Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Nchifukwa ninji Nsanja ya Olonda ya September 15, 1988, imasonyeza kuti Chiprotesitanti chadziipitsa icho chokha ngakhale kuposa Chiroma Katolika?
Ichi chinanenedwa chifukwa chakuti chimagwirizana ndi ulosi ndi zenizeni. M’bukhu la Ezekieli mutu 23, Ohola ndi Oholiba ophiphiritsira analongosoledwa kukhala alongo achisembwere. Ufumu wa mafuko khumi wa Israyeli unaimiridwa ndi Ohola, pamene kuli kwakuti Oholiba anatanthauza ufumu wa mafuko aŵiri wa Chiyuda. M’kukambitsirana akazi ophiphiritsira amenewa, Nsanja ya Olonda ya September 15, 1988, inanena pa tsamba 21 kuti:
“Chifukwa cha kulondola njira yolakwa kwambiri kuposa mkulu wake [Ohola, kapena Israyeli], Oholiba (Yuda) anavutika ndi tsoka la mtundu pa manja a Chibabulo mu 607 B.C.E. Ana ake anagwa ndi lupanga kapena anatengedwa ukapolo, ndipo iye ananyazitsidwa pakati pa amitundu. Mofanana ndi Ohola ndi Oholiba, Chikristu cha Dziko chikuchita chigololo chauzimu, chimo pamaso pa Mulungu amene chimadzinenera kumlambira. Chiprotesitanti, limodzi ndi magulu ake ambirimbiri, chadzidetsa icho chokha ndi malonda ndi mphamvu za ndale zadziko ngakhale moipirako kuposa mlongo wake wamkulu, Chiroma Katolika. Chotero, Yehova adzawona ku icho kuti Chikristu cha Dziko chonse chawonongedwa.”
Kuyambira ndi Msonkhano wa pa Nicaea mu 325 C.E., Wolamulira Constantine anayambukitsa chiphunzitso cha boma lachikunja la Chiroma ndi mpatuko Wachikristu ndipo anakhala mtsogoleri wa Tchalitchi cha Chikatolika chatsopano. Tchalitchi cha Roma Katolika mwakutero chingapeze kukhalapo kwake ku zana lachinayi la Nyengo yathu Ino. Chiprotesitanti chinali ndi kuyambika kwake m’Kukonzedwanso kwa zana la 16. Mwakutero, popeza kuti Ohola (Israyeli) anali wamkulu kuposa Oholiba (Yuda), Nsanja ya Olonda molondola inatcha Chiroma Katolika kukhala mlongo wamkulu wa Chiprotesitanti.
Komabe, nchifukwa ninji chinganenedwe kuti “Chiprotesitanti . . . chadzidetsa icho chokha ndi mphamvu za chuma ndi ndale zadziko mokulira kuposa mlongo wake wamkulu, Chiroma Katolika”? Chifukwa chakuti zenizeni zimayenderana ndi ulosi, womwe umanena kuti: “Pamene mng’ono wake Oholiba anachiwona, anavunda ndi kuwumirira kwake koposa iyeyo; ndi zigololo zake zidaposa zigololo za mkulu wake.”—Ezekieli 23:11.
Monga mbali za Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, ponse paŵiri Chikatolika ndi Chiprotesitanti zakhala zodziloŵetsa mwakuya mu mbali za chuma ndi ndale zadziko lino. (Chibvumbulutso 17:1-6; 18:1-19) Zowona, gulu limodzi la Chiprotesitanti lokha lingakhale ndi chisonkhezero chochepera kuposa Tchalitchi cha Roma Katolika champhamvu. Koma matchalitchi ochulukira a Chiprotesitanti ataikidwa pamodzi amapambana Tchalitchi cha Chikatolika chomwe chiri m’mphamvu ndi chisonkhezero. Mwachitsanzo, Chiprotesitanti chimapereka chisonkhezero champhamvu m’maiko otchuka ena okhala ndi maindastri, chokhala ndi atsogoleri a chipembedzo a Chiprotesitanti akumafunafuna malo a ntchito apamwamba a ndale zadziko. Chotero iyi ndi njira imodzi mu imene Chiprotesitanti, chokhala ndi magulu ake ochulukira, chadziipitsa icho chokha ngakhale kuposa Chikatolika.
Mu njira inanso, ngakhale kuli tero, Chiprotesitanti “chasonyeza chikhumbo chake cha chisembwere movunda” ndipo chiri cha liwongo kwambiri kuposa Chikatolika. Tero motani? Chabwino, Kukonzedwanso kunapatsa Chiprotesitanti chiyembekezo ndi kuyang’ana mtsogolo kwa kuwunikira kokulira kwauzimu. M’chenicheni, okonzanso ena anapanga magulu otsimikizirika ndi odziŵika m’chiyang’anirochi. Koma pamene chirichonse chinanenedwa ndi kuchitidwa, ziphunzitso zosakhala za m’malemba zoterozo zonga Utatu, kusafa kwa moyo wa munthu, ndi moto wa helo zinapitiriza mosasintha pakati pa Aprotesitanti. Mofanana ndi Akatolika, iwo apezedwanso aliwongo la kudziloŵetsa m’kulambira zolengedwa ndi kuika miyambo ya anthu m’malo a chowonadi cha Baibulo.—Mateyu 15:1-9; 23:9, 10.
Cha chikondwerero m’chiyang’aniro cha ichi chiri chimene chinalongosoledwa mu Vindication, Bukhu Loyamba, kumbuyoko m’chaka cha 1931. Pa tsamba 309, chofalitsidwa cha Watch Tower chimenechi (tsopano chosakhala m’sitoko) chinanena ponena za Ezekieli 23:11-13 kuti: “‘Chipembedzo cholinganizidwa’ cha Chiprotesitanti chinawona mmene Chikatolika cha Chiroma chinadzidetsera icho chokha ndi mphamvu za chuma ndi ndale zadziko lino, ndipo chinanena zochulukira motsutsana ndi Akatolika kaamba ka chifukwa chimenecho; koma kenaka Chiprotesitanti chinapitirizabe ndipo mosabisa chinachita mofananamo, ndipo ngakhale moipirako. . . . Onsweo atenga njira yofananayo; koma Chiprotesitanti chinakhala ndi kuwunikira kokulira kuposa Chiroma, ndipo chotero chiri cha liwongo koposa.”
[Chithunzi patsamba 30]
Constantine anayambukitsa Chikristu cha mpatuko ndi chiphunzitso cha Chiroma cha akunja, mwakutero kukhala wotsogolera wa Tchalitchi cha Chikatolika chatsopano
[Mawu a Chithunzi]
The Metropolitan Museum of Art, Bequest of Mrs. F. F. Thompson, 1926. (26.229)