Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 1/15 tsamba 21-24
  • Chikole—Ndimotani Mmene Akristu Ayenera Kuchiwonera Icho?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chikole—Ndimotani Mmene Akristu Ayenera Kuchiwonera Icho?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Chingayambukirire Atate
  • Mmene Chingayambukirire Mkwatibwi ndi Mkwati
  • Sungirirani Kawonedwe Kolinganizika
  • Kodi Mukudziwa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Kuika Malowolo Otsika
    Nsanja ya Olonda—1998
  • “Ukwati wa Mwambo” ku Ghana
    Galamukani!—1996
  • Kukonzekera Ukwati Wachipambano
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 1/15 tsamba 21-24

Chikole​—Ndimotani Mmene Akristu Ayenera Kuchiwonera Icho?

MWAMBO wakale wa kupereka chikole udakachitidwabe m’maiko ambiri. Mu nkhani zambiri, malipiro amakhala mu mtundu wa ndalama, limodzi ndi mphatso za mtengo wake. Malipilowo amasiyana kuchokera ku malo ndi malo ndi kuchokera ku banja ndi banja, kudalira pa mkhalidwe wa mayanjano, maphunziro, ndi nsonga zina. Iwo ukhazikitsidwa ndi lamulo m’maiko ena, ngakhale kuti anthu ochepera amasunga mtengo wokhazikitsidwawo.

Kulingalira kosamalitsa kwasonyeza kuti miyambo yamakono imaphatikizamo koposa kupereka chikole. Chotero, chiri chanzeru kulingalira mmene ichi chingayambukire inu monga Mkristu.

Mu Papua New Guinea, kulipira kwa chikole kuli monga kusamutsa kwa zinthu kuchokera ku gulu la banja limodzi, banja lofutukuka la mkwati, ku gulu lofanana nalo ku mbali ya mkwatibwi wa ukwatiwo. Malipirowo angayambire kuchoka pa K1,000 kufika ku K460,000 (Zambia), kudalira pa kulemera kwa banja la mkwatilo. Mu Sri Lanka, mkhalidwewo uli m’njira inayo. Makolo a mkwatibwi ayenera kupereka ziwiya za m’nyumba kwa mkwati. Izi zingaphatikizepo zokometsera, katundu, nyumba, ndi ndalama. Ndi cholinga chakuti katundu asachoke m’banja, chiri cha mwambo kukwatira msuweni woyamba.

Mu mbali zambiri za Africa, malipiro ali amodzi a ziyeneretso za mwambo zomwe zimapangitsa pangano la ukwati kukhala lotheratu ndi logwira ntchito. “Pakati pa Igbos,” akutero tate wa ku Nigeria amene mwana wake wamkazi anali kukonzekeretsedwa kaamba ka ukwati, “kulipira kwa chikole kuli koyenerera kaamba ka ukwatiwo kukhala ndi kuzindikiridwa kwa mwambo. Kulandira kwa icho kuli chisonyezero cha kugwirizana kwa banja la mkaziyo. Chimakhutiritsa chivomerezo cha anthu cha ukwati. Kaamba ka chifukwa ichi, ngakhale ukwati womangidwira mu tchalitchi kapena malo olembetsera a boma sungazindikiridwe m’mudzi wa kumaloko kusiyapo kokha ngati chikole chinalipiridwa.”

Mmene Chingayambukirire Atate

Pakati pa anthu a ku Africa amenewa, malipiro anali kugwiritsiridwa ntchito monga chisonyezero cha kusonyeza kuthekera kwa mwamunayo kwa kusungirira banja. Ziwalo za banja lake zikachezera makolo a mkaziyo kaamba ka cholinga cha kukambitsirana za chikole. M’malo ambiri ichi sichirinso tero, popeza kuti atate tsopano m’chenicheni amapempha kaamba ka mtengo wapamwamba koposa womwe angathe kupeza. Unyinji wosiyana kuchokera ku chifupifupi K120, womwe uli woikidwa ndi lamulo m’mbali zina za Nigeria, kufika ku K14,000 kapena zowonjezerako umafunidwa. Ndalama kapena mphatso zingayembekezeredwe ngakhale pambuyo pa ulendo woyamba wa makolo a wofuna kukwatirayo. Kenaka, monga mu Zaire, zambiri ziyenera kuperekedwa “kutsegula pakamwa pa atate,” uko ndiko kuti, kuwasonkhezera iwo kukambitsirana kaamba ka mtengo wa mwana wawo wamkazi. Ngakhale pambuyo pakuti unyinji wina wa ndalama walipiridwa, malipiro ena ndi mphatso zingafunidwe.

Machitachita oterowo angalimbikitse umbombo kaamba ka ndalama. Komabe, Baibulo limanena kuti: “Muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama.” (1 Timoteo 6:10) Chifukwa cha umbombo, anthu angakhale olanda, ndipo ichi chimabweretsa kupanda chiyanjo kwa Mulungu. Baibulo limatiuza ife kuti “wosirira​—amene apembedza mafano​—alibe cholowa mu ufumu wa Kristu ndi Mulungu.”​—Aefeso 5:5; yerekezani ndi Miyambo 20:21; 1 Akorinto 5:11; 6:10.

Komabe, palibe china chirichonse cholakwika m’kupereka chikole kwa atate monga chisonyezero cha chibwezero kaamba ka kusoweka kwa mwana wamkazi yemwe anamulera ndi kumphunzitsa. Mwana wamwamuna woyembekezera kukhala mpongozi moyenerera angawone malipiro amenewa monga chisonyezero cha chiyamikiro chake kaamba ka kuphunzitsa koperekedwa kwa mkazi wake wotomeredwayo. Ngakhale kuli tero, makolo ena amayesera kubwezera zonse zomwe anataya, akumadzimva kuti ana akazi okwatiwa sadzathandiza m’kuphunzitsa ana ocheperako. Makolo oterowo amayang’ana kaamba ka chikole chapamwamba koposa chothekera, ngati kuti ana awo akazi anali kokha zinthu zogulitsa. Koma iwo ali ndi thayo la kulera bwino ana awo. Kunyada kwawo kuyenera kukhala kukwaniritsa thayo limeneli, osati kuwona kuti ndi zochuluka chotani zomwe angabwezeredwe m’nkhani ya ndalama kapena kutchuka kupyolera mu mtengo wosalingalirika wa chikole. M’malo mwa kutsogoza makolo kulingalira za mapindu a zinthu zakuthupi amene ana angabweretse, Baibulo limanena kuti: “Ana sayenera kuwunjikira atate ndi amayi, koma atate ndi amayi kuwunjikira ana.”​—2 Akorinto 12:14.

Zokhumba zopangidwa ndi atate ena odzinenera kukhala Akristu sizimalingalira njira ya zachuma ya oyembekezera kukwatira achichepere Achikristu. Nkulekeranji, popeza kuti pali nkhani mu zimene atate oterowo akana kupereka koyenerera kopangidwa ndi abale Achikristu chifukwa chakuti amuna a ku dziko anapereka zochulukira! Ena amafikira pa kusiira kukambitsiranako kwa anansi a ku dziko, omwe kenaka amalamulira mtengo waukulu koposa. Pamene kukambitsirana kumeneku kupitiriza, mkhalidwewo ungasonkhezere achicheperewo kuloŵa mu chisembwere. Ichi ndi chomwe chimachitika pakati pa anthu a ku dziko. Icho kaŵirikaŵiri chimachitika kuti achichepere aŵiri okwiyitsidwawo amagwiritsira ntchito mimba monga njira yopepuka kwambiri ya kukakamizira banja la mtsikanalo kulandira chomwe woyembekezera kukwatirayo ali wokhoza kulipira.

Akristu sayenera kuchita m’njiraiyi. Mawu a Mulungu amaletsa dama, ndipo awo ochita ilo angatulutsidwe kuchoka mu mpingo. (1 Akorinto 6:9; Ahebri 13:4) Atate sangadzichotsere iwo eni liwongo ngati zofuna zawo zolanda zithandizira ku kugwera mu mkhalidwe wa chisembwere kwa mwana wawo wamkazi. Liwongo loterolo lingayambukire mowopsya kaimidwe kawo mu mpingo. Mofananamo, kulandira ndalama za chikole mu unyinji uliwonse kuchokera kwa munthu wa ku dziko ndi cholinga cha kukwatitsa mwana wamkazi Wachikristu wodzipereka kwa iye sikuli kwa teokratiki. Kuchita ichi sikumayeneretsa mbale chifupifupi kaamba ka mwaŵi wina wapadera mu mpingo. Makolo Achikristu ayenera kufuna achichepere kukhalabe amphamvu mu mpingo Wachikristu ndipo ayenera kuwathandiza iwo kusungirira mkhalidwe woyera. Iwo ayenera kukhumba kuti ana awo akazi akwatiwe mwachimwemwe “kokha mwa Ambuye,” kwa amuna omwenso amakonda Yehova ndipo ali ndi ulemu wozama kaamba ka malamulo ake ndi maprinsipulo.​—1 Akorinto 7:39.

Sichiri chachikristu kuchita ndi chikole monga njira ya kupangira ndalama kuchokera kwa mwana wanuyo, molanda kufunsira zoposa zomwe ziri zoyenera. Tate Wachikristu ayenera kudzichinjiriza molimbana ndi umbombo ndi dyera, popeza kuti ichi chingayambukire mowopsya uzimu wake ndi mwaŵi umene amasangalala nawo mu mpingo.​—1 Akorinto 6:9, 10.

Mwachimwemwe, atate ambiri Achikristu asonyeza kulingalira mu chomwe afunsira monga chikole, ndipo ichi chimavumbula mkhalidwe wabwino. Ena afikira ngakhale pa kusankha kuti asapemphe chikole china chirichonse, kotero kuti adzichinjirize molimbana ndi kugwiritsira ntchito molakwa miyambo ndi kupangitsa mavuto auzimu.

Mmene Chingayambukirire Mkwatibwi ndi Mkwati

Dyera la mtsikana, m’nkhani zambiri, lasonkhezera unyinji umene makolo amaika monga chikole. Pali awo omwe amafunsa kaamba ka ukwati wa mtengo ndi wa chiwonetsero, ngakhale kukakamiza makolo awo mokhazikika kaamba ka ichi. Ena amalamulira kuti makolo awo agule ziwiya za mtengo koposa kaamba ka kugwiritsira ntchito m’nyumba yatsopano. Ndi cholinga chotenga chisamaliro cha zinthu zoterozo, atate angachimve kukhala choyenerera kuwonjezera chikole.

Ichi, m’kubwezera, chimakakamiza mkwati kuyamba ukwati wake pansi pa thayo la ngongole zopangidwa kaamba ka ukwati wa mtengo koposa ndi mipando yodula. Mawu a Mulungu amanena kuti “nzeru yochokera kumwamba . . . ilingalira bwino.” Okwatirana achichepere ayenera kulola “kulingalira bwino kwawo kuwonekera kwa anthu onse” mwa kukonzekera ukwati womwe sumaika thayo lolemera la za ndalama pa aliyense.​—Yakobo 3:17, NW; Afilipi 4:5.

Pambuyo pa ukwati, mkazi angayambe kuyesa chikondi cha mwamuna wake kaamba ka iye mwa unyinji womwe analipira monga chikole. Iye angadzimve wopanda chisungiko ngati iye anapanga malipiro ochepera. Iye angalingalire kuti ngati angatope naye ndi kukhumba kumuthamangitsa iye, mwamunayo angachite tero mopepuka, akumakhala wofunitsitsa kutaya unyinji wochepera umene iye analipira. Chiri chowona kuti amuna ena abweza akazi awo kwa makolo awo kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana, zonga ngati kusakhala wokhoza kubala ana kapena kusonyeza mzimu wowukira. Ichi mopanda chifundo chimalimbikitsidwa ndi awo omwe amanena kwa mwamuna wachichepere yemwe wangopereka kumene chikole kuti: “Wagula mkazi.” Ngati iye analipira mtengo wokulira, iye angakhale woyesedwa kuwona mkazi wake monga kapolo wogulidwa m’malo mwa kukhala bwenzi lake lathithithi. Ndiponso, kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana, azitate abweza chikole ndi kukakamiza ana awo akazi kusiya amuna awo.

Pali awo omwe amatsutsa kuti mtengo wachikole wapamwamba wathandiza kusalimbikitsa ichi chifukwa cha vuto la kupezanso kapena kubwezera unyinji wokulira wa ndalama. Iwo amadzimvanso kuti mtengo wapamwamba umachepetsako maukwati a mwamsanga, popeza kuti chimatenga nthaŵi yotalikirapo kwa mwamuna kusunga ndalama kulinga ku kukwatira. Malingaliro amenewa, iwo amadzimva kuti, amatulukamo mu amuna achikulire ndi okhala ndi thayo ndi maukwati okhazikika kwenikweni.

Zowona monga mmene ichi chingakhalire mu nkhani zina, kukhazikika kwa ukwati Wachikristu sikuyenera kuzikidwa pa zolingalira zakuthupi zoterozo. Kukhulupirika kwa mwamuna Wachikristu sikuyenera kudalira pa chomwe iye angataye mwakuthupi ngati ukwati usweka. M’malomwake, iye ayenera kulamulidwa ndi prinsipulo la m’Malemba lakuti: “Chimene Mulungu anachimanga pamodzi munthu asachilekanitse.” (Mateyu 19:6) M’malo mwa kuwona akazi awo monga katundu wogulidwa, amuna akulamulidwa ‘kuwapatsa iwo ulemu.’ (1 Petro 3:7) Yesu ananena kuti mwamuna ndi mkazi amakhala “thupi limodzi” pamene akwatirana. (Mateyu 19:5; Genesis 2:24) Baibulo limachenjeza amuna kukonda akazi awo, kuwalera iwo ndi kuwasamalira iwo, monga mmene amachitira ndi matupi awo enieni. (Aefeso 5:28, 29) M’kuwonjezerapo, muyezo weniweni wachikondi cha mwamuna uyenera kukhala njira imene amachitira ndi mkazi wake mkati mwa zaka za pambuyo pa ukwati. Kaya mwamuna wapereka chikole chirichonse kapena ayi, ngati iye amapereka chisamaliro chabwino kwa mkazi wake ndipo ali wokhulupirika m’chikondi chake, kodi wina aliyense angakaikire ngati iye amakonda mkaziyo?

Chikole chingayambukirenso njira imene mwamuna amawonera makolo a mkazi wake. Pokhala atapereka chikole chachikulu, angamalize kuti iye alibenso thayo lirilonse kwa iwo, ngakhale ngati iwo agwera m’kusowa. Komabe, Baibulo limanena kuti: “Koma ngati wamasiye ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo ndi kubwezera akuwabala, pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.” (1 Timoteo 5:4) Akristu amatsatira uphunguwu, koma vuto lingayambike ngati mwamuna alola chenicheni chakuti iye anapereka chikole kukhotetsa lingaliro lake la thayo.

Sungirirani Kawonedwe Kolinganizika

Machitachita ena ogwirizana ndi chikole angapangitse mavuto apadera kaamba ka mwamuna wachichepere yemwe akufuna kukwatira mlongo wauzimu amene makolo ake sali Akristu. Iwo angamufune iye kutengamo mbali m’miyambo ina yozikidwa pa kulambira makolo ndi chikhulupiriro m’kusafa kwa moyo. (Mlaliki 9:5, 10; Ezekieli 18:4) Koma kodi iye angachite ichi popanda kutaya chiyanjo cha Mulungu ndi dalitso limene Yehova amasunga kaamba ka awo omwe ‘ayeretsa miyoyo yawo ndi chimvero ku chowonadi’? (1 Petro 1:22; Chibvumbulutso 18:4) Akumayang’anizana ndi zifunsiro zoterozo, Mkristu wodzipereka ayenera nthaŵi zonse kugamulapo “kumvera Mulungu [monga wolamulira, NW] koposa anthu.”​—Machitidwe 5:29.

Ndemanga zomwe zangotchulidwazi ponena za kulanda, kupewa dama, ndi kukwatira kokha akhulupiriri anzathu zimagwira ntchito mofananamo pamene banja la mkwatibwi lipereka ziwiya za m’nyumba. M’tsikana Wachikristu ndi makolo ake sayenera kutsogozedwa ndi miyezo ya dziko m’chosankha cha mwamuna. Kukwatira wosakhala Mkristu kuli kachitidwe ka kusamvera kwa Mulungu. Kupyolera mwa Mose, Iye anauza Aisrayeli kuti: “Ndipo musakwatitsane nawo. Musampatse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, [ndi, NW] kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wa mwamuna.” (Deuteronomo 7:3, 4; 1 Akorinto 7:39) Mwachidziŵikire, chikakhala chosayenera kwa amuna kapena akazi Achikristu kudzisatsa malonda iwo eni mu manyuzipepala apoyera kukhala monga akufuna anzawo a mu ukwati oyenerera. Pali pakati pa abale ndi alongo awo Achikristu pamene iwo ayenera kufuna anzawo a mu ukwati oyenerera.

Ukwati uli kakonzedwe kopatulika ka Yehova, ndipo tonsefe tiyenera kutsogozedwa ndi chimene iye amanena ponena za iwo m’Mawu ake. Chikondi chenicheni kaamba ka Yehova, ana athu, ndi akhulupiriri anzathu chiyenera kutitsogoza ife kuchotsa kotheratu machitachita onse omwe amaipsya chomwe chiri cholondola ndi chabwino. (Salmo 119:105; Ahebri 4:12) Dalitso la Yehova liri lotsimikizira kupitiriza ndi awo omwe amalola Mawu ake kuwatsogoza iwo m’zosankha ponena za osati kokha chikole ndi ziwiya za m’nyumba komanso nkhani zina zonse za moyo.​—Miyambo 10:22.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena