Kukongola Kungakhale Kokha kwa pa Khungu
HAVA, mkazi woyamba yekha wolengedwa ndi Mulungu, anali mwachidziŵikire mkazi wokongola koposa yemwe anakhalapo ndi moyo. Koma iye ndi mwamuna wake, Adamu, anawukira motsutsana ndi Yehova. Chotero Hava anataya chiyanjo chake chathithithi ndi Mulungu ndipo anagawanamo m’kubweretsa tsoka loipitsitsa pa fuko la munthu. Pambuyo pake, iye mosakaikira anali adakali wokongola, koma kukongola kwake kunali kokha kwa pa khungu.
Kukongola kuli kotheratu mphatso ya Mulungu, ndipo ena alandira yochulukira ya iyo kuposa ena. Ena amakhumba kuti iwo anali okongola koposa—kapena owoneka bwino—kuposa mmene aliri, ndipo ambiri amathera yochulukira ya nthaŵi ndi ndalama akumapanga zochulukira za kawonekedwe kabwino kalikonse komwe iwo ali nako. Koma monga mmene chitsanzo cha Hava chikusonyezera, kukongola kokha kuli kopanda kanthu m’kupita kwa nthaŵi kusiyapo kokha ngati kwatsagana ndi mikhalidwe ina. Mikhalidwe ina iti? Chokumana nacho kumbuyoko m’masiku a Mfumu Solomo chimatithandiza ife kuyankha chimenecho.
Chinachake Choposa Kukongola
Bukhu la Baibulo la Nyimbo ya Solomo limanena za mtsikana wachichepere wokongola, m’Sulami, yemwe anali m’chikondi ndi mbusa wachinyamata wa kumaloko. Kukongola kwake kunakoka chisamaliro cha mfumu, ndipo iye anapangitsa mkaziyo kubweretsedwa ku Yerusalemu m’chiyembekezo cha kumpanga iye kukhala mkazi wake. Unali mwaŵi wotani nanga kaamba ka mkazi wachichepereyo! Kumeneko, iye akakhoza kudyerera kawonekedwe kake kabwino ndi kupeza mkhalidwe wa chuma, mphamvu, ndi chisonkhezero mu ufumuwo. Koma mtsikana wachichepereyo mogamulapo anapewa kufikira kwachikondi kwa mfumuyo. Iye ananyalanyaza kukongola ndi chuma cha Yerusalemu ndi kukhala wokhulupirika kwa mbusa wake wachinyamatayo. Mu nkhani yake, kukongola kunali koposa pa khungu. Iye sanali wopanda chidziŵitso chakuya, wokonda mwaŵi, kapena wa umbombo. M’malomwake, iye anali ndi kukongola kwa mkatikati kumene kholo lake Hava analibe.—Nyimbo ya Solomo 1:15; 4:1; 8:4, 6, 10.
Misampha ya Kukongola Kwakuthupi
Kukongola kwakuthupi, pamene kuli kwakuti kuli kokhumbirika, kungatsogolere ku mavuto omwe kukongola kwa mkatikati sikumayambitsa. Chifupifupi zaka 4,000 zapitazo, mwachitsanzo, kholo Yakobo anali ndi mwana wamkazi wotchedwa Dina yemwe mosakaikira anali wokongola kwenikweni. Pamene iye anatsiriza nthaŵi mopanda nzeru mkuyanjana ndi “ana akazi a m’dziko,” mnyamata wachichepere wotchedwa Sekemu anakokedwa kwenikweni ndi iye chakuti iye anaipitsa mtsikanayo.—Genesis 34:1, 2.
Mowonjezereka, kuwoneka bwino kwakunja, ngati sikunagwirizane ndi kukongola kwa mkatikati, kungapereke kulinganiza kwaumwini kwa munthu wokhala nakoyo. Mfumu Davide anali ndi mwana wamwamuna wotchedwa Abisalomu, ponena za amene timaŵerenga kuti: “Mu Israyeli monse munalibe wina anthu anamtama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu.” (2 Samueli 14:25) Koma kukongola kwakuthupi kwa Abisalomu kunabisa kukhotakhota kwa mkatikati: Iye anali wachabe, wonkitsa, ndi wopambanitsa. Mwamuna wachichepereyo mwaluso anagwiritsira ntchito kukongola kwake kwaumwini kupanga kutsatiridwa mu Israyeli ndipo kenaka anawukira molimbana ndi atate ake a m’banja lachifumu. Potsirizira pake iye anaphedwa koma osati pamene mnyamata wokongolayu asanalowetse ufumuwo m’nkhondo ya chiweniweni.
Kukongola Kwaumuna
Monga mmene nkhani ya Abisalomu yasonyezera, Baibulo limalankhula za amuna limodzinso ndi akazi kukhala okongola. Chitsanzo cha mwamuna yemwe sanaikidwe msampha ndi kukongola kwaumuna kumeneku chiri Yosefe, mbale wamng’ono wa Dina wa m’banja lina. (Genesis 30:20-24) Pamene iye anali mnyamata wachichepere, abale a Yosefe chifukwa cha nsanje anamgulitsa iye monga kapolo kuti atengedwe kupita ku Igupto. Kumeneko, iye anagulidwa ndi nduna ya gulu lankhondo yotchedwa Potifa, ndipo chifukwa cha kukhala wowona mtima ndi wanzeru, iye anakhala woyang’anira wa nyumba ya Potifa. Pa nthaŵiyo, “Yosefe anali wokoma thupi ndi wokongola.”—Genesis 39:6.
Mkazi wa Potifa anakulitsa chikondi kaamba ka Yosefe ndipo mopanda manyazi anayesera kum’nyenga iye. Koma mwamuna wachichepereyo anasonyeza kuti iye anali ndi kukongola kwa mkatikati limodzinso ndi kukongola kwakuthupi. Iye anakana kuchimwa molimbana ndi mbuye wake, Potifa, ndipo anamthaŵa mkaziyo. Monga chotulukapo chake, iye anaponyedwa m’ndende. Chifukwa ninji? Mkazi wa Potifa wogwiritsidwa mwalayo anampatsa iye mlandu wabodza wa kukhala atayesera kumuipsya mkaziyo! Ngakhale kuli tero, ngakhale chokumana nacho chowawachi sichinaipitse kaimidwe ka Yosefe, ndipo chitsanzo chake chabwino koposa pansi pa mavuto oipitsitsa chalimbikitsa anthu owona mtima chiyambire pamenepo.
Monga mmene zitsanzo zimenezi zikusonyezera, kukongola kwa mkatikati—kukongola kwaumunthu makamaka pamene kwazikidwa pa chikhulupiriro mwa Mulungu—kuli kofunika koposa kuposa kawonekedwe kabwino kakuthupi. Anthu achichepere ofuna kukwatira ayenera kukhala ogalamuka za ichi. Olemba ntchito ofunafuna antchito ayenera kukumbukira chimenechi. Ndipo tonsefe tiyenera kusunga m’maganizo kuti kaya tadalitsidwa ndi kukongola kapena ayi, tingakulitse kukongola kwa mkatikati kofunika kwambiri kumeneku. Koma kodi ichi chimaphatikizapo chiyani? Ndipo kodi ndimotani mmene mungachikulitsire icho? Tidzakambitsirana za chimenechi mu nkhani yotsatira.