“Kristu, Mwana wa Mulungu Wamoyo”
PAMBUYO pa kusimba kwa ophunzira ake amene anthu anali kunena kuti iye anali, Yesu anafunsa: “‘Koma, inu mutani, kuti Ine ndine yani?’ M’kuyankha Simoni Petro anati: ‘Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.’”—Mateyu 16:15, 16.
Kodi Petro anali yekha m’kufikira mapeto amenewa? Kutalitali! Dziŵani enanso amene anatero, ndipo dziŵani maziko awo kaamba ka chizindikiritso chimenechi.
ACHIRIKIZI OYAMBIRIRA: Yohane Mbatizi, ophunzira Natanieli ndi Malita, ndi Saulo wa ku Tariso, pakati pa ena, onse anatcha Yesu Mwana wa Mulungu. (Mateyu 14:33; Yohane 1:33, 34, 49; 11:27; Machitidwe 9:20) Chitsimikiziro chawo chinalimbikitsidwa pamene anawona mmene maulosi okonzekeretsedwa kuzindikiritsa Mesiya wolonjezedwayo anakwaniritsidwira mwa Yesu.
ATSUTSI OYAMBIRIRA: Ayuda omwe anafuna kupha Yesu analozera kwa iye monga Mwana wa Mulungu, monga mmene anachitira asilikari omwe analipo pa kupachikidwa kwake. (Mateyu 27:54; Yohane 19:7) Ngakhale kuti ichi m’chenicheni sichisonyeza chikhulupiriro ku mbali ya otsutsa oterowo, mwapang’ono icho chikusonyeza kuti iwo anali ozoloŵerana ndi zimene ena anali kunena ponena za Yesu; ndipo zochitika zoposa zachilengedwe zozungulira kupachikidwa kwake mwachidziŵikire zinapangitsa ena a iwo kulingaliranso funso la chizindikiritso chake.
ANGELO: Pamene anali kulengeza kubadwa kwa Yesu, mngelo Gabrieli anamutcha iye Mwana wa Mulungu. (Luka 1:32, 35) Ngakhale anthu ogwidwa ndi ziwanda pansi pa chisonkhezero cha angelo oipa anafuula: “Tiri nanu chiyani inu, Mwana wa Mulungu?” (Mateyu 8:28-32) Chifukwa cha kukhalapo kwa Yesu asanakhale munthu kumwamba, chiri chachidziŵikire kuti ponse paŵiri angelo abwino ndi oipa akadziŵa amene iye anali.
YESU IYEMWINI: Yesu sanadzikweze ponena za kukhala Mwana wa Mulungu m’kuyesera kupeza chiyanjo ndi ena kapena kudziwonetsera m’malo apamwamba amene unansi wake unapereka. Mosiyanako, m’nkhani zambiri iye modzichepetsa analozera kwa iyemwini monga “Mwana wa munthu.” (Mateyu 12:40; Luka 9:58) Koma pa zochitika zingapo iye anavomereza ku kukhala Mwana wa Mulungu.—Yohane 5:24, 25; 10:36; 11:4.
YEHOVA MULUNGU: Ndani yemwe akazindikiritsa Yesu Kristu ndi ulamuliro wokulirapo kuposa Yehova Mulungu iyemwini? Kaŵiri Yehova anachitira umboni kuchokera kumwamba kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga, wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.”—Mateyu 3:17; 17:5.
Mulungu Anavomereza Yesu—Kodi Mumatero?
M’zana loyamba, zikwi za anthu zinalandira Yesu kaamba ka chimene iye anali: Mesiya wolonjezedwa, kapena Kristu, wotumizidwa pa dziko lapansi kudzalemekeza ufumu wa Yehova ndi kupereka moyo wake monga dipo kaamba ka mtundu wa anthu. (Mateyu 20:28; Luka 2:25-32; Yohane 17:25, 26; 18:37) M’chiyang’aniro cha chitsutso chowopsya, anthu sakanasonkhezeredwa nkomwe kukhala otsatira a Yesu ngati iwo sanali otsimikizira za chizindikiritso chake. Mwachangu ndi molimba mtima, iwo anakupatira ntchito imene iye anawapatsa iwo, “kupanga ophunzira a mitundu yonse.”—Mateyu 28:19.
Lerolino, mamiliyoni a ophunzira Achikristu amadziŵa kuti Yesu sali nthano. Iwo amamlandira iye monga Mfumu yoikidwa ya kumwamba ya Ufumu wokhazikitsidwa wa Mulungu, amene tsopano mopita patsogolo akutenga ulamuliro wa dziko lapansi ndi zochita zake. Boma la umulungu likudzali liri mbiri yolandiridwa chifukwa limalonjeza mpumulo kuchokera ku mavuto a dziko. Akristu owona amenewa amachitira chitsanzo kuchirikiza kwawo kowona mtima kwa Wolamulira wosankhidwa wa Mulungu mwa kulengeza “mbiri imeneyi ya ufumu” kwa ena.—Mateyu 24:14.
Awo amene amachirikiza makonzedwe a Ufumu kupyolera mwa “Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo,” adzakhala ndi moyo kudzasangalala ndi madalitso osatha. Madalitso amenewa angakhalenso anu!
[Mawu Otsindika patsamba 8]
Mamiliyoni amene poyamba anali osatsimikizira ponena za chizindikiritso cha Yesu tsopano ali ogwirizana m’kuchirikiza iye monga Wolamulira wa Ufumu wa Mulungu
[Chithunzi patsamba 7]
Petro anazindikiritsa Yesu monga “Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” Chotero zimateronso mboni za Yehova zoposa 3,000,000 lerolino