Yehova Wandichirikiza Ine monga Bwenzi
Monga momwe yasimbidwira ndi Maria Hombach
MONGA mtsikana wam’ng’ono wa zaka zisanu nchimodzi, ndinaphunzira pa sukulu nyimbo yamwambo wa ku Germany yokoma yakuti: “Kodi ukudziŵa ndi nyenyezi zingati zimene ziri m’mlengalenga mobiriŵira? . . . Mulungu, Ambuyeyo, waziŵerenga zonse, osati ngakhale imodzi isoŵeka . . . Adziŵa iwenso ndipo akukonda kwambiri.” (Yotembenuzidwa kuchokera mu Chigerman.) Ndinali kuimba iyo tsiku lina pamene amayi anga ananena kuti: “Iye amakudziŵa ndi kukukonda nawenso.” Kuchokera pa nthaŵi imeneyo kumka mtsogolo, Mulungu anakhala monga bwenzi kwa ine. Ndinagamulapo kumukonda iye nanenso. Chimenechi chinali Nkhondo ya Dziko ya I isanachitike pamene tinkakhala mu Bad Ems pa mtsinje wa Lahn.
Zaka khumi ndi zisanu mphambu ziŵiri pambuyo pake, mkati mwa tchuthi mu 1924, ndinakumana ndi mtsikana wa msinkhu wanga. Iye anali mmodzi wa Ophunzira Baibulo, lerolino odziŵika monga Mboni za Yehova. Kwa milungu inayi, tinadzutsa kukambitsirana kwamphamvu pa chipembedzo. Kenaka nkhani ya “helo” inabwera. “Sungaike mphaka wamoyo mu uvuni yotentha, kodi ungatero?” iye anafunsa tero. Chimenecho chinandikantha monga bingu, ndipo ndinazindikira kuti ndinanyengedwa mwachisoni. Tsopano ndikaphunzira zonse ponena za Mulungu—chimene iye kwenikweni ali, m’chenicheni, chirichonse chimene ndinafuna kudziŵa ponena za iye chiyambire pamene ndinali mwana!
Kwa ine chinali ngati kupeza “chuma chobisika m’munda.” (Mateyu 13:44) Nditabwerera kunyumba, ndinathamangira motenthedwa maganizo kwa anansi, mtima wanga ukung’ambika ndi kufuna kugawana zinthu zatsopano zophunziridwazo. Mwamsanga pambuyo pake, ndinasamukira ku tauni ya kum’mwera kwa Germany ya Sindelfingen, kumene gulu la chifupifupi Ophunzira Baibulo 20 linkakhala. Ndinagwirizana nawo mwachangu m’ntchito yatsopano yolengeza imeneyi kuchokera kunyumba ndi nyumba.
Nthaŵi yoyamba pamene ndinamva ponena za utumiki wa upainiya munali mu 1929 mkati mwa nkhani yoperekedwa ndi mbale mtumiki woyendayenda. Iye anafunsa amene akakhala ofunitsitsa kukhala mpainiya. Ine pandekha ndinatukula dzanja langa. Panalibe ma ngati ndi ma koma kwa ine. “Ndine pano; munditumize ine,” mtima wanga unatero.—Yesaya 6:8.
Ndinasiya ntchito yanga ya mu ofesi ndipo pa October 1, 1929, ndinayamba utumiki wa upainiya wapadera, monga mmene ukutchedwera lerolino, kum’mwera cha kumadzulo kwa Germany. Mu Limburg, mu Bonn, pa maboti aakulu a mitundu yonse mu doko la Cologne, ndi m’malo ena, mofulumira ndi mowoloŵa manja tinafesa mbewu za chowonadi m’mkhalidwe wosindikizidwa.—Mlaliki 11:1.
Kukumanizana ndi Ubwenzi wa Mulungu
Pamene Adolf Hitler anakhazikitsa ulamuliro wake wotsendereza ufulu mu Germany mu 1933, ndinafunikira kuleka utumiki wa upainiya ndi kubwerera ku Bad Ems. Aulamuliro mwamsanga anapeza kuti sindinavote m’masankho. Masiku aŵiri pambuyo pake, apolisi angapo anabwera kufufuza chipinda changa. Woimirira wokha m’ngondya imodzi unali mtanga wotairamo zinyalala mu umene, kokha kanthaŵi kang’ono pasadakhale, ndinali nditatairamo makeyala anga onse a Mboni zinzanga. Panalibe nthaŵi yotsala yokachotsamo zinyalalazo! Apolisiwo anafufuza kotheratu chinthu chirichonse—kusiyapo mtanga umenewu.
Ndinayamikira chotani nanga kuti mbale wanga Anna, pa nthaŵi imeneyo, nayenso analandira ubwenzi ndi Mulungu wowona! Pamodzi, mu 1934, tinasamukira ku tauni ya Freudenstadt ndipo kumeneko mosamala tinayamba kufalitsa mabukhu a Baibulo. Kamodzi, mkati mwa tchuthi, tinakhoza kupanga kuchezera kwamwadzidzidzi ndi sitima ku tauni yakwathu ya Bad Ems, mofulumira kufalitsa bokosi lathunthu la mabroshuwa 240, ndipo kenaka tinazimiririka. Kuvutitsa kwa a Gestapo mu Freudenstadt kunatikakamiza kusamukira ku mzinda wina, ndipo mu 1936 tinapita ku Stuttgart. Kumeneko, ndinafunafuna chigwirizano ndi kayendetsedwe kathu kakabisira—ndipo mosataya nthaŵi ndinapatsidwa “ntchito” yoichita. Mokhazikika ndinalandira mapostcard a zithunzi okhala ndi moni. M’chenicheni, iwo anali mauthenga obisidwa. Ntchito yanga inali kuwabweretsa iwo ku malo a mseri mu mzindawo. Kotero kuti ndisaike m’ngozi ntchitoyi, ndinauzidwa kusafalitsanso mabukhu alionse. Zonse zinayenda bwino kufikira mu August 1938.
Tsiku lina, ndinalandira kardi yondilangiza kukaimirira kutsogolo kwa tchalitchi chodziŵika bwino pa madzulo ena. Kumeneko ndikalandira chidziŵitso chowonjezereka. Ndinapita ku malo okumanirawo. Kunali mdima wa ndiweyani. Mwamuna wina anazidziŵikitsa iyemwini monga Julius Riffel. Limeneli, ndinadziŵa, kuti linali dzina la mbale wokhulupirika yemwe anagwira ntchito mwa kabisira. Iye mwamsanga anandiwuza kupanga ulendo wopita ku Bad Ems pa deti linalake kotero kuti ndikakumane ndi winawake. Iye mwamsanga anapita.
Ngakhale kuli tero, pa pulatiformu mu Bad Ems, kokha m’Gestapo anali kundiyemekeza ine. Kodi nchiyani chinalakwika? Mwamunayo kutsogolo kwa tchalitchi—m’chenicheni yemwe kale anali mbale wochokera ku Dresden, Hans Müller, yemwe anadziŵa chirichonse ponena za ntchito ya kabisira mu Germany ndipo anali atayamba kugwirizana ndi a Gestapo—anali atanditchera msampha. Koma icho sichinagwire ntchito. Mwamsanga chisanachitike, amayi anga anali atandidziŵitsa kuti iwo anali atavutika ndi stroke, ndipo ine, m’kuyankha, ndinalonjeza kuwachezera iwo mu Bad Ems pa deti linalake. Ichi mwachimwemwe chinawombana ndi “ntchitoyo,” ndipo makalata athu anapereka pothaŵira pa kuzengedwa mlandu kwanga kwa pambuyo pake. Kukudabwitsidwa kwanga, ndinamasulidwa. Inde, mu February 1939, pambuyo pa miyezi isanu ndi theka ya kubindikiritsidwa, ndinali womasuka kachiŵirinso!
Kuvomereza ku Ubwenzi Wake
Ndithudi, sindinakonzekere kukhala wosakangalika, makamaka popeza kuti abale ambiri koposa anali kuvutika m’misasa yachibalo kapena anali pansi pa kumangidwa kwina kulikonse.
Pambuyo pakuti abale athayo a ku Germany anamangidwa ndi thandizo la Müller, Ludwig Cyranek anatenga mbali ya kugaŵira chakudya chauzimu. Mbale ameneyu, poyambapo wogwira ntchito pa Beteli mu Magdeburg, anali atangomasulidwa kuchokera ku kubindikiritsidwa, ndipo iye anandichezera mu Bad Ems. “Bwera, Maria! Tiye tigwirebe ntchito,” iye anatero. Ananditenga kubwerera ku Stuttgart, kumene ndinatenga ntchito yakuthupi. Ntchito yanga yeniyeni, ngakhale kuli tero, kuyambira mu March 1939, inali ija ya kugawira masutikesi odzaza ndi makope olembedwanso a magazini a Nsanja ya Olonda mu Stuttgart ndi malo ozungulira. Mboni zina molimba mtima zinagawanamo mu ntchito imeneyi.
Pa nthaŵiyo, Mbale Cyranek anakwaniritsa mbali yonse ya kumpoto cha kum’mawa kwa dzikolo. Popeza kuti nyumba za Mboni zinali kuyang’aniridwa, iye anafunikira kuyenda ndi kuchenjera kokulira ndipo nthaŵi zina ngakhale kugona m’nkhalango. Masitima osaimaima anam’bweretsa iye nthaŵi ndi nthaŵi ku Stuttgart, kumene iye analankhula kwa ine maripoti apadera onena za mkhalidwe wathu mu Germany. Ndinalemba makalata a nthaŵi zonse, ndikumaika mauthenga amenewa pakati pa mizera m’kulemba kosawoneka ndipo kenaka kuwatumiza iwo, mwa keyala yachiphamaso, ku Beteli ya Netherlands.
Chachisoni kuchinena, mbale wachiŵiri anatembenuka kukhala wopereka m’chiyembekezo cha kupulumuka kubindikiritsidwa. Chaka chimodzi pambuyo pake, iye anapereka magulu mu Stuttgart ndi kwina kulikonse kwa a Gestapo. Pa February 6, 1940, ife tinamangidwa. Ludwig Cyranek anapita kunyumba ya Müller mu Dresden—akulingalira kuti Müller anali adakali Mboni inzathu—ndipo anagwidwa kumeneko. Mbale Cyranek pambuyo pake anaweruzidwira ku imfa ndipo anadulidwa mutu pa July 3, 1941.a
Adani athu tsopano anakhulupirira kuti iwo anapuwalitsa ntchito yathu yonse mu Germany. Koma makonzedwe anali atapangidwa kale kutsimikizira kuti madzi a chowonadi anapitirizabe kuyenda, ngakhale kuti anachepetsedwa ku dontho. Mwachitsanzo, gulu mu Holzgerlingen linakhoza kukhalabe lokangalika kufikira mapeto a nkhondo mu 1945.
Iye Samataya Konse Mabwenzi Ake
Tonse aŵiri Anna ndi ine, limodzi ndi alongo okhulupirika ena, tinatumizidwa ku ndende ya Stuttgart. Kaŵirikaŵiri ndinkamva andende akumenyedwa. Kubindikiritsidwa kwa wekha wopanda chochita chirichonse kuli chokumana nacho choipitsitsa. Koma popeza sitinaphonye konse misonkhano Yachikristu ndipo tinali chikhalirebe achichepere, tinkakhoza kukumbukira chifupifupi nkhani zonse za Nsanja ya Olonda. M’kupita kwa nthaŵi, chikhulupiriro chathu chinapitirizabe kulimba, ndipo tinali okhoza kupirira.
Tsiku lina, amuna a Gestapo aŵiri anabwera kuchokera ku Dresden kudzatenga wandende mnzanga Gertrud Pfisterer (tsopano Wulle) ndi ine kaamba ka kudzidziŵikitsa. Kaŵirikaŵiri, andende analoledwa kuyenda kokha mu sitima yoyenda pang’onopang’ono, yomwe inatenga masiku. Koma kwa ife chipinda chonse chinasungidwa pa sitima yosaimaima, mosasamala kanthu za chenicheni chakuti iyo inadzala mopambanitsa. “Inu muli ofunikira kwambiri kwa ife. Sitikufuna kukutayani,” zinalongosola tero ndunazo.
Mu Dresden, m’Gestapo anayang’anizana nane ndi wopereka wachitatu wochokera pakati pa mathayo athu. Ndinazindikira kuti chinachake chinalakwika, chotero ndinakhala chete, osati ngakhale kumpatsa moni. Kenaka ndinabweretsedwa pamaso m’pamaso ndi mwamuna wamtali, wamkulu thupi wovala yuniformu ya msilikari: woperekayo Müller, yemwe ndinakumana naye kutsogolo kwa tchalitchi. Ndinasiya chipindacho popanda kunena liwu lirilonse. M’Gestapoyo sanapeze chirichonse kuchokera kwa ine.
Opereka amenewa aliyense anabwera ku mathedwe oipa. Monga momwe Anazi ananenera, iwo anakonda kuperekako osati woperekayo. Onse atatu anatumizidwa ku gulu lomenya nkhondo ku malire akum’mawa ndipo sanabwerere konse. Chinatembenuka kukhala chosiyana chotani nanga kaamba ka awo omwe sanaleke konse ubwenzi ndi Mulungu ndi anthu ake! Ambiri a okhulupirika, pakati pa iwo Erich Frost ndi Konrad Franke, amene anavutika kwambiri chifukwa cha Ambuye ndipo pambuyo pake kukhala oyang’anira a nthambi mu Germany, anabwerera amoyo kuchokera ku ng’anjo yamoto ya kuzunzidwa.b
A Gestapo mu Stuttgart—onyada kwambiri kaamba ka “kugwira” kwawo—anafunsa anzawo mu Dresden mu May 1940 kutibweza. Milandu yathu inafunikira kuzengedwa kum’mwera kwa Germany. Koma a Gestapo kumpoto ndi kum’mwera mwachiwonekere sanali omvana, chotero ofesi ya ku Dresden inakana, pamene kuli kwakuti aja ochokera ku Stuttgart anabwera ndi kutiguza kuthaŵa nafe mwaumwini. Nchiyani tsopano? Kuyenda m’galimoto kupita ku sitesheni kunakhala ulendo wokondweretsa m’mphepete mwa mtsinje wa Elbe; m’ndende zathu sitinawone mitengo yobiriŵira ndi mlengalenga wobiriŵira modera kwa nyengo yaitali. Monga kale, chipinda chonse cha sitima chanasungidwa kaamba ka ife tokha, ndipo tinaloledwa ngakhale kuyimba nyimbo za Ufumu. Pamene tinasintha masitima, tinalandira chakudya m’chipinda chodyera pa sitesheni. Tangolingalirani, m’mawa tinali titadya kokha chidutswa chowuma cha mkate, ndipo tsopano ichi!
Mlandu wanga unapita ku bwalo lamilandu mu Stuttgart pa September 17, 1940. Mwa kulemba ndi kutumiza makalata a Ludwig Cyranek, ndinali nditadziŵitsa anthu okhala m’maiko akutali ponena za ntchito yathu yakabisira ndi kuzunzidwa kwathu. Kumeneku kunali kuwukira boma kowopsya, komwe kunali ndi chilango cha imfa. Icho chotero chinawoneka ngati chozizwitsa kuti ine, wamlandu wamkulu mu Stuttgart, ndinaweruzidwa kokha ku zaka zitatu ndi theka za kubindikiritsidwa ndekha! Mosakaikira, mkulu wa Gestapo wotchedwa Schlipf, yemwe anatiyang’anira mwachiyanjo ndi amene chikumbumtima chake chinamvutitsa, anagwiritsira ntchito chisonkhezero chake. Iye nthaŵi ina anali atatchula kuti sakagona chifukwa cha ife “atsikana.” Mu Dresden sindikanalekedwa mopepuka chotero.
Kupindula Kuchokera ku Ubwenzi Wokhalitsa
Ngakhale kuti chakudya m’ndende sichinali choipa monga cha m’misasa yachibalo, ndinawonda ndipo potsirizira ndinali kokha khungu ndi mafupa. Zaka za 1940 mpaka 1942 zinapita, ndipo kaŵirikaŵiri ndinaganizira kuti: ‘Pamene kumangidwa kwako kwatha, adzakuika mu msasa wachibalo kumene udzakhoza kukhala ndi gulu la alongo ndipo sudzakhalanso wekha.’ Ndinadziŵa zochepera.
Alonda anali odabwitsidwa kotheratu pamene pempho kaamba ka kumasulidwa kwanga, lofunsiridwa ndi makolo anga Achikatolika, linavomerezedwa. (Ine kaŵirikaŵiri ndinakana kupanga kufunsira kwaumwini koteroko.) Pamene kunali kwakuti akhulupiriri anzanga anaponyedwa m’misasa yachibalo, ine—woweruzidwa kaamba ka kuwukira boma kowopsya ndipo wosagonjera konse—ndinafunikira kuchoka ndi kupita mopepuka chotero! Chotero ndinali waufulu kachiŵirinso mu 1943 ndipo chotero kukhala m’malo, kugwiritsira ntchito chisamaliro chachikulu, kutenga zinthu za teokratiki kuchokera ku Holzgerlingen. Pambuyo pa kuzijambula izo, ndinazibisa pakati pa makoma a thermos flask yodzaza ndi kofi ndi kutengera iyo kwa abale okhala m’mphepete mwa Mtsinje wa Rhine ndi m’chigawo cha Westerwald cha Germany. Kuyambira pa nthaŵi imeneyo mpaka mapeto a nkhondo, ndinali wokhoza kugwira ntchito mosasokonezedwa. Pambuyo pake ndinaphunzira kuti akuluakulu a polisi aubwenzi omwe analandira zidziŵitso zotivumbula motsutsana nafe sanapereke izo kwa Gestapo.
Ndipo itapita 1945? Ndinali ndi chikhumbo cha kuchita upainiya kachiŵirinso mwamsanga monga mmene kukanathekera. Mosayembekezera kwenikweni chinabwera chiitano chabwino koposa chomwe sindinalandire ndi kalelonse. M’maloto anga ndinali ndisanalingalirepo mpang’ono ponse za kuitanidwa kukagwira ntchito pa Beteli mu Wiesbaden!
Ndipo chiyambire March 1, 1946, ndakhala ndiri kumeneko, mu Beteli (tsopano mu Selters/Taunus). Kwa zaka zambiri ndinakhala ndi chisangalalo cha kugwira ntchito mu ofesi yoyang’aniridwa ndi woyang’anira nthambi wakale Konrad Franke. Ndinagwiranso ntchito mwachisangalalo m’madipartimenti ena, mwachitsanzo, m’chipinda chochapiramo. Ngakhale lerolino, pa msinkhu wa 87, ndimagwirabe ntchito kumeneko maora angapo pa mlungu kupinda mataulo. Ngati inu munachezerapo konse Beteli yathu, mwinamwake tinawonanapo.
M’kupita kwa nthaŵi, ndinali ndi mwaŵi wa kuthandiza anthu ambiri kulandira chowonadi, kuphatikizapo amayi anga ndi mlongo wina wakuthupi. Mawu a amayi, “Iye amakudziŵa ndi kukukonda,” ndawapeza kukhala owona, monga momwe analiri mawu a wamasalmo, “Iye adzakugwirizitsa.” (Salmo 55:22) Chakhala chosangalatsa chotani nanga kukonda Yehova pamene kuli kwakuti ndikuchirikizidwa ndi iye monga bwenzi!
[Mawu a M’munsi]
a Onani 1974 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 179-80.
b Onani Nsanja ya Olonda, April 15, 1961, masamba 244-9, ndi March 15, 1963, masamba 180-3 (Chingelezi).