Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w89 10/15 tsamba 4-7
  • Chiukiriro—Cha Ayani Ndipo Liti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiukiriro—Cha Ayani Ndipo Liti?
  • Nsanja ya Olonda—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Anthu Amaferanji?
  • Kodi Nchiyani Chimene Chiri Mkhalidwe wa Akufa?
  • Chiukiriro Chapadziko Lapansi
  • Chiukiriro​—Magwero a Chitonthozo
  • Chiukirirocho​—Liti?
  • Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Njira Yokhayo Yothetsera Imfa
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Akufa Adzaukitsidwa
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1989
w89 10/15 tsamba 4-7

Chiukiriro​—Cha Ayani Ndipo Liti?

CHINACHITIKA m’chaka cha 32 C.E. ku Betaniya, kwawo kwa Lazaro ndi alongo ake aŵiri, Malita ndi Mariya. Alongowo anali atatuma uthenga kwa Yesu kuti Lazaro anali kudwala. Yesu anamkonda Lazaro ndi alongo ake, kotero kuti Iye anayamba ulendo wopita ku Betaniya. Ali panjira, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali mtulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” Ophunzirawo analingalira kuti Yesu anatanthauza tulo teniteni. Chotero Yesu analongosola momvekera bwino kuti: “Lazaro wamwalira.”​—Yohane 11:1-15.

Alendowo anafika masiku anayi Lazaro atamwalira. Pamene Yesu anawona Mariya ndi ena akulira, iyenso “analira,” kusonyeza chikondi chake chachikulu ndi chifundo. (Yohane 11:17, 35) Mtembo wa Lazaro unali utaikidwa m’manda osemedwa m’phanga. Yesu analamula kuti mwala wotseka khomo la manda uchotsedwe. Anapemphera kwa Atate wake nafuula ndi mawu aakulu kuti: “Lazaro, tuluka.” Lazaro anatuluka. Zimenezi ziyenera kukhala zitabweretsa chisangalalo chachikulu chotani nanga kwa alongo ake!​—Yohane 11:38-45.

Chochitika chimenechi chimapereka chiyembekezo chenicheni cha chiukiriro. Komabe, kaŵirikaŵiri, imfa ndiyo mdani wokakala amene amatenga okondedwa athu popanda chiyembekezo chakuti Yesu awawukitse nthaŵi yomweyo. Monga momwe tidziŵira bwino lomwe, ambiri a anthu okondedwa amenewa ali anthu abwino ndi okoma mtima kambiri. Chifukwa chake, funso lachiwonekere limabuka . . .

Kodi Anthu Amaferanji?

Ngati tifuna yankho lolondola, ndi lodalirika, tiyenera kuyang’ana m’mbuyo ku chiyambi cha anthu m’munda wa Edene. Akumayesa kumvera kwa Adamu, Mulungu kumeneko anamlamulira kusadya chipatso cha mtengo umodzi. Ngati iye ndi Hava anadya chipatsocho, Mulungu adati, “udzafa ndithu.” (Genesis 2:17) Atayesedwa ndi Satana, sanamvere Mulungu ndipo analephera chiyeso chofunika kwambiri chimenecho. Chotulukapo chake chinali imfa.

Kodi nchifukwa ninji panali chilango chotero kaamba ka upandu wowonekera kukhala waung’ono? Chochita chawo chinali chaching’ono, koma upanduwo unali wobweretsa imfa kwadzawoneni​—chipanduko chochitidwa ndi anthu angwiro, Adamu ndi Hava, motsutsana ndi Mlengi wawo. Iwo sanalinso angwiro, ndipo Mulungu anapereka chilango cha imfa. Komabe, Mulungu walinganiza kuti chilango cholungama chimenecho chichotsedwe pa mbadwa za Adamu. Motani? Paulo adalemba kuti “Kristu Yesu . . . anadzipereka yekha chiwombolo m’malo mwa onse.”​—1 Timoteo 2:5, 6; Aroma 5:17.

Kodi Nchiyani Chimene Chiri Mkhalidwe wa Akufa?

Lazaro anali wakufa kwa masiku anayi. Ngati inu munali wakufa ndipo munalidi wamoyo m’dziko lamizimu kwa masiku anayi ndiyeno munaukitsidwa, kodi simukanafuna kusimbira anzanu za chochitikacho? Komatu Lazaro sadanene kanthu ponena za kukhala kwake wamoyo m’dziko lina. Baibulo limati: “Akufa, sadziŵa kanthu bii.”​—Mlaliki 9:5; Salmo 146:3, 4.

Talingalirani kuti zimenezo zimatanthauzanji. Anthu mamiliyoni ambiri amakhulupirira kuti kuli purigatoriyo, ngakhale kuti liwulo silimawonekera m’Baibulo. Ena ambiri amakhulupirira kuti kuli helo wamoto. Komabe, inu simungatenthe ngakhale mdani wanu m’moto wosatha. Ngati inu mungakane kuchita chinthu chankhanza chimenecho, kodi Mlengi wathu wachikondi akanatero mwa kuchititsa anthu kuzunzika m’helo wamoto? Komabe, onani chonde chitsimikiziro chotonthoza cha Baibulo chotchulidwa pamwambapo​—akufa “sadziŵa kanthu bii.”

Mogwirizana ndi Malemba, chiŵerengero cha amene adzalamulira ndi Kristu kumwamba nchaching’ono kwenikweni. Yesu anawalongosola kukhala “kagulu kankhosa.” (Luka 12:32) Mtumwi Yohane anawona ‘Mwanawankhosa [Yesu Kristu] alikuimirira pa Phiri la Ziyoni [la kumwamba], ndipo limodzi naye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi . . . amene agulidwa kuchokera ku dziko lapansi.’ (Chibvumbulutso 14:1-3) Pamenepa, zimenezi zitanthauza kuti anthu amenewo anali anthu, adamwalira, ndipo pambuyo pake adawukitsidwa kukakhala ndi moyo kumwamba limodzi ndi Kristu.

Monga momwe mungayerekezere, anthu athandizidwa mwa kumvetsetsa chowonadi cha Baibulo chimenechi​—kuti kulibe purigatoriyo kapena helo woyaka moto ndi kuti pali chiyembekezo chakuti anthu akufa angawukitsidwire kumwamba. Komabe, ngati oukitsidwira kumwamba ali ochepa motero, kodi nchiyembekezo chotani chimene enawo ali nacho?

Chiukiriro Chapadziko Lapansi

Yesu Kristu anatsegula khomo, kapena kulambula bwalo, njira youkitsidwira kumoyo kumwamba. (Ahebri 9:24; 10:19, 20) Chifukwa chake, Yohane Mbatizi sadzakhala ndi mbali m’chiukiriro cha kumwamba chifukwa chakuti anaphedwa mwambanda Yesu asanafe ndi kutsegula njira yamoyo wakumwamba. Yesu adati: “Indetu ndinena kwa inu, sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wakumwamba amkulira iye.” (Mateyu 11:11) Kodi ndi mphotho yotani imene Mulungu wasungira mwamuna wokhulupirika ameneyu ndi ena ofanana naye amene amwalira?

Tembenuzirani Baibulo lanu ku Luka 23 ndi kuŵerenga mavesi 39 mpaka 43. Mmodzi wa ochita zoipa amene anapachikidwa pambali pa Yesu adati: “Yesu ndikumbukireni mmene muloŵa ufumu wanu.” Yesu anamtsimikizira kuti akakhala m’Paradaiso. Kumeneko sikumwamba, koma ndiyo paradaiso ya padziko lapansi, monga momwe Paradaiso yoyamba inaliri.

Chiukiriro​—Magwero a Chitonthozo

Chiyembekezo chotsimikizirika Chabaibulo chimenecho chiyenera kukhala chotonthoza kwambiri, monga momwe tiriri ndi chifukwa chabwino chochiyembekezerera. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Yehova ndiye chikondi. (1 Yohane 4:8) Pamene iye adalola Mwana wake kufa imfa yochititsa manyazi, kwenikweni Mulungu anali kusonyeza mkhalidwe wake wodabwitsa wachikondi. Nthaŵi ina m’mbuyomo, Yesu adati: “Mulungu adakonda dziko lapansi [la mtundu wa anthu] kotero kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wokhulupirira iye asataike, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

Nayenso Yesu anasonyeza chikondi chapadera kupereka moyo wake monga dipo la anthu okhulupirira. Yemweyo adati: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.”​—Mateyu 20:28.

Carolann, wotchulidwa m’nkhani yoyambayo kukhala atatayikiridwa ndi okondedwa ake angapo m’ngozi yowopsya, anakomoka pambuyo pake. Koma anatonthozedwa ndi chidziŵitso chakuti akufa okondedwawo sanali kuzunzika. Kodi nchiyaninso chimene chinamthandiza kupirira? Chikondi ndi mawu otonthoza mowona mtima zosonyezedwa ndi abale ake auzimu, Mboni za Yehova, anatsimikizira kukhala othandiza kwambiri.​—Salmo 34:18.

Pemphero kwa Yehova nalonso linathandiza kwambiri. Masiku ambiri ankagalamuka ndi kulingalira kuti anali kulota maloto oipa, komano anali kukanthidwa powona kuti ndi zenizeni. Pembedzero kwa Yehova linali kumtonthoza, ndipo anayamikira kwambiri zimene Paulo adalemba kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”​—Afilipi 4:6, 7.

Shirley akupereka chitsanzo china cha mmene chiyembekezo cha chiunikiriro chiriri chotonthoza. Mwana wake wamwamuna wachichepere Riccardo anaphedwa mwadzidzidzi pamene ntchintchi yolemera ya konkire inagwera pa chifuwa pake, ndi kuphwanya mtima wake waung’onowo. Pambuyo pa ngozi imeneyi, m’January 1986, Shirley anauza mabwenzi ake kuti: “Kuli ngati kuti ndikulota atulo oipa.” M’tchalitchi cha Katolika anamvamo mawu awa: “Mulungu adzaweruza amoyo ndi akufa.” Shirley anayamba kulingalira kuti, ‘Ngati Mulungu adzaweruza amoyo ndi akufa, pamenepo kodi munthu angadziŵe bwanji kumene anthu amapita pambuyo pa imfa? Ndipo ngati iwo ali kumwamba, kodi angadzawaukitsirenji pambuyo pake kuti aweruzidwe? Ndiponso, kodi iwo angaukitsidwe bwanji ngati ali amoyo kumwamba?’ Palibe pamene Baibulo limatchula chiukiriro cha amoyo koma kokha cha akufa.

Shirley anafunsa mwamuna wake za vuto limeneli, chifukwa chakuti mwamunayo anali wozoloŵerana ndi Baibulo. Pamene iye anamvetsetsa zina za zimene Malemba amanena pa nkhaniyo, Shirley sanabwererenso ku tchalitchi. Wachibale wina amene ali mmodzi wa Mboni za Yehova anayamba kuphunzira Baibulo ndi Shirley ndi mwamuna wake m’March 1986, ndipo pasanapite nthaŵi yaitali iwo anabatizidwa. Pakali pano iye akuti: “Kuli kosangalatsa kwambiri kudziŵa chowonadi, kudziŵa za chiukiriro, ndi kudziŵa mmene Yehova aliri munthu wokondweretsa kwambiri.”

Chiukirirocho​—Liti?

M’masomphenya, mtumwi Yohane anawona “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, kuchokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa.” (Chibvumbulutso 7:9) Kunena kuti khamu lalikulu ‘likuimirira pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu’ kuli kogwirizana ndi nsonga yakuti iwo adzakhala ndi moyo padziko lapansi. (Yesaya 66:1) Ngati ena a iwo amwalira tsopano, kodi adzaukitsidwa liti? Baibulo silimatipatsa tsiku, koma kudzakhala pambuyo pa nkhondo yoyandikirayo mu imene Mulungu adzachotsa pa dziko lapansi onse osafunitsitsa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo yake yolungama. (2 Atesalonika 1:6-9) Zimenezo zidzalambula njira ya Tsiku Lachiweruzo ndi chiukiriro cha onse amene Mulungu amawawona kukhala mu mzere wa chiukiriro cha pa dziko lapansi. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Baibulo kumatsimikizira kuti zochititsa nthumanzi zodabwitsa zimenezi zidzachitika posachedwapa!​—Chibvumbulutso 16:14-16.

Nthaŵi ina ophunzira a Yesu anamfunsa kuti: “Kodi chizindikiro cha kufika kwanu nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” Poyankha Yesu anatchula nkhondo, kupereŵera kwa chakudya, zivomezi, miliri, ndi kulalikidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu pa dziko lapansi.​—Mateyu 24:3-14; Luka 21:7-11.

Ulosi wochititsa nthumanzi umenewu wakhala ukukwaniritsidwa chiyambire 1914, pamene Nkhondo ya Dziko ya I idayamba. Inapha anthu mamiliyoni ambiri ndi kuchititsa njala ndi kupereŵera kwa chakudya m’maiko ambiri. Mkhalidwe wa dziko mkati ndi pambuyo pa Nkhondo ya Dziko ya II unali woipirapo kwambiri.

Ponena za miliri, ambiri amalingalira kuti chitsanzo choipitsitsa ndicho AIDS. “Mliriwu ngwofalikira kwambiri ndipo wakupha kwambiri kotero kuti akatswiri akuuyerekezera ndi Mliri Wachaola umene unapha nusu ya chiŵerengero cha Yuropu m’zaka za zana lakhumi ndi zisanu ndi zinayi.”​—Reader’s Digest, June 1987.

Chifukwa cha zowopsya zamakono zotero, chiukiriro chidzakhala chochitika chabwino kwambiri chotani nanga! Idzakhala nthaŵi ya chisangalalo chosaneneka pamene mabanja osweka ndi imfa, onga a Carolann ndi Shirley, adzagwirizanitsidwanso! Mwachiwonekere, njira yanzeru kwa aliyense wa ife ndiyo kulamulira miyoyo yathu tsopano mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo motero kuyeneretsedwa kudzakhalapo pamene chiukirirocho chichitika.

[Chithunzi patsamba 7]

Baibulo limanena kuti monga mtengo ungagwetsedwe ndipo komabe kuphukiranso, Mulungu angathe kuukitsa akufa okhala m’chikumbukiro chake.​—Yobu 14:7-9, 14, 15

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena