Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 2/1 tsamba 30-31
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Kuzindikira Zimene Ife Tiri’—Panthawi ya Chikumbutso
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • N’chifukwa Chiyani Timachita Mwambo Wokumbukira Imfa ya Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi Mgonero wa Ambuye Tiziukumbukira Motani?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kusonkhanitsa Zinthu za Kumwamba ndi za Padziko Lapansi
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 2/1 tsamba 30-31

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

◼ Nchifukwa ninji zochepera za Mboni za Yehova zimadyako mkate ndi vinyo pa chikumbukiro cha chaka ndi chaka cha Mgonero wa Ambuye?

Ichi chiri chifukwa chakuti Mboni za Yehova, mosiyana ndi matchalitchi a Chikristu cha Dziko, zimalandira chiphunzitso cha Baibulo chakuti chiŵerengero chochepa cha anthu adzapeza moyo wa kumwamba ndipo otsalira a atumiki okhulupirika a Mulungu adzafupidwa ndi moyo wosatha pa dziko lapansi.

Matchalitchi kwa nthaŵi yaitali aphunzitsa kuti kumwamba iri mphoto kaamba ka awo amene amasangalatsa Mulungu; ena onse amapita ku moto wa helo. Baibulo limanena mosiyanako. Malemba mwachiwonekere amasonyeza kuti kokha anthu ena, monga ngati atumwi, adzalamulira ndi Kirstu kumwamba. Yesu ananena kuti, awa ali “kagulu ka nkhosa.” Baibulo limanena kuti iwo amafika pa chiŵerengero cha 144,000. (Luka 12:32; Chivumbulutso 14:3, 4) Ambiri omwe anatumikira Yehova mokhulupirika ndipo anali ndi chivomerezo chake anafa Yesu asanatsegule njira ya kumoyo wa kumwamba. (Mateyu 11:11; Ahebri 10:19-21) Ndipo pambuyo pa kusankhidwa kwa “kagulu ka nkhosa,” mamiliyoni a ena akhala Akristu owona. Kaamba ka okhulupirika onsewa osakhala a “kagulu ka nkhosa,” Baibulo limapereka chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso wobwezeretsedwanso wa padziko lapansi. (Masalmo 37:20, 29; Chivumbulutso 21:4, 5) Koma nchifukwa ninji oterowo sadyakonso mkate ndi vinyo? Yesu anasonyeza kuti kudyako ziphiphiritso mkati mwa Mgonero wa Ambuye kunali kokha kaamba ka awo oitanidwa kaamba ka moyo wa kumwamba, awo amene ali m’pangano latsopano.

Ndithudi, chikhulupiriro mu nsembe ya Yesu chiri chofunika kaamba ka onse omwe adzafunikira kupeza chikhululukiro cha Mulungu ndi moyo wosatha, kaya moyo kumwamba kapena moyo pa dziko lapansi la paradaiso. Kristu anasonyeza ichi pa Yohane 6:51-54: “Mkate wa moyo wotsika kumwamba Ndine amene. Ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha. . . . mkate umene ndidzapatsa Ine, ndiwo thupi langa, ukhale moyo wa dziko lapansi [mtundu wa anthu owomboledwa] . . . Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha.”

Komabe, chiri chodziŵikiratu kuti Yesu analunjikitsa mawu amenewo kwa oposa ophunzira ake. Tsiku limodzi pambuyo pa kudyetsa mozizwitsa zikwi, khamu linabwera kwa Yesu m’gawo la Kapernao. Khamu limeneli linamuloŵetsa iye m’kukambitsirana komwe kunaphatikizapo mawu ake a pa Yohane 6:51-54. Chotero Yesu sanali kulankhula makamaka kwa ophunzira ake pamene iye ananena kuti iye anali “mkate wophiphiritsira womwe unabwera kuchokera kumwamba” womwe ukapereka ziyembekezo zopambana za moyo kuposa mana omwe anadyedwa m’chipululu.​—Yohane 6:24-34.

M’kulingalira chokumana nacho chakale chimenecho m’chipululu, kumbukirani ndani amene anatuluka m’Igupto kupita m’chipululu. Anali ‘ana Aisrayeli ndi zikwi mazana asanu ndi limodzi oyenda okha, ndiwo amuna, osaŵerengera ana, ndi anthu ambiri osakanizana (NW.)’ (Eksodo 12:37, 38; 16:13-18) “Anthu osakanizana” amenewa anaphatikizapo Aigupto omwe anakwatiwa ndi Aisrayeli ndi Aigupto ena omwe anasankha kuyenda ndi Aisrayeli. Ponse paŵiri Aisrayeli ndi “anthu osakanizana” anafunikira mana kuti akhale ndi moyo. Ngakhale kuli tero, kodi “anthu osakanizana,” anali ndi ziyembekezo zofanana ndi Aisrayeli? Ayi, iwo analibe. Ngakhale kuti iwo akalambira pakati pa Israyeli ndi kuyembekezera kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, iwo sakakhala mafumu kapena ansembe pansi pa Pangano la Chilamulo. Chotero kudya mana enieni m’chipululu sikunapatse aliyense ziyembekezo zofanana.

Uku ndi kusiyana kumene muyenera kukumbukira pamene mukuwunikira pa zimene Yesu ananena kwa ophunzira ake chifupifupi chaka chimodzi pambuyo pa kulankhula mawu a pa Yohane 6:51-54. Pa chochitika chochedwerapo chimenechi, Yesu anali kulongosola kachitidwe katsopano kokhudza mkate weniweni ndi vinyo zomwe zimayenera kuimira thupi lake ndi mwazi. Pamene iye anali kukhazikitsa chikondwerero cha Mgonero wa Ambuye, Yesu ananena kwa atsatiri ake kuti: “Chikho ichi ndi pangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.” Ku gulu laling’ono limodzimodzilo la atumwi, iye anawonjezera kuti: “Koma inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuŵeruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.”​—Luka 22:20, 28-30.

Onani kuchokera ku mawu omalizira amenewa kuti awo amene anayenera kudya mkate weniweni ndi kumwa vinyo weniweni monga ziphiphiritso zoimira thupi ndi mwazi wa Kristu anali ophunzira a mu “pangano latsopano.” Oterowo akakhalanso mu pangano lina limene Yesu akupanga ndi iwo kotero kuti iwo angagawane mu ulamuliro ‘mu ufumu wake.’ Mwachiwonekere, pano Yesu anali kulozera kwa awo amene ‘anapangidwa ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu, kulamulira monga mafumu pa dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 5:10) M’zana loyamba, Mulungu anayamba kusankha a 144,000 omwe akagawana mu ufumu wa kumwamba. Akristu a ku Korinto anali a gulu limenelo, popeza iwo analongosoledwa monga amene anali “oyeretsedwa mwa Kristu Yesu, oitanidwa akhale oyera mtima.” (1 Akorinto 1:2; yerekezani ndi Aroma 1:7; 8:15-17.) “Oyera mtima” oterowo anayenera kugawana mu Mgonero wa Ambuye, kudyako ndi chiyamikiro mkate wophiphiritsira ndiponso vinyo wotanthauza “pangano latsopano mwazi [wake].”​—1 Akorinto 11:23-26.

Lerolino padakali amoyo pa dziko lapansi kokha kagulu kochepa ka otsalira ka awo osankhidwa ndi Mulungu kaamba ka moyo wakumwamba. Kokha oterowo omwe ali “m’pangano latsopano” amavomerezedwa kudya ziphiphiritso, mkate ndi vinyo, mkati mwa chikondwerero cha Chikumbutso cha chaka ndi chaka.

Ndithudi, Akristu onse owona lerolino omwe amayang’ana kutsogolo ku kukhala ndi moyo kosatha pa dziko lapansi pansi pa ulamuliro wa Ufumu amadziŵa kuti ichi chiri chothekera mwa kusonyeza chikhulupiriro mu nsembe ya Yesu. Monga mmene Yesu anauzira khamu, iye ali “mkate wa moyo wochokera kumwamba.” (Yohane 6:51) Komabe, chimenecho sichimatanthauza kuti awo amene ali ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi ayenera kudyako ziphiphiritso zenizeni za chikumbutso, popeza iwo sali “m’pangano latsopano,” ndiponso iwo sali “m’pangano” ndi Yesu kudzakhala ‘mu ufumu wake, kukhala pa mipando yachifumu.’

Chotero, gulu lalikulu limeneli lokhala ndi ziyembekezo za pa dziko lapansi silidyako ziphiphiritso, mkate ndi vinyo. Koma ichi m’njira iriyonse sichimawunikira kusoweka kwa chikhulupiriro kapena kuyamikira kaamba ka thupi ndi mwazi wa Yesu. M’chenicheni, chifukwa cha chiyamikiro chawo chozama kaamba ka nsembe yake ndi chiyembekezo chosangalatsa cha pa dziko lapansi kutsogolo kwawo, iwo motsimikizirika kwambiri amapezekapo chaka chirichonse monga openyerera aulemu a chikondwerero cha Mgonero wa Ambuye. M’njira imeneyi, iwo amawunikira chikhulupiriro chawochawo ndi kupereka chitsimikiziro chachimwemwe kuti otsalira a “kagulu ka nkhosa” ndi khamu lalikulu la “nkhosa zina” ali m’chigwirizano chotentha.​—Yohane 10:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena