Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w88 10/1 tsamba 20-25
  • Moyo Wathu Wodzetsa Mphoto Monga Amishonale mu Africa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo Wathu Wodzetsa Mphoto Monga Amishonale mu Africa
  • Nsanja ya Olonda—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Wogwira Ntchito m’Munda wa chiAmerica Aphunzira Chowonadi
  • Kugwira Ntchito Kulinga ku Chonulirapo cha Utumiki Waumishonale
  • Kuchokera ku Gileadi kupita ku Africa
  • Moyo Wodzetsa Mphoto M’nkhalango
  • Kusinthira Kwathu Kupita ku Denga la Africa
  • Ubale Wathu Wapadziko Lonse Wandilimbikitsa
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Yehova Anandiphunzitsa Kuchita Chifuniro Chake
    Nsanja ya Olonda—2012
Nsanja ya Olonda—1988
w88 10/1 tsamba 20-25

Moyo Wathu Wodzetsa Mphoto Monga Amishonale mu Africa

Monga momwe yasimbidwira ndi John Miles

CHOCHITIKACHO chiri mosungira nyama kumpoto cha kumadzulo kwa Zimbabwe. Mkazi wanga, Val, ndi ine tikuyendetsa galimoto kulinga ku Victoria Falls yotchuka. Ayi, sitiri ochezera malo. Ndife amishonale ndipo tatumizidwa kuno kudzagwira ntchito pakati pa anthu omwe ali nzika za ku Africa. Pamene tikuzunguluka pokhota, kumeneko, yoimirira kumbali kwa msewu, iri njovu yaikulu. Ndiimitsa galimoto ndi kusunzumira pa zenera kuti ndijambule chithunzi. Ndiri pafupi kutenganso china pamene Val afuula kuti:

“Iyo ikubwera kaamba ka ife!”

Mwamsanga ndiliza galimoto, koma ilephera. Ndi choipa chotani nanga! Njovuyo itsiriza kubangula kwake ndi kusendera kudzatitswanya ife. Kokha pa nthaŵi yake galimoto iyamba ndipo titembenukira m’nkhalango. Mwamwaŵi, mulibe miyala kapena mitengo yoimitsa kuthaŵa kwathu. Tigamulapo kupatsa Bambo Jumbo njira yabwino ndi kupitiriza m’njira ina yosiyana.

Chochitika china. Nthaŵi ino tiri mu ufumu wa mapiri wa Lesotho, kum’mwera kwa Africa. Pali pa Sande masana mumzinda waukuluwo, Maseru. Tikubwerera kunyumba pambuyo pa kusangalala ndi kusonkhana kwa Chikristu ndi akhulupiriri anzathu a kumaloko. Mwadzidzidzi, taukiridwa ndi achifwamba achichepere aŵiri. Mmodzi andimenya ine ndi nkhonya ndipo winayo alumphira ku msana kwanga. Ndimkankha iye, ndipo atembenukira kwa Val, ndi kugwira chola chake. Val aitana mofuula: “Yehova! Yehova! Yehova!” Panthaŵi yomweyo, mwamunayo aleka chola chake ndipo ndi kawonekedwe kosokonezeka iye abwerera m’mbuyo. Yemwe ankandimenya ineyo abwereranso m’mbuyo​—nkhonya zake zikumakantha mphepo. Tifulumira, opumitsidwa kwakukulukulu kukakumana ndi akhulupiriri anzathu pa malo okwerera basi.​—Miyambo 18:10.

Chirichonse cha zochitika zomwe ziri pamwambapo chinatha kokha kwanthaŵi zochepa, koma ziri pakati pa zikumbukiro zambiri zosaiwalika za zaka zathu zapitazo 32 monga amishonale mu Africa. Ndimotani mmene tinabwerera kuno? Nchifukwa ninji tinakhala amishonale? Kodi iko kwakhala moyo wodzetsa mphoto?

Wogwira Ntchito m’Munda wa chiAmerica Aphunzira Chowonadi

Zonsezo zinayamba mu 1939 pamene ndinakumana ndi Val Jensen mu Yakima, Washington, U.S.A. Panthaŵi imeneyo, ndinali kugwira ntchito pa munda ndipo Val analembedwa ntchito monga wogwira ntchito m’nyumba. Iye kaŵirikaŵiri ankalankhula kwa ine ponena za Baibulo. Chinthu chimodzi chomwe chinandisangalatsa ine chinali kulongosola kwake kwakuti helo sali malo otentha. (Mlaliki 9:5, 10; Machitidwe 2:31; Chivumbulutso 20:13, 14) Ngakhale kuti sindinapitepo ku tchalitchi, ndinadziŵa kuti atsogoleri achipembedzo anaphunzitsa ponena za helo, ndipo chimene Val anandisonyeza ine kuchokera m’Baibulo chinakhala chomveka kwenikweni.

Atate a Val ndi amayi ake anakhala Mboni za Yehova mu 1932. Val nayenso anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo anabatizidwa mu September 1935. Pamene tinakhala ozoloŵerana, Val anandiitana ine kupita ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Ndinalandira ndipo ndinasangalala kuyanjana ndi anthu omwe ndinakumana nawo kumeneko, uko ndiko kuti, nthaŵi iriyonse pamene kulima kunandilola ine ntahŵi ya kupitako. Umoyo wa kumunda unakhala woyambabe m’moyo wanga. Mwapang’onopang’ono, ngakhale ndi tero, ndinayamba kuwona misonkhano kukhala yofunika koposa, ndipo Mboni za kumaloko zinandiitana ine kugawana m’kulalikira kwa kunyumba ndi nyumba . Kuchita ichi m’mzinda wa kwathu kunawoneka kukhala monga chiyeso chokulira kwa ine. Koma ndinachipambana icho.

Zinthu ziŵiri zokumbukirika zinachitika mu 1941. Mu March, ndinabatizidwa monga mboni yodzipereka ya Yehova, ndipo pambuyo pake Val ndi ine tinakwatirana. Kenaka, mu October 1942, tinayamba ntchito yolalikira ya nthaŵi zonse monga apainiya kum’mwera cha kum’mawa kwa North Dakota.

Sitidzaiwala nkomwe chomwe chinachitika chaka chotsatira. Unali mwala wolumphira m’mbiri ya Mboni za Yehova. Pa February 1, 1943, kuphunzitsa kwa umishonale kunayamba kaamba ka kalasi loyamba la chimene panthaŵiyo chinakatchedwa Watchtower Bible College of Gilead. Miyezi iŵiri pambuyo pake tinapezeka ku msonkhano wa “itanirani ku Ntchito” mu Aberdeen, South Dakota. Madalitso a utumiki wa umishonale m’maiko achilendo analongosoledwa, ndipo chikhumbo chokapezeka ku Gileadi ndi kukhala amishonale chinadzutsidwa m’mitima yathu.

Kugwira Ntchito Kulinga ku Chonulirapo cha Utumiki Waumishonale

Zaka zisanu ndi zinayi zinafunikira kupita tisanafikire chonulirapo chathu. Mkati mwa nthaŵi imeneyo, tinali ndi mwaŵi wina wabwino kwambiri wa utumiki, limodzinso ndi zobweza m’mbuyo. Pambuyo pa kuchita upainiya kwa chaka chimodzi ndi theka ku North Dakota, tinafunsira kaamba ka gawo la upainiya mu Missouri. Ichi cinavomerezedwa, ndipo tinakhala mu mzinda wa Rolla. Gawo lathu linaphatikizapo Phelps County yonse kumene kunali kokha Mboni ykangalika imodzi. Tinatha zaka zitatu zosangalatsa kumeneko ndipo tinagawana m’kukhazikitsidwa kwa mpingo.

Kenaka tinakumanizana ndi vuto lomwe linazimiriritsa ziyembekezo zathu za kukhala amishonale. Chuma chathu chinatha. Kulinganiza koipa ndi kusoweka kwa chikhulupiriro chakuti Yehova akakhoza kupereka kunatipangitsa ife kuleka kuchita upainiya. Chinali chikhumbo chathu kuti ichi chikakhala kokha kwa miyezi yoŵerengeka, koma chinafikira ku chaka ndi theka tisanayambe kuchita upainiya kachiŵirinso. Nthaŵi ino tinagamulapo kusakhoza kubwereza zolakwa athu zapitazo. Gawo lathu latsopano linali ndi mpingo mumzinda wa Reardan kum’mawa kwa Boma la Washington. Ntchito ya ganyu inali yovuta kuipeza, chotero tinafunikira kudalira pa Yehova mokulira kupereka zosowa zathu za tsiku ndi tsiku.​—Matthew 6:11, 33.

Gawo lathu linaphatikizapo mizinda yaing’ono yochulukira yapafupi. Tsiku lina tinafunikira kupanga ulendo wobwerera wa makilomita 130 kuchezera anthu ndi uthenga wa Ufumu. Tinali ndi mafuta osakwanira koma sitinalole ichi kutiimitsa ife. Pa ulendo wathu wotuluka mumzinda, tinaimirira pa positi ofesi, ndipo nchiyani chimene muganizira kuti tinapeza? Kumeneko, ikumayembekezera kaamba ka ife inali kalata yochokera kwa msuweni wanga yemwe anangoyamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Iyo inali ndi cheke ya ndalama zokwanira kudzaza tanki yathu ndi kukhala ndi zowonjezereka. “Tinafuna kupanga zimenezi kukhala chopereka ku Mzinda wa Boy,” iwo analemba tero, “koma tinagamulapo kuti inu munazifunikira izo mokulira kuposa Bambo Flanagan.” Anali olondola chotani nanga!

Zokumana nazo zonga izi zinagogomezera kuwona kwa lonjezo la Yesu lakuti: “Komatu funafunani ufumu [wa Mulungu], ndipo izi [zinthu zakuthupi] adzakuwonjezerani.” (Luka 12:31) Ichi chinali chiphunzitso cha mtengo wapatali chomwe chikatithandiza ife kupitirizabe poyang’anizana ndi mavuto ena.

Nyengo ya chisanu ina, tinali kokha ndi unyinji wochepera wa malasha. Kodi tikanalola mkhalidwewo kusintha kugamulapo kwathu kwa kupitirizabe kuchita upainiya? Tinaika nkhaniyo kwa Yehova m’pemphero ndi kupita kukagona. Pa ora lachisanu ndi chimodzi m’mawa wotsatira, panamveka kugogoda pakhomo pathu! Iye anali mbale ndi mkazi wake amene, pobwerera pa ulendo wawo kuchokera kwa achibale, anagamulapo kutichezera. Tinayatsa moto, ndi kuika chidutswa chotsirizira cha malasha, ndi kuikapo m’phika wa kofi. Pamene timasangalala ndi kukhala nawo, mbaleyo mwadzidzidzi anafunsa kuti, “Ndimotani mmene mukukhalira ndi malasha?” Val ndi ine tinayang’anana wina ndi mnzake ndipo tinayamba kuseka. Malasha anali chinthu chimodzi chomwe tinafunikira mwamsanga. Iwo anatipatsa ife madola khumi, amene m’masikuwo akakhoza kulipira chifupifupi theka la tani ya malasha.

Pa chochitika china msonkhano wadera unali pafupi kuchitika, ndipo tinali kokha ndi madola asanu m’manja. Ndiponso, kulipirira msonkho wa galimoto lathu kunali kofunikira mwamsanga pambuyo pa msonkhano. Tinagamulapo kuika zinthu zoyamba poyamba ndipo tinapezeka ku msonkhano. Chiyamiko ku mzimu woolowa manja wa abale, tinabwerera ku gawo lathu ndi $15. Msonkhowo umagulidwa pa $14.50!

Tinasangalala ndi utumiki wathu waupainiya kum’mawa kwa Washington, ndipo unyinji wa mabanja amene tinaphunzira nawo Baibulo potsirizira pake anakhala mboni zokhulupirika za Yehova. Pambuyo pa zaka ziŵiri m’gawo limenelo, ngakhale ndi tero, nidnalandira kalata kuchokera ku Watch Tower Sosaite yolongosola kuti ndinayamikiridwa kutumikira monga mtumiki woyendayenda, uko ndiko kuti, mmodzi yemwe amachezera ndi kulimbikitsa mipingo ya Mboni za Yehova m’dera. “Ngati utaikidwa, kodi udzalandira gawo limeneli?” Sosaite inafaunsa tero, ikumawonjezera kuti: “Chonde tidziŵitse mwamsanga.” Modsakaikira, yankho langa linali inde. Kuyambira mu January 1951, tinathera chaka chimodzi ndi theka m’dera lalikulu lokuta theka la kumadzulo kwa North Dakota ndi theka la kum’mawa kwa Montana.

Mkati mwa nyengoyi, tinalandira chodabwitsa china​—kuitanidwa kukapezeka ku kalasi la Gileadi la 19! Kodi chikhumbo chathu chikafikiritsidwa potsirizira pake? Mwatsoka, kalata ina inatsatira ikumanena kuti kalasilo linadzazidwa ndi abale kuchokera ku maiko ena. Chimenecho chinali chobweza m’mbuyo, koma sitinalefulidwe! Miyezi ingapo pambuyo pake, tinalandira chiitano cha ku kalasi ya 20 ku limene tinalandiridwa mu September 1952.

Kuchokera ku Gileadi kupita ku Africa

Tinayamikira chotani nanga ubwino wa Yehova m’kutibweretsa ife pamodzi limodzi ndi ophunzira oposa zana limodzi kuchokera ku mbali zochulukira za dziko lapansi​—Australia, New Zealand, India, Thailand, Philippines, Scandinavia, England, Egypt, ndi Central Europe! Ichi chinatithandiza ife kuwona ukulu ku umene Yehova anali kulola uthenga wa Ufumu kulalikidwa.​—Mateyu 24:24.

Nthaŵi ku Gileadi inatha mofulumira, ndipo tinatsiriza maphunziro mu February 1953. Limdozi ndi anayi ena, tinagawiridwa ku Nothern Rhodesia (tsopano Zambia) mu Africa. Sosaite, ngakhale ndi tero, mwachifundo inatilola ife kukhala mu United States kaamba ka msonkhano wa mitundu yonse womwe unachitidwira pa Yankee Stadium pambuyo pake chaka chimenecho mu July. Mkati mwa mweziwo msonkhano usanachitike ndi kwa nthaŵi yochepa pambuyo pake, ndinatumikira monga woyang’anira wadera kum’mawa kwa Oklahoma.

Mu November 1953, Val ndi ine, limodzi ndi amishonale ena asanu ndi mmodzi, tinakwera sitima ya m’madzi yopita ku Africa. Tinafikira pa Durban, South Afria, ndipo tinayenda cha kumpoto ndi sitima ya pamtunda kupita ku Southern Rhodesia (tsopano Zimbabwe). Kuno aŵiri anatisiya kuti ayambe gawo lawo mu Salisbury (tsopano Harare), pamene otsalafe tinapitirizabe kupita ku Kitwe, Nrothern Rhodesia.

Val ndi ine tinapatsidwa gawo mumzinda wa ku mgodi wa Mufulira kumene kunali mabanja ochepera okondwerera koma kunalibe mpingo. Yehova anadalitsa ntchito yathu yolalikira ya munyumba ndi nyumba. Tinayamba maphunziro a Baibulo ochulukira, ndipo mwamsanga chiŵerengero cha okondwerera chinayamba kupezeka ku misonkhano ya Chikirstu. Pambuyo pa miyezi yoŵerengeka tinaitanidwa kukadzaza malo pa ofesi ya nthambi ya Watch tower Sosaite mu Luanshya. Pambuyo pake, tinapatsidwa gawo lina kukatumikira monga amishonale ku Lusaka. Pamene tinali kumeneko, ndinatumikira kwa nthaŵi ndi nthaŵi monga woyang’anira wadera ku chiŵerengero chochepa cha mipingo yolankhula Chingelezi.

Moyo Wodzetsa Mphoto M’nkhalango

Kenaka, mu 1960, tinasinthidwira ku Southern Rhodesia kumene ndinagawiridwa kutumikira monga woyang’anira wachigawo pakati pa abale akuda. Mwapang’ono, ichi chinaphatikizapo kuchezera mipingo ndi kuayng’anira misonkhano ya dera ndi ya chigawo. Yochulukira ya mipingo imeneyi inali m’madera a ku midzi chotero tinafunikira kuphunzira kukhala m’nkhalango. Tinadzimva kuti ngati abale athu angakhoze kukhala m’nkhalango, chotero nafenso tingatero.

Ofesi ya nthambi ya Watch Tower Sosaite inatikonzekeretsa ife ndi galimoto ya tani limodzi ndi theka. Kumbuyo kwake kunakutidwa ndi lata la chitsulo ndi zitseko ziŵiri kaamba ka kulonga zinthu. Mazenera pakati pa chakumbuyocho ndi mutu wa galimotoyo anali okulira mokwanira kulowamo, ndipo anakutidwa ndi maketani a pulasitiki. Ziŵiya zathu za m’nyumba zinaphatikizapo kama lopangidwira mkati ndi matresi a mpira. Tinali ndi makabati a mabokosi ndi chophikira chogwiritsira ntchito parafini. Tinalinso ndi moika zovala mokhoza kunyumulidwa ndi hema.

Mwamsanga pambuyo pa kuyamba gawo lathu ku mbali ya kumadzulo kwa dzikolo, ndinalumidwa ndi kachirombo kosadziŵika. Chimenecho chinapangitsa mwendo wanga kutupa ndipo chinabweretsa malungo okulira. Kupangitsa zinthu kuipirako, mphepo inaipirako ndipo kunayamba kugwa mvula yamphamvu. Ndinakachotsa thukuta kwambiri kotero kuti zofunda zanga za pa kama zinafunikira kusinthidwa mobwerezabwereza. Chifupifupi pakati pa usiku, Val anagamulapo kuti ndiwone dokotola. Iye anayendetsa galimoto kulinga ku msewu waukulu, koma galimotolo linatitimira m’matope. Chiyambukiro chokha cha kuyesayesa kwa Val kuliyendetsa ilo kutsogolo ndi kumbuyo kunali kundipatsa ine kugwedezeka kwabwino. Pamene ankhutiritsidwa kuti panalibe chirichonse chomwe akakhoza kuchita, iye anadziphimba iyemwini mu bulangeti lotsirizira lowuma ndipo anagwirizana ndi ine m’galimotomo pamene mvula inkagwabe.

M’mawa munabweretsa mpumulo. Ndinadzimva bwinopo, mvula inali italeka, ndipo abale omwe anadza kudzakonzekera kaamba ka msonkhano anachotsa galimoto lathu m’matopemo. Mu Bulawayo abale ena achifundo anandipereka ine ku chipatala, ndipo pambuyo pa kupatsidwa mankhwala ndinali wokhoza kubwerera ndi kupitirizabe ndi makonzedwe a msonkhano.

Munali mkati mwa nyengoyi, pamene ndinkayenda pakati pa mipingo, pamene tinakumana ndi njovu. Tinakumananso ndi zolengedwa zazing’ono zochulukira. Ena a ochezera athu mu hema, pambali pa ntchentche ndi udzudzu, zinali nyerere. Mu nthaŵi yochepa kwambiri, izi zinakhoza kupanga zibowo m’chovala chirichonse kapena malaya omwe anasiidwa pansi. Mitundu yosiyanasiyana ya abuluzi ndi akangaude osaka omwe anatichezera inali yosavulaza, koma njoka ya mamba yomwe inabwera inachotsedwamo mwamsanga. Ndipo anakalizi sanalonjeredwenso. Val analongosola kuluma kwawo kukhala kudzimva konga ngati kuti msomali wotentha ndi moto wakhomeredwa mwa inu ndi nyundo yaikulu. Iye walumidwa nthaŵi zinayi!

Mwinamwake, zinthu zimenezi zimapangitsa umoyo wa m’nkhalango kumveka wodzetsa mphoto, koma sitinauwone mwanjirayo. Kwa ife, anali malo otseguka, a umoyo wachangu, waumoyo, ndi madalitso auzimu oposa zosakhalitsa bwino zirizonse zakuthupi.

Chinali nthaŵi zonse cholimbikitsa chikhulupiriro kuwona kuyesayesa kopangidwa ndi abale a kumbali ya ku midziko kupezeka ku misonkhano. Mpingo umodzi unapangidwa ndi magulu aŵiri okhala pa makilomita 23 mosiyana ndi kokha kanjira kolumikiza iwo. “Nyumba yawo ya Ufumu,” chapakati pa gululo, inali mtengo waukulu kaamba ka mthunzi ndi miyala kaamba ka kukhalapo. Abale kuchokera ku gulu lirilonse anayenda makilomita 11.5 ulendo uliwonse kukapezeka ku misonkhano yawo kawiri pa mlungu. Timakumbukiranso okwatirana aŵiri achikulire omwe anayenda makilomita 120 ndi masutikesi awo ndi mabulangeti kukapezeka ku msonkhano wadera. Izi ziri kokha zitsanzo ziŵiri za mmene abale a ku Africa amayamikirira kulangiza kwa ‘kusaleka kusonkhana kwawo pamodzi.’​—Ahebri 10:25.

M’madera ena nzika za kumaloko zinakhala zokaikira ponena za cholinga chathu, ena anakhoza ngakhale kuipidwa ndi kukhala kwathu pafupi nawo. Pa chochitika chimodzi, ndinaika hem wathu pafupi ndi malo a msonkhano pa malo ozunguliridwa ndi udzu wautali. Pambuyo pa kutha kwa gawo la msonkhano ndipo pamene tinali mu kama maora angapo, ndinadzutsidwa ndi phokoso kunja. Mwakugwiritsira ntchito nyali yanga yowunikira, ndinakhoza kuzindikira winawake ali chiimilire kumbuyo kwa mtengo waung’ono.

“Ukufuna chiyani?” Ndinafuula tero. “Nchifukwa ninji ukubisala kumbuyo kwa mtengo umenewo?”

“Khala chete mbale,” linatero yankho, “tinamva anthu akunena kuti anali kufuna kuwotcha udzu uwu. Chotero talinganiza mlonda kaamba ka inu mkati mwa usiku.”

Iwo sanatiuze ife ponena za mgoziyo kuti asasokoneze tulo tathu. Komabe anali ofunitsitsa kuwononga tulo tawo ndi cholinga chofuna kutichinjiriza ife! Pamene msonkhano unatha pa Sande masana, iwo anakonzekera galimoto limodzi likumayenda kutsogolo kwathu ndi limdozi kumbuyo kufikira titapyola m’dera langozilo.

Chinalinso chodzetsa mphoto kuwona ubwino umene anthu odzichepetsa amenewa amaika pa Baibulo. Mpingo umdozi umene tinachezera unali m ‘dera limene anthu a m’midzimo anali kulima ntedza. Mkati mwa mlunguwo, tinagulitsa mabukhu ndi maBaibulo kaamba ka mabokosi a ntedza wosatongola. Pamene kuchezera kwathu kunatha, tinalonga ziŵiya zathu, mabukhu, ndi ntedza ndi kuyamba kupita ku malo a msonkhano wotsatira. Mwamsanga pambuyo pa kuchoka pa malopo, tinafunsidwa kuimirira chifukwa chkuti winawake ankatitsatira. Tinaimirira ndi kuyembekeza. Zinachitika kuti anali mayi wachikulire kwambiri wonyamula bokosi la ntedza pamutu pake. Panthaŵi imene iye anatipeza ife, iye anali atatoperatu kwenikweni kotero kuti anagwa pansi ndipo anagona pamenepo kufikira atayamba kupuma bwino. Inde, iye anafuna Baibulo! Tinayenera kuchotsanso zinthu zonse, koma chinali chosangalatsa kukhutiritsa chikhumbo chake. Baibulo limodzi lowonjezereka m’manja achikondi​—ndipo bokosi limodzi lowonjezereka la ntedza m’galimoto lathu!

Chinalinso chosangalatsa kuwona mmene Yehova anadzetsera oyang’anira adera kuchezera mipigo yochulukira m’nkhalango za Africa. Panthaŵi imeneyo chinali chovuta kaamba ka Sosaite kupeza abale oyeneretsedwa omwe analibe mathayo a banja. Chotero sichinali chachilendo kaamba ka woyang’anira woyendayenda kupita kuchokera ku mpingo umodzi kupita ku mpingo wina, kaya ndi basi kapena pa njinga, ndi mkazi wake ndi ana aŵiri kapena atatu, sutikesi, mabulangeti, ndi mabukhu. Abale amenewa ndi mabanja awo anagwiradi ntchito mwamphamvu ndipo popanda kudandaula kutumikira mipingo. Unali mwaŵi wokulira kutumikira ndi iwo.

Mu ma 1970 nkhondo ya chiweniweni inayamba kupangitsa mavuto kaamba ka abale, ndipo nkhani ya uchete inkaika ochulukira a iwo ku chiyeso chokulira cha chikhulupiriro. (Yohane 15:19) Sosaite inachilingalira icho kukhala choyenera kusintha gawo langa kotero kuti ndisaipitse mkhalidwe kaamba ka abale mosayenera. Chotero, mu 1972, ndinaitanidwa kukatumikira pa ofesi ya nthambi mu Salisbury. Ichi chinandipatsa ine mwaŵi wa kuthandiza ndi kumangidwa kwa ofesi ya nthambi yatsopano. Nthaŵi ina pambuyo pake ndinagawiridwa monga woyang’anira wadera kaamba ka mipingo yomwazikana mokulira yolankhula Chingelezi. Ichi chinafunikira kuyenda mu litali ndi mu lifupi mwa Zimbabwe. M’madera ena mkhalidwe unali wowopsya kwambiri kotero kuti tinafunikira kuyenda mu unyinji wa magalimoto wolinganizidwa ndi boma ndi kutetezeredwa ndi asirikari ndi ndege ndi kuchinjiriza kwa helicopter.

Kusinthira Kwathu Kupita ku Denga la Africa

Kenaka kunadza kusintha kwina kokulira kwa gawo. Tinayenera kukatumikira ku Maseru, likulu la Lesotho. Iri ndi dziko la mapiri, nthaŵi zina lotchedwa denga la Africa, ndipo liri ndi malo ambiri akongola.

Ngakhale kuti timayamikira ndi kusangalala ndi malo ozungulira, chimenecho sichinali chifuno chathu m’kubwera kuno. Tiri kuno kuthandiza kupeza “zinthu zofunika” zolankhulidwa pa Hagai 2:7. Iri ndi dziko laling’ono lokhala ndi chiŵerengero cha anthu cha kokha miliyoni imdozi ndi theka. Pamene tinafika mu 1979, Mboni 571, pa avereji, zinali kugawanamo m’kulalikira “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu” mwezi uliwonse. (Mateyu 24:14) Mpingo mu Maseru unakula kumlingo wakuti unafunikira kugawidwa kukhala iŵiri. Posachedwapa, mu April 1988, tinasangalatsidwa koposa pa kufikira chiŵerengero chapamwamba chatsopano cha ofalitsa a Ufumu 1,078.

Panthaŵi ino, ntchitoyo ikupitirizabe kupita patsogolo m’magawo athu akale a umishonale mu Zambia ndi Zimbabwe. Pamene choyamba tinafika mu Africa zaka zina 35 zapitazo, panali chiwonkhetso cha ofalitsa a Ufumu 36,836 m’maiko aŵiriwo. Lerolino, chiŵerengero choikidwa pamodzi chiri 82,229. Mwaŵi wa kugawana m’njira yochepera m’kuwonjezeka kumeneku wakhala mphoto yozizwitsa kwa ife.

“Talawani ndi kuwona kuti Yehova ndiye wabwino,” analemba tero wamasalmo Davide. (Salmo 34:8) “Kulawa” kwathu kwa utumiki wa umishonale kwatikhutiritsa ife za kukhulupirika kwa mawu amenewa. M’chenicheni, chiyambire 1942 pamene tinayamba mu utumiki wa nthaŵi zonse pamodzi, miyoyo yathu yadzazidwa ndi madalitso pamene takumana ndi ubwino wochulukira wa Yehova. Padakali ntchito ina yowonjezereka yofunikira kuchita. Tiri oyamikira chotani nanga kwa Yehova kuti tikali ndi mlingo wamphamvu ndi umoyo wa kugwiritsira ntchito mu utumiki wake!

[Chithunzi patsamba 24]

John Miles ndi mkazi wake, Val

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena