Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 7/15 tsamba 31
  • Chidziŵitso pa Nyuzi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chidziŵitso pa Nyuzi
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Akatolika ndi Ubatizo
  • Mawu Osamvedwa Konse
  • Amuna, Muzitsanzira Umutu wa Khristu
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Tanthauzo la Ubatizo Wanu
    Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Ubatizo Ungakuthandizeni Kuti Mukhale Ndi Tsogolo Labwino
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Munthu Ayenera Kubatizidwa Kuti Akhale Mkhristu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 7/15 tsamba 31

Chidziŵitso pa Nyuzi

Akatolika ndi Ubatizo

Chiŵerengero chowonjezereka cha achikulire akubatizidwa ndi Tchalitchi cha Roma Katolika mu France, ikusimba tero Le Monde, nyuzipepala ya Chifrench. M’chenicheni, pepalalo likudzinenera kuti “ziŵerengero zawirikiza kaŵiri mkati mwa zaka zinayi zapitazo.” Makalasi a ubatizo usanakhale akuchitidwa ndi anthu achikulire a Chifrench oposa 4,000 ofunafuna kukhala Akatolika obatizidwa. Mbali ziŵiri mwa zitatu ali akazi a msinkhu wa pakati pa 20 ndi 40. Kota ali a chiyambi chosakhala cha Chifrench.

Kukonzekera kaamba ka ubatizo wa achikulire, ngakhale kuli tero, kungatenge zaka ziŵiri kapena zitatu. Wansembe Guy Cordonnier, wokhala ndi thayo kaamba ka makalasi a ubatizo usanakhale oterowo m’dera la ku Versailles, ananena kuti: “Kuti ubatizidwe, sikuli kokwanira kunena kuti wina amakhulupirira mwa Mulungu. Chiri choyenerera kuphunzira mmene angakhalire mkati mwa chitaganya.”

Ubatizo wa achikulire siuli, ndithudi, chinthu chatsopano. Yesu iyemwini anabatizidwa pa msinkhu wa zaka 30. Kunena kuti choposa chikhulupiriro chokha mwa Mulungu chiri chofunikira kaamba ka ubatizo chiri mofananamo chosakhala chatsopano. Lamulo la Yesu kwa atsatiri ake linali la “kupanga ophunzira . . . , kuwabatiza iwo” ndi “kuwaphunzitsa iwo” kusunga malamulo ake.​—Mateyu 28:19, 20.

Ngakhale kuli tero, popeza kuti Tchalitchi cha Katolika kwa mazana angapo chachita ubatizo wa makanda, katengedwe ka tchalitchi pa kubatiza achikulire kali kozizwitsa. Maulamuliro a tchalitchi amanena kuti chimatenga zaka ziŵiri kapena zochulukira kukonzekera wachikulire kaamba ka ubatizo, komabe iwo amasungilira kuti ubatizo wa makanda uli wolondola. Iwo amadzinenera kuti ubatizo umayeretsa makanda ku machimo awo achibadwa, koma mtumwi Yohane analemba kuti: “Mwazi wa Yesu . . . umayeretsa machimo athu onse.” (1 Yohane 1:7) Popeza kuti makanda ali osakhoza kusonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu ndi m’mwazi wokhetsedwa wa Kristu, nchifukwa ninji kuwabatiza iwo?

Mawu Osamvedwa Konse

Chifupifupi theka la akazi 3,800 ofunsidwa ndi kampani ya insuwaransi ku Japan “sanamvepo mawu akuti ‘ndimakukonda iwe’ kuchokera kwa amuna awo m’zaka zoŵerengeka,” ikusimba tero The Daily Yomiuri. Peresenti ya akazi osamva mawu amenewa imawonjezereka ndi msinkhu, ndipo kwa aja a m’zaka zawo za m’ma 50, peresenti yozizwitsa ya 82 inanena kuti samamva konse mawu amenewa kuchokera kwa amuna awo. Ngakhale pakati pa akazi a m’zaka zawo za m’ma 20, kokha 10 peresenti amamva amuna awo akulankhula mawu amenewa tsiku lirilonse.

Mu nkhani yachikondi ya Mfumu yanzeru Solomo yoloŵetsamo mnyamata wachibusa ndi mtsikana wa m’dziko wokongola wochokera ku mzinda wakale wa Shunemu, chinali kupyolera mwa “kalongosoledwe kachikondi” kamene mnyamatayo anakhutiritsa mtima wa mtsikanayo. (Nyimbo ya Solomo 1:2) Mwamsanga amuna atakhutiritsa mitima ya akazi awo, kodi chimakhalabe choyenerera kulongosola chikondi chawo? Inde! Baibulo limalangiza kuti: “Amuna inu kondani akazi anu monganso Kristu anakonda [mpingo, NW] nadzipereka yekha m’malomwake.”​—Aefeso 5:25.

Pa usiku wa kuperekedwa kwake, Yesu analongosola mobwerezabwereza chikondi chake kaamba ka ophunzira ake. (Yohane 13:34; 14:19-21; 15:9, 10, 12) Mwamuna ayenera kulingalira kufunika kwa mkazi wake kwa kukhala wotsimikiziridwa za chikondi chake. Amuna ayeneranso kukumbukira kuti Kristu ‘anadzipereka yekha kaamba ka mpingo.’ Chotero, iye analongosola chikondi ponse paŵiri m’mawu ndi m’kachitidwe. Mowonekera, amuna amachita bwino kutsatira chitsanzo cha Kristu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena