Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w87 10/15 tsamba 4-7
  • Chikondi Kaamba ka Mulungu Chisonkhezero cha Makhalidwe Abwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikondi Kaamba ka Mulungu Chisonkhezero cha Makhalidwe Abwino
  • Nsanja ya Olonda—1987
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Malamulo Khumi​—Chisonkhezero cha Ubwino
  • Kodi Chikondi kaamba ka Mulungu Chimatanthauzanji?
  • Chikondi cha Mulungu Chisonkhezero cha Ubwino
  • Chikondi Sichilephera
  • Zimene “Kukonda Mulungu Kumatanthauza”
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Lamulo la Chikondi Lolembedwa M’mitima
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Kondani Mulungu Amene Amakukondani
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Tanthauzo la Kukonda Mnansi Wathu
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1987
w87 10/15 tsamba 4-7

Chikondi Kaamba ka Mulungu Chisonkhezero cha Makhalidwe Abwino

ANTHU olingalira mwamsanga angavomereze kuti mkhalidwe woipa ufunikira kuletsedwa. Monga mmene minisitala wa United Church of Canada anachiikira icho: “Zotulukapo zake, pamene anthu ndi chitaganya anyalanyaza lamulo la makhalidwe abwino, ziri zochititsa mantha; nkhondo, kupereŵera kwa ndalama, kugwiritsira ntchito udindo molakwa, ndi ulamuliro.” Monga mmene chasonyezedwera m’nkhani yapitayo, zipembedzo zazikulu zadziko iri sizinatsimikizire kukhala chisonkhezero champhamvu cha makhalidwe abwino. Chotero ngati ife mwaumwini tifuna kukhala miyoyo ya makhalidwe abwino tiyenera kuyang’ana ku ulamuliro wina kupereka mphamvu yoteroyo ndipo kenaka kukhala ofunitsitsa kugwirizana ndi ulamuliro umenewo.

Chisonkhezero cha maulamuliro a akulu oterowo chinali chowonekera m’nkhani ya moyo wa Yosefe, woyang’anira wa Chihebri wa bwalo la nduna ya Igupto. Pamene anakakamizidwa ndi mkazi wa nduna kukhala ndi mayanjano a kugonana ndi iye, Yosefe anakana, akumanena kuti: “Ndingachite bwanji choipa chachikuluchi ndi kuchimwira Mulungu?” (Genesis 39:7-9) Kuzindikira ulamuliro wa Mulungu ndi kukhumba kum’sangalatsa iye kunam’patsa Yosefe mphamvu ya makhalidwe abwino ya kupewa ziyesero zake.

Zaka mazana aŵiri pambuyo pake, mtundu wa Israyeli, mbadwa za atate wa Yosefe, Yakobo, unalandira Malamulo Khumi monga mbali ya Lamulo loperekedwa kupyolera mwa Mose. Pamene kuli kwakuti kusamvera kunapangitsa kupanda chiyanjo kwa Yehova Mulungu, kumvera ku Lamulo limeneli kunabweretsa madalitso aumulungu. Chotero malamulo amenewa anatumikira monga zitsogozo za makhalidwe abwino ku mtunduwo.

Malamulo Khumi​—Chisonkhezero cha Ubwino

Kodi Malamulo Khumiwo anali chisonkhezero cholimba motani? Chisonkhezero chawo chidakamvekabe mu zana lino la 20. Mu 1962 amene panthaŵiyo anali nduna yaikulu ya boma la New Zealand ananena kuti: “Ndikulingalira kuti anthu ena amalingalira kuti Malamulo Khumi ali akale. Koma sichingakhale chopanda zenizeni kuti ngati tonse mokhulupirika tisamalira iwo lerolino, lamulo wamba la dziko lingakhale lopindulitsa kwenikweni.”

Mosasamala kanthu za chimenecho, m’kukambitsirana ndi wolamulira wachichepere wa Chiyuda, Yesu Kristu anasonyeza kuti chinachake chowonjezereka kuposa kusunga Malamulo Khumi chinali chofunikira. Mwamuna wachichepereyo anali atafunsa kuti: “Nchiti ndichichite, kuti ndikhale nawo moyo wosatha?” Pamene Yesu ananena kuti ayenera “kusunga malamulo,” akumandandalitsa ena a Khumiwo, wolamulirayo anayankha kuti: “Zonsezi ndinazisunga, ndisowanso chiyani?” Yesu anayankha kuti: “Pita kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphaŵi, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba, ndipo ukadze kuno, unditsate.” Mbiriyo ikupitiriza kuti: “Koma mnyamatayo mmene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.”​—Mateyu 19:16-22.

Kuyerekeza kwa nkhaniyi yokhala ndi kufanana kumodzimodziko mu Luka 10:25-28 imatithandiza ife kuzindikira vuto lenileni la wolamulira wachichepereyo. Timaŵerenga kuti: “Wachilamulo wina anaimirira namuyesa iye [Yesu], nanena: ‘Mphunzitsi, ndidzalowa moyo wosatha ndi kuchita chiyani?’” Yesu anamuthandiza iye kulingalira pa nkhaniyo, ndipo monga chotulukapo chake, mwamunayo anali wokhoza kuyankha funso lake, akumanena molongosola: ‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.’ Yesu kenaka anamaliza kuti: “Chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.”

Kodi tsopano mungawone vuto la wolamulira wachichepere wotchulidwa poyambirirapo? Chikondi chake kaamba ka Mulungu ndi mnansi chinaphimbidwa ndi chikondi chake kaamba ka zinthu zakuthupi. Nchomvetsa chisoni chotani nanga! Mosasamala kanthu za kuyesayesa kwake kwa kusunga Malamulo Khumi, iye anali m’tsoka la kutaya moyo wosatha.

Kodi Chikondi kaamba ka Mulungu Chimatanthauzanji?

Timakhala m’nthaŵi pamene chikondi kaamba ka Mulungu ndi mnansi chalowedwa m’malo ndi kudzikonda, zinthu zakuthupi, ndi kugonana. Nkulekelanji, popeza ngakhale chikhulupiriro mwa Mulungu monga Mlengi chalowedwa m’malo m’malingaliro ambiri ndi chikhulupiriro m’nthanthi yosatsimikiziridwa ya chisinthiko. Nchiyani chimene chabweretsa zonsezi?

Kwa zaka mazana angapo, atsogoleri a chipembedzo a Dziko la Chipembedzo agwiritsira ntchito chiphunzitso chosazikidwa pa Baibulo cha moto wa helo wowopsya m’kuyesera kulamulira makhalidwe a anthu. Encyclopedia International ikunena kuti: “Chisonkhezero champhamvu kwambiri kaamba ka ubwino ndi anthu wamba kupyolera mu Mibadwo ya Pakati chinali mosakaikira mantha a helo, chimene chinapangitsa ngakhale Mafumu ndi Olamulira kukhala ogonjera ku Tchalitchi, ndipo chinali mwinamwake chiletso chokha chimene chinaletsa zikhumbo zawo.” Chiphunzitso cha moto wa helo chimenechi chinapangitsa chisonyezero chakuti Mulungu anali wopanda chikondi, wopanda chifundo, ndi wobwezera. Ngakhale kuti chiphunzitsocho chingakhale chinagwira ntchito monga chiletso kwa anthu ena, icho chinatembenuza ena kukhala kutali ndi Mulungu, kuwasiya iwo kukhala minkhole yopepuka ku ziphunzitso ndi nthanthi zosakhala za m’malemba, monga ngati zija za chisinthiko.

Baibulo, ngakhale kuli tero, siliphunzitsa kuti Mulungu amazunza miyoyo m’moto wa helo. M’malo mwake, mtumwi Yohane akutiuza ife kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” “Ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu.” Mose analemba kuti: “Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi.” (1 Yohane 4:8; 1:9; Eksodo 34:6) Iyi iri kokha mikhalidwe yochepa yosangalatsa ya Mulungu. Imatikokera ife kwa iye. Mikhalidwe imeneyi, makamaka chikondi chake, iri imene imatipangitsa ife kufuna kumkonda iye. “Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Chiri chikondi chimenechi kaamba ka Mulungu chimene chiri mphamvu yaikulu koposa kaamba ka makhalidwe abwino; chingatsogoze ku moyo wosatha!

Chikondi chenicheni kaamba ka Mulungu sichiri kokha mkhalidwe wosakhoza kuwoneka. Icho chimafulumiza munthu kuchita m’chikondwerero cha ena. Mtumwi Paulo anandandalitsa njira zambiri zimene chikondi chimenechi chingasonyezedwere. Kutchula zochepa zokha: “Chikondi chikhala chilezere, chiri chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsya mtima, sichilingalira zoipa.” (1 Akorinto 13:4, 5) Kusonyeza kwathu chikondi chimenechi kuli kuyesera kutsanzira Atate wathu wa kumwamba. Yesu ananena kuti: “Pa malamulo awa aŵiri [kukonda Mulungu ndi mnansi] mpokolowekapo Chilamulo chonse ndi Aneneri.” (Mateyu 22:40, An American Translation) M’mawu ena, ngati tisonyeza chikondi chimenechi, sitidzaba kuchokera kwa mnansi wathu kapena kumupha iye kapena kuchita chigololo ndi mkazi wake. Mtumwi Yohane anavomereza, akumanena kuti: “Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.”​—1 Yohane 5:3.

Chikondi cha Mulungu Chisonkhezero cha Ubwino

Dziŵani chotulukapo chimene chikondi choterocho kaamba ka Mulungu chinali nacho pa Akristu oyambirira, monga mmene chasonyezedwera ndi Tertullian, wa m’zana lachiŵiri. Iye anatokosa otsutsana nawo ake kuloza Mkristu mmodzi pakati pa apandu awo. Pamene iwo analephera, iye anawonjezera kuti: “Ife, chotero, tokha tiri opanda upandu.” Bukhu la The Old Roman World likuchirikiza kawonedweka, likumanena kuti: “Tiri ndi umboni ku kukhala kwawo miyoyo yopanda liwongo, ku makhalidwe awo opanda chitonzo.” Ndiponso, Christianity Today yagwira mawu wodziŵa mbiri yakale ya tchalitchi Roland Bainton kuti: “Kuchokera ku mapeto a nyengo ya m’Chipangano Chatsopano kufika ku nyengo ya zaka khumi 170-180 palibe chitsimikiziro cha mtundu uliwonse chakuti Akristu anali m’gulu la nkhondo.” Chikondi kaamba ka Mulungu chinawafulumiza iwo kumvera iye mwa kukhala miyoyo ya makhalidwe abwino. Inu mungadabwe, ngakhale kuli tero kuti, ‘Kodi pali chitsimikiziro cha mphamvu ya makhalidwe abwino yopindulitsa imeneyo lerolino?’

Ndithudi iripo! Wolemba nkhani m’danga la nyuzipepala Mike McManus analemba mu Herald & Review kuti iye anali asanamvepo nkomwe ulaliki wotsutsa kugonana kwa otomerana. Mwezi umodzi pambuyo pake iye anasimba kuti pakati pa makalata olandiridwa m’kuyankha panali imodzi kuchokera kwa wa zaka za kubadwa 14, mmodzi wa Mboni za Yehova, amene analemba kuti: “Kokha lingaliro la kutenda matenda amenewa liyenera kukhala lokwanira kuletsa anthu ambiri [ku kugonana kwa otomerana]. Koma chifukwa chimene Mboni zimapewera chiri chakuti Yehova amatilamulira ife kuthawa dama.” (Kanyenye ngwathu.) Kuchitira ndemanga pa kalatayo, McManus anafunsa: “Ndi a zaka za kubadwa 14 angati mu mpingo mwanu amene angagwire mawu St. Paul momvekera chotero (1 Akor. 6:18)?”

Prinsipulo limodzimodzilo la kumvera malamulo a Yehova, logwidwa mawu ndi mpsikana wachichepere ameneyo, likugwiritsiridwa ntchito kwa Mboni m’madera ena. Nsonga ya ena a malamulo a Mulungu olembedwa m’Malemba iri yakuti: ‘Khalani owona mtima mu zinthu zonse,’ ‘pewani mafano,’ ‘Salani mwazi ndi dama,’ ‘Khalani owona,’ ‘Phunzitsani ana anu njira za Mulungu.’ (Ahebri 13:18; 1 Yohane 5:21; Machitidwe 15:29; Aefeso 4:25; 6:4) Kodi mwawona kuti Mboni za Yehova m’malo anu kapena ku malo antchito zimayesera kumvera malamulo amenewa? Kodi munayamba mwadabwa kuti nchifukwa ninji zimachita tero, nchifukwa ninji zimakana kuthiridwa mwazi, nchifukwa ninji zimakana kupita ku nkhondo, nchifukwa ninji zimakuchezerani pa khomo lanu, m’njira ya pafupi nchifukwa ninji izo ziri zosiyanako? Chikondi chawo kaamba ka Mulungu ndilo yankho.

Chikondi Sichilephera

Kufuna kusangalatsa Mulungu, Mboni za Yehova zimatenga ku mtima uphungu wakuti: “Koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chiri chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Pamene izo ziphunzira chimene chiri “chifuno cha Mulungu” kaamba ka izo, zimafuna kuchita icho. Chikondi chawo kaamba ka Mulungu chiri mphamvu kumbuyo kwa chikhumbo chimenechi. Kodi mumadzimva kuti kumeneku kuli koseketsa, kosagwira ntchito m’nthaŵi yathu? Sinkhasinkhani kwa kamphindi pa zochitika zenizeni zotsatirazi.

Kubwerera m’mbuyo mu 1963, José, wa ku São Paulo, Brazil, anayamba kukhala ndi Eugênia, amene anali wokwatiwa kale. Zaka ziŵiri pambuyo pake, iwo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Kuchokera ku phunziro limeneli aŵiri amenewa anaphunzira kuti Mulungu amafuna kuti “ukwati uchitiridwe ulemu pakati pa onse.” (Ahebri 13:4) Iwo anazindikira kuti anayenera kukwatirana, koma dziko la Brazil linalibe lamulo la chilekaniro mwa limene Eugênia akanakhala womasuka kukwatiwa ndi José. Ngakhale kuli tero, mu 1977, pamene lamulo la chilekaniro linayamba kugwira ntchito, iye anafunsira kaamba ka chilekaniro, ndipo mu 1980 iwo anali okhoza kukwatirana, kukwaniritsa zifuno za Mulungu. Chikondi chawo kaamba ka Mulungu chinali ndi mphoto yake.

Inire anali atayesera anamgoneka osiyanasiyana mu New York. Iye anali kukhala ndi bwenzi lake lachikazi, Ann. Akufuna ndalama, iye anamuuza mtsikanayo kutumiza zithunzi zake ku magazini yotchuka kwambiri ya amuna. Iye anapatsidwa ndalama zochulukira kuti akaime wamaliseke pa gawo la kutengedwa zithunzithunzi. Panthaŵiyo, Inire anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndipo kenaka Ann anagwirizana naye. Inire analeka kugwiritsira ntchito anamgoneka. Pambuyo pa milungu itatu iwo, pa iwo okha, anasankha za kukwatirana. Kenaka, kuphunzira kuchokera m’Baibulo kuti Mkristu ayenera kuvala modzichepetsa, Ann analingalira kuti sakayenera kuvomereza mwa chikumbumtima ku gawo la kutengedwa chithunzilo, mosasamala kanthu kuti ndi ndalama zochuluka chotani zimene zinaperekedwa. (1 Timoteo 2:9) Kodi nchiyani chimene mukulingalira kuti chinasonkhezera masinthidwe oterowo? Ann akunena kuti pamene anazindikira kuti kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova sikunali kokha nkhani ya kugwirizana ndi chipembedzo komanso kumaphatikizapo kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu, iye anadziŵa kuti anayenera kuchita masinthidwewo mofulumira. Zowonadi, chikondi kaamba ka Mulungu chiri chisonkhezero champhamvu kaamba ka ubwino.

Winawake angadzimve kuti, ‘Chabwino, izi ziri nkhani za kamodzikamodzi.’ Koma izi siziri. Masinthidwe ofananawo achitika nthaŵi zambiri m’malo osiyanasiyana kumene Mboni za Yehova ziri zokangalika. Bwanji osayang’ana m’nkhaniyo mowonjezereka? Tsimikizirani kaamba ka inumwini kuti chikondi kaamba ka Mulungu monga mmene chasonyezedwera m’chipembedzo chowona chidakali mphamvu kaamba ka makhalidwe abwino.

[Mawu Otsindika patsamba 6]

Ponena za Akristu oyambirira, bukhu la “The Old Roman World” linanena kuti, “Tiri ndi umboni ku miyoyo yawo yopanda banga ku makhalidwe awo opanda chitonzo.” Nchiyani chimene chinali mphamvu kumbuyo kwa “makhalidwe awo abwino opanda chitonzo”?

[Chithunzi patsamba 7]

Chikondi kaamba ka Mulungu Chingakuthandizeni kupewa kuyesedwa kulowa mkachitidwe kolakwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena