Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 2/1 tsamba 28-29
  • Chifukwa Chimene Inu Muyenera Kukhala ndi Chikondwerero

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifukwa Chimene Inu Muyenera Kukhala ndi Chikondwerero
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Pamene Ambiri Sanasonyeze Chikondwerero
  • Awo Amene Sanali Okondwerera M’tsiku la Yesu
  • Sonyezani Chikondwerero​—Chimatanthauza Moyo Wanu!
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amabwereranso Kunyumba za Anthu Omwe Anakana Kuti Awalalikire?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Konzekerani Kaamba ka Chipulumutso Kuloŵa M’dziko Latsopano
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Tifunika Kukhala Maso Kwambiri Tsopano
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1988
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 2/1 tsamba 28-29

Chifukwa Chimene Inu Muyenera Kukhala ndi Chikondwerero

‘KUKONDWERETSEDWA m’chiyani’? Kusintha kwakukulu kwambiri komwe kudzachitika m’mbiri ya mtundu wa munthu! Boma latsopano lotheratu lopangidwa ndi Mulungu liri pafupi kulanda chiwonetsero cha dziko lapansi. (Danieli 2:44) Kulandako kudzayambukira mwamuna aliyense, mkazi, ndi mwana​—kaya kaamba ka ubwino kapena kaamba ka kuipa. Kusintha kowonekera kumeneku kudzachitika mkati mwa mbadwo wotchulidwa pa Mateyu 24:34. Chotero, uthenga wonena za kusinthako ufunikira chikondwerero chenicheni chowona mtima cha anthu onse. Ndithudi, chidzakhala cholakwa kunena kuti, ‘Sindiri wokondweretsedwa.’

Pamene Ambiri Sanasonyeze Chikondwerero

Nthaŵi yathu yamakono siiri nthaŵi yoyamba kuti uthenga wofunika kwambiri ndi wachangu ukulengezedwa womwe uyenera kudzutsa chikondwerero cha awo omwe anaitanidwa kudzamva iwo. Tsiku la Nowa linali limodzi la nthaŵi yoteroyo. Chifukwa cha kuipa kwa anthu, makhalidwe oipa, ndi umunthu wachiwawa pa nthaŵiyo, Yehova Mulungu anakonzekera kuwononga mtundu wa anthu mu chigumula chachiwunda chonse cha dziko. (Genesis 6:5-7, 13) Komabe, asanachitepo kanthu kuwononga opanda umulungu, iye anakonzekeretsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, kuwachenjeza iwo za chigumula chomadzacho ndi njira ya kachitidwe imene iwo anafunikira kuilondola kuti adzasungidwe amoyo. Wofunika monga mmene uthengawo unaliri, mwachisawawa anthu amene anamva iwo “sanadziŵa.” (Mateyu 24:39; Luka 17:26, 27; 2 Petro 2:5) Iwo analibe chikondwerero, osiyana​—sanali okondweretsedwa nkomwe! Chifukwa cha ichi, iwo anataya chirichonse.

Mkhalidwe wofananawo unalipo m’masiku a nzika za mizinda ya mikhalidwe yoipa ya Sodomu ndi Gomora. Ngakhale kuti anachenjezedwa za chiwonongeko chawo chomayandikira chifukwa cha kuipa kwawo, iwo sanamvetsere. Iwo nawonso sanali okondweretsedwa mwa aliyense yemwe akasokoneza njira yawo ya moyo yozoloŵereka. Mwamuna Loti anali yekha amene anapatulidwa.​—Genesis 18:20-30; 19:1-29; Luka 17:28-30

Chotero, uthengawo unali wachilendo pakati pa nzika za mizinda imeneyi. Mwinamwake iwo anali odera nkhaŵa kwambiri ponena za chimene anansi awo akalingalira ponena za iwo ngati anasonyeza chikondwerero. Kapena mwinamwake iwo anawopa kuti iwo akafunikira kupanga masinthidwe m’miyoyo yawo omwe iwo sanali ofunitsitsa kupanga. Mwachiwonekere, iwo anasangalala ndi njira yawo ya moyo yoipa. (Yuda 7) Chotero kufikira ku tsiku limene chiwonongeko chawo chinabwera, iwo sanakaikire chirichonse ndipo sanagwire lingaliro la chimene chinali pafupi kuchitika.

Awo Amene Sanali Okondwerera M’tsiku la Yesu

Pamene Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, anali pa dziko lapansi, iye anatumiza atsatiri ake kukalalikira mbiri yabwino yonena za boma la kumwamba la Mulungu. (Mateyu 10:7) M’chenicheni, iye analangiza ophunzira ake m’njira imene iwo anayenera kuperekera uthenga wachilendo ndi wofunika kwambiri umenewo pa khomo lirilonse ndi masitepi oyenera kuwatenga pamene eninyumba analephera kusonyeza chikondwerero chenicheni. Mvetserani kwa iye pamene akupitiriza kuphunzitsa ophunzira ake: “Ndipo polowa m’nyumba muwalankhule. Ndipo ngati nyumbayo iri yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siiri yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene mulikutuluka m’nyumbayo, kapena m’mudzimo, sansani fumbi m’mapazi anu.”​—Mateyu 10:12-14.

Dziŵani kuti Yesu analangiza ophunzira ake “kusansa fumbi m’mapazi [awo]” pamene iwo anachoka ku nyumba kapena mudzi kumene kunalibiretu chikondwerero mu Ufumu wa Yehova. Nchiyani chimene iye anatanthauza ndi langizo limeneli? Kusansa fumbi m’mapazi a wina kumasonyeza kudzichotsera thayo kapena kuŵerengera zotulukapo za mwininyumba amene adzavutika chifukwa cha kusoweka kwake kwa chikondwerero mu uthenga wa Mulungu. Chinasonyeza kuti atsatiri a Yesu anali kuchoka mwamtendere ndipo anasiya nyumba imeneyo kapena mudziwo ku zotulukapo zomwe zidzabwera kuchokera kwa Mulungu.

Sonyezani Chikondwerero​—Chimatanthauza Moyo Wanu!

Chiri chosangalatsa kudziŵa kuti Yesu Kristu anayerekeza chivomerezo cha tsiku lathu ndi chija cha masiku a Nowa ndi a Sodomu ndi Gomora. (Mateyu 24:37-39; Luka 17:26-30) Mkhalidwe woipa wa chisembwere ndi chiwawa zinali zofala ponse paŵiri m’masiku a Nowa ndi m’masiku a Loti. Ndithudi, munthu wolungama Loti anazunzidwa ndi kuvutitsidwa mtima pamene anawona kusayeruzika ndi kumwerekera mu mkhalidwe woipa kwa nzika za Sodomu ndi Gomora.​—2 Petro 2:6-8.

Komabe, pamene Yesu analozera ku tsiku la Nowa ndi ku tsiku la Loti, iye analunjikitsa chidwi chathu, osati pa mkhalidwe woipa wachisembwere ndi chiwawa cha nthaŵi imeneyo, koma, m’malomwake, pa zodera nkhaŵa za tsiku ndi tsiku​—kudya, kumwa, kukwatira, kukwatiwa, kugula, kugulitsa, kumanga, ndi kubzyala. Iye anasonyeza kuti ambiri sadzavomereza ku uthenga wa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu koma adzakhala otanganitsidwa kotheratu ndi zochitika za tsiku ndi tsiku za moyo ndipo chotero sadzasonyeza chikondwerero mu zimene Yehova akukonzekera kuchita. Uthengawu uli umodzi wa kufunika kwa moyo kapena imfa. Kulephera kumvetsera kudzakhala kosakaza. Kusadziŵa kapena kusasonyeza chikondwerero liri chimo lalikulu.​—Yerekezani ndi Mateyu 6:31, 32.

Kodi iko kuli koipa motani? Yesu anapitiriza kulongosola kuti: “Pa Tsiku la Chiweruzo Mulungu adzasonyeza chifundo chochuluka kwa anthu a Sodomu ndi Gomora kusiyana ndi anthu a mudzi umenewo” omwe sanamvetsere kapena kusonyeza chikondwerero. (Mateyu 10:15, Today’s English Version) Ngati munthu asonyeza chikondwerero, kumvetsera, ndi kukhulupirira uthengawo, ngakhale ngati iye angakhale wa mkhalidwe woipa ndi wachiwawa, iye angasinthe umunthu wake ndi kupeza chiyanjo m’maso mwa Yehova kuyenerera monga nzika ya ufumuwo, monga mmene anachitira Akristu oyambirira ku Korinto.​—1 Akorinto 6:9-11.

M’kukambitsirana kwake konse ndi ophunzira ake, Yesu Kristu anawafulumiza iwo kumvetsera, kupereka chisamaliro, ndi kusonyeza chikondwerero mu uthenga wofunika kwambiri wa Ufumu wa Mulungu. Kuti akoke chidwi cha awo omwe analankhulako, iye anachenjeza kuti: “Yang’anirani mamvedwe anu.” “Amene ali nawo makutu amve.” “Mverani ine nonsenu, ndipo dziŵitsani.” “Imvani nimudziŵitse.”​—Luka 8:18; Marko 4:9; 7:14; Mateyu 15:10.

Chotero, nthaŵi ina pamene m’modzi wa Mboni za Yehova adzaitanira pa nyumba yanu, chidzakhala ku phindu lanu kunena kuti: ‘Lowani, ndiri wokondweretsedwa.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena