Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 4/15 tsamba 10-15
  • Nthaŵi Zathu Zowopsya, Kodi Ndani Amene Ungakhulupirire Kwenikweni?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nthaŵi Zathu Zowopsya, Kodi Ndani Amene Ungakhulupirire Kwenikweni?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chikhulupiriro Chomazimiririka
  • Kawonedwe Kabwino Koikidwa Polakwa
  • Mmodzi Amene Tingakhulupirire Kotheratu
  • Kawonedwe ka Mulungu ka Chipembedzo cha Dziko
  • Pangani Yehova Kukhala Chikhulupiriro Chanu
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kukhulupirira Ena N’kofunika Kwambiri Kuti Munthu Akhale Wosangalala
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Muzikhulupirira Abale Anu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wanu Wonse
    Nsanja ya Olonda—2003
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 4/15 tsamba 10-15

Nthaŵi Zathu Zowopsya, Kodi Ndani Amene Ungakhulupirire Kwenikweni?

“Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.”​—MASALMO 146:3.

1. Kodi nchiyani chimene chiri chizindikiro cha nthaŵi yathu, ndipo kodi ndichosowa chotani chimene icho chimasonyeza?

PAMENE tinali ana ndipo titachititsidwa mantha, tinathaŵira kwa makolo athu achisamaliro kaamba ka chitonthozo ndi chinjirizo chifukwa tinali ndi chikhulupiriro mwa iwo. Monga achikulire, nafenso timafuna awo omwe tingakhulupiriremo. Ichi chiri makamaka tero m’masiku ano pamene zinthu zambiri zochititsa mantha zikuchitika. Ikumachitira ndemanga pa nthaŵi zathu, nyuzipepala ya ku German inati: “Mosiyana ndi kale lonse, dziko liri lodzala ndi mantha.” Nthaŵi ndi nthaŵi, anthu otchuka, alembi azinkhani, ndi ena alongosola mantha awo ponena za mavuto othetsa nzeru amene tsopano akuyang’anizana ndi mtundu wa anthu.

2. Ndimotani mmene mantha ndi kusweka kwa chikhulupiriro zinanenedweratu kaamba ka mbadwo uno?

2 Ndemanga zoterozo zimawunikira chimene Yesu Kristu ananeneratu ponena za nthaŵi yathu pamene ananena kuti zidzazindikiritsidwa ndi “chisauko cha mitundu, osadziŵa njira yotulukiramo, . . . anthu akukomoka ndi mantha kaamba ka zinthu zowopsya zomwe akupenya ziri nkumadza pa dziko.” (Luka 21:25, 26) Baibulo linaneneratu kuti “m’masiku ano otsiriza zidzafika nthaŵi zovuta kuchita nazo” ndipo kuti anthu adzakhala ‘odzikonda okha, osayera mtima, akudyerekeza, osakonda abwino.’ Kalongosoledwe kameneka kamasonyeza kuti chizindikiritso chimodzi cha mbadwo wathu chikakhala kusoweka kowopsya kwa kukhulupirira.​—2 Timoteo 3:1-4, NW.

Chikhulupiriro Chomazimiririka

3. Kodi ndi umboni wotani umene ulipo wakuti kukhulupirira kuli ngozi ya mbadwo wathu?

3 M’nthaŵi zino zowopsya, ife mokulira timafuna ena amene tingakhulupirire, awo amene angakhale okhulupirika, athandizo m’nthaŵi zosowa. Koma ambiri amadzimva okhumudwitsidwa ndi awo amene anawakhulupirira. Nyuzipepala ya m’dziko lina inalengeza kuti: “Anthu Sakhulupirira Masukulu Ambiri Aunyinji.” Okhulupiridwa pang’ono ali atsogoleri a ndale ndi a bizinesi. Kusakhulupirira kwawonjezekanso m’banja, monga mmene zachitiridwa umboni ndi kukula kwa liŵiro la kulekana. M’mitundu ina, pali kulekana kumodzi pa maukwati atatu aliwonse kapena ngakhale umodzi pa maukwati aŵiri aliwonse. M’dziko limodzi, 70 peresenti ya maukwati onse atsopano amathera m’kulekana mkati mwa zaka khumi! Chotero kukhulupirira kuli ngozi yomakulakulabe. Kusakhulupirira kukutenga malo ake. Sikalinso kachilendo kanenedwe ka munthu amene ananena kuti: “Sindikhulupiriranso aliyense.”

4. Ndimotani mmene anthu achichepere ambiri akuyambukiridwira ndi mantha?

4 Pali kusakhulupirika kokulira chifukwa ino iri nthaŵi yowopsya kwambiri m’mbiri yonse ya umunthu. Zana lino lawona nkhondo zadziko ziŵiri ndi unyinji wa nkhondo zina zomwe zatenga miyoyo yoposa pa mamiliyoni zana limodzi. Tsopano, zida za nyukliya zikuwopsyeza kuwononga moyo wonse pa dziko lapansi. Ndipo ichi chimayambukira chikhulupiriro cha ngakhale achichepere. Magazini ya zamankhwala inasimba kuti: “Ana ochulukirachulukira, ngakhale achichepere kwenikweni akuchititsidwa mantha ndi chiwopsyezo cha nkhondo ya nyukliya.” Nyuzipepala ya ku Canada inanena kuti tsopano kuli “kusakhulupirira, chisoni, kuwawidwa ndi kudzimva opanda thandizo” mwa anthu achichepere ambiri. Wachichepere mmodzi ananena kuti: “Sitikudzimva ochinjirizidwa ndi anthu achikulire. Mwina tingakule kukhala mbadwo wosowa chikhulupiriko kuposa kale lonse.”

5. Ngati iwo akanalankhula, ndimotani mmene gulu lina la achichepere lopanda liwongo ndi thandizo koposa likanadzimverera?

5 Ndipo, nchiyani chimene gulu lina la achichepere lanena​—ngati iwo angalankhule​—ponena za kusadzimva kukhala ochinjirizidwa ndi achikulire? Tikutanthauza awo amene anaphedwa asanabadwe mwa kuchotsa mimba. Chiyerekezo chimodzi chimaika chiŵerengero cha kuchotsa mimba kwa dziko lonse pa chifupifupi 55 miliyoni chaka chirichonse. Iko kuli kutaya chikhulupiriro kotani nanga kulinga ku mbali yopanda liwongo ndi yopanda thandizo ya mtundu wa anthu!

6. Ndimotani mmene upandu wawonjezera ku kusakhulupirira kwa nthaŵi yathu?

6 Kusakhulupirira kwawonjezereka chifukwa cha mantha ena omakulakula m’tsiku lathu: mantha akukhala nkhole wa upandu. Ambiri tsopano amachita monga mkazi amene ananena kuti amagona ndi mfuti yaifupi kunsi kwa ntsamiro wake. Mkazi wina wa mantha ananena kuti: “Ndimatsutsana nacho. . . . Agogo anga akazi sanali kutseka zitseko zawo.” Chotero, mkonzi wa nyuzipepala mu Puerto Rico analengeza kuti: “Amene aikidwa m’ndende tiri ife,” inde, m’nyumba zathu zochinjirizidwa ndi zotsekedwa. Mantha amenewa ali oyenerera. Mu United States, mwachitsanzo, mkazi mmodzi mwa atatu mosakaikira ali wokhoza kuvutitsidwa mkati mwa moyo wake. Dokotala wotumbula anthu wamkulu kumeneko anadziŵitsa kuti “anthu a chiAmerica mamiliyoni anayi amakanthidwa ndi chiwawa chowopsya chaka chirichonse​—kupha, kugwiriridwa chigololo, kumenyedwa kwa akazi okwatiwa, kuipsidwa kwa ana, zipolowe.” Upandu woterowo uli wofala m’maiko ambiri, chikumawononga mowonjezereka chikhulupiriro chimene anthu ali nacho mwa ena.

7. Nchifukwa ninji mikhalidwe yoipa ya zamalonda imagawirirako ku kusakhulupirira?

7 Mu mitundu yosatukuka, anthu ambiri amakhala mu umphaŵi. Ochepera amakhulupirira aliyense kuwachotsa iwo mu izo. Prezidenti wa limodzi la maiko oterowo ananena kuti m’gawo limodzi, pa makanda 1,000 aliwonse obadwa, 270 amafa asanafike chaka chimodzi cha kubadwa. Kokha imodzi mwa nyumba 100 ziri ndi madzi. Boma la dziko lina linanena kuti 60 peresenti ya ana ake ali osowa, ndipo ana osiidwa mamiliyoni asanu ndi aŵiri “akukula monga osadziŵa kuŵerenga, opatulidwa ndipo osakhoza kulembedwa ntchito.” Mu United States, chiŵerengero cha achichepere opanda nyumba chikuyerekezedwa kukhala 500,000, koma ena amanena kuti chiŵerengero chenicheni chiri chokulirapo kwenikweni. Ndi kukhulupirira kotani kumene achichepere oterowo angakhale nako mwa makolo awo, m’chitaganya, m’malamulo ndi dongosolo, kapena m’malonjezo a atsogoleri?

8. (a) Ndimotani mmene kukhazikika kwa mitundu yolemera ndi chuma cha dziko lonse kukuwopsyezedwera? (b) Kodi ndi kumlingo wotani kumene akatswiri angakhulupiriridwe kuthetsa mavuto a zachuma?

8 Mavuto a za chuma amakantha ngakhale mitundu yolemera. Posachedwapa, United States inali ndi chiŵerengero chachikulu koposa cha kulephera kwa mabanki kuyambira mu Kupsyinjika Kwakukulu kwa m’ma 1930. Katswiri wa zamalonda analemba kuti: “Chotulukapo chachikulu ndicho dongosolo la banki lomwe liri lofooka kwenikweni lerolino monga mmene linaliri m’ma 1920,” lisanagweretu. Mpenyereri wina analankhula za “kuyandikira kwa mkuntho womayandikira wa chivulazo” m’dziko la zamalonda. Wina ananena kuti: “Lingaliro la kufulumira limabwera chifukwa chakuti zipsyinjo zimenezi za dongosolo la mitundu yonse siziri kuyandikira; izo zafika.” Kodi akatswiri a zamalonda angakhulupiriridwe kutsogoza mitundu kuchoka mu vuto limeneli? Mmodzi wa iwo ananena kuti zolembera zawo za kuneneratu “ziri zofooka kotero kuti palibe chikaikiro chakuti iwo akuwanditsa msokonezo.”

Kawonedwe Kabwino Koikidwa Polakwa

9. (a) Kodi nchiyani chimene chachitika ku kawonedwe kabwino komwe kanalipo posinthira pa zana lino? (b) Nchifukwa ninji Mboni za Yehova sizikanafuna kusaina cholembera cha Mitundu Yogwirizana mu 1945?

9 Zonsezi ziri zosiyana chotani nanga kuchokera ku kawonedwe kabwino komwe kanakhalapo pamene dziko linalowa m’zana la 20. Pakhala makumi a zaka za mtendere, ndipo kunamveka kuti mtendere ndi kupita patsogolo zidzafika ku mlingo wapamwamba watsopano. Koma mu 1914 Nkhondo ya Dziko I inaswa kapenyedwe koteroko. Mu 1945, itatha nkhondo ya dziko yachiŵiri yoipa kwenikweni, Tchata cha Mitundu Yogwirizana chinasainidwa. Mitundu inaika m’kulemba masomphenya awo a mtendere wa pambuyo pa nkhondo ya pa dziko, kupita patsogolo, ndi chilungamo. Ripoti laposachedwapa linanena kuti: “Cholembera chomalizira chinasainidwa ndi maiko 51, choimira dziko lirilonse, fuko ndi chipembedzo.” Komabe panali chipembedzo chimodzi chimene sichinaimiridwe, ndiponso sichinafune kutero, Mboni za Yehova. Iwo anadziŵa kuti malonjezo oterowo a mtendere, kupita patsogolo, ndi chilungamo sadzazindikiridwa ndi mtundu uliwonse wa dziko iri kapena mwa mayanjano aliwonse ndi iwo, monga ngati Mitundu Yogwirizana.

10. Kodi nchiyani chimene chiri chenicheni lerolino choyerekezedwa ku loto la Mitundu Yogwirizana kubwerera mu 1945?

10 Ripoti limodzimodzilo linanena kuti: ‘Zaka makumi anayi pambuyo pake chinawoneka choyenera kuzipenda zenizeni motsutsana ndi zoganiziridwa. Umboni unali wochititsa chisoni. Dziko la chisungiko chochepera, ndi chiwawa chomakulakulabe, ndizo zenizeni. Anthu a m’dziko opanda chakudya, madzi, pogona, chisamaliro cha umoyo, ndi maphunziro ziri kumakulakulabe. Ichi sichinalimo mu loto la 1945.’ Linawonjezera kuti: ‘Zaka makumi anayi pambuyo pa kugwirizana pamodzi kwa mitundu kutsimikizira kuti anthu onse angakhale aufulu ku mantha ndi kusowa, dziko lenileni la m’ma 1980 lakhala limodzi la umphaŵi wokantha wa chifupifupi kota imodzi ya mtundu waumunthu. Imfa zochititsidwa ndi njala zimapanga avereji ya 50,000 pa tsiku.’ Komabe, mitundu ikuwononga oposa madola mamiliyoni zana limodzi ora lirilonse pa nkhondo!

11. Kodi malonjezo kaamba ka dziko labwinopo ali okhulupirika chotani?

11 M’chiyang’aniro cha cholembedwachi cha kupereŵera pambuyo pa kukhala nawo mwaŵi wa zaka mazana, kodi tingakhulupirire malonjezo a anthu kuthetsa mavuto amenewa? Malonjezo oterowo angakhale okhulupirika mofanana ndi mawu a kaputeni wa sitima yaikulu ya m’madzi yemwe anati: “Sinditha kuganiza khalidwe lirilonse lomwe lingachititse sitima yamakono [yaikulu] kumira. . . . Kamangidwe kamakono ka masitima kapita patsogolo.” Chiwalo chimodzi cha m’sitima yake chinanena kwa mmodzi wa okweramo kuti: “Mulungu mwiniyo sangakhoze kumiza sitimayi.” Komabe, sitima imeneyo, Titanic, inamira mu 1912 limodzi ndi kutaika kwa miyoyo 1,500. Kachiŵirinso, Mu 1931 Bungwe la Maphunziro a M’dziko mu United States linanena kuti kupyolera mwa maphunziro “upandu udzachotsedwapo chisanafike chaka cha 1950.” Mu 1936 mtola nkhani wa chiBritish analemba kuti “chakudya, zovala ndi pogona zidzagulidwa pa ndalama zochepera monga mphepo” pofika 1960. Kodi simumavomereza kuti zenizeni za lerolino zimawonetsa malonjezo amenewo kukhala monga njerengo?

Mmodzi Amene Tingakhulupirire Kotheratu

12. Ndi mwandani mmene tingakhulupirire kotheratu, ndipo ndi chitsogozo chotani chimene iye watipatsa?

12 Chotero, tikufunitsitsa magwero omwe tingakhulupirire kuti tipyole nthaŵi zino zowopsya. Magwero amenewo sangakhale munthu. Mtundu wa anthu wadzibweretsera iwo wokha mavuto akulu kotero kuti suuli wokhoza kudzitulutsamo. Magwero omwe angakhulupiridwe kotheratu ali Mlengi wa anthu, Yehova Mulungu. Iye amadziŵa nchifukwa ninji dziko liri mu mkhalidwe wake umene lirimo, kumene likupita, ndi chimene iye adzachita ponena za icho. Iye wavumbulutsanso chidziŵitso chake chimenechi m’bukhu limene iye anatipatsa ife kaamba ka chitsogozo chathu, Baibulo. Za icho, 2 Timoteo 3:16, 17, amanena kuti: “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo; kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iriyonse yabwino.”

13. Kodi nchiyani chimene Mboni za Yehova zimayamikira ponena za Baibulo?

13 Dziŵani ndemanga zogogomezera zimenezo. Mawu ouziridwa a Mulungu amakhazikitsa zinthu mowongoka. Amatidziŵitsa zimene ziri zabwino. Amatipangitsa ife kukhala okonzekera kotheratu. Amatikonzekeretsa ife kotheratu kuchita chimene chiri chabwino. Zowona, anthu ambiri samalandira Baibulo kaamba ka chomwe ilo liri​—Mawu a Mulungu. Koma Mboni za Yehova zimatero. (1 Atesalonika 2:13) Timayamikira kuti Mlengi wa chilengedwe chochititsa mantha chimenechi cha mabiliyoni a milalang’amba ndi matriliyoni a nyenyezi mowona ali nako kukhoza kwa kuyambitsa bukhu. Iye alinso ndi kuthekera kwa kuwona kuti kulongosoka kwake kwasungiliridwa kaamba ka phindu la ofunafuna chowonadi.​—1 Petro 1:25.

14. Ndimotani mmene Baibulo limagwirizanirana ndi zenizeni za lerolino?

14 Mu nthaŵi zathu zowopsya, kodi Mawu a Mulungu amanenanji pa nkhaniyi ya kukhulupirira? Ndemanga zake zimagwirizana kotheratu ndi mikhalidwe yeniyeni yomwe iripo. Yeremiya 10:23 molongosoka amanena kuti: “Ndimadziŵa, O Yehova, kuti njira ya munthu siri mwa iyemwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Ndipo Masalmo 146:3, molondola anafulumiza kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.”

15. Kodi ndi uphungu wotani umene Baibulo limatipatsa ife ponena za kukhulupirira?

15 Mawu a Mulungu amatichirikiza ife kusakhulupirira ngakhale mwa ife eni chifukwa chakuti anthu ali opanda ungwiro. (Aroma 5:12) Yeremiya 17:9 yadziwitsa kuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa.” Kaamba ka chifukwa ichi Miyambo 28:26 imalengeza kuti: “Wokhulupirira mtima wake wake ali wopusa. Koma woyenda mwanzeru adzapulumuka.” Ndi kuti kumene tingapeze nzeru imeneyi imene ingapereke chipulumutso? Miyambo 9:10 ikuyankha kuti: “Chiyambi cha nzeru ndicho kuwopa Yehova, kudziŵa woyerayo ndiko luntha.” Inde, kokha nzeru ya Mlengi ingatitsogoze ife kupyola m’nthaŵi izi zowopsya. Chotero, Miyambo 3:5, 6 imachenjeza kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako. Umlemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako.”

Kawonedwe ka Mulungu ka Chipembedzo cha Dziko

16. Ndi chiyerekezo cholakwika chotani chimene zipembedzo zadziko iri zimapanga, monga mmene anachitira Afarisi a m’nthaŵi ya Yesu?

16 Nzeru imeneyi yochokera kwa Mulungu idzatitheketsa ife kupewa msampha wopatsa imfa umene zipembedzo za m’dziko iri zagweramo. Izo zimaganiza kuti ziri zolungama chifukwa chakuti ziri za chipembedzo. Mkhalidwe wawo uli wofanana kwambiri ndi uja wolongosoledwa pa Luka 18:9, NW: “Iye [Yesu] analankhula fanizo iri kwa enanso anakhulupirira mwa iwo okha kuti anali olungama.” Mfarisi anayamikira Mulungu kuti iye sanali wochimwa, koma wosonkhetsa msonkho anapitiriza kupempha kuti: “Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwa.” Yesu ananena kuti: “Ndikuwuzani, munthuyu [wochimwa] anapita kunyumba kwake ali wovomerezeka wolungama kuposa munthu uja [Mfarisi]; pakuti aliyense wakudzikuza yekha adzachepetsedwa, koma wodzichepetsa yekha adzakwezedwa.”​—Luka 18:10-14, NW.

17. Ndimotani mmene Mulungu amawonera zoyesayesa zachipembedzo za awo onga Afarisi?

17 Mfarisi sanadzichepetse iyemwini pamaso pa Mulungu. M’malomwake, iye anadzimva kuti mwa miyezo yake anali wolungama. Koma mmenemo simunali mmene Mulungu anachiwonera icho. (Mateyu 23:25-28) Anali wochimwa wodzichepetsa yemwe anawunikira chimene Mawu a Mulungu amanena pa Yesaya 66:2: “Ndidzayang’anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi Mawu anga.” Atsogoleri achipembedzo a Chiyuda sananthunthumire pa Mawu a Mulungu. Iwo ananyalanyalaza iwo. Iwo anachita zomwe anafuna ndipo kenaka kuganiza kuti Mulungu adzawavomereza iwo. Komabe, Yesu ananena kwa iwo kuti: “Siyense wakunena kwa ine, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa mu ufumu wakumwamba; koma wakuchita chifuniro cha Atate wanga wakumwamba. Ambiri adzati kwa ine tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri?’ Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo: sindinakudziŵani inu nthaŵi zonse; chokani kwa ine, inu akuchita kusayeruzika.”​—Mateyu 7:21-23.

18. Kodi ndimotani mmene Mulungu adzaŵeruzira zipembedzo zomwe zimadzinenera kutumikira iye koma zomwe sizigwirizana ndi malamulo ake?

18 Atsogoleri achipembedzo amenewo m’zana loyamba sanakhulupirire mwa Mulungu. M’malomwake, anaika chikhulupiriro chawo m’miyambo yomwe inaswa malamulo a Mulungu. (Mateyu 15:3, 9) Chotero Yesu anawauza: “Nyumba yanu yasiidwa kwa inu ya bwinja.” (Mateyu 23:38) Monga umboni wakuti Mulungu mowona anachisiya chipembedzo chawo cha Chiyuda, m’chaka cha 70 cha Nyengo yathu Yachisawawa iwo, likulu la mtundu wawo, Yerusalemu ndi kachisi wawo anasakazidwa ndi magulu ankhondo Achiroma. Sichiri chosiyana lerolino. Zipembedzo zadziko lino zakhazikitsa miyezo yawo ya kulambira yomwe simagwirizana ndi miyezo ya Mulungu. Chotero iwo akuchita osati chifuniro chake koma chifuniro chawo. Chotero, m’maso mwa Mulungu, iwo amalingaliridwa antchito osayeruzika. (Tito 1:16) Monga umboni wakuti Mulungu wasiya zipembedzo zimenezi, iwo posachedwapa adzasakazidwa ndi amitundu, monga mmene Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwera ndi magulu ankhondo Achiroma m’zana loyamba.​—Onani Chivumbulutso, mitu 17, 18.

19. Kodi ndi mafunso otani amene angafunsidwe ponena za chipembedzo?

19 Kodi kusanthula kwa zipembedzo zadziko kumeneku kuli koipa monkitsa? Ndimotani mmene tingatsimikizire kuti ziŵeruzo za Mulungu posachedwapa zidzabweretsedwa kwa iwo? Nchiyani chimene chipembedzo chiyenera kuchita kuti chikumane ndi chivomerezo cha Mulungu? Kodi pali zitsanzo za m’mbiri zomwe zimasonyeza kuti Yehova amachinjiriza awo amene mowonadi amatembenukira kwa iye ndi kugonjera ku malamulo ake? Nkhani yotsatira idzachitira ndemanga pa mafunso amenewa.

Mafunso a Kubwereramo

◻ Kodi nchiyani chimene chathandizira ku kusakhulupirira kwa m’nthaŵi yathu?

◻ Nchifukwa ninji kawonedwe kabwino ka dziko iri kanasokeretsedwa?

◻ Ndani amene tingakhulupirire kotheratu, ndipo kodi ndi chitsogozo chotani chimene iye watipatsa?

◻ Nchifukwa ninji sitiyenera kukhulupirira mwa ife eni kapena anthu ena?

◻ Ndimotani mmene Mulungu amawonera zipembedzo zadziko iri?

[Zithunzi patsamba 13]

Mfarisi anaganiza kuti anali wolungama, koma munthu wochimwa modzichepetsa anapempha kaamba ka chifundo cha Mulungu

[Chithunzi patsamba 15]

Mulungu amatsutsa zipembedzo zimene sizikuchita chifuniro chake monga mmene iye anatsutsira Chiyuda m’zana loyamba pamene magulu ankhondo a Aroma anawononga Yerusalemu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena