Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 3/15 tsamba 15-20
  • Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuikidwa “Kapitao wa pa Zonse Ali Nazo”
  • “Phoso Lawo pa Nthaŵi Yake”
  • Kuyenga Kopitirizabe
  • Losiyana Ndi Bungwe la Otsogolera
  • Kugwirizana Kokangalika Ndi Bungwe Lolamulira
  • Kodi Ndi Ndani Akutsogolera Anthu a Mulungu Masiku Ano?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
  • Kodi “Kapolo Wokhulupirika Ndi Wanzeru” Ndi Ndani, Nanga Amachita Zotani?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mmene Bungwe Lolamulira Limasiyanirana ndi Bungwe Lalamulo
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 3/15 tsamba 15-20

Kugwirizana ndi Bungwe Lolamulira Lerolino

“Adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo.”​—LUKA 12:44.

1. Kodi ndi mu ufumu uti umene Kristu anayamba kulamulira mu 33 C.E., ndipo kupyolera mwa chiyani?

PA PENTEKOSTE wa 33 C.E., Yesu Kristu, Mutu wa mpingo, anayamba kulamulira mokangalika mu ufumu wa akapolo ake odzozedwa ndi mzimu. Motani? Kupyolera mwa mzimu woyera, angelo, ndi bungwe lolamulira lowoneka ndi maso. Monga mmene mtumwi Paulo anasonyezera, Mulungu ‘analanditsa odzozedwa ku ulamuliro wa mdima nawasamutsa kuwaloŵetsa m’ufumu wa Mwana wa chikondi chake.’​—Akolose 1:13-18; Machitidwe 2:33, 42; 15:2; Agalatiya 2:1, 2; Chibvumbulutso 22:16.

2. Kodi ndi mu Ufumu waukulu uti umene Kristu anayamba kulamulira mu 1914?

2 Pamapeto pa “nthaŵi zoikidwiratu za mitundu,” Yehova anawonjezera ulamuliro waufumu wa Kristu, kuufutukula kupyola malire a mpingo Wachikristu. (Luka 21:24, NW) Inde, m’chaka cha 1914, Mulungu anapatsa Mwana wake ulamuliro waufumu pa “amitundu,” “Ufumu wa dziko lapansi,” mtundu wonse wa anthu.​—Salmo 2:6-8; Chibvumbulutso 11:15.

Kuikidwa “Kapitao wa pa Zonse Ali Nazo”

3, 4. (a) M’fanizo la Yesu la ndalama, kodi ndani amene anaimiridwa ndi munthu wa fuko lomveka? (b) Kodi ndi zochitika Zaufumu zotani zimene zinachitika mu 1918 ndi 1919?

3 Lofunika koposa pano liri fanizo la Yesu la munthu wa fuko lomveka. (Luka 19:11-27) Asanapite paulendo ku dziko lakutali kukafunafuna ulamuliro waufumu, anapatsa akapolo ake ndalama (minas) zogwira nazo ntchito. Atabwerera, mwamuna ameneyu, amene akuimira Kristu, anaitanitsa “akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziŵe umo anapindulira pochita malonda.” (Luka 19:15) Kodi zimenezi zinagwira ntchito motani pambuyo pakuti Yesu wapeza ulamuliro waufumu?

4 Mu 1918 Mfumu Yesu Kristu woikidwa pampando wachifumu anapeza kagulu kakang’ono ka Akristu kamene kanatuluka kale m’matchalitchi a Dziko Lachikristu ndipo kanali kotanganitsidwa kusamalira zabwino za padziko lapansi za Mbuye wawo. Pambuyo powayenga monga ndi moto, Yesu anapatsa akapolo ake ulamuliro wowonjezereka mu 1919. (Malaki 3:1-4; Luka 19:16-19) Iye anawaika iwo “kapitao wa pa zonse ali nazo.”​—Luka 12:42-44.

“Phoso Lawo pa Nthaŵi Yake”

5, 6. (a) Kodi ndi ntchito yokulitsidwa yotani imene mdindo wa Kristu analandira? (b) Kodi ndi maulosi ati amene anali pafupi kukwaniritsidwa itapita 1914, ndipo kodi ndimotani mmene kagulu ka mdindo kanakhalira ndi phande lokangalika m’kukwaniritsidwa kwawo?

5 Mfumu yolamulira Yesu Kristu inapereka ntchito yofutukulidwa kwa mdindo wake, kapena manijala wa nyumba, pa dziko lapansi. Akristu odzozedwa anafunikira kukhala “atumiki” a Mulungu m’malo mwa mfumu yovekedwa chisoti chaufumu yopatsidwa mphamvu kulamulira anthu onse a dziko lapansi. (2 Akorinto 5:20; Danieli 7:14) Thayo lawo la onse pamodzi silinafunikirenso kungokhala lopereka ku gulu la akalinde odzozedwa a Kristu “mulingo wa phoso lawo pa nthaŵi yake.” (Luka 12:42, NW) Iwo anafunikira tsopano kutenga mbali yokangalika m’kugwira ntchito kwa maulosi omwe anafunikira kukwaniritsidwa pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu mu 1914.

6 Kodi izi zinatanthauzanji m’kachitidwe kenikeni? Zinatanthauza kufutukula kulalikira ‘mbiri yabwino imeneyi ya ufumu ku dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.’ (Mateyu 24:14, NW) Kuwonjezerapo, zinatanthauza kufalitsa uthenga wamphamvu wa chiweruzo chotsutsa dongosolo loipa la Satana ndi achirikizi ake. Zimenezi zinali ndi chiyambukiro cha ‘kugwedeza amitundu.’ Chotero, “zofunika,” “nkhosa zina” za Kristu, zinayamba kudza. (Hagai 2:7; Yohane 10:16) Kuyambira mu 1935 kunka mtsogolo, “khamu lalikulu” linayamba kupita ku gulu la Yehova la dziko lonse. (Chibvumbulutso 7:9, 10) Zimenezi zinaitanira kuwongokera kopita patsogolo m’gulu. Kulankhula mophiphiritsira, miyala inafunikira kuloŵedwa m’malo ndi chitsulo, mtengo ndi mkuwa, chitsulo ndi siliva, ndipo mkuwa ndi golidi. (Yesaya 60:17) Zonsezi zachitika chiyambire 1919 pansi pa chitsogozo chokangalika ndi chosamalitsa cha Yesu Kristu, yemwe wapereka zabwino zake zonse Zaufumu za pa dziko lapansi, kapena zinthu, kwa kagulu kake ka kapolo wokhulupirika ndi Bungwe lake Lolamulira.

7. Kodi mathayo owonjezereka a mdindo analoŵetsamo chiyani?

7 Tingamvetsetse mosavuta kuti katundu wowonjezereka ameneyu wa thayo amene ali pa kapolo, mdindo, kapena manijala wa nyumba wa Mbuyeyo anaphatikizapo ntchito yokulira yolemba ndi kukonza. Phoso lauzimu linafunikira kufalitsidwa mokhazikika pa nthaŵi yake mu Nsanja ya Olonda. Mu 1919 The Golden Age (magazine anzake pambuyo pake yodzakhala Consolation, ndipo kenaka Galamukani!) inayamba kufalitsidwa kuti idzutse chidwi cha aunyinji, kuwonjezera pa kumangirira “a pa banja.” (Mateyu 24:45) Unyinji wa mabuku, timabuku, ndi matrakiti atulutsidwanso kwa zaka zonsezi.

Kuyenga Kopitirizabe

8. Kodi ziŵalo za Bungwe Lolamulira poyamba zinazindikiritsidwa ndi chiyani, ndipo kodi ndi ndemanga yotani imene The Watchtower inapanga mu 1944?

8 Kuyang’ana m’mbuyo ku “nthaŵi ya chimaliziro” ino, sitikudabwa kuti ziŵalo za Bungwe Lolamulira poyambapo zinazindikiritsidwa mwathithithi ndi ogwira ntchito ya ukonzi a Watch Tower Society. (Danieli 12:4) Nkhani yakuti “The Theocratic Alignment Today” (Kulungamitsidwa kwa Teokratiki Lerolino), yofalitsidwa mu The Watchtower ya November 1, 1944, inati: “Mwanzeru, awo omwe anaikizidwa kufalitsa zowonadi za Baibulo zovumbulidwa anawonedwa kukhala bungwe lolamulira losankhidwa la Ambuye kutsogoza awo onse omwe anakhumba kulambira Mulungu mumzimu ndi m’chowonadi ndi kumtumikira iye mogwirizana m’kufalitsa zowonadi zovumbulidwa zimenezi kwa ena akumva njala ndi ludzu.”

9. Kodi Bungwe Lolamulira pambuyo pake linadzazindikiritsidwa ndi chiyani, ndipo nchifukwa ninji?

9 Panali ziyeneretso zalamulo zoloŵetsedwamo m’kufalitsa magazine ndi zothandizira zina za phunziro la Baibulo. Chotero, Watch Tower Bible and Tract Society inakhazikitsidwa ndi kulembetsedwa m’boma la Pennsylvania, U.S.A. Kwa zaka zingapo, Bungwe Lolamulira lowoneka ndi maso linadzazindikiridwa ndi bungwe la otsogolera la ziŵalo zisanu ndi ziŵiri la gulu limeneli lokhazikitsidwa kuti lidzifalitsa zothandiza za phunziro la Baibulo zofunikira ndi kugwiritsidwa ntchito ndi anthu a Ambuye pa dziko lonse.

10, 11. Kodi n’kuyenga kotani kumene kunachitika mu 1944, ndipo kodi ndi ndemanga yotani imene inapangidwa ponena za zimenezi mu The Watchtower?

10 Otsogolera asanu ndi aŵiri a Sosaitewo anali Akristu okhulupirika. Koma mbali yawo m’gulu lalamulo ingakhale inasonyeza kuti iwo anali ndi malo awo m’Bungwe Lolamulira m’kukhala osankhidwa ndi ziŵalo zalamulo za Watch Tower Society. Kuwonjezerapo, mwalamulo umembala woterowo ndi mwaŵi wake wakuchita masankho poyambirira unaperekedwa kokha kwa awo amene ankapereka zopereka ku Sosaite. Kakonzedwe kameneka kanayenera kusinthidwa. Zimenezi zinachitidwa pa msonkhano wa pachaka wa gulu la Pennsylvania la Watch Tower Society wochitidwa pa October 2, 1944. Malamulo a Society anawongoleredwa kotero kuti umembala sukakhalanso pamaziko a ndalama. Ziŵalozo zikasankhidwa pakati pa atumiki okhulupirika a Yehova, ndipo izi zaphatikizapo ambiri otumikira nthaŵi zonse pa malikulu a Sosaite mu Brooklyn, New York, ndi m’nthambi zake kuzungulira dziko lonse.

11 Posimba za kuwongolera kumeneku, The Watchtower ya November 1, 1944, inalongosola kuti: “Ndalama, zoimiridwa m’zopereka zachuma, siziyenera kukhala ndi mphamvu yolamula, ndiponso siziyenera kukhala ndi chirichonse chochita ndi kukwaniritsa ziŵalo za bungwe lolamulira la mboni za Yehova pa dziko lapansi. . . . Mzimu woyera, mphamvu yogwira ntchito imene imachokera kwa Yehova Mulungu kupyolera mwa Kristu Yesu, uli umene uyenera kulamula ndi kutsogoza m’nkhaniyo.”

Losiyana Ndi Bungwe la Otsogolera

12. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Yehova anadalitsa kuyengako pansi pa chitsogozo cha Bungwe Lolamulira?

12 Kupita patsogolo kwa ntchito yolalikira mkati mwa zaka makumi otsatira kumatsimikizira kuti Yehova anadalitsa kuyengedwa kumeneku m’kumvetsetsa kwa Bungwe Lolamulira. (Miyambo 10:22) Nkulekeranji, popeza kuti chiŵerengero cha olengeza Ufumu pa dziko lonse lapansi chinakwera kuposa pa ochepera pa 130,000 mu 1944 kufika ku 1,483,430 mu 1970! Koma kuwongolera kowonjezereka kunalinkudza.

13. (a) Kufikira mu 1971, kodi mkhalidwe unali wotani ponena za Bungwe Lolamulira? (b) Kodi nchiyani chimene chinachitika pa msonkhano wapachaka wa Sosaite mu 1971?

13 Kufikira 1971 a Bungwe Lolamulira anali adakali ozindikiritsidwabe ndi ziŵalo zisanu ndi ziŵiri za bungwe la otsogolera la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania. Prezidenti wa Sosaite anali ndi thayo lalikulu lopanga zosankha zokhudza kugwira ntchito kwa nthambi za Sosaite pa dziko lonse. Koma nkhani zopanga mbiri zinaperekedwa pa msonkhano wapachaka wochitidwa pa October 1, 1971. Prezidenti wa Sosaite analankhula pamutu wakuti “Kubweretsa Malo Oyera mu Mkhalidwe Wolondola,” ndipo wachiŵiri kwa prezidenti pankhani yakuti “Bungwe Lolamulira Monga Losiyana ndi Gulu la Lamulo.” Kodi ndi kusiyana kotani kumene kulipo pakati pa Bungwe Lolamulira ndi gulu la lamulo?

14. Kodi ndi kusiyana kotani kumene kulipo pakati pa gulu la lamulo ndi Bungwe Lolamulira?

14 Monga tanenera kale, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania iri ndi bungwe la otsogolera lokhala ndi chiŵerengero cholekezera pa ziŵalo zisanu ndi ziŵiri. Amuna odzipatulira Achikristu ameneŵa amasankhidwa kwa nyengo ya zaka zitatu ndi ziŵalo za gululo zofika ku osaposa pa 500, ambiri a ameneŵa sali Akristu odzozedwa. Kuwonjezerapo, popeza kuti kukhalapo kwa gululo kuli m’chenicheni kwalamulo, kokhala ndi malikulu oikidwa m’dziko limodzi, lingathetsedwe ndi Kaisara, uku ndiko kuti, Boma. (Marko 12:17) Komabe, Bungwe Lolamulira siliri chiwiya chalamulo. Ziŵalo zake sizimasankhidwa. Izo zimaikidwa kupyolera mwa mzimu woyera pansi pa chitsogozo cha Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu. (Yerekezerani ndi Machitidwe 20:28.) Ndiponso, awo opanga Bungwe Lolamulira ali amuna oikidwa ndi mzimu popanda malo oikiridwa mwalamulo a dziko kapena malikulu.

15. Kodi ndi ndemanga yotani yonena za kulinganiza imene imapangidwa mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1972, ndipo nchiyani chimene chinganenedwe ponena za Bungwe Lolamulira lamakono?

15 Ponena za kuyenga koteroko m’kumvetsetsa, Nsanja ya Olonda ya May 15, 1972, inanena kuti: “Mothokoza mboni Zachikristu za Yehova zimadziŵa ndipo zimavomereza kuti siliri konse gulu lachipembedzo la munthu mmodzi, koma kuti ilo liri ndi bungwe lolamulira la Akristu odzozedwa ndi mzimu.” Bungwe Lolamulira la kagulu ka kapolo wodzozedwa ndi anzawo mamiliyoni angapo pakati pa nkhosa zina lalinganizidwa mopita patsogolo kutenga chisamaliro cha ntchito yake ya uyang’aniro.

16. Kodi ndimotani mmene zinthu zapadziko lapansi za Kristu zinawonjezekera chiyambire 1971, ndipo ena a ameneŵa ndani kwa amene waikiza chisamaliro cha kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, woimiridwa ndi Bungwe lake Lolamulira?

16 Zinthu zapadziko lapansi za Mfumu Yesu Kristu zapitirizabe kukula. Chiyambire 1971 chiŵerengero cha Mboni chawonjezeka kuchoka pa ochepera pa 1,600,000 kufika ku chiŵerengero chapamwamba choposa pa 3,700,000 mu 1989. Ndi umboni wotani nanga wa dalitso la Mulungu! (Yesaya 60:22) Kukula kumeneku kwatheketsa kufutukulidwa kwa zimango pa malikulu a Sosaite ndi m’nthambi zake, limodzinso ndi kupanga njira za kupanga zinthu ndi kuzigaŵira kukhala zamakono. Izi zatulukapo m’kumanga Nyumba Zaufumu zambiri ndi Nyumba Zosonkhaniramo kuzungulira dziko lonse lapansi. Nthaŵi yonseyi, Bungwe Lolamulira lakhala likupitirizabe kutenga thayo la kuyang’anira ntchito yolalikira, ya kupanga ziwiya zothandizira phunziro la Baibulo, ndi kuika oyang’anira m’nthambi, zigawo, madera, ndi mipingo. Izi ndizo zabwino Zaufumu zimene Kristu waika ku chisamaliro cha kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, woimiridwa ndi Bungwe lake Lolamulira.

17. Kodi ndi kuwongolera kowonjezereka kwa uyang’aniro kotani kumene kunapangidwa mu 1971, 1974, ndi 1976?

17 Bungwe lolamulira la zaka za zana loyamba linakulitsidwa kuphatikizapo oposa atumwi a Yesu. Pamene nkhani ya mdulidwe inalingaliridwa, mwachiwonekere bungwe limenelo linaphatikizapo ‘atumwi ndi akulu a ku Yerusalemu.’ (Machitidwe 15:1, 2) Moyerekezera, Bungwe Lolamulira linakulitsidwa mu 1971 ndipo kachiŵirinso mu 1974. Kotero kuti lipeputse ntchito yawo ya uyang’aniro, Bungwe Lolamulira linakonzekera makomiti asanu kuyamba kugwira ntchito pa January 1, 1976. Komiti iriyonse imapangidwa ndi ziŵalo zitatu kufika ku zisanu ndi mmodzi, onsewo okhala ndi mphamvu yofanana m’nkhani zomwe zikulingaliridwa. Tcheyamani wa komiti iriyonse amatumikira kwa chaka chimodzi, ndipo chiŵalo chirichonse cha Bungwe Lolamulira chimatumikira mu imodzi kapena angapo a makomiti ameneŵa. Iriyonse ya makomiti asanu ameneŵa imapereka chisamaliro chapadera ku mbali yachindunji ya zinthu za Kristu zapadziko lapansi. Komiti yachisanu ndi chimodzi​—Komiti ya Tcheyamani, imene ziŵalo zake zimasintha chaka chirichonse, imasamalira mavuto a mwamsanga.

Kugwirizana Kokangalika Ndi Bungwe Lolamulira

18. Kodi ndimotani mmene Bungwe Lolamulira limagwirira ntchito, ndipo kodi ndinjira imodzi iti imene tingasonyezere kugwirizana nalo kwathu?

18 Makomiti a Bungwe Lolamulira amakumana mlungu ndi mlungu kubwereramo m’nkhani zofunika, ndi kupanga zosankha pambuyo pa kulingalira kwapemphero, ndi kukonzekera kaamba ka ntchito yateokratiki ya mtsogolo. Monga kwasonyezedwa kale, Machitidwe mutu 15 ukusonyeza kuti funso lalikulu lofunikira chigamulo linalozeredwa ku bungwe lolamulira la zaka za zana loyamba kaamba ka chisamaliro. Mofananamo lerolino, mafunso ofunika amalozeredwa ku Bungwe lonse Lolamulira, limene limakumana mlungu ndi mlungu kapena mobwerezabwereza pamene kuli kofunika. Ziŵalo za Bungwe Lolamulira, pa nthaŵi ino zomwe ziri zokwanira 12, zimafunafuna chitsogozo cha Yehova Mulungu kupyolera m’Malemba ndi kugwiritsira ntchito pemphero. Njira imodzi imene timasonyezera kugwirizana kwathu ndi Bungwe Lolamulira iri mwa kukumbukira oikidwa mwapadera ameneŵa m’mapemphero athu a tsiku ndi tsiku.​—Aroma 12:12.

19. Kodi ndimotani mmene malangizo a Bungwe Lolamulira amafikira mipingo?

19 Kodi malangizo ndi zosankha za Bungwe Lolamulira zimafikira motani mipingo? Pambuyo pakuti ziŵalo za bungwe lolamulira la zaka za zana loyamba lafikira chosankha chawo ndi thandizo la mzimu wa Mulungu, iwo anatumiza kalata ku mipingo. (Machitidwe 15:22-29) Komabe, njira yaikulu masiku ano iri mwa mabuku Achikristu.

20. (a) Kodi ndi kuyenga kowonjezereka kwa gulu kotani kumene kunapangidwa mu 1976? (b) Kodi ndimotani mmene Makomiti a Nthambi amagwirizanirana ndi Bungwe Lolamulira?

20 Kuyambira pa February 1, 1976, iriyonse ya nthambi za Watch Tower Society yakhala ndi Komiti ya Nthambi yopangidwa ndi amuna ofikapo oikidwa ndi Bungwe Lolamulira. Monga oimira a Bungwe Lolamulira a dziko kapena maiko okhala pansi pa uyang’aniro wa ntambi yawo, abale ameneŵa ayenera kukhala amuna okhulupiririka, odalirika. Zimenezi zimatikumbutsa za amuna ofikapo, owopa Mulungu, okhulupirika amene anathandiza Mose kuweruza anthu mu Israyeli wakale. (Eksodo 18:17-26) Ziŵalo za Komiti ya Nthambi zimagwiritsira ntchito malangizo olandiridwa kupyolera m’mabuku ndi magazine a Sosaite ndi Utumiki Wathu Waufumu, limodzinso ndi makalata achisawawa ndi makalata apadera ochita ndi mavuto a kumaloko. Makomiti a Nthambi amadziŵitsa Bungwe Lolamulira za kupita patsogolo kwa ntchito m’dziko lirilonse ndi mavuto aliwonse omwe angabuke. Malipoti oterowo olandiridwa kuchokera ku dziko lonse amathandiza Bungwe Lolamulira kusankha nkhani zimene zingalingaliridwe m’mabuku a Sosaite.

21. Kodi oyang’anira oyendayenda amaikidwa motani, ndipo kodi mathayo awo amaphatikizapo chiyani?

21 Pansi pa chitsogozo cha mzimu woyera, Makomiti a Nthambi amayamikira amuna achikulire, auzimu kutumikira monga oyang’anira amadera ndi achigawo. Pamene aikidwa mwachindunji ndi Bungwe Lolamulira, amatumikira monga oyang’anira oyendayenda. Abale ameneŵa amachezera madera ndi mipingo ndi cholinga chofuna kuwamangirira iwo mwauzimu ndi kuwathandiza kugwiritsira ntchito malangizo olandiridwa kuchokera ku Bungwe Lolamulira. (Yerekezerani ndi Machitidwe 16:4; Aroma 1:11, 12.) Oyang’anira oyendayenda amatumiza malipoti ku ofesi ya nthambi. Ndi thandizo la mzimu woyera ndi Malemba owuziridwa, iwo amagawana ndi akulu a kumaloko m’kuyamikira abale oyeneretsedwa kuikidwa monga atumiki otumikira ndi akulu ndi Bungwe Lolamulira kapena ndi oimira ake.​—Afilipi 1:1; Tito 1:5; yerekezerani ndi 1 Timoteo 3:1-13; 4:14.

22. (a) Kodi akulu a mpingo amagwirizana motani ndi Bungwe Lolamulira? (b) Kodi nchiyani chimene chikutsimikizira kuti Yehova akudalitsa kakonzedwe kateokratiki kameneka?

22 Pambuyo pake, awo opanga mabungwe a akulu ‘amadzipenyerera ndi gulu lonse, pakati pa limene mzimu woyera wawaika oyang’anira.’ (Machitidwe 20:28, NW) Oyang’anira ameneŵa amafuna mokhulupirika kugwiritsira ntchito malangizo olandiridwa kuchokera kwa Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu kupyolera mwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndi Bungwe lake Lolamulira. Yehova akudalitsa kakonzedwe kateokratiki kameneka, popeza kuti ‘mipingo ikulimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nichuluka m’chiŵerengero chawo tsiku ndi tsiku.’​—Machitidwe 16:5.

23. Ponena za Bungwe Lolamulira, kodi tiyenera kugamulapo kuchita chiyani?

23 Nchabwino chotani nanga kuti kupyolera mwa Bungwe Lolamulira, Yehova Mulungu ndi Mbuyeyo, Yesu Kristu, akusonyeza kuchirikiza anthu a Mulungu! (Salmo 94:14) Monga mbali ya gulu la Yehova, aliyense wa ife amapindula ndi chilikizo loterolo. (Salmo 145:14) Zimenezi ziyenera kulimbitsa chigamulo chathu cha kugwirizana ndi makonzedwe a Mulungu. Ndithudi, lolani kuti nthaŵi zonse tipezedwe tikugwirizana ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova pamene tikupita patsogolo ku nthaŵi imene “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”​—Yesaya 11:9.

Nsonga Zazikulu Zofunika Kukumbukira

◻ Kodi ndi mathayo owonjezeka otani amene gulu la kapolo linalandira mu 1919?

◻ Kwa zaka zambiri, kodi Bungwe Lolamulira lowoneka ndi maso linazindikiritsidwa ndi chiyani?

◻ Kodi ndi kuwongolera kopita patsogolo kotani kumene kunapangidwa m’kuikidwa kwa ziŵalo za Bungwe Lolamulira?

◻ Kodi ndi ati amene ali ena zinthu zapadziko lapansi za Kristu amene wawaikiza kwa kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndi Bungwe lake Lolamulira?

◻ Kodi tingagwirizane motani ndi Bungwe Lolamulira?

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Kuchokera ku malikulu ake a dziko mu Brooklyn, New York, Bungwe Lolamulira limayang’anira ntchito yofalitsa ndi kulalikira ya Mboni za Yehova mu nthambi 93 za Watch Tower Society

Germany

Japan

South Africa

Brazil

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena