Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w90 4/15 tsamba 8-9
  • Anamwali Anzeru ndi Opusa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anamwali Anzeru ndi Opusa
  • Nsanja ya Olonda​—1990
  • Nkhani Yofanana
  • Kuunika Kaamba ka “Mapeto a Dongosolo la Zinthu”
    Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Fanizo la Anamwali Limatiphunzitsa Kufunika Kokhala Tcheru
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kudikira Mkati mwa “Mapeto a Dongosolo la Zinthu”
    Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Chizindikiro cha Masiku Otsiriza
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda​—1990
w90 4/15 tsamba 8-9

Moyo ndi Uminisitala za Yesu

Anamwali Anzeru ndi Opusa

YESU amayankha pempho la atumwi ake kaamba chizindikiro cha kukhalapo kwake m’ulamuliro wa Ufumu. Tsopano iye akupereka mbali zowonjezereka za chizindikirocho m’miyambi itatu, kapena mafanizo.

Kukwaniritsidwa kwa fanizo lirilonse kukawonedwa ndi awo okhala ndi moyo m’nthaŵi ya kukhalapo kwake. Iye akudziŵikitsa fanizo loyamba ndi mawu awa: “Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zawo, natuluka kukakomana ndi mkwati. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera.”

Mwa mawu akuti “Ufumu wa Kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi,” Yesu sakutanthauza kuti theka la awo oloŵa Ufumu wakumwamba ali anthu opusa ndipo theka ali ochenjera! Ayi, koma akutanthauza kuti m’chigwirizano ndi Ufumu wakumwamba, pali mbali yonga iyi kapena ija, kapena kuti chimene chiri chofunika ponena za Ufumu chidzakhala chonga chakuti chakuti.

Anamwali khumiwo akuphiphiritsira Akristu onse amene ali pa mzera kapena amene akudzinenera kukhala pa mzera kaamba ka Ufumu wakumwamba. Panali pa Pentekoste wa 33 C.E. pamene mpingo Wachikristu unalonjezedwa kukwatiwa kwa Mkwati woukitsidwa, wolemekezedwayo, Yesu Kristu. Koma ukwatiwo unayenera kuchitikira kumwamba pa nthaŵi yamtsogolo yosadziŵitsidwa.

M’fanizolo, anamwali khumiwo akupita ndi cholinga chokalandira mkwati ndi kugwirizana ndi operekeza ukwati. Pamene iye afika, iwo adzawunikira njira yopitamo aukwati ndi nyali zawo, mwakutero kumlemekeza pamene akubweretsa mkwatibwi wake ku nyumba yokonzedwera iye. Komabe, Yesu akulongosola kuti: “Opusawo, m’mene anatenga nyali zawo, sanadzitengeranso mafuta; koma anzeruwo anatenga mafuta m’nsupa zawo, pamodzi ndi nyali zawo. Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anaodzera, nagona tulo.”

Kuchedwa kotalika kwa mkwati kumeneko kumasonyeza kuti kukhalapo kwa Kristu monga Mfumu yolamulira kuli patali mtsogolo. Pomalizira pake akubwera ku mpando wake wachifumu m’chaka cha 1914. Mkati mwa usiku wautali iye asanafike, anamwali onse akugona tulo. Koma iwo sakukanidwa kaamba ka chimenechi. Kukanidwa kwa anamwali opusa kuli kaamba ka kukhala kwawo opanda mafuta m’supa zawo. Yesu akufotokoza mmene anamwaliwo akugalamukira mkwatiyo asanafike:

“Pakati pa usiku panali kufuula, Onani, mkwati! tulukani kukakomana naye. Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zawo. Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zirikuzima. Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.”

Mafutawo akuphiphiritsira chija chimene chimakhalitsa Akristu owona kuwala monga zowunikira, ndicho, Mawu ouziridwa a Mulungu, pa amene akugwira mwamphamvu, pamodzi ndi mzimu woyera, umene umawathandiza kumvetsetsa Mawuwo. Mafuta auzimu amakhozetsa kagulu ka anamwali ochenjera kuunikira polandira mkwati pamene akupita ku phwando la ukwati. Koma gulu la anamwali opusa alibe mwa iwo, m’nsupa zawo, mafuta auzimu ofunikira. Chotero Yesu akulongosola zimene zikuchitika:

“Pamene [anamwali opusa] analikumuka kukagula [mafuta], mkwati anafika; ndipo okonzekawo analoŵa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo. Koma pambuyo pake anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife. Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziŵani.”

Pambuyo pa kufika kwa Kristu mu Ufumu wake wakumwamba, kagulu ka anamwali ochenjera ka Akristu odzozedwa enieni kanagalamukira ku mwaŵi wawo wapadera wa kuwunikira m’dziko lino lamdima m’chitamando cha kubweranso kwa Mkwati. Koma aja ochitiridwa chithunzi ndi anamwali opusa anali osakonzekera kupereka chitamando cholonjera chimenechi. Chotero pamene nthaŵi ifika, Kristu sakuwatsegulira khomo lopita ku phwando laukwati kumwamba. Iye akuwasiya kunja ku mdima wadziko wa ndiwe yani, kuti awonongeke limodzi ndi onse ochita kusayeruzika. Yesu akumaliza kuti: “Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.” Mateyu 25:1-13.

◆ Kodi ndani amene akuphiphiritsiridwa ndi anamwali khumiwo?

◆ Kodi lonjezo lokwatiwa kwa mkwatiyo likupangidwa liti, koma kodi nliti pamene iye afika kudzatengera mkwatibwi wake ku phwando la ukwati?

◆ Kodi mafuta akuimira chiyani, ndipo kodi kukhala nawo kumakhozetsa anamwali ochenjerawo kuchitanji?

◆ Kodi phwando la ukwatilo likuchitikira kuti?

◆ Kodi ndi mphotho yaikulu yotani imene anamwali opusawo akuiphonya, ndipo kodi chimaliziro chawo nchiyani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena