Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 6/1 tsamba 15-20
  • Khalani Audongo M’maganizo ndi Thupi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalani Audongo M’maganizo ndi Thupi
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Udongo wa Maganizo
  • Ukhondo Waumwini
  • Nyumba ndi Magalimoto Audongo
  • Udongo Popereka Nsembe Zauzimu
  • Audongo ndi Aukhondo kaamba ka Utumiki wa m’Munda ndi Misonkhano
  • Mulungu Amakonda Anthu Oyera
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Anatiyeretsa Kuti Tichite Ntchito Zokoma
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Yehova Amafuna Kuti Anthu Ake Akhale Oyera
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Atumiki a Mulungu Ayenera Kukhala Oyera
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 6/1 tsamba 15-20

Khalani Audongo M’maganizo ndi Thupi

‘‘Mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, [yolandirika kwa, “NW”] Mulungu.’’​—AROMA 12:1.

1. Mogwirizana ndi mtumwi Paulo, nchifukwa ninji udongo wa maganizo ndi thupi uli woyenerera?

MUNTHU yemwe amakhumba kutumikira Mulungu woyera Yehova ayenera kukhala woyera mwauzimu ndi mwamakhalidwe. Mwanzeru, ichi chimatanthauzanso kukhala waudongo m’maganizo ndi thupi. Dongosolo lamakono la zinthu pokhala chomwe ilo liri, anthu otuluka mu ilo ndi cholinga chofuna kutumikira Yehova ayenera kupanga masinthidwe osati kokha m’zizoloŵezi zawo za kuganiza koma kaŵirikaŵiri m’zizoloŵezi zawo zaumwininso. Mtumwi Paulo analemba kwa Akristu mu Roma kuti: “Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifuno za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, [yolandirika kwa, NW] Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyera. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chiri chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:1, 2) Nchiyani chimene udongo wa maganizo ndi thupi umaphatikizapo?

Udongo wa Maganizo

2. Ndimotani mmene maso athu ndi mtima zingatipangitsire ife kuloŵa mu mkhalidwe woipitsitsa, ndipo nchiyani chimene chiri choyenerera kuti tipeŵe chimenechi?

2 Ngakhale Chilamulo chisanaperekedwe, Yobu wokhulupirika anasonyeza kuti maso athu ndi mtima zingatipangitse kuchita mkhalidwe woipitsitsa ngati sitizilamulira. Iye ananena kuti: “Ndinapangana ndi maso anga, Potero ndipenyeranji namwali? Ngati mtima wanga wakopeka ndi mkazi, . . . pakuti icho ndi choipitsitsa, ndicho mphulupulu yoyenera oweruza anene mlandu wake.” (Yobu 31:1, 9-11) Ngati tiri ndi maso owunguzawunguza ndi mtima wosakhazikika, tifunikira chilango cha maganizo, “chilango chimene chimapereka chidziŵitso.”​—Miyambo 1:3, NW.

3, 4. (a) Nchiyani chimene chitsanzo cha Davide ndi Bateseba chimasonyeza, ndipo nchiyani chomwe chiri choyenerera ndi cholinga chofuna kusintha zizoloŵezi zoipa za kuganiza? (b) Nchifukwa ninji akulu Achikristu afunikira kukhala osamala mwapadera?

3 Maso a Mfumu Davide anamtsogolera iye m’kuchita chigololo ndi Bateseba. (2 Samueli 11:2, 4) Chitsanzo chimenechi chimasonyeza kuti ngakhale amuna omwe amagwiritsiridwa ntchito motchuka ndi Yehova angagwere mu chimo ngati iwo salanga maganizo awo. Chingatenge kuyesayesa kwamphamvu kuti tisinthe zizoloŵezi zathu za kuganiza. Kuyesayesa koteroko kuyenera kutsagana ndi pemphero lachangu kaamba ka thandizo la Yehova. Pambuyo pa kulapa chimo lake ndi Bateseba, Davide anapemphera kuti: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; Mukonze mzimu wokhazikika mkati mwanga.”​—Salmo 51:10.

4 Akulu Achikristu mwachindunji ayenera kukhala osamala kusasunga zikhumbo zolakwika zomwe zingawatsogolere iwo ku chimo lalikulu. (Yakobo 1:14, 15) Kwa mkulu Wachikristu Timoteo, Paulo analemba kuti: “Koma chitsiriziro cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m’chikumbumtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga.” (1 Timoteo 1:5) Chikakhala chinyengo motsimikizirika kwa mkulu kusamalira mathayo ake auzimu pamene akulola diso lowunguzawunguza kubweretsa mumtima mwake malingaliro a kuchita zopanda udongo.

5. Nchiyani chimene chiyenera kupeŵedwa ndi cholinga cha kusungirira udongo wa maganizo?

5 Tonsefe monga Akristu tiyenera kuchita zomwe tingathe kukhala audongo m’maganizo. Ichi chimatanthauza kupeŵa akanema aliwonse, maprogramu a pa TV, kapena kuŵerenga nkhani zomwe zikakhala ndi chisonkhezero choipitsa pa kuganiza kwathu. Ukhondo wamaganizo umaphatikizapo kuyesayesa kwa chikumbumtima kukhala pa zinthu zomwe ziri “zowona, . . . zolungama, . . . zoyera.” Mtumwi Paulo akuwonjezera kuti: “Ngati kuli chokoma china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.”​—Afilipi 4:8.

Ukhondo Waumwini

6. (a) Perekani zitsanzo kuchokera m’bukhu la Levitiko zosonyeza kuti ukhondo waumwini limodzinso ndi waunyinji unafunikira mu Israyeli. (b) Nchiyani chimene chinali chifuno cha malamulo oterowo?

6 Chanenedwa kuti “udongo uli wotsatira ku umulungu.” Zowona, munthu yemwe ali waudongo mwamakhalidwe ndi kuthupi sangakhale waumulungu. Koma munthu waumulungu ayenera, moyenerera, kukhala waudongo mwamakhalidwe ndi kuthupi. Chilamulo cha Mose chinapereka malangizo osamalitsa pa kuyeretsa nyumba zoyambukiridwa ndi pa kusamba kwaumwini m’nkhani zosiyanasiyana za zopanda udongo. (Onani Levitiko, mitu 14 ndi 15.) Aisrayeli onse anafunikira kudzitsimikizira iwo eni kukhala oyera. (Levitiko 19:2) Chofalitsidwa cha Insight on the Scriptures chimalongosola kuti: “Malamulo a kadyedwe, kuyeretsa, ndi malamulo a makhalidwe amene Mulungu anapatsa [Aisrayeli] anali zokumbutsa zokhazikika kwa iwo ponena za kupatulika kwawo ndi chiyero cha Mulungu.”​—Volume 1, tsamba 1128.

7. Nchiyani chomwe chiri chowona ponena za Mboni za Yehova monga anthu, koma kodi nchiyani chimene oyang’anira oyendayenda ena achitira ripoti?

7 Pamene kuli kwakuti Mboni za Yehova monga anthu ali audongo m’chidetso chirichonse cha chipembedzo chonyenga cha Chibabulo ndipo samalekerera mkhalidwe wa chidetso pakati pawo, maripoti ochokera kwa oyang’anira oyendayenda akusonyeza kuti anthu ena amanyalanyaza ukhondo ndi udongo waumwini. Ndimotani mmene tingatsimikizire kuti tirinso audongo mu nkhaniyi? Chitsanzo chabwino kaamba ka nyumba zonse Zachikristu chiri Beteli, dzina limene limatanthauza “Nyumba ya Mulungu.”

8, 9. (a) Ndi uphungu wotani womwe umaperekedwa ku ziŵalo zonse zatsopano za banja la Beteli? (b) Ndi maprinsipulo otani otsatiridwa m’Nyumba za Beteli amene ayenera kulamulira banja lirilonse Lachikristu?

8 Pamene munthu akhala chiŵalo cha banja la Beteli pa malikulu a Watch Tower Society kapena pa iriyonse ya nthambi zake kuzungulira dziko, iye amapatsidwa broshuwa yokonzedwa ndi Bungwe Lolamulira. Chofalitsidwachi chimalongosola chomwe chikuyembekezeredwa kwa iye m’njira ya chizoloŵezi cha ntchito ndi chizoloŵezi chaumwini. Pansi pa mutu wakuti “Kusamalira Chipinda ndi Udongo,” iyo imalongosola kuti: “Moyo wa pa Beteli umaitanira kusungirira miyezo yapamwamba yakuthupi, makhalidwe ndi yauzimu. Aliyense pa Beteli ayenera kukhala ndi nkhaŵa ya kudzisunga iyemwini ndi chipinda chake zaudongo. Ichi chimathandizira ku umoyo wabwino. Palibe chifukwa cha kukhalira walitsiro kwa aliyense. Kali kachitidwe kabwino kusamba tsiku lirilonse. . . . Kusamba isanafike nthaŵi yakudya kuli kofunika ndipo kumayembekezeredwa kwa onse. M’kulingalira mnzanu wa m’chipinda ndi woyeretsa zipinda, mosambira kapena tub muyenera kuyeretsedwa pambuyo pa kugwiritsiridwa ntchito kulikonse.”

9 M’nyumba za Beteli, zimbudzi zimasungidwa zaudongo mosamalitsa, ndipo makonzedwe anapangidwa kutheketsa awo ozigwiritsira ntchito kusamba manja awo mwamsanga atangotha. Ziŵalo za banja zimayembekezeredwa kusiya chimbudzi chiri chaudongo pambuyo pa kugwiritsira ntchito, chomwe chimatanthauza kufufuza ndi kuwona kuti chimbudzi chagujumulidwa mwaubwino. Ichi chimasonyeza kulingalira kaamba ka wogwiritsira ntchito wotsatira kapena woyeretsa zipinda. Kodi maprinsipulo okoma achikondi oterewa, sayenera kulamulira nyumba Yachikristu iriyonse?

10. (a) Nchifukwa ninji mosambira mokometseredwa monkitsa simuli moyenerera ndi cholinga cha kudzisunga inumwini ndi ana anu kukhala audongo? (b) Ndi malamulo otani mu Israyeli omwe anali oyenerera ku umoyo wabwino, ndipo ndi phunziro lotani limene anthu a Yehova lerolino angaphunzire kuchokera mu ichi?

10 Mwachibadwa, mikhalidwe imasiyana kuchokera ku dziko ndi dziko. M’malo ena, nyumba ziribe zosambira zonga bathtub kapena ngakhale shower. Kulankhula mwachisawawa, ngakhale ndi tero, amuna ndi akazi Achikristu angapeze sopo yokwanira ndi madzi kusunga matupi awo kukhala audongo ndi kuwona kuti ana awo ali audongo.a Nyumba zambiri kuzungulira dziko siziri zolumikizidwa ku dongosolo lotayira zonyansa. Koma kutaya zonyansa kungachitidwe mwachisungiko mwa kufotsera, monga momwe zinafunikira pakati pa Aisrayeli ngakhale m’misasa yankhondo. (Deuteronomo 23:12, 13) Pambali pa ichi, malamulo a Yehova olamulira moyo wa mumsasa anaitanira kuchapa zovala kwakaŵirikaŵiri ndi kusamba, kufufuza ndi kuchiritsa kwa nthenda kwamsanga, kusamalira bwino mitembo, ndi kusungirira zoperekera zakudya ndi madzi zaudongo. Malamulo onsewa anathandizira ku umoyo wa mtunduwo. Kodi anthu a Yehova lerolino ayenera kukhala aukhondo wochepera m’zizoloŵezi zawo zaumwini?​—Aroma 15:4.

Nyumba ndi Magalimoto Audongo

11. (a) Nchiyani chomwe chiyenera kukhala chowona ponena za ngakhale nyumba yosawoneka bwino kwenikweni Yachikristu? (b) Ndi kugwirizana kotani komwe kumafunikira ku ziŵalo zonse za banja la Beteli?

11 Nyumba zathu, ngakhale zikhale zosawoneka bwino chotani, zingakhale za dongosolo ndi zaudongo, koma ichi chimafunikira kugwirizana kwabwino pa mlingo wabanja. Amayi Achikristu adzafuna kuthera nthaŵi yochulukira kumene kuli kothekera pa zinthu zauzimu, kuphatikizapo ntchito yolalikira, chotero safunikira kutaya nthaŵi tsiku lirilonse kuyeretsa za ziŵalo za banja zomwe zinasiya zovala, mabukhu, mapepala, magazini, ndi zina zotero, ziri paliponse. Mu Beteli, ngakhale kuti kuli osamalira zipinda amene amayeretsa, chiŵalo chirichonse cha banja chimayembekezeredwa kuyala kama yake ndi kusiya chipinda chiri chaudongo m’mawa. Tonsefe timayamikira Nyumba zathu za Ufumu ndi Nyumba Zosonkhaniramo zoyera ndi zaudongo. Lolani kuti nyumba zathu nazonso zichitire umboni kuti ndife mbali ya anthu a Yehova audongo ndi oyera!

12, 13. (a) Ndi uphungu wotani womwe waperekedwa ponena za magalimoto ogwiritsiridwa ntchito mu utumiki wa Yehova, ndipo nchifukwa ninji izi siziyenera kukhala zakutha nthaŵi? (b) Ndi chifukwa chauzimu chotani chomwe chiripo kaamba ka kudzisunga audongo mwakuthupi ndi kukhala ndi nyumba ndi magalimoto audongo?

12 Atumiki ambiri a Yehova lerolino amagwiritsira ntchito magalimoto kaamba ka kupita ku misonkhano ndi utumiki wa m’munda. M’maiko ena galimoto yafikira kukhala kwenikweni chinthu chosasiika monga chiwiya chogwiritsira ntchito kutumikira Yehova. Chotero, iyenera kusungidwa yoyera ndi yaudongo, mongadi mmene nyumba yathu iliri. Kukhala otsimikizira, Akristu sangawononge nthaŵi yochulukira kukometsera magalimoto awo m’njira imene anthu a kudziko amachitira. Koma popanda kupita m’kupambanitsa koteroko, atumiki a Yehova ayenera kuyesetsa kusunga magalimoto awo kukhala audongo ndi a dongosolo labwino. M’maiko ena kutsuka galimoto pa malo omwetsera mafuta kuli kosadula ndi kosataya nthaŵi. Ponena za mkati mwa galimoto, mphindi khumi za kuyeretsa ndi kusamalira zingachite zozizwitsa. Akulu ndi atumiki otumikira, makamaka, ayenera kuyesayesa kukhala chitsanzo m’nkhaniyi, popeza kuti iwo kaŵirikaŵiri amagwiritsira ntchito magalimoto awo kupereka magulu a ofalitsa mu utumiki wa m’munda. Pamene wofalitsa anyamula munthu wokondwerera kumupereka iye ku msonkhano, motsimikizirika sichiri umboni wabwino ngati galimoto iri yauve ndi yosakhala yaudongo.

13 Chotero, ndi zoyesayesa zathu za kukhala audongo kuthupi ndi kukhala ndi nyumba ndi magalimoto audongo ndi aukhondo, timalemekeza Yehova monga ziŵalo za gulu lake laudongo.

Udongo Popereka Nsembe Zauzimu

14. Ndi malamulo otani amene analamulira udongo wa mwambo mu Israyeli, ndipo nchiyani chimene malamulo amenewa amasonyeza?

14 Udongo wa mwambo m’chigwirizano ndi kulambira unali wofunika mu Israyeli, pansi pa chilango cha imfa. Yehova anawuza Mose ndi Aroni kuti: “Motero muzipatula ana a Israyeli kwa kudetsedwa kwawo; angafe m’kudetsedwa kwawo, pamene adetsa kachisi wanga ali pakati pawo.” (Levitiko 15:31) Pa Tsiku la Chitetezero, mkulu wansembe anayenera kusamba thupi lake m’madzi kaŵiri. (Levitiko 16:4, 23, 24) Beseni la mkuwa pa chihema, ndipo pambuyo pake thawale lalikulu la mkuwa pa kachisi, zinapereka madzi kaamba ka ansembe kusambiramo asanapereke nsembe kwa Yehova. (Eksodo 30:17-21; 2 Mbiri 4:6) Bwanji ponena za Aisrayeli mwachisawawa? Ngati anakhala odetsedwa mwa mwambo kaamba ka chifukwa chirichonse, iwo anali kuletsedwa kutengamo mbali m’kulambira kufikira atakwaniritsa zofunikira kaamba ka kuyeretsa. (Numeri 19:11-22) Zonsezi zinagogomezera kuti udongo wa kuthupi uli wofunikira kwa awo olambira Mulungu woyera Yehova.

15. Nchifukwa ninji nsembe za nyama sizirinso zoyenerera, koma kodi ndi mafunso otani omwe akudzutsidwa?

15 Zowona, anthu a Yehova lerolino safunikira kupereka nsembe za nyama pa kachisi ya padziko lapansi. Nsembe pansi pa Chilamulo zaloŵedwa m’malo ndi “chopereka cha thupi la Yesu Kristu, kamodzi, kwatha.” (Ahebri 10:8-10) “[Tima]lambira Atate mu mzimu ndi chowonadi.” (Yohane 4:23, 24) Koma kodi ichi chimatanthauza kuti tiribe nsembe zopereka kwa Mulungu wathu woyera Yehova? Ndipo kodi kuyera sikuli kofunikira kwa ife kuposa mmene zinaliri ndi Aisrayeli?

16. Ndimotani mmene ulosi wa Malaki 3:3, 4 wakwaniritsidwira pa Akristu odzozedwa chiyambire 1918, ndipo ndi nsembe zolandirika zotani zimene angapereke kwa Yehova?

16 Ulosi wa Malaki umasonyeza kuti Akristu odzozedwa pa dziko lapansi mu nthaŵi ya mapeto akayengedwa, kapena kuyeretsedwa, kaamba ka utumiki wa pakachisi. Mbiri yakale imasonyeza kuti kuyenga kumeneku kunayamba mu 1918. Chiyambire 1919 otsalira odzozedwa akhala “akupereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo,” ndipo kupereka mphatso kwawo kuli “kwachiyamikiro kwa Yehova.” (Malaki 3:3, 4) Chotero, iwo ali okhoza “kupereka nsembe zauzimu [zolandirika kwa, NW] Mulungu mwa Yesu Kristu.” (1 Petro 2:5) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Potero mwa iye tipereke chiperekere nsembe ya kuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.”​—Ahebri 13:15.

17. Ngakhale kuti “khamu lalikulu” siliri mbali ya ansembe achifumu, nchifukwa ninji ayenera kukhala audongo mwakuthupi, maganizo, makhalidwe, ndi uzimu?

17 Pamene kuli kwakuti “khamu lalikulu” silinaitanidwe ku utumiki wa pa kachisi wa unsembe mofanana ndi otsalira odzozedwa, iwo “akupereka kwa [Yehova] utumiki wopatulika usana ndi usiku” m’mabwalo a kachisi yauzimu ya padziko lapansi. (Chibvumbulutso 7:9, 10, 15) Chidzakumbukiridwa kuti Aisrayeli osakhala ansembe anafunikira kukhala oyera mwa mwambo kuti agawanemo m’kulambira pa chihema kapena, pambuyo pake, pa kachisi. Mofananamo, khamu lalikulu la nkhosa zina lifunikira kukhala laudongo mwakuthupi, mwa maganizo, mwa makhalidwe, ndi mwauzimu ngati iwo akukhumba kutumikira pa kachisi ndi kugawanamo ndi otsalira ‘kupereka kwa Mulungu nsembe ya chitamando’ mwa kupanga “kulengeza kwapoyera ku dzina lake.”

Audongo ndi Aukhondo kaamba ka Utumiki wa m’Munda ndi Misonkhano

18. Pamene tadziloŵetsa mu ntchito yapoyera yochitira umboni ndi kupezeka ku misonkhano, nchiyani chimene chiyenera kukhala chodera nkhaŵa chathu ponena za udongo waumwini, zovala, ndi nsapato?

18 Kodi ichi chimatanthauzanji m’mikhalidwe yogwira ntchito? Chimatanthauza kuti chikakhala chosayenera kwenikweni ndi chopanda ulemu kwa Yehova kumuimira iye mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, m’makwalala, kapena m’nyumba ya wina ngati sitinali audongo mwakuthupi ndi osavala bwino. Chotero, sitifunikira kukhala osasamala ponena za nkhani zoterozo. Tiyenera kuzipatsa izo chisamaliro chosamalitsa, kotero kuti tichite m’njira yoyenerera atumiki okhala ndi dzina la Yehova. Zovala zathu sizifunikira kukhala za mtengo, koma ziyenera kukhala zaudongo, zabwino, ndi zachikatikati. Nsapato zathu ziyeneranso kukhala mumkhalidwe wabwino ndi zowoneka bwino. Mofananamo, pa misonkhano yonse, kuphatikizapo pa Phunziro la Bukhu la Mpingo, matupi athu ayenera kukhala audongo, ndipo tifunikira kuvala mwaukhondo ndi moyenera.

19. Ndi mapindu auzimu otani omwe amatulukapo kuchokera ku kawonekedwe kathu kaudongo ndi kaukhondo monga atumiki Achikristu?

19 Kawonekedwe kathu kaudongo ndi kaukhondo pamene tadziloŵetsa mu ntchito yochitira umboni ndi pa misonkhano yathu kali njira imodzi “yakukometsera chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu, Mulungu.” (Tito 2:10) Chiri umboni mwa icho chokha. Anthu ambiri asangalatsidwa ndi udongo ndi ukhondo wathu, ndipo ichi chawasonkhezera kumvetsera ku uthenga wathu wonena za zifuno zodabwitsa za Yehova kaamba ka miyamba yatsopano yolungama ndi dziko lapansi latsopano loyeretsedwa.​—2 Petro 3:13.

20. Ndi chipatso chabwino chowonjezereka chotani chomwe chimadza kuchokera m’kukhala kwathu audongo m’maganizo ndi thupi?

20 Pamene dongosolo laudongo latsopano la Yehova likuyandikira pafupi, tonsefe tifunikira kudzisanthula ife eni ndikuwona ngati tifunikira kupanga masinthidwe m’kuganiza kwathu kapena mu zizoloŵezi zathu zaumwini. Paulo analemba kuti: “Ndilankhula manenedwe a anthu, chifukwa cha kufooka kwa thupi lanu; pakuti monga inu munapereka ziŵalo zanu zikhale akapolo a chonyansa ndi a kusayeruzika kuti zichite kusayeruzika, inde kotero tsopano perekani ziŵalo zanu zikhale akapolo a chilungamo kuti zichite chiyeretso.” (Aroma 6:19) Udongo wauzimu ndi udongo wakuthupi umabweretsa zipatso zabwino ngakhale tsopano, “chipatso m’njira ya kuyera, ndipo pamapeto [chidzakhala] moyo wosatha.” (Aroma 6:22) Tiyeni, chotero, tikhale audongo m’maganizo ndi thupi pamene ‘tipereka matupi athu nsembe yamoyo, yoyera, [yolandirika kwa, NW] Mulungu.’​—Aroma 12:1.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka malingaliro ogwira ntchito pa ukhondo pansi pa mikhalidwe yovuta, onani nkhani yakuti “Kukumaniza Chitokoso cha Udongo,” yofalitsidwa mu Galamukani! ya October 8, 1988, masamba 26-29.

Nsonga Zofunika Kukumbukira

◻ Ndimotani mmene maso athu ndi mtima zingatipangitsire ife kudziloŵetsa mu mkhalidwe woipitsitsa?

◻ Ndi mapindu otani amene Aisrayeli analandira pamene anamvera malamulo a Yehova pa ukhondo waunyinji ndi mmodzi ndi mmodzi payekha?

◻ Ndi maprinsipulo otani otsatiridwa m’Nyumba za Beteli amene ayenera kulamulira banja lirilonse Lachikristu?

◻ Ndi liti, makamaka, pamene tiyenera kukhala osamala ponena za kawonekedwe kathu?

◻ Ndi zifukwa zauzimu zotani zimene atumiki a Yehova ali nazo kaamba ka kusunga nyumba zawo ndi magalimoto zaudongo ndi zaukhondo?

[Chithunzi patsamba 17]

“Moyo wa pa Beteli umaitanira kaamba ka kusungirira miyezo yapamwamba yakuthupi, makhalidwe ndi yauzimu”

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi amayi afunikira kuthera nthaŵi yapambali tsiku lirilonse kuyeretsa pambuyo pa ziŵalo za banja zosalingalira?

[Chithunzi patsamba 19]

M’mphindi khumi, zozizwitsa zingachitidwe kuyeretsa mkati mwa galimoto

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena