Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 4/1 tsamba 7-10
  • Kodi Adzatsogolera Anthu ku Mtendere Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Adzatsogolera Anthu ku Mtendere Ndani?
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoposa Ziyeneretso Zaumunthu
  • Njira za Kumtendere
  • Njira Yotsatira
  • Dziko Pamtendere
  • Chiyembekezo Cholimba
  • Lolani “Mtendere wa Mulungu” Uchinjirize Mtima Wanu
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mtendere Weniweni—Kodi Udzachokera Kuti?
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Funafunani Mtendere Weniweni ndi Kuulondola!
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kodi Nliti Pamene Mtendere Wokhalitsa Udzabweradi?
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 4/1 tsamba 7-10

Kodi Adzatsogolera Anthu ku Mtendere Ndani?

KODI chenicheni chakuti anthu sangadzetse mtendere chimatanthauza kuti sitidzawona konse mtendere? Ayi. Monga momwedi Satana, amene ali wamphamvu kwambiri kutiposa, ndiye chopinga chachikulu cha mtendere padziko lapansi, chotero pali Uyo wamphamvudi kwambiri kuposa Satana amene potsirizira pake adzatsogolera anthu ku mtendere. Baibulo, limene limatiwuza za Satana, limatiwuzanso za Ameneyu. Ilo limati: “Ulamuliro udzakhala paphewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate wosatha, kalonga wamtendere.” (Yesaya 9:6, 7) Kodi Kalonga Wamtendere ameneyu ndani? siwina koma Yesu Kristu, ndipo iye angathe kubweretsa mtendere chifukwa chakuti ngoyeneretsedwa kwambiri kutiposa. Mwanjira zotani?

Zoposa Ziyeneretso Zaumunthu

Choyamba, Yesu ngosakhoza kufa, sangafe. Nzowona, kuti anakhala ndi moyo monga munthu naafa imfa yopereka nsembe. Komatu iye anaukitsidwira ku moyo wosakhoza kufa kumwamba, ndipo uli mkalidwe umenewu chakuti amakhala Kalonga Wamtendere. Ndicho chifukwa chake ulosiwo umati: “Ufumu wake sudzatha.” (Luka 1:32, 33) Mosiyana ndi mfumu Yakummawa Aśoka, Yesu adzakhala ndi moyo kosatha kutsimikizira kuti ntchito yake yabwino sikuwonongedwa ndi omloŵa mmalo osanunkha kanthuwo.

Ndiponso, Yesu ngwosakhathamira ndi uchimo. Ulamuliro wake ngwozikidwa pa nzeru yaumulungu ndi malamulo amakhalidwe abwino olungama. Mneneri Yesaya adaneneratu kuti: “Mzimu wa Yehova udzam’balira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziŵa ndi wakuwopa Yehova . . . Sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera koma ndi chilungamo adzaweruza aumphaŵi, nadzadzudzulira ofatsa amdziko owongoka.” (Yesaya 11:2-4) Mosiyana ndi a Kuulaya amake dzana, Yesu sadzasunga mtendere kwao kokha nakachita nkhondo ku maiko achilendo. Mtendere wapadziko lonse lapansi, udzakhala pansi pake.

Kuwonjezera apa, Yesu ali ndi mphamvu ya kudzetsa mtendere. Ulosiwo umati: “Mzimu wa Yehova . . . mzimu wauphungu ndi mphamvu,” uli pa iye. Mzimu umenewu unachititsa kulengedwa kwa chilengedwe kudzanso ntchito zamphamvu zonse za chilungamo zosimbidwa m’Baibulo. Ngakhale wotsutsa wamkulu, Satana, alibe chida chimene chidzatsutsa mwachipambano mphamvu ya mzimu wa Mulungu.

Njira za Kumtendere

Kodi Yesu adzatsogolera motani anthu ku mtendere? Inu mungadabwe kudziŵa kuti iye wayamba kale. Bukhu laulosi la Chivumbulutso, Yesu akuwonedwa kulandira kuchokera kwa Mulungu ulamuliro mu Ufumu wa kumwamba. (Chivumbulutso 11:15) Ngati ife tipenda mosamalitsa maulosi a Baibulo ndi kuwayerekezera ndi zochitika m’zaka za zana lathu, tikuwona kuti kuikidwa pampando wachifumu kwa Yesu monga Mfumu kunachitika kalelo m’mwamba mu 1914. (Mateyu 24:3-42) Imeneyo inali njira yaikulu mkudzetsa mtendere kudziko lapansi.

Komabe, ngati zimenezo ziri choncho, kodi nchifukwa ninji Nkhondo Yadziko I inaulika mu 1914? Ndipo kodi nchifukwa ninji zaka za zana lathu zakhala ndi nkhondo zoipa kwambiri kuposa nthawi ina iriyonse m’mbiri? Chifukwa chakuti chochita choyamba cha Mfumu ya kumwamba chinali kuchotsa Satana ku umuyaya wonse kuchokera kumiyamba ndi kum’ponyera pansi m’chigawo cha dziko lapansi. N’chotulukapo chotani? Ulosiwo umati: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdierekezi watsikira kwa inu wokhala nawo udani waukulu podziŵa kuti kam’tsarira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:7-12) Nkhondo zazikulu za zaka za zana lathu zikuchititsidwa ndi mkwiyo wa Satana. Komatu tawonani: mkwiyo wa Satana uli ‘wakanthaŵi.’ Vutolo lidzatha msanga!

Komabe, lisanathe, Kalonga Wamtendere akupanga zikonzekero zina zofunika za mtendere. Choyamba, anthu afunikira kudziŵa chifuno cha Mulungu chakudzetsa mtendere kudzera mwa Kristu. Mogwirizana ndi izi, Yesu analosera kuti m’nthaŵi yathu “uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse.” (Mateyu 24:14) M’kukwaniritsidwa kwa ulosiwu, uthenga wabwino ukulalikidwa lerolino ndi Mboni za Yehova m’ngondya iriyonse ya chiwundachi.

Pamenepa, anthu owona mtima afunikira kuphunzitsidwa njira zamtendere. Baibulo limalonjeza kuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13) Mamiliyoni ambiri aanthu owongoka mtima akulandira maphunziro amenewa ngakhale tsopano.

Njira Yotsatira

Tsopano iri pafupifupi nthaŵi ya njira ina yotsimikizirika m’makonzedwe a mtendere. Kodi imeneyo nchiyani? Ndiyo imene ambiri amadziŵa mwa dzina koma ochepekera amadziŵa chifuno chenicheni. Baibulo limaitcha “nkhondo ya tsiku lalikulu la tsiku la Mulungu wamphamvuyonse,” kapena Armagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Ambiri amalingalira Armagedo kukhala nkhondo ya nyukliya imene idzawononga kutsungula. Mosiyana ndi zimenezo, ndiyo chochita chachindunji cha Yesu, Kalonga Wamtendere, kukwaniritsira zinthu zimene ziri zofunika kaamba ka mtendere.

Choyamba, Armagedo idzachotsa zopinga zaumunthu zonse zamtendere. Ulosiwo pa Salmo 37:10 umati: “Katsala kanthaŵi ndipo oipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe.” Inde, Yesu adzachotsa “oipa”​—ochita nkhondo, apandu, zigawenga, kudzanso onse amene amakana kuvomereza Kalonga Wamtendere wamkulu​—padziko lapansi. Iwo sadzakhalanso ndi kuyenera kwina kwa kupitirizabe kukhala pa planeti lino.​—Chivumbulutso 19:19-21.

Chachiŵiri, pa Armagedo ulosi wa Danieli uwu udzakwaniritsidwa: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka kunthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Malire autundu amene kaŵirikaŵiri achititsa nkhondo adzathetsedwa. Pomalizira pake, padzakhala boma ladziko pansi pa wolamulira amene tingadalire!

Kodi Armagedo idzadza liti? Baibulo silimanena. Koma zochitika zadziko m’kukwaniritsidwa kwaulosi zikusonyeza kuti idzadza mwamsanga kwambiri. Baibulo limalosera momvekera bwino chochitika chimene chidzakhala kalambula bwalo wa mwamsanga. Mtumwi Paulo akuti: “Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera.” (1 Atesalonika 5:3) Pamenepa, mwamsanga pambuyo pa chiwonongeko cha mwadzidzidzi chimene kaindeinde wake ali Armagedo, chopinga chachikulu koposa cha mtendere chidzakhala chitachotsedwa. “Kanthaŵi” ka Satana kadzakhala katatha, ndipo iye adzaikidwa mumkhalidwe umene sangathenso kuchititsa vuto pano padziko lapansi. (Chivumbulutso 20:1-3) Ndi chitonthozo chotani nanga!

Dziko Pamtendere

Tayerekezerani mkhalidwewo panthaŵiyo. Wamasalmo analosera kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:11) Ofatsa amenewa adzapitirizabe kukwaniritsa ulosi wokongola wa Yesaya wakuti: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”​—Yesaya 2:4.

Potsirizira pake, kwa nthaŵi yoyamba chiyambire mu Edeni, anthu onse amoyo adzasangalala ndi dalitso la Yehova Mulungu, ndipo iye adzakwaniritsa lonjezo lake lakuti: “Tawonani, chihema cha Mulungu chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalnso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Chiyembekezo Cholimba

Pamenepa, kodi ndani, adzatsogolera anthu ku mtendere? Yesu Kristu, Kalonga Wamtendere woikidwayo. Kodi chimenechi chiri chiyembekezo chogwira ntchito kwa ife lerolino? Eya, ngati malonjezo a Baibulo anali osadalilika, sipakanakhala chiyembekezo chenicheni cha mtendere. Anthu akanapitirizabe kumenyana ndi kuphana mosayembekezera kutha. Komatu Baibulo liri lodalirika, ndipo Ufumu wa Mulungu pansi pa Kristu udzadzetsa mtendere. Tikukulimbikitsani kumvetsera mbiri yabwino ya Ufumuwo imene Mboni za Yehova zimabweretsa panyumba panu ndi kudziwonera nokha. Pamenepa, pamene nthaŵizo zidza, mukhaletu pakati pa ofatsawo amene adzalandira dziko lapansi nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.

Chiyembekezo cha mtendere chokambitsiridwa m’nkhani ino chachokera m’Baibulo. Lerolino, pamene ambiri sakukhulupiriranso Baibulo, inu mungakaikire ngati chiyembekezo chimenechi chiri chothandiza. Mboni za Yehova zimakhulupirira mwamphamvu kuti icho chiri. Izo zimavomereza Baibulo kukhala Mawu ouziridwa a Mulungu, chifukwa chake monga lodalirika kotheratu. Mu 1989 izo zinafalitsa bukhu lotchedwa The Bible​—God’s Word or Man’s? lopereka maumboni ambiri a chenicheni chimenechi. Mawu ena a m’bukhu limenelo akambitsiridwa m’nkhani ziŵiri zotsatira, zimene tikukupemphani kuti muŵerenge.

Mawu owonjezereka onena za lonjezo la Baibulo lamtendere adzawonekera m’nkhani yakuti “Mtendere Wadziko Lonse​—Kodi kwenikweni Uwo Udzatanthauzanji?” imene idzatulutsidwa m’kope la April 15, 1990 la Nsanja ya Olonda.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Yesu yekha ali ndi ziyeneretso zakutsogolera anthu ku mtendere

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Lerolino, mbiri yabwino ya Ufumu ikulalikidwa m’ngondya iriyonse ya chiwundachi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena