoneka kukhala chovomerezeka mu chitaganya.” Achichepere omwe samatenga mbali mu njira zadziko amapangidwa kudzimva kuti iwo ali achikale ndipo kuti akusowa zinthu zosangalatsa kwambiri. Kodi mumadzimvapo mwanjira imeneyo? Ena amene amayanjana ndi mpingo amatero, ndipo iwo alibe chosankha chenicheni. Pamene anafunsidwa ponena za kubatizidwa, wachichepere mmodzi anati: ‘Sindikufuna kutero tsopano chifukwa mwina ndingachite chinachake kaamba ka chimene ndingachotsedwe mu mpingo.’ Koma simungaime pamwamba pa mpanda ndi miyendo yotangadza kapena kukhala pa zosankha ziWiri zosiyana. Mneneri wa Mulungu kamodzi ananena kuti: “Ngati Yehova ali Mulungu wowona, mutsatireni iye; koma ngati Baala ali, mutsatireni iye.”​—1 Mafumu 18:21.

9. Kodi ndi chitetezero chotani chimene chimazindikiridwa mwakukhala wopita patsogolo mwauzimu?

9 Ndithudi, mwakupewa njira za makhalidwe oipa zadziko, zonse zimene mukupewa ziri ma- vuto ochuluka. “Lingaliro lalikulu la kudzimva kwa kuipidwa ndi kudzimverera chisoni kaamba ka moyo kumene ndakhala ndikutsatira kunandimiza ine,” anavomereza motero mkazi mmodzi. “Ndinadzipeputsa ndi kudzinyenga inemwini ndi mwana amene ndinali ndi pakati pake.” Inde, kuwala ndi kunyezimira kwa pakanthawi kwa dziko la Mdyerekezi kuli kokha chochitika cha pakanthawi, kunyenga. Silipereka chirichonse cha mtengo wapatali. Kutsatira njira zadziko kumatsogolera ku kukhala ndi pakati musanakwatiwe, mabanja osweka, matenda opatsirana mwa kugonana, ndi kukwiyitsidwa ndi chisoni chosaneneka. Chotero mvetserani ku uphungu, khalani opita patsogolo mwauzimu. “Patukani pa choipa nimuchite chabwino.”​—1 Petro 3:11.

10. Kodi ndi chenjezo lotani ndipo ndi zitsanzo za ndani za kupita patsogolo zimene achichepere ayenera kulabadira?

10 Wachichepere wopita patsogolo mwauzimu adzalabadira chenjezo la mtumwi Paulo: “Khalani makanda mu choipa, koma mu chidziwitso akulu msinkhu.” (1 Akorinto 14:20) Timoteo wachichepere mwachidziwikire anagwiritsira ntchito uphungu umenewo. Kodi mungalingalire kufunafuna kwake ubwenzi wa achichepere amakhalidwe oipa, akudziko mu dziko lake? Kutalitali! Mabwenzi ake anali atumiki anzake a Mulungu. (Miyambo 13:20) Tsatirani chitsanzo chake. Pamene muli pafupi kulowa mu mkhalidwe wokaikiritsa, dzifunseni inumwini: Kodi Timoteo kapena Yesu akanachita ichi?

Kutsimikiziridwa ndi Phunziro la Baibulo

11. Kodi ndi masomphenya otani amene achichepere a kudziko amawasowa, ndipo kodi ndimotani mmene iwo amapezedwera ndi kusungidwira?

11 Nkhani yochokera mu Italy yofalitsidwa mu World Press Review inanena kuti: “Malingaliro a kusatsimikizirika ndi kuchita zinthu mwamsanga chifukwa cha kutaya chiyembekezo kwa achichepere kumawonjezeka tsiku liri lonse, ndipo palibe wina aliyense yemwe angawapatse iwo mtsogolo molimbikitsa.” Maso ochititsidwa khungu a awo amene ali mu dziko la Satana alibe masomphenya a dziko latsopano lolonjezedwa ndi Mulungu ndi mtsogolo mwaulemerero momwe mukuyembekezera omwe amayeneretsedwa kaamba ka moyo mmenemo. (2 Akorinto 4:4; Miyambo 29:18; 2 Petro 3:13) koma achichepere opita patsogolo mwauzimu ali ndi masomphenya otero omwe amasungidwa owala ndi kumvekera bwino kupyolera mu kuphunzira Baibulo mokhazikika.

12. (a) Kodi ndimotani mmene tingachitire kuti tipeze chidziwitso cha Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji chidziWitso chimenechi chiri chofunikira kuyesayesako?

12 Kodi dziko latsopano la Mulungu liri lenileni kwa inu? ilo lingakhaledi, koma kulipeza kumafunikira kuyesetsa kwakukulu ku mbali yanu. Mufunikira kukulitsa chikhumbo chanu cha changu kaamba ka kumvetsetsa Baibulo kotero kuti “mukaifunefune ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika.” (Miyambo 2:1-6) Kodi nchiyani chimene chimapangitsa munthu wosaka chuma kufunafuna ndi kukumba, mwinamwake ngakhale kwa zaka? Iye mwachikondi amakhumba kulemera kumene chuma chidzabweretsa kwa iye, koma chidziwitso chiri chofunika koposa chuma chakuthupi. “Ichi chitanthauza moyo wosatha,” anatero Yesu, “kutenga kwawo chidziwitso cha inu, Mulungu yekha wowona, ndi cha uyo amene munamutuma Yesu Kristu.” (Yohane 17:3) Ngati inu mowonadi mumakhulupirira zimene Yesu ananena pamenepo, phunziro la Baibulo lidzakhala chonulirapo chanu chimene chidzakufupani inu ndi chimene chiri cha mtengo wapatali kuposa miyala yamtengo wapatali.​—Miyambo 3:13-18.

13. Kodi ndi malingaliro otani a kuphunzira amene achichepere opita patsogolo mwauzimu adzatsatira?

13 Mudzachipeza kuti pamene muphunzira mokulira, chikhumbo chanu cha kufuna chakudya chauzimu chidzakhala chokuliranso. Phunzirani njira za kuphunzira kwabwino. Musangoika kokha mizere pansi pa mayankho, koma yang’anani malemba a Baibulo osonyezedwa, ndipo kenaka londolani malemba oyandikana nawo kupyolera mwa kulozera ku Baibulo. Mungachitenso kufufuza kowonjezereka kugwiritsira ntchito zolozera, monga ngati Watch Tower Publications Index 1930-1985. Ndanda- litsani mmene nkhanizo zimagwirira ntchito ndi mmene zingagwiritsidwire ntchito. Lankhulani kwa ena ponena za zimene mwaphunzira. Izi zidzasindikiza nsonga mu maganizo mwanu ndipo zidzatumikira kulimbikitsa ena kuchita kufufuza mofananamo. Mwakudzigwiritsira ntchito inu eni kwenikweni, mudzakhala mukulabadira uphungu wopatsidwa kwa Timoteo wachichepere: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale, kuti kukula mtima kwako kuwonekere kwa onse.”​—1 Timoteo 4:15; 2 Timoteo 2:15.

Kusonyezedwa pa Misonkhano ndi mu Utumiki

14. Kodi nchiyani chimene chimathandiza kupanga misonkhano ya Chikristu kukhala ya chisangalatso chokulira, ndipo ndi mwanjira zotani mmene mungalimbikitsire ena pamene mukupezekapo?

14 Pamene musangalala ndi phunziro la Baibulo ndipo mwakonzekera bwino, misonkhano ya Chikristu imakhala chisangalatso chokulira. (Masalmo 12’2:1; Ahebri 2:12) Inu kenaka mumayang’ana kutsogolo mokulira ku kugawana mu mbali za kutengamo mbali kwa gulu ndi kupereka nkhani mu Sukulu ya Utumiki Wateokratiki. Koma pamene mupezeka pa misonkhano, pali njira zina zimene mungakwaniritsire malangizo a ‘kulimbikitsana wina ndi mnzake’ ndi “kufulumizana ku chikondano ndi ntchito zabwino.” (Ahebri 10:24, 25) Kodi inu, mwachitsanzo, mumatenga mwawi wa kuyamba kulankhula ndi ena? Kunena mwaubwenzi, kuti, “Moni, ndiri wokondwera kukuwonani!” kapena kufunsa kowona mtima, “Kodi mukumva bwanji?” kungakhale kolimbikitsa kwenikweni, makamaka pamene kuchokera kwa munthu wachichepere.

15. Kodi ndimotani mmene mungadzipangire inu eni kukhalapo kupanga mautumiki ofunika, ndipo kodi nchifukwa ninji chiri chofunika kusunga m’maganizo chitsanzo cha Kristu?

15 Ntchito yokulira iri yolowetsedwamo m’kugwira ntchito kwa mpingo. Kodi mungagawanemo? MwachidziWikire, Timoteo wachichepereyo anachita mautumiki ambiri othandiza mtumwi Paulo​—kupereka makalata, kukapeza zinthu zofunika, kupereka mauthenga, nai zina zotero. Ngati simunachitepo zotero, bwanji osauza akulu kufunitsitsa kwanu kwakuthandiza. Mwinamwake mudzafunsidwa kugawira magawo a msonkhano, kukonza holo, kapena kupanga mautumiki ena ofunikira. Kumbukirani, Kristu anatsuka mapazi a ophunzira ake, chotero palibe ntchito imene iri yopanda ulemerero kwa wina amene akupita patsogolo mwauzimu.​—Yohane 13:4, 5.

16. Kodi ndi machitachita otani amene nvuzipepala ya Chikatolika inazindikira kukhala thayo la Chikristu?

16 Pamene tiyang’ana pa zipembedzo zina, tingakhaledi oyamikira kaamba ka kuphunzitsidwa kumene timalandira pa misonkhano yathu kaamba ka ntchito yofunika kopOsa ya kulalikira. Akulemba mu U. S. Catholic September wapita, Kenneth Guentert ananena kuti: “Ndinakula mu masiku amene Akatolika sanayembekezeredwe kuwerenga Baibulo chifukwa chowopa kupeza malingaliro achilendo​—onga ngati Akristu olingalira ayenera kupita ndi kumagogoda pa zitseko kuvesa kutembenuza anthu. Kenaka kunabwera Vatican II, ndipo ndinayamba kuWerenga Baibulo. Motsimikizirika kwenikweni; tsopano ndikuganiza kuti Akristu ayenera kupita ndi kugogoda pa zitseko ndi kuyesa kutembenuza anthu.” Iye anawonjezera: “Sichiri chakuti ndiri wokhazikika kotheratu ndi lingalirolo, inu mungamvetsetse, koma ngati muwerenga Chipangano Chatsopano, icho chiri chifupifupi chosatheka kupewa mapeto amenewa.​—Mateyu 10:11-13; Luka 10:1-6; Machitidwe 20:20, 21.

17. Kodi ndimotani mmene utumiki ungakhalire wosangalatsa kwambiri kwa inu?

17 Inde, Akristu oyambirira anali okangalika m’kulalikira kunvumba ndi nyuinba. ndipo mwachiwonekere achichepere monga Timoteo nawonso anapita mu utumiki wa m munda ndi achikulire. Komabe, movomerezeka, kwa ena lerolino iyi siiri ntchito yosangdatsa kwambiri. Chifukwa ninji ayi? Luso liri nsonga yaikulu. Mwachitsanzo, pamene mumachita bwino mu masewera kapena mu mpikisano, kodi simumasangalala ndi iwo moposerapo? Chiri chofanana ndi mu utumiki wa m’munaa. Pamene mukhala wodziwa bwino kwambiri kugwiritsira ntchito Baibulo ndi kukambitsirana nkhani za Baibulo, utumiki umakhala magwero achisangalatso, makamaka pamene inu mupeza wina wogawana naye chidziwitso chopatsa moyo. Chotero khalani opita patsogolo mwauzimu! Bwereranimo mu zopereka zanu za ku khomo ndi khomo. Pezani malingaliro kuchokera kwa ena. Pemphani Yehova kaamba ka thandizo.​—Luka 11:13.

Mwa Mayanjano ndi Achikulire

18. Kodi ndi maunansi a mtundu wanji amene Yesu ndi Timoteo anasangalala nawo ndi achikulire?

18 Pamene iye anali wachichepere wa zaka 12, Yesu anasangalatsidwa kuwononga nthawi ndi achikulire, kukambitsirana zinthu zauzimu. Kamodzi makolo ake “anampeza iye ali mu kachisi, kukhala pakati pa aphunzitsi ndi kumvetsera kwa iwo ndi kuwafunsa mafunso.” (Luka 2:46) Chinah chimodzimodzinso ndi Timoteo. Pamene mtumwi Paulo ndi anzake anachezera ku Lustra, Timoteo mwachiwonekere anasangalala kukhala nawo ndipo anapereka chisamaliro chofunikira ku ziphunzitso zawo. Iye anali ndi chizolowezi ndi abale a kumaloko amene anamuyamikira iye mokulira.​—Machitidwe 16:1-3.

19. Kodi nchifukwa ninji mwapadera Paulo anasankha Timoteo monga woyenda naye, ndipo kodi ndimotani mmene Timoteo anasonyezera kukhala thandizo?

19 Ngakhale kuti Timoteo anali wofunitsitsa kuchita ntchito za kuthupi kaamba ka ena, Paulo anamusankha iye monga woyenda naye makamaka kaamba ka kuthekera kwake kwa kutumikira anthu mu zosowa zawo zauzimu. M’chiyang’aniro cha chimenecho, pamene khamu linakakamiza Paulo kuchoka ku Tesalonika, iye anatumiza Timoteo wachichepere kukathandiza ndi kulimbikitsa ophunzira atsopano. Chotero Timoteo sanali kokha wofunitsitsa kuphunzira kuchokera kwa achikulire ndi kusangalala ndi kukhala nawo; iye analinso thandizo lauzimu lenileni kwa iwo.​—Machitidwe 17:1-10; 1 Atesalonika 3:1-3.

20. Kodi nchiyani chimene inu mudzakhala wanzeru kudzachita, ndipo kodi ndi mautumiki otani amene mungachite m malo mwa okalamba?

20 Mungakhale wanzeru kutsanzira Yesu ndi Timoteo ndi wofunitsitsa kuphunzira kuchokera ku zizolowezi ndi chidziwitso cha achikulire. Funafunani kukhala nawo ndi kuwafunsa iwo mafunso. Ndiponso sonyezani kupita kwanu patsogolo mwauzimu mwakukhala thandizo kwa iwo. Kodi muli ndi okalamba ndi opunduka omwe angayamikire ngati mutapita kukawagulira zinthu ndi kuchita mautumiki ena ofunikira? Mwinamwake mungangowachezera iwo, ndi kuwawerengera iwo, ndi kugawana nawo zokumana nazo zanu zomwe munasangalala nazo mu utumiki.

Ntchito ya Makolo ndi Ena

21. Kodi ntchito ya makolo iri yofunika motani, ndipo kodi nchiyani chimene sichingagogomezeredwe mopambanitsa?

21 Umoyo wauzimu wa achichepere uli wodalira pa malangizo ndi zitsanzo zoperekedwa ndi makolo awo. (Miyambo 22:6) Yesu motsimikizirika anapindula kuchokera ku chitsogozo choperekedwa ndi makolo ake owopa Mulungu a padziko lapansi. (Luka 2:51, 52) Ndipo motsimikizirika Timoteo sakanakhala mnyamata wopita patsogolo mwauzimu amene iye anali popanda kuphunzitsidwa ndi mayi wake ndi agogo wake. (2 Timoteo 1:5; 3:15) Kufunika kwa langizo la Baibulo lokhazikika sikungachite kugogomezeredwa mopambanitsa! Monga makolo, kodi inu mukupereka ichi? Kapena kodi icho chikunyalanyazi awa?

22. (a) Ngati makolo alingalira phunziro la banja la Baibulo kukhala lofunika kwambiri, kodi ndimotani mmene ana amakhudzidwira? (b) Kodi ndi chitsogozo chotani chimene makolo ayenera kupereka kwa ana awo?

22 Munthu wachichepere wa ku malikulu a dziko lonse a Mboni za Yehova analongosola kuti kupyolera mu zaka za kukula, mbali yofunika kwambiri ya moyo wawo wa banja inali kuphunzira Baibulo kwa mlungu ndi mlungu ndi ana. “Nthawi zina Atate anali kukhala otopa pamene anali kuchokera ku ntchito kotero kuti sakanatha kukhala ogalamuka, koma phunzirolo linatsogozedwa mosasamala kanthu za chimenecho, ndipo ichi chinatithandiza ife kuwona kufunika kwake kwailo.”Makolo, chiri chosatheka kuti ana anu angayamikire mozama zinthu zauzimu kusiyapo kokha ngati inu mumatero. Chotero ikani patsogolo zonulirapo za kuchita upainiya ndi umishonale ndi utumiki wa pa Beteli. Athandizeni iwo kuyamikira kuti utumiki iri ntchito mwenimweni ku ntchito ya kudziko.​—Yerekezani 1 Samueli 1:26-28.

23. Kodi ndimotani mmene ena mu mpingo angakhalire thandizo kwa achichepere kukhala opita patsogolo mwauzimu?

23 Ena, nawonso, angathandize achichepere kupita patsogolo mwauzimu. Mungachipange icho kukhala chonulirapo kulankhula nawo pa msonkhano. Ndiponso, yesani kuwaphatikiza iwo mu ena a machitachita anu. Ndi chilolezo cha makolo, Mkulu, angakonze kutenga wachichepere pa thayo lokalankhula kapena kumuphatikiza iye pamene akupita kunja. (Yobu 31:16-18) Chimene chingawonekere kukhala chinthu chaching’ono chingatanthauze zokulira. Woyang’anira woyendayenda, powona kuti mnyamata amene anali kumvetsera ku nkhani yake analibe Baibulo, pambuyo pake analipanga limodzi kukhala mpnatso kwa iye. Mnyamatayo anasangalatsidwa osati kokha ndi mphatsoyo komanso ndi chikondwerero chosonyezedwa mwa iye. Zoposa zaka 30 pambuyo pake, mnyamatayo, tsopano mkulu iyemwini, amakumbukirabe ndi chikondi chisonyezero chachikondi cha mbaleyo.

24. Kodi nchiyani chimene chiri chosangalatsa kuchizindikira, ndipo kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chigamulo chathu?

24 Kodi sichiri chosangalatsa kuzindikira kuti mazana a zikwi za “achichepere monga madontho a mame” amene akufalitsa uthenga wa Ufumu wodzetsa mpumulo ndipo kuti pali chifupifupi chiwerengero chofananacho cha akazi achichepere omwe akupanga ‘khamu lalikulu lopereka mbiri vabwino’? Lolani onse a iwo adzipereke iwo eni kukhala opita patsogolo mwauzimu, ndipo lolani kuti tonse a ife tiwathandize iwo kufika ku mapeto amenewo.​—Masalmo 110:3; 68:11.

Mafunso Akubwereramo

◻ Kodi nchiyani chimene chingathandize achichepere kugamulapo kuti ndi liti pamene akabatizidwa?

◻ Kodi ndimotani mmene khalidwe la wachichepere limalingira ku kupita kwake patsogolo kwauzimu?

◻ Kodi nchiyani chimene chingathandize achichepere kusangalala ndi misonkhano ndi utumiki wa m’munda?

◻ Kodi ndi unansi wotani umene achichepere ayenera kukulitsa ndi achikulire?

◻ Kodi ndimotani mmene makolo ndi ena achikulire angathandizire achichepere?

Mafunso

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi nchiyani chimene chimakuletsani inu kubatizidwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena