Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
◼ Kodi ndiliti pamene kuombedwa kwa malipenga asanu ndi aŵiri a Chivumbulutso kunayamba kumveka?
Mu Chivumbulutso mitu 8, 9, ndi 11, timaŵelenga za angelo asanu ndi aŵiri amene anawomba malipenga asanu ndi aŵiri, akumalalikira milili yaikulu kwambiri pa mbali za anthu. Uku kumaimira kulengezedwa kwa ziweruzo za Yehova zimene zakhala zikulengezedwa ndi anthu a Yehova m’nthŵi yonse yamapeto kuyambiradi ndi msonkhano wa mu 1922 pa Cedar Point.—Wonani Revelation—Its Grand Climax At Hand!, mitu 21 mpaka 23 ndi mutu 26.
Kuwombedwa kwa malipenga anayi oyambirira kumavumbula mkhalidwe wakufa mwauzimu wa mbali ya “dziko lapansi” ndi “nyanja” ya Chikristu Chadziko, limodzinso ndi mkhalidwe wakugwa wa atsogoleri achipembedzo ndi mdima wauzimu wa Chikristu Chadziko.—Chivumbulutso 8:7-12.
Mbiri yakale imasonyeza kuti kuvumbulidwira poyera kwa zenizenizi kunayambika kwenikweni 1922 isanafike. Mwachitsanzo, nkhani yakuti “Mamiliyoni Omwe ali Moyo Tsopano Sangafe Konse,” choyamba yoperekedwa mu 1918 ndi kufalitsidwa mumpangidwe wa kabukhu mu 1920, inasimba za kulephera kwa Chikristu Chadziko ndi mapeto oyandikira adziko lino. The Golden Age ya September 29, 1920, inavumbula poyera Chikristu Chadziko kukhala chachigololo, cha bodza lamkunkhuniza, ndi chosokeretsa anthu.
Pamenepa, kodi nchifukwa ninji bukhu la Revelation Climax limanena kuti malipenga anayi amenewa anayamba kokha kuombedwa pamsonkhano wa pa Cedar Point mu 1922? Chifukwa chakuti panali panthaŵiyo pamene chiitano chinafalitsidwa chakuti “lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi Ufumuwo,” chikumaika chigogomezero chokulira ku ntchito yolalikira. Kope la November 1, 1922, la Watch Tower, linati: “Mabwenzi . . . anailingalira kukhala nkhani yaikulu ya msonkhano kuti mwayi weniweni ndi ntchito ya odzipereka omwe tsopano ali padziko lapansi ndiyo kulengeza kukhalapo kwa Ambuye, Mfumu yaikulu ya mafumu, ndikuti ufumu wake uli pano, ndikuti ichi ndicho chinthu chofunika koposa chakuti iwo achite.”
Kuyeneranso kudziŵidwa kuti pamene kuli kwakuti mauthenga achiweruzo onse anayiwo alengezedwa ndi Mboni za Yehova chiyambire 1922, uliwonse motsatizana ndi wina unalandira chigogomezero champhamvu kuyambira pa kulandiridwa kwa zitsimikiziro zinayi pa misonkhano yochitidwa pakati pa 1922 ndi 1925. Makope makumi mamiliyoni ambiri a zitsimikiziro pambuyo pake anagaŵiridwa mumpangidwe wosindikizidwa, akumavumbula mwamphamvu mkhalidwe wakufa mwauzimu wa Chikristu Chadziko.—Wonani bukhu la Revelation Climax, tsamba 133, ndime 15.
Kuombedwa kwa malipenga otsirizira atatu kukuphatikizapo “masoka.” (Chivumbulutso 8:13) Iwo ngosiyana ndi kuombedwa kwa malipenga anayi oyambirira m’chakuti iwo amasonya ku zochitika zenizeni. Kuombedwa kwachinayi kwa lipenga nkogwirizanitsidwa ndi kumasulidwa kwa anthu a Mulungu mu 1919 kutuluka “m’phompho.” Kwachisanu ndi chimodzi kukuphatikizapo “apakavalo” ndi mkupiti wa kulalikira kwadzawoneni m’mitundu yonse umene unayambira mu 1922. Kwachisanu ndi chiŵiri kwagwirizanitsidwa ndi kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu mu 1914.—Chivumbulutso 9:1-19; 11:15-19.
Chirichonse cha zochitikazi chinabweretsa tsoka kwa Satana ndi dziko lake. Kumasulidwa kwa otsalira mu 1919 kutuluka m’phompho ya kusagwira ntchito kunavutitsa atsogoleri a Chikristu Chadziko ndipo kunasonyeza kukanidwa kwake kotheratu ndi Yehova. Kuyambira mu 1922 kudzafika lerolino, ankhondo apakavalo ochulukirawo apha Chikristu Chadziko, kunena mwauzimu, kuvumbula mkhalidwe wake wakufa ndi kuchenjeza za chiwonongeko chake chirinkudza. Ndipo pambuyo pa kubadwa kwa Ufumu mu 1914, Satana anapitikitsidwa kumwamba, akumayambitsa vuto loipitsitsa pa anthu. Posachedwapa Ufumuwo udzachotsa chitaganya cha anthu chowonekera kukhala chokhazikikachi chimene Satana wamanga (dziko lapansi), kuchotsa anthu oipa (nyanjayo) pa Armagedo.—Chivumbulutso 11:17–12:12; 21:1.
Pamsonkhano wa pa Cedar Point mu 1922, “masoka” onse atatu anawonekera padziko lonse lapansi. Mkupiti wolalikira woyambitsidwa panthaŵiyo unachimveketsa kuti “dzombe” linali litatuluka “m’phompho” ndipo ntchito ya “apakavalo” inkachitika. Ndipo chiitano chochititsa nthumanzi cha kulengeza Mfumu ndi Ufumu chinagwirizana ndendende ndi kuombedwa kwa lipenga lachisanu ndi chiŵiri. Kope la Nsanja ya Olonda, ya March 1, 1925, linalongosola kuti zochitika mu 1914, 1919, ndi 1922 zinanenedweratu mu Chivumbulutso mutu 12. Uku kunali kudziŵika kwa kuya kwambiri kwa kubadwa kwa Ufumu, ndipo kunafalitsidwa mokhulupirika ndi Mboni za Yehova. Kuwonjezera apa, kulengezedwa kwa mawu okantha amenewa kunakhala ndi chigogomezero chokulira kuyambira pa kulandiridwa kwa zitsimikiziro ndi kugaŵiridwa kwa pambuyo pake pamsonkhano wochitidwa kuyambira mu 1926 mpaka mu 1928.—Wonani Revelation—Its Grand Climax At Hand!, masamba 147, 149, 172.
Chotero, kuombedwa kwa malipenga asanu ndi aŵiri kunayambira mu 1922 ndipo kunadzapitirizidwa bwino lomwe m’ma 1920. Chiyambire nthaŵiyo, anthu a Yehova agwirizana ndi angelo mopanda mantha m’kuuza anthu onse kuti Chikristu Chadziko nchakufa mwauzimu, atsogoleri ake achipembedzo ali atsogoleri akugwa, ndipo posachedwapa icho ndi dziko lonse lotsala lasatana adzawonongedwa.