Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 2/15 tsamba 3
  • Kodi Kuwona Mtima Kuli Kwachikale?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Kuwona Mtima Kuli Kwachikale?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Chimatanthauzanji Kukhala Wowona Mtima?
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Chitani Zinthu Zonse Moona Mtima
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Muzichita Zinthu Zonse Mwachilungamo
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kuchita Zinthu Mwachilungamo N’kothandiza
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 2/15 tsamba 3

Kodi Kuwona Mtima Kuli Kwachikale?

KUSUNGILIRA kuwona mtima monga njira ya moyo​—Kodi iko kuli kwachikale m’dziko lamakono, kosiidwa kukhala kosagwiranso ntchito kapena kopanda phindu lenileni? Chingawoneke tero. Tangolingalirani zitsanzo zochepera za mmene kusawona mtima kuliri kofalikira, mkhalidwe umene kumatenga, ndi ukulu ku umene iko kwalowerera, ndipo ndi kusakaza kotani nanga kumene thayo lake lakhalira.

M’zaka zaposachedwapa, chiŵerengero cha ndalama za kunyenga kwa misonkho mu West Germany chayerekezedwa pa $10 biliyoni (U.S.) pa chaka, ndipo mu Sweden chiŵerengero cha ndalama za pa chaka zikufika ku $720 (U.S.) pa munthu mmodzi. Chotero ngati mumakhala mu lirilonse la maikowa, kusawona mtima kumayambukira zimene mumapereka m’misonkho. Kunyenga pa misonkho yolipiridwa kuli kofala kwambiri mu United States chakuti boma limataya kuyerekeza kwa $100 biliyoni m’misonkho ya pa chaka. Tangolingalirani ndi thandizo lotani limene ndalama zonsezo zikanakhala m’kulipira ngongole yosatha ya ndalama za boma! Kuwonjezerapo, mabizinesi opanda lamulo amabera boma la U.S. ndalama zina zokwanira $10 biliyoni. Kuba zinthu mu golosale ndi kuba kwapang’onopang’ono mu United States kumathera masitolo $4 biliyoni pa chaka, kukumawonjezera mitengo ya zinthu. Kusawona mtima kwa kulipiritsa ndalama zambiri pa lamya yotumizidwa kutali pa nambala ya winawake kukuthera anthu a ku America $1 miliyoni pa chaka.

Mu Canada “akuba nthaŵi,” awo amene amawononga nthaŵi pa ntchito, amawonongera owalemba ntchito $15 biliyoni (Canadian) pa chaka, “kuposa nthaŵi zitatu chiwonkhetso chonse chotaika kupyolera mwa olembedwa ntchito akuba, kusakaza ndalama, kunyenga kwa ndalama zoikidwa kaamba ka chisungiko, kusakaza katundu, kulandira ndalama za chinyengo, kutentha zinthu ndi maupandu ena enieni otsutsana ndi bizinesi.” Mogwirizana ndi phunziro la mu 1986, thayo la kuba nthaŵi mu United States liri $170 biliyoni pa chaka.

Makampani a chipambano a madola mamiliyoni ochuluka mwadyera amaba kuchokera ku maboma awo. Motani? Mwakuwagulitsa iwo zipangizo ndi ziwiya pa mtengo wapamwamba koposa: maallen wrenches a 12 cents pa $9,606 (U.S.); matransistors a 67-cents pa $814; zotsekera za pulasitiki za miyendo ya timatebulo za 17-cents pa $1,118. “Mukulankhula ponena za mabiliyoni a madola” otaikiridwa ndi boma, chinatero chiwalo cha boma la U.S.

Kuwonjezera zapamwambazi, zitsanzo zoipa kulikonse zochitidwa ndi anthu otchuka zimakhumudwitsa kuwona mtima. Monga mmene mungakhale munawonera, atsogoleri m’maiko ena amanama, kuimira molakwika, kubisa, ndipo ngakhale kulanda mathayo awo​—inde, ngakhale kupha opikisana nawo anzawo andale zadziko ndi kuchipanga icho kuwoneka kuti winawake ayenera kukhala ndi liwongo.

Chotero kodi kukhala wowona mtima kuli kwachikale? Kodi iko sikulinso mchitidwe wabwino koposa? Kodi kuwona mtima kuli kwabwino koposa kokha chifukwa chakuti Mawu a Mulungu amatiuza ife kuti tiyenera kukhala owona mtima? Nkhani yotsatira iri yofunika koposa kwa inu ngati mukufuna mayankho ku mafunso amenewa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena