Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 8/15 tsamba 4-7
  • Chipambano—Pa Mtengo Wonse?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chipambano—Pa Mtengo Wonse?
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kusokeretsedwa​—Motani?
  • Zowawa za “Chipambano”
  • Mtundu Wabwinoko wa Chipambano
  • Pitirizani Kufunafuna Chipambano Chauzimu
  • Mukhoza Kukhala ndi Moyo Wabwino Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Mungatani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino?
    Galamukani!—2014
  • Kodi AKristu Amafunika Kuti Azikhala Osauka?
    Galamukani!—2003
  • Mfundo 6 Zokuthandizani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1988
w88 8/15 tsamba 4-7

Chipambano​—Pa Mtengo Wonse?

CHIKHUMBO cha kupambana chimasonyeza kuti munthu ayenera kukhala ndi chonulirapo chotsimikizirika. Nchiyani chomwe chiri chonulirapo chanu m’moyo? Nchiyani chomwe mwakonzekera kuchita ndi cholinga chofuna kuchifikira icho? Ndithudi, nchiyani chomwe chiyenera kukhala cholondola chanu choyambirira ndi cholinga chofuna kukhala wokhutiritsidwa mowanadi ndi wachimwemwe?

M’maiko ambiri a Maiko Otukuka Kumene, muyezo wa chisawawa wa kakhalidwe umasiya zokulira kuti ukhumbiridwe. M’chiyang’aniro cha mavuto oyang’anizidwa kumeneko, kulingalira uphungu woyenerera kuchokera m’Mawu a Mulungu kudzatithandiza ife kusanthula bwino lomwe zonulirapo zathu zenizeni ndi chipambano, mosasamala kanthu za kumene timakhala.

Ndi kufalikira kwa umphawi, anthu ambiri alondola chipambano cha chuma kupatulapo china chirichonse. Ena amakhoterera ku kusawona mtima kotero kuti afikire chimenechi. Pa kukhala Akristu owona, ngakhale ndi tero, iwo ayenera kukhala anasiya kotheratu mkhalidwe umenewo kumbuyo ndi cholinga chofuna kugwirizana ndi miyezo yolungama ya Baibulo.

Ngakhale kuli tero, ngakhale Akristu ena amagwidwa kachiŵirinso m’kulunjikitsa chidwi pa zonulirapo zakudziko. Iwo angagwere mu mkhalidwe wosakhala Wachikristu ndi cholinga chofuna kupeza chipambano. Makolo amanyalanyaza mabanja awo. Aliyense payekha amanyalanyaza utumiki wawo kwa Mulungu. Nchiyani chomwe mukulingalira kuti chidzakhala chotulukapo ponena za chokwaniritsa m’moyo ndi chimwemwe?

Likumatigalamutsa ife ku chotulukapocho, Baibulo likuchenjeza kuti: “Koma iwo akufuna kukhala ahuma amagwa m’chiyesero ndi mumsampha ndi m’zilakolako zambiri zoposa ndi zopweteka . . . Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama, chimene ena pochikhumba anasokera nataya chikhulupiriro nadzipyoza ndi zowawa zambiri.”​—1 Timoteo 6:9, 10.

“Zilakolako zambiri zoposa ndi zopweteka.” ‘Nadzipyoza ndi zowawa zambiri.’ Chimenecho ndithudi sichikumvekera monga kalongosoledwe ka chikhutiritso ndi chimwemwe, kodi chikutero? Komabe, chokumana nacho cha mamiliyoni a anthu mkati mwa zaka mazana, ngakhale kufikira tsopano lino, chikutsimikizira mmene irili yowona ndemanga ya Baibulo imeneyo. Chotero, nchiyani, chimene ichi chikuyamikira ponena za zonulirapo ndi njira ya moyo ya Mkristu?

Kusokeretsedwa​—Motani?

Ndi mwanjira zotani mmene Akristu angasokeretsedwere kuchoka ku chikhulupiriro? Ena afikira ku utali wa kukana kotheratu makhalidwe ndi zikhulupiriro zaumulungu. Mu nkhani zina anthu akokedwa kucoka pa njira ya kudzipereka kwa umulungu, kufikira pa kugwiritsira ntchito molakwa kudzipereka koteroko monga njira ya kupezera chisonkhezero pa ena. Chotero Baibulo limalankhula za “anthu oipsyika nzeru ndi ochotseka chowonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa.” (1 Timoteo 6:5) Pamene kuli kwakuti iwo sakusiya kotheratu Chikristu, iwo angadzipeze iwo eni akulakwira maprinsipulo a Baibulo omwe ali zinthu zofunika kwambiri za chikhulupiriro cha Mkristu.

Yesu anauza atsatiri ake kusakhala monga anthu a kudziko omwe amapondereza ena. Iye anenena kuti: “Sikudzakhala chomwecho kwa inu ayi; koma amene aliyense akafuna kukhala wamkulu kwa inu adzakhala mtumiki wanu.” M’kutsutsa atsogoleri achimpembedzo Achiyuda, Yesu anapita patsogolobe. Iye anasonyeza kuti chikondi chachikulu cha kutchuka kwa kudziko chimapeza kupanda chivomerezo kwa Mulungu. (Mateyu 20:26; 23:6-9, 33) Chotero, Akristu ayenera kufuna kutumikirana wina ndi mnzake m’malo mwa kuwala kapena kulamulira ena. Wokonda ndalama yemwe amafunafuna chipambano pa mtengo uliwonse angasokeretsedwe mopepuka kuchoka ku njira imeneyi.

Ndimotani mmene mumadziyerekezera m’chigwirizano ndi ichi? Kodi mumadzipeza inu eni mukulinga chipambano chanu ndi ukulu ku umene mumaika ulamuliro pa ena? Kodi mumawongolera kapena kupotoza maprinsipulo Achikrust ndi ziphunzitso ndi cholinga chofuna kusonyeza ulamuliro kapena kupeza iwo? Kodi mumadzimva kuti muyenera kufikira zapamwambapo kuposa anzanu a m’zaka zofanana mosasamala kanthu za mtengo wake? Kodi mumatenga chikondwerero chokulira m’kulankhula ponena za kupeza kwanu chuma kapena ntchito? Ngati ndi tero, chotero mufunikira kusanthulanso kaya ngati mukusokeretsedwa kuchoka ku chikhulupiriro.

Zowawa za “Chipambano”

Yesu ananenanso kuti: “Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi . . . Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko udzakhala mtima wanunso . . . Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.” (Mateyu 6:19-24) Kodi makolo amene akutsogoza ana awo choyambirira kulinga ku zonulirapo za zinthu zakuthupi ndi ntchito za kudziko akutsatira uphungu umenewu? Kodi chigogomezero pa chipambano cha kudziko chiri choyenerera pa mtengowo ngati ana asiya chowonadi ndi kusinthira ku njira za moyo zosakhala zachikristu? Kodi chiri choyenerera kupereka nsembe kapena, chifupifupi, kuika mu ngozi miyoyo yawo yauzimu kaamba ka cholinga cha “Kudzikundikira chuma pa dziko lapansi”? Makolo amene amachita ichi kaŵirikaŵiri amapeza kuti ‘adzipyoza ndi zowawa zambiri’ chifukwa chodera nkhaŵa za ana awo ndi kudandaula kaamba ka kutaika kwawo​—kwauzimu​—ndipo nthaŵi zina kwa kuthupi.

Chikondi cha chuma chiri mbuye wolamulira. Icho chimatha nthaŵi ya anthu, mphamvu, ndi kuthekera; ndipo chimatsamwitsa kudzipereka kwaumulungu. Icho kaŵirikaŵiri chimawanyenga anthu kufunafuna ngakhale chuma chokulira ndi kunyada kwa kudziko, motero kuwakokera iwo kutali ndi chikhulupiriro. Baibulo molondola limanena kuti: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva, ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu.”​—Mlaliki 5:10.

Ngakhale pambuyo pa kukhala Mkristu, chikondi kaamba ka chipambano cha zachuma cha mwamuna wina wa bizinesi wa ku Africa chinapitiriza kutenga malo oyamba m’moyo wake. Iye ananyalanyalaza machitachita Achikristu m’kuyanja maulendo a mayanjano ndi mabwenzi a malonda a kudziko. Iye sanapange kupita patsogolo kwauzimu, mosasamala kanthu za zoyesayesa zopangidwa ndi akulu a mu mpingo wake kumthandiza iye. Iye chotero anadzipeza iyemwini m’kuzizwitsidwa mwauzimu​—m’dziko lopanda mwini kumene iye sanali Mkristu komabe anafuna kuzindikiridwa monga mmodzi. Tonsefe tingayamikire kuti mkhalidwe wake sunali woyenerera ku chikhutiritso chozama m’moyo kapena ku chimwemwe chosatha.

Anthu oterowo ali otsimikizika kukumanizana ndi zowawa zauzimu. Malonda ndi kumvana mwa mayanjano ndi anthu omwe ali odera nkhaŵa mochepera ponena za kuwona mtima kapena mkhalidwe woipa wa chisembwere kumawunikiritsa munthu ku zisonkhezero zoipa. Akristu omwe mwakutero ali owunikiridwa ayenera kumenyera molimbana ndi zisonkhezero zimenezi ndipo kaŵirikaŵiri amakhala ndi kulimbana ndi chikumbumtima chawo. Ena potsirizira pake amakhala monga oyanjana nawo awo ndipo asokeretsedwa kotheratu kuchoka ku chikhulupiriro. (1 Akorinto 15:33) Kodi ndi cha phindu lotani chipambano cha zachuma chomwe chimatsogolera ku kulephera koteroko kwauzimu ndi kwa makhalidwe abwino? Monga mmene Yesu ananenera kuti: “Pakuti munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse nataya moyo wake?”​—Mateyu 16:26.

Mtundu Wabwinoko wa Chipambano

Chokumana nacho chatsimikizira kuti chiri chanzeru kulabadira uphungu uwu wa Baibulo; “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano, koma . . . mukazindikire chimene chiri chifuno cha Mulungu chabwino ndi chokondweretsa ndi changwiro.” “Musakonde dziko lapansi kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye.” Inde, tiri anzeru ngati sititsanzira dziko kapena kutsatira chimene limapereka. Chodera nkhaŵa chathu chokulira chiyenera kukhala kaamba ka chivomerezo cha Mulungu, chomwe sichingapezedwe mwa kulondola, zinthu za kudziko.​—Aroma 12:2; 1 Yohane 2:15, 16.

Yesu anachitira ichi fanizo ndi mlimi yemwe anakhulupirira mwa chuma chake koma kwa amene Mulungu ananena kuti: “Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako. Ndipo, zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?” Akumafupikitsa fanizo lake, Yesu ananena kuti: “Atero iye wa kudziwunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma kwa Mulungu.” Yesu anali kusonyeza kuti “ngakhale pamene munthu ali nazo zochuluka moyo wake sutuluka kuchokera ku zinthu ali nazo.”​—Luka 12:15-21.

Yesu anagwiritsira ntchito chitsanzo cha moyo cha wolamulira wachichepere wolemera kusonyeza chinthu chimodzimodzicho. Munthu ameneyu anali wachipambano m’lingaliro la kudziko, ndipo iye mwachiwonekere anafuna kukhala wowongoka mwa makhalidwe. Ngakhale kuli tero, Yesu sanamusonyeze iye monga chizindikiro cha chipambano. M’malomwake, Yesu ananena kuti chikakhala chovuta kwa anthu otero “kulowa mu ufumu wa Mulungu.” Anthu ambiri mu mkhalidwe umenewo sali okonzekera kupereka nsembe zikondwerero zawo zakuthupi ndi kufunafuna Ufumu wa Mulungu monga chonulirapo choyamba m’miyoyo yawo.​—Luka 18:18-30.

Akumagogomezera mowonjezereka pa chiyambi cha zikondwerero zauzimu, Yesu ananena kuti: “Chifukwa chake musadere nkhaŵa ndi kuti, ‘Tidzadya chiyani?’ kapena, ‘Tidzamwa chiyani?’ kapena, ‘Tidzavala chiyani?’ Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo. Pakuti Atate wanu wakumwamba adziŵa kuti musowa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” Chotero, ngakhale m’chigwirizano ndi zinthu zofunikira koposa, tiyenera kukhala ndi zinthu zathu zoyambirira zitaikidwa molondola. Kwa ife kuti tikhale achipambano​—kufikira chimwemwe ndi kupeza chikhutiritso chowona​—zauzimu ziyenera kukhala patsogolo pa zakuthupi.​—Mateyu 6:31-33.

Pitirizani Kufunafuna Chipambano Chauzimu

Chotero njira yanzeru mwachidziŵikire iri kufunafuna chipambano mwa kulondola Ufumu wa Mulungu ndi chilungamo chake. Ichi chimaphatikizapo kuphunzira Baibulo kotero kuti “mukadzitsimikizire inu eni chimene chiri chifuno cha Mulungu chabwino ndi chokondweretsa ndi changwiro.” Chifuno chake chimaphatikizapo kuika kwanu utumiki wake kukhala woyambirira m’moyo wanu, kukhala kwanu ndi kugawanamo kotheratu mu utumiki Wachikristu, kusanyalanyaza kwanu misonkhano ya Chikristu, ndi kutsogoza kwanu moyo wowongoka mwa makhalidwe m’chigwirizano ndi chilungamo cha Mulungu. Zinthu zimenezi siziyenera kuikidwa pambali kaamba ka, kapena kuphimbidwa ndi, zikondwerero zakuthupi. Ichi ndicho chimene chinatanthauzidwa ndi uphungu wa Yesu kwa wolamulira wachichepere wolemera: “Gulitsa zirizonse uli nazo nugawire osauka, ndipo udzakhala nacho chuma chenicheni m’mwamba; ndipo ukadze kuno unditsate ine.”​—Aroma 12:2; Luka 18:22.

M’kuchita ichi, mudzakhala mukumangirira uzimu wanu ndi uja wa banja lanu. M’malo mwa kukhala wa maganizo okwezeka kapena kuyedzamitsa chiyembekezo chanu pa chuma chosatsimikizirika, mudzakhala pakati pa awo amene “akuchita zabwino nachuluka ndi ntchito zabwino, . . . nadzikundikira iwo okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.” Inde, chonulirapo chanu chingakhale moyo wosatha m’Paradaiso wobwezeretsedwanso pa dziko lapansi chifukwa “dziko lapansi lipita ndi chilakolako chake, koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.” Palibe chipambano chokulirapo chomwe mungachifikire.​—1 Timoteo 6:17-19; 1 Yohane 2:17.

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi ndalama ziri mfungulo?

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi makolo adzatumiza ana awo kuti alondole chipambano kupyolera m’maphunziro apamwamba?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena