Mtanda Wachikristu Asanafike Constantine?
”CHIZINDIKIRO cha mtanda chakhala chizindikiro cha zinthu zakale kwambiri, chopezeka chifupifupi mu miyambo iriyonse yodziwika. Tanthauzo lake lachititsa kakasi akatswiri odziwa za mafuko a anthu, ngakhale kuti kugwiritsiridwa ntchito kwake kwa mu zaluso zosonyeza maliro modziwika bwino kungaloze ku kuchinjiriza molimbana ndi choipa. Kumbali ina, crux ansata yotchuka ya ku Igupto, yosonyezedwa kukhala ikuchokera mkamwa, iyenera kulozera ku moyo kapena mpweya. Kugwiritsiridwa ntchito kwa dziko lonse kwa chizindikiro cha mtanda kumamveketsa maganizo kwambiri kusoweka kowonekera kwa mitanda mu zotsalira za Chikristu choyambirira, makamaka chisonyezero chachindunji chirichonse ku chochitika cha pa Golgota. Ophunzira ambiri tsopano amavomereza kuti mtanda, monga cholozera cha luso ku chochitika cha chikondi, sungapezeke kumayambiriro nthawi ya Constantine isanadze.”—Ante Pacem—Archaeological Evidence of Church Life Before Constantine (1985), ya Professor Graydon F. Snyder, tsamba 27.