Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 1/15 tsamba 6
  • Wachikulire Woyamikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wachikulire Woyamikira
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Banja Lachikristu Limathandiza Okalamba
    Nsanja ya Olonda—1993
  • “Muziyamika pa Chilichonse”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
  • Kusamalira Okalamba ndi Udindo wa Akristu
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kumayang’anitsitsa pa Zikondwerero za Okalamba
    Nsanja ya Olonda—1987
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 1/15 tsamba 6

Wachikulire Woyamikira

Mkazi wa zaka zakubadwa 79 wa ku Japan anafulumizidwa kulemba kalata yotsatirayi pambuyo pa kuŵerenga kope la June 1, 1987, la Nsanja ya Olonda pa mutu wakuti “Ndani Adzasamalira Okalamba?”

Kwa Abale Amene Ndimawakonda,

Pambuyo pa kuphunzira kope la June 1, 1987, lonena za okalamba, ndikupeza nkhaniyo kukhala yomvetsetsa ndi yachifundo. Pamene ndinafika pa ndime 11, ndinayenera kutenga kansalu kanga kominira chifukwa ndinangolira ndi kulira ndipo sindinathe kuleka. Iyo inali misozi ya chiyamikiro chozama. Ndi chikondi ndi kukoma mtima kotani nanga! Ndinangotha kokha kuchita zimene Masalmo 150 amanena​—lemekezani Ya! Modzichepetsa ndikupereka kuyamikira kwanga kozama kwa inu abale kaamba ka kufalitsa nkhani zolingalirika zimenezi pa kusonyeza kukoma mtima kwa anthu okalamba, kufikira ku tsatanetsatane wabwino koposa. Ndithudi, ndiri woyamikira kaamba ka nkhani zabwino zimene mumafalitsa mwezi uliwonse, ndipo palibe mawu akulongosolera chiyamikiro changa mokwanira. Kachiŵirinso, ndikuthokozani.

Mwachimwemwe, aliyense mu mpingo mwathu ali wachikondi ndi wachifundo. Amanditenga ine kupita ndi kuchoka m’gawo lolalikira m’magalimoto awo, ndipo chifukwa cha utumiki wawo wachifundo, ndine mpainiya wothandizira. Ndiri woyamikira mozama kaamba ka tsiku lirilonse limene ndingakhale ndi moyo mu gulu losangalatsa ndi lotetezera lotereli.

M’dziko lerolino, kumene anthu achikulire akukhala ochuluka koposa koma olandiridwa mochepera, palibe china chirichonse cha mtengo wapatali kuposa madalitso amene timalandira kuchokera kwa Mulungu wachikondi woteroyo. Liri pemphero langa kuti ndingathandize anthu ambiri monga mmene ndingathere kuphunzira chowonadi kotero kuti iwo angasangalale limodzi ndi ife.

Ulemerero upite kwa Yehova ndi chiyamikiro kwa inu, abale anga okondedwa. Chonde ndikhululukireni kaamba ka kalembedwe kanga koipa, kamene ndichita nako manyazi. Lolani Yehova akudalitseni ndi kukupatsani umoyo wabwino.

Mkazi wachikulire wosayenera,

[anasaina] Nogami

Mawu ndi ziyamikiro zonga izi zimatsimikizira chenicheni chakuti chikondi cha Chikristu chowona sichimadziŵa malire kapena malire a msinkhu. Mboni za Yehova, zachichepere ndi zachikulire, zimasonyeza kukhala kwawo ophunzira mwa kukhalira moyo ku mawu a Yesu akuti: “Mwa ichi adzadziŵa kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano pakati pa inu nokha.”​—Yohane 13:35.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena