‘Tidziŵa Kuti Iwo Adzawuka mu Chiwukiriro’
MULUNGU WAMPHAMVUYONSE anapatsa mtundu wa anthu moyo. Iye angabwezeretsenso iwo kwa anthu omwe amwalira. Kuchokera kwa iye, kachiŵirinso, tiri ndi magwero odalirika koposa a chidziŵitso ponena za moyo ndi imfa: Malemba Achihebri ndi Achikristu Achigriki, mbali ziŵiri zimene zimapanga Baibulo. Ilo liri ndi uthenga wozikidwa pa nsonga wakuti ochulukira a omwalira angathe ndipo adzabwereranso.—Yohane 5:28, 29.
Kuti tichitire fanizo, lingalirani cholembedwa cha m’mbiri cha Lazaro wa ku Betaniya, yemwe anali wodziŵika bwino kwa Yesu Kristu. Lazaro anali kudwala, ndipo kenaka anamwalira. Pambuyo pake, Yesu anawuza mlongo wa Lazaro Marita kuti: “Mlongo wako [womwalira] adzawuka.” Mkaziyo anayankha kuti: “Ndidziŵa kuti adzawuka m’kuwuka tsiku lomaliza.” (Yohane 11:23, 24) Inde, iye anadziŵa icho. Chozikidwa pa chidziŵitso chodalirika, iye analibe chikaikiro chakuti mlongo wake wokondedwa Lazaro akabweranso pa “tsiku lomaliza.”
Pamene mukuŵerenga m’cholembera cha m’mbiri mu Yohane mutu 11, mudzapeza tsatanetsatane wa chimene kenaka chinachitika. Yesu anawukitsa mwanuna ameneyo kubwerera ku moyo, ngakhale kuti Lazaro anali wakufa kwa masiku anayi. Chiwukiriro chimenecho chiri umboni wakuti Mulungu angakwaniritse malonjezo ake a kubweretsanso akufa pa “tsiku lomaliza.” Koma kodi ndi kuti kumene Marita anayembekezera kuwonanso Lazaro? Ndi kuti kumene Ayuda ena okhulupirika anaganizira kuti chiwukiriro chomadzacho chikachitikira?
‘Dziko Losabwerera’?
Dziko lapansi linasankhidwa ndi Mulungu kukhala malo okhalako achilengedwe kaamba ka munthu. Wamasalmo akuchilongosola icho m’mawu awa: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova, koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” (Salmo 115:16) Palibe chirichonse m’Malemba Opatulika chimene chimasonyeza kuti ngati Adamu ndi Hava akanakhalabe okhulupirika kwa Mulungu, iwo akanakhala ndi moyo wamuyaya kwinakwake osati pa dziko lapansi. M’chenicheni, kodi “mtengo wa moyo” sunali pano pa dziko lapansi, m’Paradaiso imene anthu aŵiri oyambirira anasangalala asanagwere m’njira ya kusamvera Mulungu? (Genesis 2:9; 3:22) Popeza kuti panalibe chidziŵitso china chochokera kwa Mulungu chosiyanako, atumiki ake okhulupirika kunja kwa munda wa Edeni (kuyambira pa mwana wa Adamu wowopa Mulungu Abele kupita mtsogolo) akakhoza, moyenerera, kukhala anagwirizanitsa chiwukiriro ndi malo okha amene anawadziŵa kaamba ka munthu—dziko lapansi.
‘Tsopano, tadikirani,’ anthu ena ozoloŵerana ndi Baibulo angatsutse tero, ‘kodi Yobu sananene mu mutu 16, vesi 22, kuti “njira imene” iye “sakabwererako” iye “adzamukako”? Ndipo pa Yobu 7:9 iye analoza kuti: “Wakutsikira kumanda [Shelo, NW] sadzakwerakonso.” Yobu anawonjezera mu vesi 10 kuti: “Sadzabweranso kunyumba yake, osamdziwanso malo ake.”’
Chotero, monga mmene ophunzira ena amadzinenera, kodi mavesi amenewo ndi ndemanga zofananazo sizimasonyeza kuti Yobu anawona imfa monga ‘dziko losabwerera’? Kodi ndemanga zoterozo zimatanthauza kuti Yobu sanakhulupirire m’chiwukiriro chamtsogolo? Kaamba ka yankho, tiyenera kutenga mawu amenewa m’makhazikitsidwe awo, ndiponso kuwayerekeza iwo ndi malingaliro ena omwe Yobu analongosola pa nkhaniyo.
Yobu sanadziŵe zifukwa zimene zinali kumbuyo kwa kuvutika kwake. Kwa kanthaŵi iye molakwika analingalira kuti Mulungu anali ndi thayo kaamba ka chisautso chake. (Yobu 6:4; 7:17-20; 16:11-13) Atafooka, anadzimva kuti malo okha a mpumulo wamwamsanga anali manda. (Yobu 7:21; 17:1; yerekezani ndi 3:11-13.) Kumeneko, kuchokera ku kawonedwe ka mabwenzi ake, iye sakawonedwa, sakabwerera kunyumba yake, sakapezanso chidziŵitso chowonjezereka, sakabweranso kapena kukhala ndi chiyembekezo chirichonse cha kutero nthaŵi yoikidwiratu ya Mulungu isanakwane. Atasiyidwa kwa iwo eni popanda kuloŵereramo kwa Mulungu, Yobu ndi mbadwa zonse za Adamu analibe mphamvu ya kuwuka kuchokera kwa akufa.a—Yobu 7:9, 10; 10:21; 14:12.
Chikhulupiriro m’Chiwukiriro
Sitiyenera, ngakhale ndi tero, kumvetsetsa kusatsimikizirika kwa Yobu ponena za zimene anali kukumana nazo ndi ndemanga zopanda chiyembekezo zonena za mtsogolo mwake mwa posachedwa kutanthauza kuti iye sanakhulupirire m’chiwukiriro. Kunena kuti iye ndithudi anakhulupirira m’chiwukiriro cha mtsogolo kuli komvekera bwino kuchokera ku Yobu 14:13-15. Mu ndime imeneyo, Yobu analankhula za kukhumba ‘kubisidwa mu Shelo’ ndipo pambuyo pake ‘kukumbukiridwa’ ndi Mulungu. M’kuwonjezerapo, pa Yobu 19:25-27 mwanuna wa chikhulupiriro ndi umphumphu ameneyu analankhula za kukhala ndi “mombolo” ndipo pambuyo pake za ‘kupenya Mulungu.’ Inde, Yobu anakhulupirira m’chiwukiriro. Iye anakhulupirira kuti Mulungu akanakhoza ndipo angakhoze kumubwezeranso ku moyo, mongadi mmene kalelo Abrahamu anakhutiritsidwa za kuthekera kwa Mulungu kwa ‘kuwukitsa akufa.’—Ahebri 11:10, 16, 19, 35.
Kufikira ku nthaŵi zanthu zamakono, Ayuda akhulupirira m’chiwukiriro cha mtsogolo ku moyo pa dziko lapansi. Encyclopædia Judaica (1971) ikulongosola kuti: “Chikhulupiriro chakuti kotheratu akufa adzawukitsidwanso m’matupi awo ndi kukhalanso pa dziko lapansi” chiri “chikhulupiriro chachikulu” cha Chiyuda. Bukhu lanazonselo likupitiriza kuti: “Lingaliro limeneli latengedwa mosamalitsa chotero ndi m’lingaliro lenileni kotero kuti Ayuda olemekeza chipembedzo amakhala kaŵirikaŵiri odera nkhaŵa ponena za zovala zimene adzaikidwa nazo, kukwiriridwa kwa ziŵalo zonse, ndi kukhala ataikidwa mu Israyeli.”
Mosangalatsa, Baibulo silimanena kuti m’chiwukiriro Mulungu adzalumikizanso matupi owola a anthu akufa. Maatom enieni a awo omwe kwa nthaŵi yaitali akhala akufa anamwazikana pa dziko lapansi ndipo kaŵirikaŵiri m’kupita kwa nthaŵi anasakanizikana mu zamasamba ndi moyo wa nyama—inde, ngakhale mwa anthu ena, omwe pambuyo pake anafa. Chiri chodziŵikiratu kuti m’chiwukiriro maatom amodzimodziwo sangagwiritsidwe ntchito kaamba ka anthu oposa pa mmodzi yemwe wawukitsidwa. M’malomwake, Mulungu akabweretsa ku moyo anthu m’matupi oyenerera, popanda kusoŵeka kwa mbali zina ndi kupunduka kwina komwe anavutika nako asanafe, monga mmene chidzamukondweretsa iye.—Yerekezani ndi 1 Akorinto 15:35-38.
Kodi owukitsidwa amenewa adzazindikiridwa ndi mabwenzi ndi achibale awo omwe abweretsedwanso ku moyo? Chimenecho chikuwoneka cha nzeru, popeza kuti ngati sitikanatha kuzindikira akufa omwe awukitsidwa ndipo iwo kusazindikira ife, kodi tikanadziŵa bwanji kuti akufa athu okondedwa abwereradi? Ngakhale kuti thupi la Lazaro linali kuwola, iye anazindikiridwa ndi achibale ndi oyanjana nawo pambuyo pakuti Yesu anamuwukitsa iye. Chotero, nafenso tingayembekezere kuti Yehova Mulungu mwachikondi adzatilola kuwona ndi kudziwana wina ndi mnzake m’chiwukiriro ku moyo pa dziko lapansi.
Chiyembekezo cha Kumwamba kaamba ka Ochepera
Monga momwe tawonera, dziko lapansi liri malo a munthu opatsidwa ndi Mulungu. Komabe, Yesu Kristu anawunikira pa chiyembekezo chakuti chiŵerengero chosankhidwa chochokera pakati pa mtundu wa anthu akawukitsidwa ku moyo wauzimu wopanda chivundi, wosafa limodzi naye kumwamba. (2 Timoteo 1:10) Kwa kanthaŵi pambuyo pakuti Yesu anatsegula “njira yatsopano ndi yamoyo” kupita ku moyo wakumwamba, Akristu onse anali kuitanidwa kugawana m’chiyembekezo chimenecho. (Ahebri 9:24; 10:19, 20) Kodi ndi angati amene pomalizira akalandira mphotoyo? ‘Chivumbulutso, [chowuziridwa] chimene Mulungu anampatsa Yesu kuti awonetse akapolo ake zinthu zoyenera kuchitika,’ chikuika chiŵerengerocho pa 144,000, iwo “ogulidwa kuchokera ku dziko.”—Chibvumbulutso 1:1; 7:4-8; 14:1, 3.
Nchifukwa ninji chiŵerengero chaching’ono choterocho cha anthu “[cha]gulidwa kuchokera ku dziko” kaamba ka moyo kumwamba? Bukhu limodzimodzilo la Chibvumbulutso likutipatsa chifukwa cha chiŵerengero chokhala ndi polekezeracho. Timaŵerenga mu mutu 20, mavesi 5 ndi 6 kuti: “Ndiko kuwuka kwa akufa koyamba. Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nawo pa kuwuka koyamba; pa iwowa imfa yachiŵiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.”—Onaninso Chibvumbulutso 5:9, 10.
Nzika za pa Dziko Lapansi za Mfumuyo
Mwachidziŵikire kwenikweni, sianthu onse adzalamulira monga mafumu ndi ansembe, popeza ngati onse anali mafumu, kodi “akalamulira” pa yani? M’malomwake, gulu losankhidwa mwapadera limeneli, lomangidwa mozungulira atumwi okhulupirika a Yesu, lidzalamulira pa dziko lapansi lokhalidwa m’mbali ina ndi “khamu lalikulu” lolongosoledwa pa Chibvumbulutso mutu 7, mavesi 9 mpaka 17. Mamiliyoni a amenewa akuyang’ana kutsogolo ku “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” yomafika mofulumira, yomwe idzayeretsa dziko lapansi kuchotsa chisalungamo chonse. Ndi chifundo chokoma mtima cha Mulungu, iwo adzapulumuka chisautso chachikulu popanda kufa konse.—Chibvumbulutso 16:14; 21:14; Miyambo 2:21, 22.
‘Koma bwanji ponena za awo omwe anamwalira, onga ngati okondedwa anga?’ mungafunse tero. Yesu iyemwini anawuza Marita kuti ena, ‘angakhale anamwalira, adzakhala ndi moyo.’ (Yohane 11:25) Chimenecho chidzachitika m’chiwukiriro cha pa dziko lapansi. Mkati mwa kulamulira kwa Kristu ndi mafumu ndi ansembe anzake 144,000 m’mwamba, mamiliyoni ambiri amene Mulungu akuwakumbukira mwachiyanjo adzawukitsidwa ndi kukhala ndi mwaŵi wokwanira kuphunzira kulambira kowona kwa Yehova. Ngati ali okhulupirika, iwo adzapeza mphoto ya moyo wamuyaya m’paradiso ya padziko lonse lapansi. Chimenecho chidzakhala mkati mwa “tsiku lomaliza” limene Marita analozerako pamene anali kuvomerezana ndi Yesu kuti mlongo wake Lazaro akawuka ku moyo kachiŵirinso.—Yohane 5:28, 29; 11:24; Luka 23:43.
Chiyembekezo Choyedzamira pa Zitsimikizo
Ziwukiriro zolembedwa m’Baibulo ziri madongosolo ndi zitsimikizo za kuwona kwa chiyembekezo cha chiwukiriro choperekedwa ndi Malemba Opatulika. Cholembera chimenechi chimanena za ziwukiriro zochitidwa padziko lapansi ndi aneneri Eliya ndi Elisa mu nthaŵi ya Chikristu chisanakhale, ndi Mwana wa Mulungu (kuphatikizapo chija cha Lazaro), ndi atumwi Petro ndi Paulo, ndipo makamaka ndi Yehova Mulungu m’kuwukitsa Mwana wake. Mungaŵerenge maripoti oterowo m’Baibulo lanu pa: 1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; Mateyu 28:1-10; Luka 7:11-17; 8:40-56; Yohane 11:38-44; Machitidwe 9:36-42; 10:38-42; 20:7-12.b
Pamaziko a chiyembekezo champhamvu cholembedwa choterocho, Paulo akanatsimikizira anthu a ku Atene kuti: “Mulungu . . . anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu chitsimikizo, pamene anamuwukitsa Iye kwa akufa.”—Machitidwe 17:30, 31.
Inde, chiwukiriro cha Yesu chiri chitsimikizo chotheratu cha kutsimikizirika kwa chiyembekezo cha chiwukiriro. Chotero nafenso tiri ndi maziko olimba kaamba ka kukhulupirira kotheratu mu mphamvu ndi chikondi cha Yehova Mulungu. Nafenso tingalongosole chikhutiritso chimene Marita anali nacho: ‘Ife tidziŵa kuti akufa adzawuka m’chiwukiriro pa tsiku lomaliza!’
Pambuyo pakuti gulu la Paulo linamva umboni wake pa Phiri la Mars ponena za “chiwukiriro cha akufa,” linagawanika m’magulu atatu: “Ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi. . . . Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupira.”—Machitidwe 17:32-34.
Nchiyani chimene chiri yankho lanu ku chiyembekezo cha chiwukiriro? Yehova adzasunga lonjezo lake la kuwukitsa mamiliyoni, ngakhale mabiliyoni, kuchokera kwa akufa. Kaya inu mudzakhalapo kudzawawona iwo kachiŵirinso, ndi kuwonedwa ndi iwo, chimadalira mokulira pa inu. Kodi muli ofunitsitsa kuphunzira ponena za ziyeneretso za Mulungu ndi kukhala m’chigwirizano ndi izo kaamba ka kupeza moyo wamuyaya? Mboni za Yehova zidzakhala zachimwemwe kukupatsani chidziŵitso chowonjezereka ponena za chiyembekezo cha akufa ndi ponena za mmene mungapulumukire mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu.—Yohane 17:3.
[Mawu a M’munsi]
a M’dongosolo lofananalo, wamasalmo akulemba m’njira iyi ponena za mkhalidwe wokhalako pa nthaŵi imeneyo kuloŵereramo kulikonse kwa Mulungu kusanachitike: “Ndipo [Mulungu] anakumbukira kuti [Aisrayeli] ndiwo anthu; [mzimu, NW] [kapena mphamvu ya moyo yochokera kwa Mulungu] upita osabwereranso.”—Salmo 78:39.
b Mungapeze kukambitsiridwa kwatsatanetsatane kwa ziwukiriro mu nthaŵi za Baibulo ndi lonjezo la Baibulo la chiwukiriro chikudzacho mkati mwa kulamulira kwa Kristu mu Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Mutu 20 uli wakuti “Chiukiriro—Cha Yani, ndipo Kuti?” Bukhu limeneli lipezeka kuchokera kwa Mboni za Yehova m’gawo lanu kapena kuchokera ku maofesi ondandalitsidwa pa tsamba 2 la magazini ino.