Odyerera a ‘Umphaŵi ndi Umbuli’?
“MBONI ZA YEHOVA . . . zimatengera mwaŵi wa umphaŵi, kunyalanyazidwa, ndi umbuli wa mbali yabwino ya anthu athu,” anatsimikizira tero mlembi wa ku Mexico Jorge García, “ndi cholinga chakuti mopita patsogolo alamulire chikumbumtima chawo.”—Excelsior ya March 9, 1983.
Milandu yofananayo molimbana ndi Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri imamvedwa mu Latin America. ‘Palibe ndi mmodzi yense wodziŵika koposa amene amakhala mmodzi wa Mboni za Yehova,’ amatero akatswiri ena, a ndale zadziko, ndi atsogoleri a chipembedzo. ‘Mboni za Yehova zimapeza atsatiri awo kuchokera kwa osauka, anthu a umbuli.’ Chiri chowona kuti zambiri za Mboni za Yehova ziri za chuma chochepera, koma kodi chimenecho chimatanthauza kuti Mboni za Yehova ‘zikutengera mwaŵi wa umphaŵi, kunyalanyazidwa, ndi umbuli?’ Kodi chenicheni chakuti anthu ambiri odzichepetsa ndi osauka amavomereza ku ziphunzitso zawo chimatanthauza kuti ziphunzitso zoterozo ziri zolakwa?
Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tilingalire m’mbuyomu ku zana loyamba la Nyengo yathu ya Chisawawa. Ndi mtundu wotani wa anthu umene unakokeredwa ku Chikristu kubwerera nthaŵi imeneyo?
Chikristu—Chifukwa Chimene Chinali Chosangalatsa kwa Odzichepetsa
Osuliza amakono a Mboni za Yehova akungofuula chabe mawu a otsutsa Chikristu a m’zana loyamba. Lingalirani, mwachitsanzo, anzeru a Chigriki omwe anakhala mu mzinda wakale wa Korinto. Monga mmene mtumwi Paulo achiikira icho, “Agriki [an[atsata nzeru.” (1 Akorinto 1:22) Iwo anafuna, ndithudi, osati nzeru ya Baibulo, koma mikangano yovuta kumvetsetsa ya nthanthi. Ndipo pamene mtumwi Paulo “sanadza ndi kuposa kwa mawu kapena kwa nzeru” koma m’malomwake anapereka uthenga wopepuka wa “Kristu, ndiye wopachikidwa,” Chikristu chinasekedwa ndi ambiri monga “chopusa.”—1 Akorinto 1:23; 2:1, 2.
Chotero, kodi Paulo ‘anali kutenga mwaŵi wa umbuli,’ m’kudandaulira kwa ofatsa ndi odzichepetsa limodzi ndi nzika zina za Korinto? Kutalitali. Paulo analongosola kwa Akristu kumeneko: “Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi . . . koma Mulungu anasankhula zoposa zadziko lapansi, kuti akachititse manyazi anzeru . . . kuti thupi lirilonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.”—1 Akorinto 1:26-29.
Kuyambira pachiyambi penipeni, Chikristu chinakhala chipembedzo chomwe poyambirira chinakoka odzichepetsa, anthu ofatsa. Atumwi 12 a Yesu—maziko a tchalitchi chake—sanali otengedwa pakati pa alembi ndi Afarisi ophunzira. (Aefeso 2:20) M’malomwake, iwo anachokera ku magulu ogwira ntchito, anayi akumakhala asodzi a nsomba mwa ntchito. (Mateyu 4:18-22; 10:2, 3) Iwo anali amuna omwe anawonedwa ndi atsogoleri a chipembedzo monga “osaphunzira ndi opulukira,” kutanthauza kuti maphunziro awo anali oyambirira ndipo osati kuchokera m’sukulu za maphunziro apamwamba. (Machitidwe 4:13) Alembi ndi Afarisi “ophunzira” ananyoza Mesiya woyembekezedwa kwa nthaŵi yaitali, mwa kumaseka ziphunzitso zake ndi atsatiri ake. Iwo anatenga kawonedwe kakuti ‘palibe wina aliyense wotchuka amene anatsatira Yesu.’
Kumbukirani chimene chinachitika pa chochitika chimodzi pamene iwo anatumiza nduna “kukagwira” Yesu. Ndunazo zinabwera zopanda kanthu. Nchifukwa ninji? Chikutero cholembedwa cha Baibulo: “[Ndunazo] zinayankha: ‘Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.’” Inde, iwo anazizwitsidwa pa ziphunzitso za Kristu! Komabe, ndimotani mmene atsogoleri a chipembedzo ophunzitsidwa anavomerezera? “Pamenepo Afarisi anayankha iwo: ‘Kodi mwasokeretsedwa inunso? Kodi wina wa akulu anakhulupirira iye, kapena wa Afarisi?’” (Yohane 7:32, 44-48) Kunyada chotero kunawaletsa iwo kulandira Yesu. Zowona, Baibulo limanena kuti “ambiri a mwa akulu anakhulupirira iye, koma chifukwa cha Afarisi sanavomereza, kuti angaletsedwe m’sunagoge, pakuti anakonda ulemerero wa anthu koposa ulemerero wa Mulungu.”—Yohane 12:42, 43.
Tangolingalirani chimenecho! Amuna amenewa m’chenicheni anakhutiritsidwa kuti Yesu anali ndi chowonadi, koma anakana kukhala ophunzira ake chifukwa chowopa anthu. Icho sichinali kokha chotheka kwa atsogoleri amenewo kupereka kaimidwe kawo m’mayanjano, ndale zadziko, ndi mabwalo a chipembedzo kukhala atsatiri a Yesu. Nchosadabwitsa kuti Yesu ananena kuti: “Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini chuma adzalowa movutika mu ufumu wa kumwamba”! (Mateyu 19:23) Chotero, mwachisawawa, oterowo anali onyada kwambiri kuti atsatire chipembedzo chomwe chinawafuna iwo modzichepetsa ‘kunyamula mtengo wawo wozunzirapo ndi kutsatira Yesu.’ (Mateyu 16:24, NW) Kristu motero kamodzi m’pemphero ananena kuti: “Ndikuvomerezani inu, Atate, Ambuye wa kumwamba ndi wa dziko, kuti izi munazibisira anzeru ndi ozindikira, ndipo munaziululira ana amakanda.” (Luka 10:21) Mosiyana ndi anzeru a kudziko, oterowo anali ovomereza ku chowonadi.—Yerekezani ndi Mateyu 18:3.
Mulungu Alibe Tsankhu
Analemba wophunzira Yakobo: “Kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda iye?” (Yakobo 2:5) Kodi ichi chinatanthauza, chotero, kuti awo a chuma ndi maphunziro a kudziko anali oletsedwa kuchokera ku kutumikira Mulungu? Kutalitali! Pambuyo pa kulandira mzimu woyera, kwa mtembenuzi wa Kunja woyamba, Korneliyo, Petro anawona: “Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Mwinamwake Petro anakumbukira mawu a Yehova kwa Samueli, olankhulidwa zaka mazana apitawo: “Pakuti Yehova sawona monga awona anthu; pakuti munthu ayang’ana chowoneka ndi maso koma Yehova ayang’ana mu mtima.”—1 Samueli 16:7.
Mosangalatsa, chotero, Baibulo limanena kuti “khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho.” (Machitidwe 6:7) Akristu anapezekanso “m’nyumba zapamwamba za Kaisara.” (Afilipi 4:22) Ndipo ngakhale unyinji wa Akristu anali a chuma chochepera, panali ena mu mpingo omwe anali olemera.—1 Timoteo 6:17.
Nthaŵi Zamakono
Sichiyenera kukhala chozizwitsa kwa ife, chotero, kuti chowonadi lerolino chapeza chipatso choyambirira pakati pa anthu wamba. Yehova adakali kuyang’ana, osati pa akaunti ya ku banki ya munthu kapena maphunziro a kudziko, koma pa mtima. (Miyambo 21:2) Kumbukirani, kachiŵirinso, kuti Yesu ananena kuti: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye.” (Yohane 6:44) Ndithudi, Atate akakoka kwa iyemwini kokha awo amene ali odzichepetsa ndipo ophunzitsika, kodi iye sakatero?
Ngakhale kuli tero, uku sindiko kunena kuti ophunzira ndi anthu otchedwa akatswiri sakukhala Mboni za Yehova. Pamene Paulo anapereka chiwonetsero cha chowonadi chopepuka, komabe champhamvu, pamaso pa Mfumu Agripa, mfumuyo inavomereza kuti: “Ndi kundikopa pang’ono ufuna kundiyesera Mkristu.” (Machitidwe 26:27, 28) Mofananamo, ophunzira ambiri akhala okokedwera ku chowonadi ndi kalongosoledwe komvekera bwino ndi kanzeru ka chowonadi cha Baibulo kamene Mboni za Yehova zimapereka. Kumbukirani, munthu wodzichepetsa sali kwenikweni wosaphunzira. Mose anatchedwa, “wofatsa woposa anthu onse a pa dziko lapansi.” (Numeri 12:3) Komabe, iye anali “anaphunzira m’nzeru zonse za Aigupto.”—Machitidwe 7:22.
Chiri choyenera kudziŵa, ngakhale kuli tero, pamene anthu a maphunziro ochepa a kudziko ayamba kuyanjana ndi Mboni za Yehova, iwo kaŵirikaŵiri amatenga masitepi a kuwongolera maluso awo a maphunziro. Iwo amayesera kuwongolera zizolowezi zawo za kuŵerenga ndi kuphunzira kotero kuti aphunzire ziphunzitso zoyambirira za Baibulo ndi kuyendera limodzi ndi kusefukira kokhazikika kwa mabukhu a Baibulo ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Ngati munthu wowona mtima afuna kuphunzira Baibulo koma ali wotsekerezedwa ndi kusadziŵa kuŵerenga ndi kulemba, malangizo aulere kaŵirikaŵiri angakonzedwe kupyolera mu mpingo wa kumaloko.
Watchtower Sosaite imafalitsanso kabukhu kokhala ndi mutu wakuti Chithandizo cha Kuŵerenga cha Teokratiki kwa Mboni za Yehova. Kabukhu kameneka kathandiza zikwi zambiri za anthu kuphunzira kuŵerenga mu Asia, Africa, ndi Central ndi South America. M’dziko limodzi la Latin America, 51,249 aphunzira kuŵerenga ndi kulemba m’zaka 26 zapitazo ndi thandizo la kabukhu kameneka! M’mudzi umodzi wa mu Latin America, woyang’anira wa Dipartimenti ya Maphunziro anakumana pamodzi ndi oimira a magulu ambiri osiyanasiyana—kuphatikizapo Mboni za Yehova. Mboniyo kumeneko inawauza iwo ponena za kabukhu ka Chithandizo cha Kuŵerenga cha Teokratiki kwa Mboni za Yehova ndipo inaitana gululo ku umodzi wa misonkhano ya Mboni.
Gululo linapezekapo pa Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki—msonkhano wokonzekeretsedwa kuthandiza amuna ndi akazi kukhala aphunzitsi okhutiritsa. Ku kudabwitsidwa kwawo, iwo anawona mwamuna yemwe anamdziŵa kukhala wosadziŵa kulemba ndi kuŵerenga—ali pa pulatiformu ndi kumapereka nkhani ya Baibulo! Ananena mmodzi wa alendowo, prinsipulo wa pa sukulu: “Sichiri chotheka kuti munthuyu amene tinamdziŵa nthaŵi zonse kukhala wosadziŵa kulemba ndi kuŵerenga ali wokhoza kulankhula mu chiSpanish [m’malo mwa katchulidwe ka mawu ka chibadwa chake], mocheperako kulankhula ku khamu, koma iye akutero.”
Chotero m’malo mwa kudyerera anthu odzichepetsa, Akristu owona lerolino akuwathandiza iwo kudziwongolera iwo eni mwa kuwathandiza iwo kufikira chidziŵitso cha chowonadi. Akristu oterowo akuchita ntchito yophunzitsa imene Yesu anawalamulira iwo pamene ananena kuti: “Mukani phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . ndi kuwaphunzitsa zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Ndipo monga chotulukapo chake, chaka chirichonse makumi a zikwi kuchokera ku mlingo uliwonse wa chitaganya akugwirizana ndi mathayo a Mboni za Yehova.