Kufalitsa kwa Padziko Lonse kwa Mbiri Yabwino
UFUMU wa Mulungu ulamulira! Iyi ndi mbiri yabwino koposa. Chimenecho ndicho chifukwa chake mu 1989 Mboni za Yehova zoposa 3,700,000 kuzungulira pa dziko lonse motenthedwa maganizo zinalengeza “mbiri yabwino” yoloseredwa ndi Yesu ndi “uthenga wabwino” wolengezedwa ndi mngelo m’masomphenya a Yohane. (Mateyu 24:14, NW; Chibvumbulutso 14:6) Monga mmene mtumwi Paulo ananenera kuti: “Liwu lawo linatulukira ku dziko lonse lapansi, ndi maneno awo ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.” (Aroma 10:18) Ndipodi anthu a mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu akuvomereza mwachisangalalo ku chiitano chawo chakuti “opani Mulungu, mpatseni ulemerero.”—Chibvumbulutso 14:7.
Palibenso Inshuwaransi ya Moyo
Munthu wina woteroyo anali mwamuna wokhala mu England amene anapanga kakhalidwe kake kuchokera ku kusatsimikizirika kwa moyo. Ken anali wogulitsa wa inshuwaransi, ndipo pamene anafikira pa nyumba ya Mboni za Yehova, iwo anamufunsa kuti: “Kodi ungakonde kukhala m’dziko limene inshuwaransi ya moyo ikakhala yosayenerera?” Kodi iwo anatanthauzanji? Kuti mogwirizana ndi Baibulo, pansi pa Ufumu wa Mulungu zinthu zambiri zimene zimapanga moyo kukhala wosatsimikizirika tsopano, kuphatikizapo matenda ndi imfa, sizikakhalakonso.
Kodi chinthu choterocho chiridi chotheka? Inde, Mulungu iyemwini walonjeza zimenezo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti: “Mulungu yekha adzakhala Mulungu wawo [wa mtundu wa anthu], ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” (Chibvumbulutso 21:3, 4) Kodi nchiyani chimene chidzabweretsa masinthidwe oterowo? Ufumu wa Mulungu. Mogwirizana ndi Mawu a Mulungu, umenewu posachedwapa “udzaphwanya ndi kutha maufumu [amakono a ndale zadziko] awo onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
Malemba onga awa anabweretsedwa ku chisamaliro cha mazana mamiliyoni angapo a anthu ndi Mboni za Yehova mkati mwa ndawala yawo yolalikira ya dziko lonse. Ambiri, mofanana ndi Ken, anafikira pa kuzindikira kuti uku sikulota wamba. Umboniwo uli wotsimikizirika. Malonjezo aumulungu ameneŵa ali odalirika ndipo adzakwaniritsidwa posachedwapa.
Ndandanda Yosinthidwa ya Mapindu
Awo amene amamvetsera kwa Mboni za Yehova pamene zikumveketsa chilengezo chachimwemwe cha mngelo amadzazindikira kuti kuwopa Mulungu ndi kumpatsa ulemerero kumaphatikizapo zoposa kungokhulupirira m’malonjezo a Baibulo. Kumasintha kawonedwe kawo konse ndi kuwapumulitsa ku zokhumudwitsa zambiri za moyo.
Rafael ndi mkazi wake anapeza izi kukhala zowona. Iwo amakhala mu Argentina, ndipo pamene anakwatirana zoposa zaka 40 zapitazo, anapanga kukhala chonulirapo chawo m’moyo kugwira ntchito zolimba ndi kusunga ndalama kaamba ka mtsogolo mwachisungiko. Komabe, zaka 21 pambuyo pake, zonse zimene anafunikira kusonyeza kaamba ka ntchito yawo yolimba inali nyumba yawo yaing’ono yomwe inafunikira kukonzedwa mokhazikika. Iwo sanadzimve kukhala achisungiko pamene anangokwatirana kumene.
Kenaka anamva mbiri yabwino kuchokera kwa Mboni za Yehova ndipo anaphunzira mtundu wabwinopo wa chuma ndi mtundu wabwinopo wa chisungiko. Yesu, mu Ulaliki wake wa pa Phiri, analankhula za zimenezi pamene ananena kuti: “Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba; koma mudzikundikire nokha chuma m’mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba.”—Mateyu 6:19, 20.
Pamene kuli kwakuti Baibulo silimatiphunzitsa kusakhala osagwira ntchito ponena za zinthu zakuthupi, ilo limatifulumiza kusaika chiyembekezo chathu mu zinthu zoterozo. (Mlaliki 7:12) Mmalomwake, tiyenera kugwira ntchito kuti tipeze chuma chauzimu mwa kuphunzira Baibulo, kuphunzira chifuniro cha Mulungu, ndi kupanga kuchita chifuniro chimenecho kukhala chinthu choyamba m’miyoyo yathu. (Mateyu 6:33) Rafael ndi mkazi wake anayamba kukundika chuma chauzimu chimenecho, ndipo tsopano akudzimvadi olemera kwenikweni, osati chifukwa cha mkhalidwe wawo wa zandalama, koma chifukwa cha unansi wawo ndi Mulungu. (Chibvumbulutso 3:17, 18) Uthenga wa Ufumu wa Mulungu unali mbiri yabwino kwambiri kwa iwo.
Ukwati Wokonzedwanso
Mbiri yabwino iridi ndi mphamvu yeniyeni ya kukwaniritsa zabwino. Mwachitsanzo, John, amene amakhala mu England, sanali wokondweretsedwa ndi Baibulo, koma mkazi wake ndi ana anatero. Chotero anayamba kupezeka pa misonkhano ya Mboni za Yehova pamene John anapita kukamwa mowa ndi mabwenzi ake. Monga chotulukapo, iye analoŵetsedwa m’kumwa kopambanitsa, kusuta, ndipo, m’kupita kwa nthaŵi, m’chisembwere. Potsirizira pake, iye anasiya mkazi wake kukakhala ndi mkazi wina.
Makonzedwe a chisudzulo anayambika. Koma John anadabwitsidwa kuwona kuti mkazi wake—yemwe anaphunzira khalidwe Lachikristu m’kuphunzira kwake mbiri yabwino—anam’chitirabe mwaulemu. John analephera kumvetsetsa chifukwa chake. Milungu itatu chisudzulocho chisanathe, mkhalidwe Wachikristu wa mkazi wa John unali ndi chiyambukiro chake. Mwamunayo anadzimva wachisoni kwenikweni ndi mkhalidwe wake, ndipo makonzedwe a chisudzulowo analekedwa. John tsopano anadzisanthulira mbiri yabwino ndi kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Tsopano nayenso ndi Mkristu ndipo, limodzi ndi mkazi wake, iye akuwuza ena za mbiri yabwino ya Ufumu.
M’masiku ano a kugwa kwa mapindu a ukwati, ambiri amafunikira thandizo limene mbiri yabwino yozikidwa pa Baibulo ikupereka. Mmodzi wa Mboni za Yehova mu Peru anakhala pafupi ndi mkulu wa asilikali ankhondo pamene anali kuwuluka ndi ndege. Iwo anayamba kukambitsirana ndipo mkulu wa asilikaliyo anayamba kulongosola za mavuto ake abanja, kuphatikizapo nsonga yakuti mkazi wake anali womwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa ndipo anali pafupi kumuleka kuti akakwatiwe ndi mwamuna wachichepere. Mboniyo mochenjera inamuwonetsa kuti Baibulo limapereka uphungu wabwino, wamphamvu pa nkhani za banja ndipo kuti linamuthandiza iye mwaumwini kuthetsa mavuto ake abanja.—Aefeso 5:21–6:4.
Mkulu wa asilikaliyo anayamikira Mboniyo kaamba ka mawu ake otonthoza ndi kulembetsa ku magazine a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kotero kuti apititse patsogolo chidziŵitso chake cha mbiri yabwino. Kenaka, pamene Mboniyo inali kutuluka m’ndegemo, okwatirana aŵiri achichepere anamuthamangira ndi kupempha kulankhula naye. “Tinakhala kutsogolo kwanu,” iwo anatero, “ndipo tinamva kukambitsirana kwanu ndi munthu uja. Tingakonde nafenso kulembetsa ku magazine amenewo.” Nawonso anafuna kuphunzira mbiri yabwino imene ingawongolere miyoyo.
Moyo Wosinthidwa
Kuwonjezerapo, mbiri yabwino yozikidwa pa Baibulo imasintha anthu. Monga mmene mtumwi Paulo ananenera kuti: “Pakuti mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” (Ahebri 4:12) Izi zinali zowona mu nkhani ya mwamuna wachichepere wa ku Makedoniya, Grisi. Iye anadabwitsidwa kudziŵa kuti, mogwirizana ndi Baibulo, dzina la Mulungu ndilo Yehova. Chotero anapempha bwenzi kumupezera Mboni za Yehova mwamsanga monga kukathekera. Kukambitsirana kuŵiri kunakonzedwa ndi Mbonizo, kulikonse kukumatenga maola anayi. Mwamuna wachichepereyo anayamba phunziro losamalitsa la Baibulo, loyambirira linatha 2 koloko m’mawa!
Kuchokera m’phunziro loyamba limenelo, mofulumira mwamuna wachichepereyo anagwirizanitsa moyo wake ndi miyezo ya Baibulo. Iye anayamba kupezeka pa misonkhano kaamba ka kulambira ndi Mboni za Yehova ndipo anafikira pa kumkonda Mlengi kwambiri. Ndipo Yehova pambuyo pake anamdalitsa iye. Mlungu woyamba wa phunziro lake la Baibulo, anameta tsitsi lake lalitali. Mlungu wachiŵiri, analeka kupita ku macafé ndi disco kukafuna mabwenzi osangalatsa. Mlungu wachitatu, anataya ndudu yake yomalizira. Pambuyo pophunzira kwa miyezi iŵiri, iye anayamba kutsagana ndi Mboni kukauza ena za mbiri yabwino ya Ufumu. Inde, iye anali wosangalala kuti Mboni za Yehova zinamubweretsera mbiri yabwino ku mbali yake ya dziko lapansi.
Mbiri Yabwino m’Ndende
Ngakhale mipiringidzo ya ndende siiri zoletsa mbiri yabwino. Mu Spain mwamuna wachichepere wotchedwa José akutumikira chilango cha nyengo yaitali chifukwa chakuba ali ndi zida ndi machitidwe ena aupandu. Komabe, Mboni za Yehova zinali zokhoza kumuuza mbiri yabwino, ndipo uthenga wa Baibulo wasinthiratu kawonedwe kake. Yehova ‘anampatsa mphamvu.’—Afilipi 4:13.
José akuti angathere moyo wake wonse m’dongosolo lino la zinthu ali m’ndende chifukwa cha khalidwe lake lakale. Koma iye wabatizidwa ndipo tsopano ndi Mkristu. Mkazi wake akumuchilikiza kwambiri, ndipo akuyesera kupatsa mwana wawo wamwamuna maleredwe Achikristu. Pakali pano, José akugawana mbiri yabwino ndi akaidi anzake, anthu ovuta kufikiridwa ndi awo amene ali kunja kwa malinga a ndende. Tsopano mnzake wa m’lumande ndi Mkristu wobatizidwa.
Izi ziri kokha zitsanzo zoŵerengeka kusonyeza zotulukapo za ndawala ya Mboni za Yehova ya kulalikira kwa dziko lonse. Zowonadi, mbiri yabwino yolalikidwa ndi mngelo wosawoneka yamveketsedwa ndi Mboni za Yehova monga “uthenga wabwino wosatha kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu.”
Iri mbiri yabwino koposa, ndipo ndiyo chiyembekezo chokha cha mtundu wa anthu. Tikukufulumizani kuilabadira. Mofanana ndi Ken ndi John a ku England, mofanana ndi Rafael ndi mkazi wake mu Argentina, mofanana ndi José mu Spain, ndipo mofanana ndi zikwi makumimakumi ena, tikugwirizana ndi mngelo m’kufulumiza onse ‘kuwopa Mulungu ndi kumpatsa ulemerero, pakuti yafika nthaŵi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe a madzi.’—Chibvumbulutso 14:7.