Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi nchiyani chimene chinali cholakwa cha Mose chimene chinamutaitsa mwaŵi wake wa kulowa Dziko Lolonjezedwa? Kodi chifukwa chinali cha kumenya thanthwe m’malo mwa kungolankhula ku ilo kapena kuti iye analephera kulemekeza Yehova Mulungu?
Chikuwoneka kuti cholakwa cha Mose chinali choposa kuti iye anangokantha thanthwe m’malo mwa kulankhula ku ilo, monga mmene anatsogozera Mulungu.
Pafupi ndi mapeto a zaka 40 za kuyendayenda Aisrayeli anamanga msasa pa Kadesi-barinea m’chipululu cha Zini (kapena, Parana). Iwo anali atamanga msasa pamenepo zaka makumi ambiri poyambirira, mwachiwonekere chifukwa akasupe atatu m’deralo anatulutsa malo okhala ndi madzi obiliŵira, monga amene akuwonekera pa chithunzi chotsatirachi. Pa chochitikachi, ngakhale kuli tero, madzi anali osowa, chomwe mwinamwake chinatanthauza kuti anthuwo sakanapeza chakudya chambiri. Chotero iwo anakangana ndi Mose, woimira wa Yehova, akumanena kuti: “Ndipo munatikwezeranji kutitulutsa m’Igupto, kutilowetsa m’malo oipa ano? Si malo a mbewu awa, kapena mkuyu, kapena mpesa kapena makangaza; ngakhale madzi akumwa palibe.”—Numeri 20:5.
Kenaka Mulungu anauza Mose ndi Aroni: “Tenga ndodoyo, nusonkhanitse khamulo . . . munene ndi thanthwe pamaso pawo, kuti liwapatse madzi; potero uwatulutsire madzi m’thanthwe, ndi kumwetsa khamu la anthu ndi zoweta zawo.” (Numeri 20:8) Nchiyani chimene chinachitika kenaka?
“Ndipo Mose ndi Aroni anasonkhanitsa msonkhano pathanthwe, nanena nawo iye: ‘Tamvanitu, opikisana naye inu! Kodi tikutulutsireni madzi m’thanthwe umu?’ Ndipo Mose anasamula dzanja lake, napanda thanthwe kaŵiri ndi ndodo; ndipo madzi anatulukamo ochuluka.”—Numeri 20:10, 11.
Ena adziŵa kuti Mulungu anatsogoza Mose ndi Aroni “kulankhula ku thanthwe,” koma iwo “anakantha thanthwe.” Kodi kusiyana kumeneko kunakhala kosamsangalatsa Yehova kotero kuti anauza Mose ndi Aroni kuti Iye sadzawalola iwo kutsogolera Aisrayeli m’Dziko Lolonjezedwa?
Sizikuwoneka tero. Nsonga iri yakuti kokha miyezi yocheperapo pambuyo pa Kutulukako, anthuwo choyamba anadandaula chifukwa cha kusoweka kwa madzi. Pamenepo panali pafupi ndi Phiri la Sinai (Horebe), pamalo amene anadzatchedwa Meriba (m’gawo lowonekera pansipa). Dziŵani chimene Mulungu anauza Mose pa chochitika chimenecho: “Tawona ndidzaima pamaso pako pathanthwe m’Horebe. Ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe.” (Eksodo 17:2-7; 33:6) Chotero pamene, anafika pa Kadesi, Mose anauzidwa kulankhula ku thanthwe, iye angakhale anali ndi chikhoterero cha kuchita chimene anali atachita poyambirirapo pa chitsogozo cha Mulungu, ngakhale ngati Mulungu anatanthauza kuti kulankhula ndi thanthwelo kukakhala kokwanira.
Chikuwoneka ngati kuti chinachake chowonjezereka chinatsogoza Mulungu ku chiweruzo cha Mose ndi Aroni. Nchiyani chimene mwinamwake chimenecho chingakhale? Mose ananena kwa anthu okanganawo: “Kodi tikutulutsireni madzi m’thanthwe umu?” Masalmo 106:33 amatipatsa ife chidziŵitso mu ichi, popeza amasonyeza kuti Mose anachita ndi mzimu wa mkwiyo ndipo chotero iye ‘analankhula mwasontho ndi milomo yake.’ Ndi mawu aukali, iye anapereka chisamaliro kwa iyemwini ndi Aroni m’malo mwa kwa Mmodzi amene mowonadi anali kupereka madzi mozizwitsa. Chotero, Mose asanafe pa malire a Dziko Lolonjezedwa, Mulungu analozera ku chochitika cha pa Kadesi-barinea ndi kusonyeza kuti cholakwa cha Mose chinali chakuti iye analephera ‘kuyeretsa Mulungu pamaso pa anthu.’—Numeri 27:12-14.
Tingatenge phunziro kuchokera ku ichi. Pamene chiridi chofunika kwambiri kudziletsa ife eni ku m’chitidwe wa mkwiyo, chiri mofananamo chofunika koposa kulamulira mzimu wathu, makamaka pamene ena alakwa. Pamene tidzilola ife eni kukhala ovutitsidwa mopambanitsa, tingayambe kuwona atumiki a Mulungu pa maziko a anthu, m’malo mwa kuzindikira kuti adakali “nkhosa” za Mulungu. Zowona, iwo ali opanda ungwiro ndipo angachite zinthu zowaŵitsa mtima, koma iwo ali “anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake.” (Masalmo 100:3) Mulungu analola Mwana wake kufa kaamba ka anthu oterowo, chotero kodi sitiyenera kukalamira kukhala oleza mtima ndi iwo, kupereka chisamaliro chochepera pa mmene tikudzimverera kapena mmene tiyambukiridwira ndi kupereka chisamaliro chambiri pa kaimidwe kawo ndi Mulungu?
[Zithunzi patsamba 31]
Nthaŵi ya ngululu pa chidikha cha madzi pafupi ndi umodzi wa akasupe m’dera la Kadesi-barinea
[Mawu a Chithunzi]
Photos, pages 10, 31: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.