Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 6/15 tsamba 25-27
  • “Patsogolo pa Ulemerero Pali Kudzichepetsa”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Patsogolo pa Ulemerero Pali Kudzichepetsa”
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ena Omwe Anachoka ku ‘Kudzichepetsa kupita ku Ulemerero’
  • Mitundu Yosiyanasiyana ya Ulemerero
  • Nchiyani Chomwe Chinachirikiza Akristu Okhulupirika Amenewa?
  • ‘Kodi Mulungu Sindiye Amamasulira Maloto?’
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Njala Yopatsa Imfa mu Nthawi ya Mwana Alilenji
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Yosefe Aikidwa M’ndende
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yehova Amatithandiza Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 6/15 tsamba 25-27

“Patsogolo pa Ulemerero Pali Kudzichepetsa”

MWAMUNA wachichepere winawake anali m’ndende ya Chiigupto pa mulandu wonamiziridwa. Iye anavutika ndi kuchepetsedwa kokulira, ndipo sipanawoneke kukhala chiyembekezo cha kumasulidwa kuchoka m’ndende. Kenaka analamulidwa kuwonekera pamaso pa Farao. Alonda a ndende mwamsanga anamutulutsa iye. Anameta, kusintha zovala zake, ndipo kenaka anawonekera pamaso pa mfumuyo.

Chodabwitsa chinayembekezera Yosefe. Ndi thandizo la Yehova Yosefe molondola anamasulira maloto aŵiri a Farao. Farao ananena kuti: “Tawona, ndakhazika iwe wolamulira dziko lonse la Igupto.” (Genesis 41:41) Ndi chokumana nacho chosakhulupiririka chotani nanga​—kuchoka kundende kupita kunyumba yachifumu zonsezo m’tsiku limodzi! Chokumana nacho cha Yosefe chingachitire fanizo chimene Mfumu Solomo pambuyo pake anawuziridwa kulemba kuti: “Pakuti atuluka m’nyumba yandende kuloŵa ufumu.” Moyenerera, Solomo kaŵiri analemba kuti: “Patsogolo pa ulemerero pali kudzichepetsa.”​—Mlaliki 4:14; Miyambo 15:33, NW; 18:12, NW.

Kotero kuti mupindule kuchokera ku chowonadi chaumulungu chimenecho, dzifunseni inumwini: Nchiyani chomwe chinachirikiza Yosefe mkati mwa chokumana nacho chake chochepetsa? Ndimotani mmene mtumiki wokhulupirika wa Yehova ameneyu anachitira ndi mlandu wabodza umene unamuikitsa m’ndende? Kodi ndi ulemerero wotani umene Yehova anali nawo m’maganizo kaamba ka Yosefe? Kodi ndi mtundu wotani wa ulemerero umene ukudikira awo amene mkati mwa mazana mokhulupirika ndi molimba mtima avutika ndi chizunzo ndi kuchepetsedwa? Pamwamba pa zonse, nchiyani chimene chimatithandiza ife kusunga mkhalidwe wolinganizika pamene tikuvutika ndi kuchepetsedwa?

Yosefe ayenera kukhala anasinkhasinkha kaŵirikaŵiri pa maloto aulosi aŵiri oyambirira amene anasonyeza kuti abale ake ndipo ngakhale makolo ake “akaweramira pansi” kwa iye. M’chenicheni, abale ake, pakumva loto loyamba, ananena kuti: “Kodi udzakhala mfumu yathu ndithu?”​—Genesis 37:8-10.

Abale a nsanje a Yosefe anali pafupi kumupha iye! Koma pansi pa chitsogozo cha Yehova, mnyamata wa zaka 17 zakubadwa ameneyo anagulitsidwa kwa amalonda apaulendo, amene, pambuyo pake, anamugulitsa iye kwa Potifara, kazembe wa alonda a Farao.

Potsirizira pake, Yosefe anakhala woyang’anira panyumba ya Potifara, amene mkazi wake anayesera kunyenga mwamuna wachichepere wokongolayo. Komabe Yosefe anali wokhulupirika kwa Yehova ndipo anathaŵa. Mkazi wamachenjerayo monama anapatsa Yosefe mlandu wa kuyesera kumugwirira chigololo, ndipo Potifara anakhulupirira mkaziyo, chotero Yosefe wopanda thandizo anaikidwa m’ndende.

Ngakhale kuli tero, iye anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova, amene, monga kwatchulidwa kale, anakonzekera kuti iye atengeredwe kwa Farao kukamasulira maloto. Farao pambuyo pake anaika Yosefe ku malo a mwaŵi aulemerero a kulinganiza kugawira chakudya mu Igupto. Pamene njala inafalikira ku Kanani, abale a Yosefe anaweramadi pansi kwa iye kuti atenge chakudya kaamba ka banjalo.

Ena Omwe Anachoka ku ‘Kudzichepetsa kupita ku Ulemerero’

Mtumiki wina wokhulupirika wa Yehova amene njira yake ya moyo imatsimikizira chowonadi chaumulungu chakuti “patsogolo pa ulemerero pali kudzichepetsa” anali Mose. Woleredwa m’bwalo laulemerero la Farao, Mose anali ndi mtsogolo mokhumbirika patsogolo pake. Kenaka zochitika zinawoneka kusintha kukhala zoipirako. Mose anachita kokha kaamba ka chikhulupiriro mwa Yehova ndi kudera nkhaŵa kwachikondi kaamba ka anthu ake, kotero kuti iye anayenera kuthaŵa kaamba ka moyo wake kuchoka kwa Farao wokwiya. Ali yekha anayenda kupita ku Midyani. Kwa zaka 40 iye anasonyeza kudzichepetsa kwake mwa kukhala moyo wopepuka wa mbusa, akutumikira mpongozi wake Yetero. Chiyenera kukhala chinali cholimbikitsa chotani nanga kwa Mose mkati mwa zaka zake 40 za kuwongolera umunthu kusinkhasinkha pa njira ya Yehova yomuchepetsera iye ndi kulingalira chimene chinali chidakali chosungidwa kaamba ka iye!

Kenaka unadza ulemerero. Yehova anagawira Mose kukhala mthenga Wake kwa Farao ndi kutulutsa anthu Ake kuchoka mu Igupto. Ndi mwaŵi waulemerero wotani nanga umene Mose anali nawo pamene anali woloŵetsedwamo mwachindunji m’miliri khumi ndi kutsogoza Israyeli kupyola Nyanja Yofiira! Pambuyo pake, Mose analandira Chilamulo chochokera kwa Yehova pa Phiri la Sinai. Pamene iye anatsika, anthu “sanathe kuyang’anitsitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake.”​—2 Akorinto 3:7.

Lingaliraninso Yobu, wamkulu wa Akum’mawa onse. Iye anali “munthu wangwiro ndi woongoka, wakuwopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.” (Yobu 1:2, 3, 8) Kenaka, mwadzidzidzi, anataikiridwa ana ake khumi ndi zikwi zake za nkhosa, ngamila, ng’ombe zamagoli, ndi abulu aakazi.

Zimenezo sizinali zonse. Yobu anafikira kukutidwa ndi zironda zowawa, kumpangitsa iye kukhala wochititsa nseru mwakuthupi. Mkazi wake weniweni anamuseka iye nati: “Kodi uwumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano, ufe.” (Yobu 2:9) Yobu anali kuyesedwa mowopsya ndi kuchepetsedwa, koma iye anali wosazindikira kotheratu za kukangana kwa kumwamba pakati pa Yehova ndi wopanduka wamkulu, Satana. Mkhalidwewo sunawongoleredwe ndi kukambitsirana kotalika ndi “mabwenzi” atatu a Yobu. Ngakhale kuli tero, Yobu anasungirira umphumphu wake. Iye anafikira ngakhale pa kulandira modzichepetsa uphungu wanzeru wochokera kwa Elihu​—mwamuna wachichepere kwenikweni.​—Yobu 32:4.

Kodi Yobu anafupidwa? Inde. Yehova anabwezeretsa Yobu, kuŵirikiza kaŵiri ukulu wa zoŵeta zake, ndi kumpatsa iye ana aamuna asanu ndi aŵiri ndi ana aakazi atatu​—okongola koposa m’dziko lonse! Ndi chotulukapo chaulemerero chotani nanga cha kudzichepetsa kwa Yobu! Chinatsimikizira kukhala chowona chotani nanga​—“patsogolo pa ulemerero pali kudzichepetsa.”​—Yobu 42:12-15.

Mitundu Yosiyanasiyana ya Ulemerero

Mwachidziŵikire pali mitundu yambiri yosiyanasiyana ya ulemerero​—kuchokera ku ulemerero wa tsitsi la mkazi kufika ku ulemerero wa nkhope ya Mose pamene anatsika pa Phiri la Sinai. (1 Akorinto 11:15; 2 Akorinto 3:7) Kuloŵa kwa dzuŵa kowonekera kuli ndi ulemerero waukulu, ndipo nyenyezi ziri ndi ulemerero wina.​—1 Akorinto 15:41.

Mitundu yosiyanasiyana ya liwu lakuti “ulemerero” yagwiritsidwa ntchito nthaŵi mazana angapo m’Baibulo. Pamene tisanthula zilozero zimenezi ndi mawu awo ozungulira lemba, chiri chachiwonekere kuti Yehova ali magwero a ulemerero wonse. Atumiki ake okhulupirika ndi zozizwitsa za chilengedwe chake zingawunikire ulemerero umenewu m’njira zambiri ndi ku mlingo wosiyana.

M’zana lathu la 20, tiri ndi umboni wochuluka wa kuchepetsedwa komwe awo okhala ndi chiyembekezo chaulemerero cha moyo wa kumwamba avutika nako. Mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya I, ziŵalo zotsogolera za Watch Tower Society mu Brooklyn, New York, zinaweruziridwa kukhala zaka 20 m’ndende pa milandu yabodza. Chifupifupi nthaŵi imodzimodziyo, chizunzo chinawulika m’malo ambiri. Mwachitsanzo, J. B. Siebenlist anamangidwa masiku atatu popanda chikalata chotulukira ndipo popanda chakudya, kusiyapo kokha zidutswa zitatu zoipitsidwa za mkate wa ufa wa chimanga. Iye anatengedwa kuchoka m’ndende ndi gulu lowukira, kuvulidwa, kuikidwa phula lotentha, ndi kukwapulidwa ndi tsatsa lokhala ndi nsikidzi ndi waya kumapeto kwake. Pa kuzengedwa mlandu kwina loya wozenga mlanduyo ananena kuti: “Pita ku helo ndi Baibulo lako; uyenera kukhala m’helo ndi msana wako wothyoka; uyenera kupachikidwa.”

Mkati mwa Nkhondo ya Dziko ya II, ena a atumiki okhulupirika a Yehova anavutika mowopsya m’misasa yachibalo ya Nazi. Mmodzi anali Martin Poetzinger, Mboni yodzozedwa yomwe inapulumuka kukhala chiŵalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Iye analongosola Dachau monga “nyumba yoipa ya ziwanda.” Mu msasa pa Mauthausen, a “Gestapo anayesera njira iriyonse kutisonkhezera ife kuswa chikhulupiriro chathu mwa Yehova. Chakudya cha njala, maubwenzi achinyengo, nkhalwe, kuimirira pa thabwa tsiku ndi tsiku, tikumapachikidwa pa mtengo wa mapazi khumi mwa kumangidwa mfundo za manja opindidwira kumbuyo, mikwapulo​—zonsezi ndi zina . . . zinayesedwa.”

Nchiyani Chomwe Chinachirikiza Akristu Okhulupirika Amenewa?

Pansi pa mikhalidwe yoipa ndi yonyazitsa imeneyo, iwo anathandizidwa kupirira ndi chikhulupiriro chawo m’chotulukapo chotsatira, kuphatikizapo chiyembekezo cha mtsogolo mwaulemerero kaamba ka awo osungirira umphumphu wawo. Kwa “kagulu ka nkhosa” ka Mboni zodzozedwa, ichi chiri choloŵa chakumwamba. (Luka 12:32) Mtundu wapadera wa ulemerero pa dziko lapansi wasungidwa kaamba ka anthu ena okhulupirika. Ena a iwo, onga ngati Yosefe ndi Mose, alozeredwako mu Ahebri mutu 11. Chonde ŵerengani mavesi 32-40 ndi kusinkhasinkha pa kuchepetsedwa kumene kunayenera kupiriridwa ndi ena a okhulupirika amenewa. Kuwonjezerapo, “khamu lalikulu” likutumikira Yehova pa dziko lapansi lerolino. (Chibvumbulutso 7:9, 15) Kodi mtsogolo mwawo nchiyani?

Mtsogolo molemera mukuwadikira iwo. Boma lakumwamba pansi pa Yesu Kristu lidzakhala ndi oimira a padziko lapansi omwe adzagwiritsira ntchito malangizo olembedwa m’mipukutu yolozeredwako pa Chibvumbulutso 20:12. Oterowo adzakhala ndi mwaŵi waulemerero, osati monga mafumu, koma “akalonga m’dziko lonse lapansi,” ndipo limodzi nawo, anthu odzichepetsa, okhulupirika osaŵerengeka, kuphatikizapo owukitsidwa, adzafika ku moyo wamuyaya m’paradaiso ya pa dziko lapansi laulemerero.​—Salmo 45:16.

Lerolino pali mamiliyoni omwe asonyeza kudzichepetsa kwawo mwa kusiya chipembedzo chonyenga ndipo mwachimwemwe kugawanamo mu ntchito yolalikira ya kunyumba ndi nyumba ya Mboni za Yehova. Ambiri a amenewa asekedwa ndi ziŵalo za banja ndi mabwenzi, koma amamatira ku kulambira kowona. Iwo modzichepetsa alandira kuwongolera ndi chilango kotero kuti atumikire Mulungu wowona, Yehova. Chiyembekezo chawo chiri kukhala ndi moyo pa Paradaiso yobwezeretsedwa, pamene “dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziŵitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi aphimba pansi pa nyanja.”​—Habakuku 2:14.

Awa ali masiku a kuyesa kaamba ka anthu a Yehova. Chiri chifupifupi ngati kuti ndife alendo m’dziko lachilendo. Mpata pakati pa kulambira kowona ndi kulambira konyenga ukuzamirako ndi kufutukukirako. Tonsefe timavutika ndi kuchepetsedwa ku mlingo winawake. Koma monga mmene Yesu anatonthozedwera ndi kulimbitsidwa ndi chisangalalo choikidwa pamaso pake, chotero nafenso tingalake ziyeso mwa kukumbukira chotulukapo chomalizira.

Baibulo limatilangiza kuti: “Dzichepetseni pamaso pa [Yehova, NW], ndipo adzakukwezani.” (Yakobo 4:10) Pamene muikidwa pa chiyeso chowopsya, lingalirani za mawu awa: “Patsogolo pa ulemerero pali kudzichepetsa.” Kumbukirani, kachiŵirinso, kuti Yehova sangalephere!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena